Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingathandize Bwanji Achibale Omwe Si Mboni?

Kodi Tingathandize Bwanji Achibale Omwe Si Mboni?

YESU KHRISTU anauza munthu amene ankafuna kuti azimutsatira kuti: “Pita kunyumba kwa achibale ako, ndipo ukawauze zonse zimene Yehova wakuchitira ndi chifundo chimene wakusonyeza.” Iye mwina ananena zimenezi kumzinda wa Gadara, womwe unali kum’mwera cha kum’mawa kwa nyanja ya Galileya. Mawu amenewa akusonyeza kuti Yesu ankadziwa kuti pakachitika zosangalatsa, anthu amafuna kuuza achibale awo.—Maliko 5:19.

Izi zimachitikanso masiku ano ndipo zimaonekera kwambiri pakati pa mitundu ina ya anthu kuposa ina. N’chifukwa chake munthu akayamba kulambira Yehova Mulungu, kawirikawiri amafuna kuuza achibale ake zimene amakhulupirirazo. Koma kodi angawauze bwanji? Kodi angathandize bwanji achibale amene ali m’chipembedzo china kapena amene sapembedza n’komwe? Malangizo othandiza tingawapeze m’Baibulo.

“IFETU TAPEZA MESIYA”

Andireya anali mmodzi mwa anthu oyambirira kuzindikira kuti Yesu ndi Mesiya. Kodi iye atangodziwa zimenezi anauza ndani? Baibulo limati: “Choyamba [Andireya] anapeza m’bale wake Simoni, ndi kumuuza kuti: ‘Ifetu tapeza Mesiya’ (dzina lotanthauza, Khristu polimasulira).” Ndiyeno Andireya anatenga Petulo n’kupita naye kwa Yesu kuti nayenso akhale wophunzira wake.—Yoh. 1:35-42.

Patapita zaka 6, Petulo ali ku Yopa, anauzidwa kuti apite ku Kaisareya kunyumba ya kapitawo wa asilikali dzina lake Koneliyo. Kodi atafika kunyumbako anapeza ndani? Baibulo limati: “Kumeneko Koneliyo anali kuwayembekezera, [Petulo ndi anzake] ndipo anasonkhanitsa achibale ndi mabwenzi ake apamtima.” Apatu Koneliyo anapereka mwayi kwa achibale ake kuti amve uthenga wa Petulo n’kusankha zoyenera kuchita.—Mac. 10:22-33.

 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Andireya ndi Koneliyo anachitira achibale awo?

Onse awiri anachita zinazake pofuna kuthandiza achibale awo. Andireya anatenga Petulo n’kupita naye kwa Yesu, pomwe Koneliyo anasonkhanitsa achibale ake kuti amve uthenga wa Petulo. Koma sikuti Andireya ndi Koneliyo anakakamiza achibale awo kapena kuwanyengerera kuti azitsatira Khristu. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Nafenso tingathe kukambirana ndi achibale athu n’kuwathandiza kuti adziwe choonadi cha m’Baibulo komanso kuti adziwane ndi Akhristu anzathu. Koma tizikumbukira kuti iwo ali ndi ufulu wosankha ndipo sitiyenera kuwakakamiza. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira Jürgen ndi mkazi wake Petra ku Germany.

Petra ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo kenako anabatizidwa. Koma mwamuna wake anali mkulu wa asilikali. Poyamba, mwamunayu sankasangalala ndi zimene mkazi wake ankachita. Koma kenako anadzazindikira kuti a Mboni amaphunzitsa mfundo zoona za m’Baibulo. Nayenso anadzipereka kwa Yehova ndipo panopa akutumikira monga mkulu mumpingo wa kwawo. Kodi ndi malangizo ati amene mwamunayu ananena pa nkhani yothandiza achibale amene si Mboni?

Jürgen anati: “Si bwino kuwakakamiza kapena kuwapanikiza ndi zinthu zokhudza kulambira Yehova. Tikatero sangafune kuphunzira. Ndi bwino kuwauza mfundo za m’Malemba pang’onopang’ono. Mwina tingawathandize kudziwana ndi abale amsinkhu wawo kapena amene angamamvane nawo. Mukatero mukhoza kutsegula njira yoti ayambe kuphunzira.”

“Si bwino kukakamiza achibale athu kapena kuwapanikiza.”—Jürgen

Mtumwi Petulo komanso achibale a Koneliyo sanachedwe kutsatira uthenga wa m’Baibulo. Koma anthu ena kalelo anatenga nthawi kuti asankhe kutumikira Mulungu.

ZIMENE TIKUPHUNZIRA KWA ACHIBALE A YESU

Pamene Yesu ankachita utumiki wake, achibale ake ena anamukhulupirira. Mwachitsanzo, zikuoneka kuti Yakobo ndi Yohane anali pachibale ndi Yesu. Tikutero chifukwa chakuti mayi awo a Salome ndi mayi a Yesu anali munthu ndi mchemwali wake. N’kutheka kuti Salome anali m’gulu la “amayi ena ambiri, amene anali kutumikira Yesu ndi atumwiwo pogwiritsa ntchito chuma chawo.”—Luka 8:1-3.

