Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  July 2014

“Yehova Amadziwa Anthu Ake”

“Yehova Amadziwa Anthu Ake”

“Ngati munthu akukonda Mulungu, ameneyo amadziwika kwa Mulungu.”—1 AKOR. 8:3.

1. Fotokozani nkhani ya m’Baibulo yosonyeza maganizo olakwika amene anthu ena a Mulungu anali nawo. (Onani chithunzi pamwambapa.)

TSIKU lina m’mawa, Aroni yemwe anali mkulu wa ansembe anaimirira pakhomo la chihema cha Yehova atatenga chofukizira. Kora ndi amuna ena 250 anatenganso zofukizira zawo kuti akapereke zofukiza kwa Yehova. (Num. 16:16-18) Kwa ena, anthu onsewa akanaoneka ngati atumiki a Yehova okhulupirika. Koma mosiyana ndi Aroni, anthu enawo anali odzikuza ndipo ankafuna kulanda udindo wa ansembe. (Num. 16:1-11) Iwo ankaganiza kuti Mulungu angavomereze kulambira kwawo. Koma kuganiza zimenezi kunali kunyoza Yehova amene amaona zimene zili mumtima n’kudziwa ngati munthu ndi wachinyengo.—Yer. 17:10.

2. (a) Kodi Mose ananeneratu za chiyani? (b) Kodi mawu a Mose anakwaniritsidwa bwanji?

2 Dzulo lake, Mose anali ataneneratu kuti: “Mawa m’mawa, Yehova aonetsa amene ali wake.” (Num. 16:5) Yehova anasiyanitsadi pakati pa atumiki ake okhulupirika ndi achinyengo. Pa nthawiyi “panabuka moto wochokera kwa Yehova, umene unapsereza [Kora ndi] amuna 250 omwe anali kupereka nsembe zofukiza aja.” (Num. 16:35; 26:10) Popeza Aroni sanafe, Yehova anasonyeza kuti  iye anali wansembe ndiponso mtumiki wake weniweni.—Werengani 1 Akorinto 8:3.

3. (a) Kodi n’chiyani chinachitika m’nthawi ya mtumwi Paulo? (b) Kodi Paulo anadziwa bwanji kuti Yehova sangalekerere anthu ampatuko?

3 Nkhani yofanana ndi imeneyi inadzachitikanso patapita zaka 1,500 m’nthawi ya mtumwi Paulo. Anthu ena mumpingo anayamba kukhulupirira zinthu zonama n’kumasonkhanabe ndi mpingo. Kwa ena, mwina anthuwo sankaoneka osiyana ndi Akhristu ena mumpingo. Koma ampatukowo akanasokoneza Akhristu okhulupirika. Iwo anali ngati mimbulu yovala zikopa za nkhosa ndipo anayamba ‘kuwononga chikhulupiriro cha ena.’ (2 Tim. 2:16-18) Koma Yehova sangapusitsidwe. Paulo anadziwa zimenezi chifukwa cha zimene Mulungu anachitira Kora ndi anzake zaka zambiri m’mbuyomo. Tsopano tiyeni tione malemba ena ochititsa chidwi n’kuona zimene tingaphunzire pa nkhaniyi.

“INE NDINE YEHOVA, SINDINASINTHE”

4. (a) Kodi Paulo sankakayikira za chiyani? (b) Nanga anasonyeza bwanji zimenezi m’kalata yake yopita kwa Timoteyo?

4 Paulo sankakayikira zoti Yehova amadziwa anthu amene akumulambira mwachinyengo komanso anthu amene amamumvera ndi mtima wonse. Mawu amene anauziridwa kulemba m’kalata yake yopita kwa Timoteyo amasonyeza zimenezi. Atafotokoza mmene ampatuko ankasokonezera anthu ena mumpingo, Paulo analemba kuti: “Komabe, maziko olimba a Mulungu adakali chikhalire, ndipo ali ndi chidindo cha mawu akuti: ‘Yehova amadziwa anthu ake,’ ndiponso akuti: ‘Aliyense wotchula dzina la Yehova aleke kuchita zosalungama.’”—2 Tim. 2:18, 19.

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani Paulo anagwiritsa ntchito mawu oti “maziko olimba a Mulungu”? (b) Kodi mawu amenewa ayenera kuti anathandiza bwanji Timoteyo?

5 N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu amene Paulo anagwiritsa ntchito ndi ochititsa chidwi? Mawu akuti “maziko olimba a Mulungu” amapezeka pa lemba lokhali m’Baibulo lonse. M’Baibulo, mawu akuti “maziko” amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsira ponena zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, amagwiritsidwa ntchito ponena za mzinda wa Yerusalemu womwe unali likulu la Isiraeli. (Sal. 87:1, 2) Udindo umene Yesu ali nawo pokwaniritsa cholinga cha Yehova umayerekezeredwanso ndi maziko. (1 Akor. 3:11; 1 Pet. 2:6) Ndiyeno n’chifukwa chiyani Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti “maziko olimba a Mulungu”?

