Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Uzikonda Mnzako Mmene Umadzikondera Wekha”

“Uzikonda Mnzako Mmene Umadzikondera Wekha”

“[Lamulo] lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”—MAT. 22:39.

1, 2. (a) Ponena za malamulo akuluakulu m’Chilamulo, kodi Yesu anati lachiwiri ndi liti? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

MFARISI wina ankafuna kuyesa Yesu ndipo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?” Monga tinaonera m’nkhani yapitayi, Yesu anamuyankha kuti “lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba” ndi lakuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” Yesu ananenanso kuti: “Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”—Mat. 22:34-39.

2 Yesu ananena kuti tiyenera kukonda anzathu mmene timadzikondera tokha. Choncho tiyenera kudzifunsa kuti: Kodi mnzathu ndi ndani kwenikweni? Nanga tingasonyeze bwanji kuti timakonda anzathu?

KODI MNZATHU NDI NDANI KWENIKWENI?

3, 4. (a) Kodi Yesu anapereka fanizo liti atafunsidwa kuti: ‘Kodi mnzanga ndi ndani kwenikweni’? (b) Kodi Msamariya uja anathandiza bwanji munthu amene anafwambidwa? (Onani chithunzi pamwambapa.)

3 Anthu ambiri amaganiza kuti mnzawo ndi munthu amene amagwirizana  naye komanso amene amawathandiza. (Miy. 27:10) Munthu wina wofuna kudzionetsa kuti ndi wolungama anafunsa Yesu kuti: ‘Kodi mnzanga ndi ndani kwenikweni?’ Poyankha, Yesu anamuuza fanizo la Msamariya wachifundo. (Werengani Luka 10:29-37.) Mu fanizoli, anthu angayembekezere kumva kuti wansembe komanso Mlevi anathandiza munthu amene anakumana ndi achifwamba amene anamumenya n’kumusiya ali pafupi kufa. Koma iwo anangolambalala osamuthandiza. M’malomwake, munthuyo anathandizidwa ndi Msamariya. Asamariya ankalemekeza Chilamulo cha Mose koma Ayuda ankadana nawo.—Yoh. 4:9.

4 Pothandiza munthuyo, Msamariyayu anamuthira mafuta ndi vinyo m’mabala ake. Ndiyeno anapita naye kunyumba ya alendo n’kupereka madinari awiri kwa mwini nyumbayo kuti asamalire munthuyo. Ndalama zimenezi n’zimene munthu ankalandira akagwira ntchito masiku awiri. (Mat. 20:2) Fanizoli limasonyezeratu amene anali mnzake wa munthuyu. Fanizo la Yesuli likusonyeza kuti tiyenera kukonda anzathu komanso kuwachitira chifundo.

Atumiki a Yehova amakonda anzawo n’kuwathandiza mwamsanga (Onani ndime 5)

5. Kodi atumiki a Yehova anasonyeza bwanji kuti amakonda anzawo kutachitika tsoka lachilengedwe?

5 Kunena zoona, si ambiri amene angachite zimene Msamariyayu anachita. ‘M’masiku otsiriza’ ano, anthu oterewa akusowa kwambiri chifukwa chakuti anthu ambiri sakonda ngakhale achibale awo, ndi oopsa ndiponso sakonda zabwino. (2 Tim. 3:1-3) Mwachitsanzo, anthu amavutika kwambiri kukachitika masoka achilengedwe. Izi n’zimene zinachitika mphepo yamkuntho itawononga zinthu mumzinda wa New York mu October 2012. Kudera lina mumzindawu kumene zinthu zambiri zinawonongeka, ena anaba zinthu za anthu amene ankavutika chifukwa chosakhala ndi magetsi ndi zinthu zina zofunika. Koma kudera lomwelo, a Mboni za Yehova anakonza zothandiza abale ndi alongo awo komanso anthu ena. Akhristu amachita zimenezi chifukwa chokonda anzawo. Koma kodi ndi zinthu zina ziti zimene tingachite posonyeza kuti timakonda anzathu?

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI TIMAKONDA ANZATHU?

