Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  March 2014

Kodi Tingatani Kuti Tikhalebe ndi Mtima Wodzipereka?

Kodi Tingatani Kuti Tikhalebe ndi Mtima Wodzipereka?

“Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha.”—MAT. 16:24.

1. Kodi Yesu anapereka bwanji chitsanzo chabwino pa nkhani ya kudzipereka?

PAMENE Yesu anali padziko lapansi anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kudzipereka. Iye ankaika zofuna za Mulungu patsogolo osati zake. (Yoh. 5:30) Yesu anakhalabe wokhulupirika mpaka analolera kuphedwa pamtengo wozunzikirapo. Izi zikusonyeza kuti palibe chimene chikanamulepheretsa kukhala wodzipereka.—Afil. 2:8.

2. (a) Kodi tingasonyeze bwanji mtima wodzipereka? (b) Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza mtima umenewu?

2 Popeza ndife otsatira a Yesu, nafenso tiyenera kusonyeza mtima wodzipereka. Kodi kudzipereka n’kutani? Tinganene kuti munthu wodzipereka ndi amene amalolera kusiya zofuna zake kuti athandize anthu ena. M’mawu ena, tingati munthu wodzipereka ndi wosiyana kwambiri ndi munthu wodzikonda. (Werengani Mateyu 16:24.) Mtima wodzipereka ungatithandize kuganizira choyamba zofuna za ena m’malo mwa zofuna zathu. (Afil. 2:3, 4) Yesu anaphunzitsa kuti munthu ayenera kukhala wodzipereka kuti alambire Mulungu. Anatero chifukwa chakuti ophunzira ake enieni amadziwika ndi chikondi, chomwe chimathandiza munthu kukhala wodzipereka. (Yoh. 13:34, 35) Ndipotu tikusangalala ndi madalitso ambiri chifukwa chokhala m’gulu la  abale apadziko lonse omwe ali ndi mtima wodzipereka.

3. Kodi n’chiyani chingatilepheretse kusonyeza mtima wodzipereka?

3 Komabe, tili ndi mdani amene angatilepheretse mwaukathyali kusonyeza mtima wodzipereka. Mdani ameneyu ndi mtima wodzikonda umene tonsefe timalimbana nawo. Kumbukirani mmene Adamu ndi Hava anasonyezera mtima umenewu. Modzikonda, Hava ankafuna kufanana ndi Mulungu. Nayenso mwamuna wake anasonyeza mtima wodzikonda pofuna kusangalatsa mkazi wakeyo. (Gen. 3:5, 6) Mdyerekezi analepheretsa Adamu ndi Hava kutumikira Mulungu ndipo iye akupitiriza kuyesa anthu kuti azichita zinthu modzikonda. Iye anachita zimenezi poyesa Yesu. (Mat. 4:1-9) Masiku ano, anthu ambiri asocheretsedwa ndi Satana ndipo akusonyeza mtima wodzikonda m’njira zambiri. Choncho tiyenera kusamala kwambiri chifukwa tingatengere mosavuta mtima umenewu.—Aef. 2:2.

4. (a) Kodi panopa n’zotheka kupeweratu mtima wodzikonda? Fotokozani. (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

4 Mtima wodzikonda tingauyerekezere ndi dzimbiri. Chitsulo chikakhala pamalo enaake n’kunyowa chimachita dzimbiri. Vuto limakhalapo ngati dzimbirilo talilekerera chifukwa chitsulocho chikhoza kuwonongekeratu. N’chimodzimodzinso ifeyo. Ngakhale kuti sitingapeweretu mtima wodzikonda umene umabwera chifukwa chopanda ungwiro, tiyenera kudziwa kuopsa kwake n’kumayesetsa kulimbana nawo. (1 Akor. 9:26, 27) Kodi tingadziwe bwanji ngati tayamba kudzikonda? Ndipo tingatani kuti tikhale ndi mtima wodzipereka kwambiri?

MUZIGWIRITSA NTCHITO BAIBULO KUTI MUDZIWE NGATI NDINU WODZIKONDA

5. (a) Kodi Baibulo limafanana bwanji ndi galasi? (Onani chithunzi patsamba 7.) (b) Kuti Baibulo litithandize, kodi tiyenera kupewa chiyani?

5 Tikhoza kugwiritsa ntchito Baibulo ngati galasi kuti tione ngati tili ndi vuto limene tiyenera kulikonza mumtima mwathu. (Werengani Yakobo 1:22-25.) Komatu galasi limakhala lothandiza ngati tikuligwiritsa ntchito bwino. Mwachitsanzo, ngati titadziyang’anira pagalasi mongodutsa, sitingaone tinthu tina tomwe sitili bwino. Tikaliyang’ananso cham’mbali, titha kuona anthu ena m’malo modziona ifeyo. Ndi mmenenso zilili ndi Baibulo. Tikamaliwerenga mongodutsa kapena kuti tione zimene anthu ena amalakwitsa, silingatithandize kuona mavuto athu monga mtima wodzikonda.

