Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) May 2014

Magaziniyi ikufotokoza njira zitatu zimene tingatsatire poyankha mafunso ovuta mu utumiki. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyendera limodzi ndi gulu la Mulungu?

‘Chakudya Changa N’kuchita Chifuniro cha Mulungu’

Mfumu Davide, mtumwi Paulo ndiponso Yesu Khristu ankafunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu. Kodi tingatani kuti tizilalikirabe mwakhama m’madera ovuta?

Kodi ‘Tingayankhe Bwanji Wina Aliyense’?

Kodi tingagwiritse ntchito bwanji Malemba poyankha mafunso ovuta? Onani njira zitatu zimene tingagwiritse ntchito poyankha anthu mogwira mtima.

Muzichitira Anthu Zimene Mungafune Kuti Akuchitireni

Kodi tizichita bwanji tikakumana ndi anthu mu utumiki? Kodi tingatsatire bwanji mawu a Yesu a pa Mateyu 7:12 polalikira?

MBIRI YA MOYO WANGA

Yehova Wandithandiza Kwambiri

Kenneth Little akufotokoza mmene Yehova Mulungu wamuthandizira kuti asiye kuchita manyazi komanso kudzikayikira. Werengani kuti muone mmene Mulungu wamudalitsira pa moyo wake.

Yehova Ndi Mulungu Wadongosolo

Kodi chitsanzo cha Aisiraeli ndiponso Akhristu oyambirira chimasonyeza bwanji kuti atumiki a Yehova ayenera kuchita zinthu mwadongosolo?

Kodi Mukuyenda Limodzi ndi Gulu la Yehova?

Posachedwapa dziko la Satanali lidzawonongedwa pa Aramagedo. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyenda limodzi ndi gulu la Mulungu?

KALE LATHU

“Ntchito Yokolola Idakalipo Yambiri”

Ku Brazil kuli a Mboni za Yehova oposa 760,000 amene amaphunzitsa mfundo zoona za m’Baibulo. Kodi ntchito yolalikira inayamba bwanji ku South America?