6 Mu vesi limene ananena za “maziko olimba a Mulungu,” Paulo anagwiranso mawu amene Mose anauza Kora ndi anzake opezeka pa Numeri 16:5. Iye anagwiritsa ntchito zimene zinachitika m’nthawi ya Mose pofuna kulimbikitsa Timoteyo komanso kumutsimikizira kuti Yehova amadziwa ngati anthu ayamba mpatuko ndipo sawalekerera. Yehova sanalole kuti Kora asokoneze cholinga chake ndipo sakanalolanso kuti ampatuko amene anali mumpingo wachikhristu achite zimenezi. Paulo sanafotokoze kwenikweni tanthauzo la “maziko olimba a Mulungu.” Koma mawu amene anagwiritsa ntchitowa ayenera kuti anathandiza Timoteyo kukhulupirira kwambiri njira za Yehova.

7. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti Yehova adzachita zinthu mwachilungamo komanso mokhulupirika?

7 Mfundo za Yehova n’zapamwamba ndipo sizisintha. Lemba la Salimo 33:11 limati: “Zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale. Maganizo a mumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.” Malemba ena amanena kuti ulamuliro wake, kukoma mtima kwake, chilungamo chake ndiponso kukhulupirika kwake sizidzatha. (Eks. 15:18; Sal. 106:1; 112:9; 117:2) Lemba la Malaki 3:6 limati: “Ine ndine  Yehova, sindinasinthe.” Pa Yakobo 1:17 timawerenganso kuti Yehova “sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.”

“CHIDINDO” CHOTITHANDIZA KUKHULUPIRIRA YEHOVA

8, 9. Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo za pa “chidindo” chimene Paulo anatchula?

8 Mawu ophiphiritsa a Paulo pa 2 Timoteyo 2:19 akunena za maziko okhala ndi chidindo. Kale, anthu ankakonda kudinda chidindo pa maziko a nyumba. Chidindocho chinkasonyeza dzina la munthu amene anamanga kapena mwiniwake wa nyumbayo. Paulo anali woyamba kugwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa amenewa m’Baibulo. * Chidindo cha pa “maziko olimba a Mulungu” chimanena mfundo ziwiri. Yoyamba ndi yakuti: “Yehova amadziwa anthu ake.” Yachiwiri ndi yakuti: “Aliyense wotchula dzina la Yehova aleke kuchita zosalungama.” Mfundozi zimatikumbutsa zomwe zili pa Numeri 16:5.—Werengani.

9 Kodi mfundo za pa “chidindo” chimene Paulo anatchula zikutiphunzitsa chiyani? Zikusonyeza kuti mfundo zonse za Yehova zagona pa mfundo zazikulu ziwiri, zomwe ndi: (1) Yehova amakonda anthu amene ndi okhulupirika kwa iye, ndiponso (2) Yehova amadana ndi zosalungama. Kodi mfundozi zikukhudza bwanji nkhani ya mpatuko mumpingo?

10. Kodi Akhristu okhulupirika m’nthawi ya Paulo ankakhudzidwa bwanji ndi zochita za ampatuko?

10 Timoteyo ndi anthu ena okhulupirika ayenera kuti sankasangalala ndi zimene ampatuko ankachita. Mwina Akhristu ena sankamvetsa chifukwa chake anthuwo ankaloledwa kukhalabe mumpingo. N’kutheka kuti Akhristu okhulupirika ankadzifunsa ngati Yehova amasiyanitsadi pakati pa anthu okhulupirika ndi ampatuko.—Mac. 20:29, 30.

Timoteyo sakanasokonezedwa ndi anthu ampatuko (Onani ndime 10 mpaka 12)

11, 12. Kodi kalata ya Paulo iyenera kuti inalimbikitsa bwanji Timoteyo?

11 Mosakayikira, kalata ya Paulo inalimbikitsa Timoteyo pomukumbutsa zimene zinachitika m’nthawi ya Aroni ndi Kora. Yehova anasonyeza kuti Aroni anali mtumiki wake wokhulupirika koma anakana Kora ndi anzake ndipo anawawononga. Choncho Paulo anasonyeza kuti ngakhale kuti mumpingo munali Akhristu achinyengo, Yehova ankadziwa anthu ake enieni ngati mmene anachitira m’nthawi ya Mose.