6. Kodi munthu ‘wolimbikira’ kuyang’anitsitsa lamulo langwiro amatani?

6 Mwachitsanzo, n’zotheka kuwerenga Baibulo tsiku lililonse koma osadziwa zoti tikuyamba mtima wodzikonda. Kodi zingatheke bwanji? Taganizirani zimene Yakobo ananena pa nkhaniyi. Munthu amene Yakobo anamufotokoza amadziyang’anira bwinobwino pagalasi. Paja iye analemba kuti munthuyo “amadziyangana.” Apatu Yakobo anagwiritsa ntchito mawu achigiriki amene amatanthauza kuyang’anitsitsa mosamala kwambiri. Ndiyeno kodi vuto linagona pati? Yakobo anapitiriza kuti: “Akachokapo, nthawi yomweyo amaiwala kuti ndi munthu wotani.” Munthuyu anangochokapo osakonza zimene anaona. Koma munthu wochita bwino ‘samangoyang’anitsitsa m’lamulo langwiro’ koma “amalimbikira kutero.” M’malo mongowerenga lamulo langwiro m’Mawu a Mulungu n’kusiyira pomwepo, munthuyo amalimbikira kutsatira zimene waphunzirazo. Izi n’zimenenso Yesu ananena pamene anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga.”—Yoh. 8:31.

7. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji Baibulo kuti tione ngati tayamba mtima wodzikonda?

7 Choncho kuti tilimbane ndi mtima wodzikonda, choyamba tiyenera kuwerenga Mawu a Mulungu mosamala. Izi zingatithandize kudziwa zimene tiyenera kusintha. Koma sitiyenera  kuimira pomwepo. Tiyeneranso kufufuza kuti timvetse bwino nkhani za m’Baibulo. Ndiyeno tikatero tizidzifunsa mafunso ngati akuti: ‘Kodi pamenepa ndikanakhala ineyo ndikanatani? Kodi zomwe ndikanachita zikanakhala zoyenera?’ Koma chofunika kwambiri n’kuyesetsa kutsatira zimene taphunzirazo. (Mat. 7:24, 25) Tsopano tiyeni tikambirane zimene tikuphunzira pa nkhani ya Sauli ndi mtumwi Petulo. Kuchita zimenezi kutithandiza kukhalabe ndi mtima wodzipereka.

PHUNZIRANI PA ZIMENE SAULI ANACHITA

8. (a) Kodi Sauli anali ndi mtima wotani atangokhala kumene mfumu? (b) Kodi anasonyeza bwanji zimenezi?

8 Sauli, yemwe anali mfumu ya Isiraeli, anali wodzipereka koma anayamba kukhala wodzikonda. Ife tiyenera kusamala kuti tisatengere zimene anachita. Sauli atangoikidwa kukhala mfumu anali wodzichepetsa. (1 Sam. 9:21) Iye anasankhidwa ndi Mulungu kukhala mfumu ndipo zikanakhala zomveka kuti alange Aisiraeli amene ankakana zimenezi. Koma sanawalange. (1 Sam. 10:27) Sauli analola kuti mzimu wa Mulungu uzimutsogolera pa nkhondo yomenyana ndi Aamoni ndipo anapambana. Kenako ananena modzichepetsa kuti Mulungu ndi amene anamuthandiza.—1 Sam. 11:6, 11-13.

9. Kodi Sauli anayamba bwanji kukhala wodzikonda?

9 Koma kenako Sauli anayamba kudzikonda ndi kudzikweza ndipo apa zinali ngati mtima wake wayamba dzimbiri. Pamene anagonjetsa Aamaleki sanamvere Yehova koma anaika zofuna zake patsogolo. Yehova anamuuza kuti awononge zinthu za Aamaleki koma chifukwa cha dyera Sauli anazitenga. Komanso anasonyeza mtima wodzikweza pomanga chipilala cha chikumbutso chake. (1 Sam. 15:3, 9, 12) Pamene mneneri Samueli anamuuza kuti Yehova sakusangalala naye, Sauli anapereka zifukwa zodzikhululukira. Iye ananena kuti anamvera zinthu zina zimene Mulungu anamuuza komanso anaimba mlandu anthu ena chifukwa cha zimene anachitazo. (1 Sam. 15:16-21) Kuwonjezera pamenepo, chofunika kwambiri kwa Sauli chinali choti asanyozeke pamaso pa anthu osati kusangalatsa Mulungu. (1 Sam. 15:30) Kodi tingagwiritse ntchito bwanji nkhani ya Sauli ngati galasi lotithandiza kukhalabe odzipereka?