Koma achibale ena a Yesu sanam’khulupirire nthawi yomweyo. Mwachitsanzo, patatha chaka Yesu atabatizidwa, anthu anasonkhana m’nyumba ina kuti amvetsere uthenga wake. “Koma achibale ake atamva zimenezo, anapita kukamugwira, chifukwa anali kunena kuti: ‘Wachita misala.’” Nthawi ina abale ake atamupempha kuti apite kudera lina, iye sanalole chifukwa chakuti “abale akewo sanali kumukhulupirira.”—Maliko 3:21; Yoh. 7:5.

Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anachitira abale akewo? Iye sanakhumudwe ena atamunena kuti wachita misala. Ndipo Yesu ataukitsidwa, anaonekera kwa m’bale wake Yakobo. Izi zinalimbikitsa kwambiri abale akewo. Zimenezi zinathandiza Yakobo ndi abale ena a Yesu kukhulupirira kuti iyedi ndi Mesiya. Choncho iwo analipo pamene atumwi anasonkhana m’chipinda china cha m’mwamba ku Yerusalemu ndipo zikuoneka kuti  analandira nawo mzimu woyera. Patapita nthawi Yakobo ndi Yuda, omwe analinso abale ake a Yesu, anadzakhala ndi maudindo akuluakulu.—Mac. 1:12-14; 2:1-4; 1 Akor. 15:7.

ENA AMATENGA NTHAWI

“Pamafunika kudekha ndiponso kuleza mtima kwambiri kuti wachibale asinthe.”—Roswitha

Masiku anonso, anthu ena amatenga nthawi kuti ayambe kuyenda panjira ya ku moyo. Mwachitsanzo, Roswitha anali Mkatolika weniweni pamene mwamuna wake ankabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova mu 1978. Chifukwa chokhulupirira kwambiri za kutchalitchi kwawo, iye ankatsutsa mwamuna wake. Koma patapita zaka, anayamba kusintha atazindikira kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa mfundo zoona. Roswitha anabatizidwanso mu 2003. Kodi n’chiyani chinathandiza kuti asinthe? Mwamuna wake sanakhumudwe pamene iye ankatsutsa, koma ankangomuchitira zinthu zothandiza kuti asinthe maganizo. Kodi ndi malangizo otani amene Roswitha akupereka? Iye anati: “Pamafunika kudekha ndiponso kuleza mtima kwambiri kuti wachibale asinthe.”

Monika anabatizidwa mu 1974 ndipo ana ake anadzabatizidwa patadutsa zaka 10. Mwamuna wake, dzina lake Hans, sankatsutsa ayi koma anatenga nthawi yaitali kwambiri chifukwa anabatizidwa mu 2006. Kodi iwo amapereka malangizo ati, poona zimene zinachitika m’banja lawo? Amanena kuti: “Tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ndipo tisalole kuchita zinthu zosemphana ndi chikhulupiriro chathu.” Monika ndi ana ake ankachita zonse zimene angathe posonyeza kuti amakonda Hans ndipo ankayembekezera kuti tsiku lina adzakhala m’bale.

MADZI A CHOONADI AMATSITSIMUTSA

Pa nthawi ina Yesu anayerekezera uthenga wa choonadi ndi madzi opatsa moyo wosatha. (Yoh. 4:13, 14) Timafunitsitsa kuti achibale athu amwe madzi abwinowa n’kutsitsimulidwa. Koma sitikufuna kuti atsamwidwe chifukwa chowamwetsa madzi ambirimbiri nthawi imodzi. Zimene timachita powafotokozera mfundo za m’Baibulo ndi zimene zingapangitse kuti atsitsimulidwe kapena kutsamwidwa. Baibulo limanena kuti “mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe.” Komanso limati “mtima wa munthu wanzeru umamuchititsa kuti asonyeze kuzindikira ndi pakamwa pake, ndipo umachititsa milomo yake kutulutsa mawu okopa.” Kodi tingatsatire bwanji malangizo amenewa?—Miy. 15:28; 16:23.

Mkazi angafune kuuza mwamuna wake zimene amakhulupirira. Koma sayenera kudzionetsa ngati wolungama kapena wapamwamba. Ngati ‘atayamba waganiza’ asanalankhule, akhoza kusankha mawu oyenera komanso angathe kulimbikitsa mwamuna wakeyo ndipo angamakhale mwamtendere. Mwina angaganizire mafunso awa, Kodi mwamuna wake amamvetsera mwatcheru pa nthawi iti? Kodi amakonda kuwerenga kapena kumvetsera nkhani zotani? Kodi amakonda nkhani zasayansi, zandale kapena zamasewera? Kodi angatani kuti mwamunayo ayambe kuchita chidwi ndi nkhani za m’Baibulo popanda kumukhumudwitsa? Mafunso amenewa angathandize mkaziyo kulankhula komanso kuchita zinthu mosamala.

