Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Inu Ndinu Mboni Zanga”

“Inu Ndinu Mboni Zanga”

“‘Inu ndinu mboni zanga,’ akutero Yehova.”—YES. 43:10.

1, 2. (a) Kodi mawu akuti mboni amatanthauza chiyani, nanga ofalitsa nkhani alephera bwanji kukhala mboni? (b) N’chifukwa chiyani Yehova sadalira ofalitsa nkhani a m’dzikoli?

KODI mawu akuti mboni amatanthauza chiyani? Buku lina lotanthauzira mawu limati mboni “ndi munthu amene amaona zinthu zinazake n’kufotokoza mmene zinachitikira.” Mwachitsanzo, mumzinda wina ku South Africa, mumalembedwa nyuzipepala yomwe dzina lake limatanthauza mboni. (The Witness) Nyuzipepalayi yakhala ikutuluka kwa zaka zoposa 160. Dzinali ndi loyenera chifukwa chakuti cholinga cha manyuzipepala n’kufotokoza molondola nkhani zimene zachitika padzikoli. Mkonzi woyamba wa nyuzipepalayi ananena kuti aziyesetsa kulemba “zoona zokhazokha popanda kuwonjezera kapena kuchotserapo.”

2 Koma ofalitsa nkhani akhala akunyalanyaza kapena kupotoza nkhani zikuluzikulu zimene zachitika padzikoli. Mwachitsanzo, sakuthandiza anthu kuti adziwe zimene Mulungu anauza Ezekieli kalelo. Anamuuza kuti: ‘Mitundu ya anthu idzadziwa kuti ine ndine Yehova.’ (Ezek. 39:7) Koma Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse sadalira ofalitsa nkhaniwo kuti adziwitse anthu zokhudza iyeyo. Tikutero chifukwa chakuti padzikoli pali a Mboni za Yehova pafupifupi 8 miliyoni amene amauza anthu a mitundu yonse za Yehovayo komanso zimene iye wachita m’mbuyomu ndi zimene akuchita panopa. Iwo amalengezanso za madalitso amene Mulungu  adzapereke kwa anthu m’tsogolo. Tikamagwira ntchito imeneyi mwakhama ndiye kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi dzina limene Mulungu anatipatsa. Paja lemba la Yesaya 43:10 limati: “‘Inu ndinu mboni zanga,’ akutero Yehova. ‘Ndinu mtumiki wanga amene ndakusankhani.’”

3, 4. (a) Kodi ndi liti pamene Ophunzira Baibulo anayamba kudziwika ndi dzina latsopano, nanga anamva bwanji? (Onani chithunzi patsamba 23.) (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Yehova ndi “Mfumu ya muyaya” choncho kudziwika ndi dzina lake ndi mwayi waukulu kwambiri. Ponena za dzina lake, iye anati: “Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale, ndipo ndicho chondikumbukirira ku mibadwomibadwo.” (1 Tim. 1:17; Eks. 3:15; yerekezerani ndi Mlaliki 2:16.) Mu 1931, Ophunzira Baibulo anayamba kudziwika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova. Izi zitachitika anthu ambiri analemba makalata oyamikira omwe ankaikidwa m’magazini ya Nsanja ya Olonda. Mpingo wina wa ku Canada unalemba kuti: “Nkhani yoti tizidziwika ndi dzina lakuti ‘Mboni za Yehova’ yatisangalatsa kwabasi. Tiyesetsa kwambiri kuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu latsopanoli.”

4 Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira mwayi wodziwika ndi dzina la Mulungu? Kodi mungafotokoze malemba osonyeza pamene dzina lakuti Mboni za Yehova linachokera? Tikambirana mafunso amenewa m’nkhaniyi.

MBONI ZA MULUNGU ZAKALE

5, 6. (a) Kodi makolo a ku Isiraeli ankayenera kuchitira umboni m’njira ziti? (b) Kodi makolowo anauzidwanso kuchita chiyani? (c) N’chifukwa chiyani masiku anonso makolo ayenera kuchita zimenezi?