10, 11. (a) Kodi zimene zinachitikira Sauli zikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kukhalabe wodzipereka? (b) Kodi tingapewe bwanji kutengera chitsanzo choipa cha Sauli?

10 Choyamba, chitsanzo cha Sauli chikusonyeza kuti munthu amene ali ndi mtima wodzipereka ayenera kuchita khama kuti asasinthe. (1 Tim. 4:10) Kumbukirani kuti poyamba Sauli anachita zinthu zosangalatsa Mulungu koma kenako analekerera mtima wodzikonda. Choncho Yehova anakana Sauli chifukwa cha kusamvera kwake.

11 Chachiwiri, tiyenera kusamala kuti tisamangoona zinthu zokhazo zimene tikuchita bwino n’kumanyalanyaza zinthu zimene tikufunika kukonza. Izi zingafanane ndi kudziyang’anira pagalasi kuti tingoona mmene tatchenera koma osaona kuti nkhope yathu sikuoneka bwino. Ngakhale kuti sitingakhale odzikonda ngati mmene Sauli analili, tiyenera kusamala kuti tisayambe ngakhale pang’ono kusonyeza mtima umenewo. Tikalandira uphungu, tisamapereke zifukwa zodzikhululukira, kuchepetsa vuto lathu kapena kuimba mlandu anthu ena. M’malomwake, tiyenera kukhala okonzeka kulandira uphunguwo.—Werengani Salimo 141:5.

12. Kodi mtima wodzipereka ungatithandize bwanji tikachita tchimo lalikulu?

12 Koma bwanji ngati tachita tchimo lalikulu? Sauli sankafuna kunyozeka pamaso pa anthu ndipo zimenezi zinamulepheretsa kukonza ubwenzi wake ndi Yehova. Koma mtima wodzipereka ungatilimbikitse kupempha  thandizo m’malo moopa kuchita manyazi. (Miy. 28:13; Yak. 5:14-16) Mwachitsanzo, m’bale wina anayamba kuonera zolaula ali ndi zaka 12 ndipo anapitiriza kuchita zimenezi kwa zaka zoposa 10. Iye anati: “Zinali zovuta kwambiri kuuza mkazi wanga komanso akulu zimene ndinkachitazo. Koma panopa ndikumva kuti ndatula chimtolo cholemera kwambiri chifukwa ndawauza. Anzanga ena sanasangalale nane nditachotsedwa pa udindo wokhala mtumiki wothandiza. Komabe ndikuona kuti ndinachita bwino chifukwa Yehova akusangalala nane panopa kuposa pamene ndinkaonera zolaulazo. Ndipo kusangalatsa Yehova n’kofunika kuposa chinthu china chilichonse.”

PETULO ANAGONJETSA MTIMA WODZIKONDA

13, 14. Kodi Petulo anasonyeza bwanji mtima wodzikonda?

13 Mtumwi Petulo anasonyeza mtima wodzipereka pamene ankaphunzitsidwa ndi Yesu. (Luka 5:3-11) Koma ankafunikiranso kulimbana ndi mtima wodzikonda. Mwachitsanzo, iye anakwiya pamene Yakobo ndi Yohane ankafuna kuti Yesu adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu. Mwina Petulo ankaganiza kuti iyeyo ndi amene akuyenera kudzakhala pamalo amenewo chifukwa Yesu anali atamuuza kale kuti adzam’patsa udindo wapadera. (Mat. 16:18, 19) Koma Yesu anachenjeza Yakobo, Yohane, Petulo ndi atumwi ena onsewo kuti asamale ndi mtima wofuna kukhala apamwamba kuposa abale awo.—Maliko 10:35-45.

14 Ngakhale kuti Yesu anathandiza Petulo kuti asamaganize choncho, iye nthawi zina ankasonyezabe mtima wodzikuza. Yesu atauza atumwi kuti adzamuthawa, Petulo anadzikuza ponena kuti iye yekha adzakhalabe wokhulupirika. (Mat. 26:31-33) Koma zimenezo sizinali zoona chifukwa usiku womwewo analephera kusonyeza mtima wodzipereka. Pofuna kudziteteza, Petulo anakana Yesu katatu.—Mat. 26:69-75.