Pamafunika zambiri kuti uthenga wathu ufike pamtima pa wachibale amene si Mboni, osati kungowafotokozera za chikhulupiriro chathu. Khalidwe lathu labwino lingatsimikizire kuti zimene tikunena n’zoona.

MUZISONYEZA KHALIDWE LABWINO

Jürgen, amene tamutchula kale uja anati: “Muziyesetsa kutsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Mukamatero mnzanuyo amaona ndipo zimamuchititsa kuganizira zimene mumakhulupirira ngakhale kuti sagwirizana nazo kwenikweni.” Hans, amene anabatizidwa patapita zaka 30 kuchokera pamene mkazi wake anabatizidwa, ananenanso kuti: “Mkhristu akakhala ndi khalidwe labwino zimathandiza kuti wachibale wake azindikire kuti mfundo zimene timaphunzira zimatithandiza kwambiri.” Achibalewo ayenera kuona kuti ifeyo timasiyana ndi anthu ena chifukwa chakuti zimene timakhulupirira zimatichititsa kukhala anthu abwino osati okhumudwitsa ena.

“Mkhristu akakhala ndi khalidwe labwino zimathandiza kuti wachibale wake azindikire kuti mfundo zimene timaphunzira zimatithandiza kwambiri.”—Hans

Mtumwi Petulo analangiza alongo amene amuna awo ndi osakhulupirira. Iye anati: “Muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu. Ndipo kudzikongoletsa kwanu  kusakhale kwakunja, monga kumanga tsitsi, kuvala zodzikongoletsera zagolide, kapena kuvala malaya ovala pamwamba. Koma kukhale kwa munthu wobisika wamumtima, atavala zovala zosawonongeka, ndizo mzimu wabata ndi wofatsa umene uli wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.”—1 Pet. 3:1-4.

Petulo ananena kuti mwamuna akhoza kukopeka ndi khalidwe labwino la mkazi wake. Mlongo wina dzina lake Christa wakhala akutsatira malangizowa kuchokera pamene anabatizidwa mu 1972. Pa nthawi ina, mwamuna wake ankaphunzira ndi Mboni koma anali asanatsimikize kukhala wa Mboni. Anafikapo kumisonkhano ndipo amadziwana ndi abale ndi alongo. Abale ndi alongowo amachita zinthu mosamuphwanyira ufulu wake wosankha. Kodi Christa amathandiza bwanji mwamuna wakeyu?

Iye anati: “Ndatsimikiza kuti nthawi zonse ndizichita zimene Yehova amafuna. Koma ndimayesetsa kuti ndikope mwamuna wanga ‘osati ndi mawu’ koma ndi khalidwe langa labwino. Ndimayesetsa kuchita zonse zimene akufuna ngati sizikusemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Ndimadziwanso kuti iye ali ndi ufulu wosankha ndipo nkhaniyi ndaisiya m’manja mwa Yehova.”

Chitsanzo cha Christa ndi chabwino kwambiri. Iye amalimbikira pa zinthu zokhudza kulambira monga kupezeka pamisonkhano komanso kulalikira. Koma amaonetsetsa kuti apeze nthawi yocheza ndiponso kusangalala ndi mwamuna wake. Ngati tili ndi achibale amene si Mboni tiyenera kugawa bwino nthawi yochitira zinthu. Paja Baibulo limati: “Chilichonse chili ndi nthawi yake.” Choncho tiyenera kupeza nthawi yocheza ndi mwamuna wathu, mkazi wathu kapena achibale omwe si Mboni. Izi zimathandiza kuti tizilankhulana momasuka. Kupeza nthawi yolankhulana kumathandiza kuti winayo asamasungulumwe kapena kuchita nsanje.—Mlal. 3:1.

MUSATAYE MTIMA

Bambo ake a Holger anabatizidwa patapita zaka 20 anthu ena a m’banja lake atabatizidwa kale. Ndiyeno Holger ananena kuti: “Ndi bwino kusonyeza kuti anthu a m’banja mwathu timawakonda komanso timawapempherera.” Christa ananenanso kuti ‘akukhulupirira kuti mwamuna wake adzayamba kutumikira Yehova.’ Nthawi zonse tizikhala ndi chikhulupiriro choti nthawi ina achibale athuwo adzayamba kutumikira Yehova.

Tiyenera kuyesetsa kuti tizigwirizana ndi achibale athuwo, kuwathandiza kuti aone okha kuti zimene timakhulupirira n’zoona komanso kuti uthenga wa m’Baibulo uwafike pamtima. Nthawi zonse tizichita zinthu “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.”—1 Pet. 3:15.