6. Kodi ntchito yathu yolalikira imasonyeza bwanji kuti timakonda anzathu?

6 Tizithandiza anthu ndi Mawu a Mulungu. Tingachite zimenezi powasonyeza malemba olimbikitsa. (Aroma 15:4) Tikamalalikira n’kumauza anthu mfundo zoona za m’Baibulo timasonyeza kuti timawakonda. (Mat. 24:14) Ndi mwayi waukulu kwambiri kulalikira uthenga wa Ufumu wochokera kwa “Mulungu amene amapereka chiyembekezo.”—Aroma 15:13.

7. Kodi Yesu anapereka malangizo ati ndipo timadalitsidwa bwanji tikamawatsatira?

7 Tizichitira anthu zimene tingafune kuti azitichitira. Pa ulaliki wa paphiri, Yesu ananena kuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo, pakuti n’zimene Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zimafuna.” (Mat. 7:12) Tikamatsatira malangizo a Yesu amenewa, timatsatiranso mfundo yaikulu ya mu “Chilamulo” (chomwe ndi Genesis mpaka Deuteronomo) ndiponso “Zolemba za aneneri” (zomwe ndi mabuku a aneneri a m’Malemba Achiheberi). Mabukuwa amasonyeza kuti Mulungu amadalitsa anthu amene amakonda anzawo. Mwachitsanzo, kudzera mwa Yesaya, Yehova anati: “Tsatirani chilungamo ndipo chitani zolungama . . . Wodala ndi munthu amene amachita zimenezi.” (Yes. 56:1, 2) Choncho tikamachita zinthu mwachikondi ndiponso mwachilungamo kwa anzathu timadalitsidwa.

8. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda adani athu? (b) N’chiyani chingachitike tikawasonyeza chikondi?

8 Tizikonda adani athu. Yesu anati: “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnzako ndi kudana  ndi mdani wako.’ Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani, kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.” (Mat. 5:43-45) Mtumwi Paulo ananenanso kuti: “Ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse chakumwa.” (Aroma 12:20; Miy. 25:21) Chilamulo cha Mose chinkanena kuti munthu ayenera kuthandiza mdani wake kumasula chiweto chake ngati chagona chifukwa cholemedwa ndi katundu. (Eks. 23:5) Anthu odanawo akachita limodzi zinthu ngati zimenezi, akhoza kuyamba kugwirizana. Popeza kuti Akhristufe timakonda aliyense, adani athu ambiri asiya kudana nafe. Tidzasangalala kwambiri ngati adani athu ena, ngakhale amene ankatizunza koopsa, atayamba kutumikira Yehova chifukwa chakuti tinawasonyeza chikondi.

9. Kodi Yesu ananena chiyani pa nkhani yokhala pa mtendere ndi abale athu?

9 “Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse.” (Aheb. 12:14) Tiyenera kuchitanso zimenezi ndi abale athu. Paja Yesu anati: “Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.” (Mat. 5:23, 24) Mulungu adzatidalitsa tikamachita zinthu mwachikondi ndi abale athu komanso tikamayesetsa kukhala nawo pa mtendere tikasemphana maganizo.

10. N’chifukwa chiyani sitiyenera kupezera anzathu zifukwa?

10 Tisamapezere anzathu zifukwa. Yesu anati: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe, pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho. Ndipo muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo. Nanga n’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaganizira mtanda wa denga la nyumba umene uli m’diso lako? Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Taima ndikuchotse kachitsotso m’diso lako,’ pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa denga la nyumba? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatero udzatha kuona bwino mmene ungachotsere kachitsotso m’diso la m’bale wako.” (Mat. 7:1-5) Yesu anapereka  fanizo lamphamvuli pofuna kusonyeza kuti sitiyenera kudzudzula ena pa tizifukwa ting’onoting’ono pomwe ifeyo tili ndi mavuto akuluakulu.

NJIRA YAPADERA YOSONYEZERA KUTI TIMAKONDA ANZATHU

11, 12. Tchulani njira yapadera imene tingasonyezere kuti timakonda anzathu.