15. Kodi chitsanzo cha Petulo chingatilimbikitse bwanji?

15 Ngakhale kuti Petulo nthawi zina ankalakwitsa zinthu, chitsanzo chake chingatilimbikitse.  Petulo anayesetsa kulimbana ndi mtima wodzikonda ndipo mzimu woyera wa Mulungu unamuthandiza kukhala wodziletsa komanso kusonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. (Agal. 5:22, 23) Anapirira mayesero aakulu kuposa amene analephera kuwapirira aja. Anasonyeza kudzichepetsa, mtumwi Paulo atamupatsa uphungu pamaso pa anthu ena. (Agal. 2:11-14) Atapatsidwa uphungu umenewu, Petulo sanasunge chakukhosi n’kumaganiza kuti Paulo wamuwonongera mbiri yake. Iye anapitirizabe kukonda Paulo. (2 Pet. 3:15) Chitsanzo cha Petulo chimenechi chingatithandize kukhala ndi mtima wodzipereka.

Kodi Petulo anachita chiyani atapatsidwa uphungu? Nanga mukanakhala inuyo mukanatani? (Onani ndime 15)

16. Kodi tingasonyeze bwanji mtima wodzipereka tikakumana ndi mavuto?

16 Ganizirani zimene inuyo mumachita mukakumana ndi mavuto. Petulo ndi atumwi ena anaikidwa m’ndende kenako n’kukwapulidwa chifukwa choti ankalalikira. Koma iwo anasangalala “chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.” (Mac. 5:41) Inunso mukamazunzidwa muziona kuti umenewu ndi mpata wosonyeza kuti mukutsanzira Petulo komanso mtima wodzipereka wa Yesu. (Werengani 1 Petulo 2:20, 21.) Kuona zinthu m’njira imeneyi kungakuthandizeninso ngati akulu akupatsani uphungu. M’malo mokhumudwa ndi akuluwo, muzitsanzira Petulo.—Mlal. 7:9.

17, 18. (a) Kodi tingadzifunse mafunso ati okhudza zolinga zathu zauzimu? (b) Kodi tingatani ngati taona kuti tili ndi kamtima kodzikonda?

17 Chitsanzo cha Petulo chingatithandizenso pa nkhani yokhala ndi zolinga zauzimu. Tingachite bwino kukhala ndi mtima wodzipereka poyesetsa kukwaniritsa zolinga zimenezo. Koma tiyenera kusamala kuti tisachite zinthu n’cholinga chofuna kutchuka. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi n’chiyani chikundichititsa kufuna kuwonjezera utumiki wanga? Kodi mwina ndikufuna kutchuka kapena kukhala pa malo apamwamba ngati Yakobo ndi Yohane?’

18 Mukaona kuti muli ndi kamtima kodzikonda, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuchotsa kamtima koipako. Kenako yesetsani kuganizira kwambiri zimene mungachite kuti ulemerero upite kwa Mulungu osati kwa inuyo. (Sal. 86:11) Komanso mungachite bwino kukhala ndi mtima wofuna kuchita zinthu zimene si zoonekera kwa anthu. Mwachitsanzo, mungayesetse kusonyeza kwambiri khalidwe lina limene mzimu umatulutsa, lomwe mumaona kuti limakuvutani. Mwina mumakonzekera bwino misonkhano koma simukonda kwenikweni kuthandiza nawo pa ntchito yoyeretsa m’Nyumba ya Ufumu. Ngati zili choncho, mungakhale ndi cholinga chotsatira malangizo opezeka pa Aroma 12:16.Werengani.

19. Kodi tingatani kuti tisamakhumudwe ndi zimene taona pagalasi, lomwe ndi Mawu a Mulungu?

19 Nthawi zina tingakhumudwe tikadziyang’ana bwinobwino pagalasi, lomwe ndi Mawu a Mulungu, n’kuona zinthu zina zolakwika monga kudzikonda. Zimenezi zikakuchitikirani, ganizirani za munthu wa mu fanizo la Yakobo lija. Yakobo sananene kuti munthuyo anakonza vuto lake mwamsanga kapena kuti anakonza mavuto ake onse. M’malomwake, ananena kuti ‘analimbikira kuyang’anitsitsa m’lamulo langwiro.’ (Yak. 1:25) Munthuyo anakumbukira zimene anaona pagalasi paja n’kupitiriza kuyesetsa kukonza mavutowo. Choncho tikaona mavuto athu tisamadandaule kwambiri. (Werengani Mlaliki 7:20.) Koma tipitirize kuyang’anitsitsa m’lamulo langwiro n’kumayesetsa kuti tikhalebe ndi mtima wodzipereka. Yehova ndi wokonzeka kutithandiza ngati mmene wathandizira abale athu ambirimbiri. Iwonso si angwiro, koma Mulungu amawakonda ndipo akuwadalitsa.