12 Yehova sasintha ndipo ndi wodalirika. Iye  amadana ndi zosalungama ndipo salekerera anthu ochimwa amene salapa. Timoteyo anali munthu “wotchula dzina la Yehova” ndipo kalatayi inamukumbutsa kuti sayenera kutsatira Akhristu achinyengo. *

YEHOVA SADZAIWALA TIKAMAMULAMBIRA NDI MTIMA WONSE

13. Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?

13 Ifenso tikhoza kulimbikitsidwa ndi mawu a Paulo amenewa. Choyamba, n’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amaona kukhulupirika kwathu. Sikuti amangoona chabe koma amaganiziranso kwambiri anthu ake enieni. Paja Baibulo limati: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Choncho tisamakayikire kuti zimene timachita pomutumikira kuchokera “mumtima woyera” sizidzapita pachabe.—1 Tim. 1:5; 1 Akor. 15:58.

14. Kodi Yehova salekerera anthu otani?

14 Koma mfundo yakuti Yehova salekerera anthu amene amamulambira mwachinyengo ndi yofunika kuiganiziranso. Pamene “maso ake akuyendayenda padziko lonse lapansi” angathenso kuona anthu amene mtima wawo si wathunthu kwa iye. Lemba la Miyambo 3:32 limanenanso kuti: “Munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye.” Munthu wotereyu amachita machimo mobisa n’kumadzionetsa ngati wolungama. N’zoona kuti munthu wachiphamaso akhoza kupusitsa anthu ena. Koma Yehova yemwe ndi wamphamvu ndiponso wolungama amatitsimikizira kuti “wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino.”—Miy. 28:13; werengani 1 Timoteyo 5:24; Aheberi 4:13.

15. Kodi tiyenera kupewa kuchita chiyani? Perekani chifukwa.

15 Abale ndi alongo ambiri amatumikira Yehova ndi mtima wonse. Ndiye zingakhale zachilendo kwambiri ngati wina mumpingo angayambe dala kulambira Mulungu mwachinyengo. Koma ngati zinachitika m’nthawi ya Mose ndiponso nthawi ya atumwi, zikhoza kuchitikanso masiku ano. (2 Tim. 3:1, 5) Kodi pamenepa tikutanthauza kuti tizikayikira Akhristu anzathu n’kumawaona ngati sakutumikira Yehova ndi mtima wonse? Ayi, si zimenezo. Kungakhale kulakwa kwambiri kukayikira abale ndi alongo athu popanda zifukwa zomveka. (Werengani Aroma 14:10-12; 1 Akorinto 13:7.) Tisaiwalenso kuti mtima wokayikira abale athu ukhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova.

16. (a) Kodi tonsefe tiyenera kuchita chiyani kuti tisayambe mtima wachinyengo? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa bokosi lakuti “ Pitirizani Kudziyesa”?

16 Mkhristu aliyense ayenera kuganizira bwinobwino zimene amachita. (Agal. 6:4) Popeza ndife ochimwa, n’zosavuta kuyamba kamtima kachinyengo. (Aheb. 3:12, 13) Choncho tiyenera kudzifufuza nthawi ndi nthawi kuti tione ngati zolinga zathu potumikira Mulungu zili zabwino. Mwina tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimatumikira Yehova chifukwa chomukonda komanso kudziwa kuti iye ndi woyenera kulamulira? Kapena kodi ndimangomutumikira n’cholinga choti ndikasangalale m’Paradaiso basi?’ (Chiv. 4:11) Tiyeni tonse tizidzifufuza ndipo tikapeza kuti tayamba kamtima kachinyengo, ngakhale pang’ono pokha, tisinthe nthawi yomweyo.

ANTHU OKHULUPIRIKA AMAKHALA OSANGALALA

17, 18. N’chifukwa chiyani tiyenera kulambira Yehova ndi mtima wonse?

17 Tikamayesetsa kulambira Yehova ndi mtima wonse timapeza madalitso ambiri. Wamasalimo  ananena kuti: “Wodala ndi munthu amene Yehova sanamusungire cholakwa chake, amene alibe mtima wachinyengo.” (Sal. 32:2) Anthu amene amachotseratu mtima umenewu amakhala osangalala panopa komanso akhoza kudzasangalala kwambiri m’tsogolo.

18 Pa nthawi yake, Yehova adzachititsa kuti anthu achinyengo aonekere. Choncho padzakhala “kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.” (Mal. 3:18) Koma panopa tingalimbikitsidwe podziwa kuti “maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo.”—1 Pet. 3:12.

^ ndime 8 Lemba la Chivumbulutso 21:14, lomwe linalembedwa zaka zambiri Paulo atalemba makalata ake opita kwa Timoteyo, limanena za “miyala yomangira maziko yokwana 12” yokhala ndi mayina 12 a atumwi.

^ ndime 12 Nkhani yotsatira ikusonyeza zimene tingachite kuti titsanzire Yehova pa nkhani yodana ndi zosalungama.