5 Mwisiraeli aliyense m’nthawi ya Yesaya anali “mboni” ya Yehova ndipo mtundu wonse wa Isiraeli unali “mtumiki” wa Mulungu. (Yes. 43:10) Makolo mu Isiraeli ankafotokozera ana awo zimene Mulungu anachitira makolo awo akale. Imeneyi inali njira imodzi yochitira  umboni. Pamene Aisiraeli ankalandira malangizo okhudza kuchita Pasika chaka ndi chaka, anauzidwa kuti: “Ana anu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’ pamenepo mudzawauze kuti, ‘Umenewu ndi mwambo wopereka nsembe ya pasika kwa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Isiraeli mu Iguputo pamene anali kupha Aiguputo ndi mliri, koma anapulumutsa mabanja athu.’” (Eks. 12:26, 27) N’kutheka kuti makolowo anauza ana awo zimene zinachitika Mose atafika kwa Farao kukapempha zoti Aisiraeli akalambire Yehova m’chipululu. Farao anayankha kuti: “Yehova ndani kuti ndimvere mawu ake, ndi kulola Aisiraeli kuti apite?” (Eks. 5:2) Tikhoza kunena kuti funsoli linayankhidwa bwinobwino pambuyo pa miliri 10 komanso Aisiraeli atapulumutsidwa pa Nyanja Yofiira. Yehova anasonyeza kuti anali Wamphamvuyonse ndipo ndi mmene alili mpaka pano. Aisiraeli anakhalanso mboni za mfundo yakuti Yehova ndi Mulungu woona ndipo amakwaniritsa malonjezo ake.

6 Aisiraeli amene ankayamikira mwayi wawo wodziwika ndi dzina la Yehova ayenera kuti ankauza ana awo ndiponso akapolo awo a mitundu ina zinthu zabwino zimene Yehova anawachitira. Mfundo inanso yofunika yomwe Aisiraeli anauzidwa kuti aziphunzitsa ana awo inali yakuti Mulungu amafuna kuti azikhala oyera. Yehova anati: “Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.” (Lev. 19:2; Deut. 6:6, 7) Nawonso Akhristu masiku ano ayenera kuphunzitsa ana awo kuti akhale ndi makhalidwe oyera n’cholinga choti azilemekeza dzina laulemerero la Mulungu.—Werengani Miyambo 1:8; Aefeso 6:4.

Tikamaphunzitsa ana athu za Yehova timalemekeza dzina lake (Onani ndime  5, 6)

7. (a) Kodi Aisiraeli akakhala okhulupirika, mitundu ina inkachita chiyani? (b) Kodi anthu onse amene amadziwika ndi dzina la Mulungu ali ndi udindo wotani?

7 Aisiraeli akakhala okhulupirika, ankalemekeza dzina la Mulungu. Iwo anauzidwa kuti: “Mitundu yonse ya anthu padziko lapansi adzaona kuti mukutchedwa ndi dzina la Yehova, ndipo adzachita nanu mantha.” (Deut. 28:10) Koma n’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri Aisiraeli sankakhala okhulupirika ndipo ankakonda kulambira mafano. Iwo anayamba kutengera zochita za milungu ya ku Kanani imene ankalambira. Anayamba kukhala ankhanza, kupereka ana awo nsembe komanso kupondereza osauka. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Nthawi zonse tiyenera kuyesetsa kutsanzira Mulungu wathu woyera yemwe timadziwika ndi dzina lake.

“TAONANI! NDIKUPANGA ZINTHU ZATSOPANO”

8. Kodi Yehova anauza Yesaya kuti agwire ntchito iti, nanga Yesaya anatani?

8 Kudzera mwa Yesaya, Yehova anachenjeza Aisiraeli kuti adzawononga Yerusalemu ndipo anthu ake adzatengedwa kupita ku ukapolo. Koma ananeneratu kuti adzachita zodabwitsa powapulumutsa ku ukapolowo. (Yes. 43:19) Machaputala 6 oyambirira a buku la Yesaya anachenjeza za tsoka limene linali kudzagwera Yerusalemu ndi mizinda ina yozungulira. Yehova, yemwe amadziwa mitima ya anthu, anauza Yesaya kuti apitirizebe kulalikira ngakhale kuti anthu sadzamumvera. Mfundo imeneyi inadabwitsa Yesaya moti anafuna kudziwa kuti zimenezi zichitika mpaka liti. Poyankha, Mulungu anamuuza kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu.”—Werengani Yesaya 6:8-11.

9. (a) Kodi ulosi wa Yesaya wonena za Yerusalemu unakwaniritsidwa liti? (b) Kodi masiku ano anthu akhala akuchenjezedwanso za chiyani?