11 Pali njira yapadera imene tingasonyezere kuti timakonda anzathu. Tiyenera kutsanzira Yesu polalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Luka 8:1) Yesu anauza otsatira ake kuti ‘azikaphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mat. 28:19, 20) Tikamachita zimenezi, timathandiza anthu kuchoka pamsewu waukulu ndi wotakasuka wopita ku chiwonongeko n’kuyamba kuyenda pamsewu wopanikiza wopita ku moyo. (Mat. 7:13, 14) Sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatidalitsa tikamachita zimenezi.

12 Mofanana ndi Yesu, timathandiza anthu kuzindikira zosowa zawo zauzimu. (Mat. 5:3) Anthu akavomera kuti tikambirane nawo, timawathandiza kupeza zosowazo powauza “uthenga wabwino wa Mulungu.” (Aroma 1:1) Anthu amene amatsatira uthenga wa Ufumuwu amagwirizananso ndi Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu. (2 Akor. 5:18, 19) Choncho tikamalalikira uthenga wabwino, timasonyeza m’njira yofunika kwambiri kuti timakonda anzathu.

13. Kodi inuyo mumaiona bwanji ntchito yolalikira za Ufumu wa Mulungu?

13 Tikamachita maulendo obwereza komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo, timasangalala chifukwa chothandiza anthu kuti ayambe kutsatira mfundo zolungama za Mulungu. Anthu ena amene timaphunzira nawo amasintha kwambiri moyo wawo. (1 Akor. 6:9-11) Zimakhala zosangalatsa kuona Mulungu akuthandiza anthu oyenera moyo wosatha kuti asinthe n’kukhala naye pa ubwenzi wabwino. (Mac. 13:48) Ena amene ankangokhalira kukhumudwa amayamba kusangalala, pomwe ena amene ankada nkhawa kwambiri amayamba kudalira Atate wathu wakumwamba. Anthu atsopano akamasintha zimatisangalatsa kwambiri. Ndi mwayi waukulu kugwira ntchito yolalikira za Ufumu wa Mulungu chifukwa timasonyeza kuti timakondadi anthu.

ZIMENE MALEMBA AMANENA PA NKHANI YA CHIKONDI

14. Fotokozani zinthu zina zokhudza chikondi zimene zili pa 1 Akorinto 13:4-8.

14 Kutsatira zimene Paulo analemba pochita zinthu ndi anzathu kumathandiza kuti tipewe mavuto ambiri, tikhale osangalala komanso tidalitsidwe ndi Mulungu. (Werengani 1 Akorinto 13:4-8.) Tiyeni tione zimene Paulo ananena ndipo tione mmene tingatsatirire mawuwa pochita zinthu ndi anzathu.

15. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima komanso okoma mtima? (b) Kodi tiyenera kupewa nsanje komanso kudzitama pa zifukwa ziti?

15 “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.” Mulungu watilezera mtima komanso kutikomera mtima kwambiri anthu ochimwafe. Choncho ifenso tiyenera kulezera mtima ndiponso kukomera mtima anzathu pamene alakwitsa zinthu, kuchita zinthu mosatiganizira kapena kutichitira chipongwe. ‘Chikondi sichichitanso nsanje.’ Tikamakonda anthu sitingasirire mwansanje zinthu zawo kapena udindo wawo mumpingo. Komanso sitingadzitame kapena kudzikuza. Pajatu Baibulo limanena kuti: “Maso odzikweza ndi mtima wodzikuza ndizo nyale ya anthu oipa, ndipo zimenezi ndi tchimo.”—Miy. 21:4.

16, 17. Kodi tingatsatire bwanji lemba la 1 Akorinto 13:5, 6?

16 Tikakhala ndi chikondi sitingachite zinthu zosayenera kwa anzathu. Sitingawanamize, kuwabera kapena kuwachitira chilichonse chosemphana ndi malamulo ndiponso mfundo za Yehova. Tikamakonda anthu sitidzachita zinthu mongoganizira zofuna zathu zokha koma tidzaganiziranso zofuna zawo.—Afil. 2:4.