9 Yesaya anapatsidwa ntchitoyi m’chaka chomaliza cha Mfumu Uziya, cha m’ma 778 B.C.E. Iye anagwira ntchito imeneyi kwa zaka zoposa 46 mpaka pambuyo pa chaka cha 732 B.C.E., mu ulamuliro wa Hezekiya. Apa n’kuti kutatsala zaka 125 kuti Yerusalemu awonongedwe mu 607 B.C.E. Choncho tinganene kuti anthu a  Mulungu anachenjezedwa mokwanira za zinthu zimene zinali kudzawachitikira. Masiku anonso, Yehova akugwiritsa ntchito atumiki ake kuti achenjeze anthu za tsoka limene likubwera. Panopa, magazini ya Nsanja ya Olonda yakhala ikuchenjeza anthu kwa zaka 135 kuti posachedwapa ulamuliro wa Satana udzathetsedwa ndipo udzalowedwa m’malo ndi Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu Khristu.—Chiv. 20:1-3, 6.

10, 11. Tchulani ulosi wa Yesaya umene Aisiraeli anaona ukukwaniritsidwa ku Babulo.

10 Ayuda ambiri amene anamvera n’kugonjera Ababulo anapulumuka pamene Yerusalemu ankawonongedwa ndipo anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. (Yer. 27:11, 12) Patapita zaka 70, anthu a Mulungu amene anali ku Babulo anaona Mulungu akukwaniritsa ulosi wakuti: “Yehova, Wokuwombolani, Woyera wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Chifukwa cha inu, ndidzawatumiza ku Babulo. Ndidzachititsa kuti zitsulo za ndende zimasuke.’”—Yes. 43:14.

11 Pokwaniritsa ulosiwu, panachitika zinthu zodabwitsa usiku wina chakumayambiriro kwa October mu 539 B.C.E. Pa nthawiyo, mfumu ya Babulo inkamwa vinyo ndi nduna zake pogwiritsa ntchito ziwiya zopatulika zimene zinatengedwa m’kachisi ku Yerusalemu ndipo ankatamanda mafano awo. Koma asilikali a Amedi ndi Aperisiya analowa n’kugonjetsa Babulo. Ndiyeno cha mu 538 kapena 537 B.C.E., Koresi, yemwe anagonjetsa Babulo, analamula kuti Ayuda abwerere ku Yerusalemu n’kukamanga kachisi wa Mulungu. Yesaya anali ataneneratu zonsezi komanso kupereka lonjezo lakuti Yehova adzateteza anthu ake olapawo pobwerera ku Yerusalemu. Mulungu ananena kuti iwo anali ‘anthu amene anawapanga kuti akhale ake ndi kunena za ulemerero wake.’ (Yes. 43:21; 44:26-28) Pamene anthuwa anabwerera n’kukamanga kachisi wa Yehova ku Yerusalemu, anachitira umboni wakuti Yehova ndi Mulungu woona ndipo amakwaniritsa malonjezo ake.

12, 13. (a) Kodi chinachitika n’chiyani pamene Aisiraeli anabwerera kwawo n’kuyambiranso kulambira Yehova? (b) Kodi a “nkhosa zina” ali ndi chiyembekezo chotani? (c) Kodi a “nkhosa zina” ayenera kuchita chiyani pamene akuthandiza “Isiraeli wa Mulungu”?

12 Anthu ambirimbiri a mitundu ina anakhala limodzi ndi Aisiraeli amene anabwerera kwawowa n’kuyamba kulambira Yehova. Patapita nthawi, anthu enanso a mitundu ina anayamba kulambira limodzi ndi Ayuda. (Ezara 2:58, 64, 65; Esitere 8:17) Masiku ano, “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” za Yesu, limathandiza Akhristu odzozedwa omwe amatchedwa “Isiraeli wa Mulungu.” (Chiv. 7:9, 10; Yoh. 10:16; Agal. 6:16) Odzozedwawa limodzi ndi a khamu lalikulu amadziwika ndi dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova.