 17 Tikakhala ndi chikondi chenicheni sitikwiya msanga. Anthu ena akatilakwira ‘sitisunganso zifukwa’ ngati kuti tikusunga m’buku langongole. (1 Ates. 5:15) Mulungu sasangalala tikamasungira ena zifukwa. Kuchita zimenezi kuli ngati kusonkhezera moto umene ukhoza kuyaka nthawi iliyonse n’kutiwotcha ifeyo komanso anthu ena. (Lev. 19:18) Tikakhala ndi chikondi timakondwera ndi choonadi komanso ‘sitikondwera ndi zosalungama.’ Choncho ngakhale pamene zinthu zosalungama zachitikira munthu amene amadana nafe, sitisangalala.—Werengani Miyambo 24:17, 18.

18. Kodi lemba la 1 Akorinto 13:7, 8 limatiphunzitsa chiyani pa nkhani ya chikondi?

18 Paulo ananenanso kuti: “Chikondi chimakwirira zinthu zonse.” Munthu akatilakwira kenako n’kupempha kuti timukhululukire, timamukhululukiradi ngati tili ndi chikondi. Komanso tikakhala ndi chikondi ‘timakhulupirira zinthu zonse’ zopezeka m’Mawu a Mulungu ndipo timayamikira kwambiri zimene gulu limatipatsa potithandiza kuphunzira Baibulo. Chikondi chimatithandiza ‘kuyembekezera zinthu zonse’ zolembedwa m’Baibulo. Choncho tikakhala ndi chikondi timafunitsitsa kuuza anthu ena za chiyembekezo chathu. (1 Pet. 3:15) Tikakumana ndi mavuto, timapemphera ndi kuyembekeza kuti zinthu zikhala bwino. Tikakhala ndi chikondi ‘timathanso kupirira zinthu zonse’ monga kulakwiridwa kapena kuzunzidwa. Paulo ananenanso kuti: “Chikondi sichitha.” Anthu okhulupirika adzapitiriza kuchisonyeza mpaka muyaya.

PITIRIZANI KUKONDA ANZANU MMENE MUMADZIKONDERA NOKHA

19, 20. Kodi ndi malangizo ati a m’Malemba amene angatithandize kuti tipitirize kukonda anzathu?

19 Tikamatsatira malangizo a m’Baibulo tidzapitiriza kusonyeza chikondi kwa anzathu. Mmene tikuti anzathu, sitikunena za anthu amtundu wathu wokha koma anthu onse. Tisaiwalenso kuti Yesu ananena kuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mat. 22:39) Yehova ndi Khristu amafuna kuti tizikonda anzathu. Koma ngati pa nthawi ina sitikudziwa zoti tichitire mnzathu, tiyenera kupempha Mulungu kuti atitsogolere ndi mzimu wake. Tikatero, Yehova adzatidalitsa ndipo adzatithandiza kuchita zinthu mwachikondi.—Aroma 8:26, 27.

20 Lamulo lakuti uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha limatchedwa “lamulo lachifumu.” (Yak. 2:8) Paulo atatchula malamulo ena m’Chilamulo cha Mose, ananena kuti: “Lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili m’mawu awa akuti, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ Chikondi sichilimbikitsa munthu kuchitira zoipa mnzake, chotero chilamulo chimakwaniritsidwa m’chikondi.” (Aroma 13:8-10) Choncho tiyeni tisasiye kukonda anzathu.

21, 22. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda Mulungu ndi anzathu?

21 Pamene tikuganizira zifukwa zotichititsa kukonda anzathu, sitiyenera kuiwala mfundo ya Yesu yakuti Atate wake “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:43-45) Choncho tiyenera kukonda anzathu kaya akhale olungama kapena osalungama. Paja takambirana kale kuti kuuza anthu uthenga wa Ufumu ndi njira ina imene tingasonyezere chikondi. Mnzathuyo akhoza kudalitsidwa kwambiri ngati atamvetsera uthenga wathu n’kuutsatira.

22 Anthufe tili ndi zifukwa zankhaninkhani zotichititsa kukonda Yehova mopanda malire. Palinso njira zambiri zosonyezera kuti timakonda anzathu. Tikamakonda Mulungu komanso anzathu timasonyeza kuti timalemekeza zimene Yesu ananena. Koma chofunika kwambiri n’chakuti kuchita zimenezi kumasangalatsa Atate wathu, Yehova.