 13 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, a khamu lalikulu adzakhala ndi mwayi waukulu wofotokozera anthu oukitsidwa zimene zinkachitika pochitira umboni m’masiku otsiriza a dziko loipali. Koma kuti izi zidzatheke, panopa tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu komanso kuyesetsa kuti tikhalebe oyera. Popeza ndife ochimwa, nthawi zina timalephera kukhalabe oyera ngakhale titayesetsa kwambiri. Choncho tiyenera kupempha Yehova tsiku ndi tsiku kuti azitikhululukira komanso sitiyenera kuiwala kuti kudziwika ndi dzina la Mulungu ndi mwayi waukulu kwambiri.—Werengani 1 Yohane 1:8, 9.

TANTHAUZO LA DZINA LA MULUNGU

14. Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza chiyani?

14 Kuganizira kwambiri tanthauzo la dzina la Mulungu kungatithandize kuti tiziyamikira kwambiri mwayi wodziwika ndi dzinalo. Dzina lakuti Yehova linachokera ku mawu achiheberi amene amatanthauza “kukhala.” Choncho dzinali limatanthauza kuti “Iye Amachititsa Kukhala.” Dzina limeneli ndi lomuyeneradi chifukwa chakuti iye ndi amene analenga kumwamba, dziko lapansi, anthu ndiponso angelo. Iye amakwaniritsanso cholinga chake. Amapitirizabe kuchita zimenezi ngakhale ena, monga Satana, atayesa kuchisokoneza.

15. Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu kuti adziwe bwino tanthauzo la dzina lake? (Onani bokosi lakuti ““ Dzina Lokhala ndi Tanthauzo Lofunika Kwambiri.”)

15 Pamene ankauza Mose kuti apite kukatulutsa anthu ake ku Iguputo, Yehova anamuthandiza kudziwa bwino tanthauzo la dzina lake. Baibulo limati: “Mulungu anamuyankha Mose kuti: ‘NDIDZAKHALA AMENE NDIDZAFUNE KUKHALA.’ Ndiyeno anawonjezera kuti: ‘Ana a Isiraeli ukawauze kuti, “NDIDZAKHALA AMENE NDIDZAFUNE KUKHALA ndiye wandituma kwa inu.”’” (Eks. 3:14) Izi zikutanthauza kuti pa nthawi ina iliyonse, Yehova akhoza kukhala wina aliyense amene angafune kuti akwaniritse cholinga chake. Pamene Aisiraeli anali ku ukapolo, Yehova anawapulumutsa, kuwateteza, kuwatsogolera, kuwasamalira komanso kuwathandiza kuti akhale naye pa ubwenzi wabwino.

TIZISONYEZA KUTI TIMAYAMIKIRA MWAYI WATHU

16, 17. (a) Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira mwayi wodziwika ndi dzina la Mulungu? (b) Kodi tidzakambirana funso liti m’nkhani yotsatira?

16 Masiku anonso, Yehova akuchitabe zinthu mogwirizana ndi dzina lake potisamalira ndiponso kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino. Komatu pali zinanso zimene tingaphunzire pa tanthauzo la dzina la Mulungu. Dzinali limasonyezanso kuti iye angagwiritse ntchito zinthu zimene analenga kuti akwaniritse cholinga chake. Mwachitsanzo, iye amachita zimenezi pogwiritsa ntchito Mboni zake. Kuganizira mfundo imeneyi kungatilimbikitse kuchitabe zinthu zimene zingalemekeze dzina lake. M’bale wina wa ku Norway wazaka 84 dzina lake Kåre watumikira Yehova mwakhama kwa zaka 70. Iye anati: “Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri kutumikira Yehova yemwe ndi Mfumu yamuyaya komanso kukhala m’gulu la anthu odziwika ndi dzina lake loyera. Ndimamva bwino kwambiri ndikamafotokozera anthu ena mfundo za m’Baibulo n’kuona kuti iwo akumvetsa ndiponso kusangalala kwambiri ndi mfundozo. Mwachitsanzo, ndimasangalala kwambiri ndikamaphunzitsa anthu za nsembe ya dipo ya Khristu ndiponso kuti nsembeyo ingawathandize kudzapeza moyo wosatha m’dziko latsopano lamtendere.”

17 Kumadera ena kumakhala kovuta kuti tipeze anthu ofuna kuphunzira za Mulungu. Koma mofanana ndi Kåre, timasangalala kwambiri tikapeza munthu amene tingamuphunzitse tanthauzo la dzina la Yehova. Koma kodi tingakhale bwanji Mboni za Yehova komanso mboni za Yesu? Tidzakambirana funsoli m’nkhani yotsatira.