Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tamandani Khristu, Mfumu ya Ulemerero

Tamandani Khristu, Mfumu ya Ulemerero

“Upambane mu ulemerero wako.”—SAL. 45:4.

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti nkhani ya mu Salimo 45 ndi yofunika kwa ife?

SALIMO 45 limanena za mfumu yaulemerero imene inakwera pahatchi chifukwa cha choonadi ndi chilungamo ndipo inapita kukagonjetsa adani ake. Iye atagonjetsa adani onse, anakwatira mkazi wokongola. Ndiyeno salimoli likusonyeza kuti mibadwo yonse yam’tsogolo idzakumbukira mfumuyi ndi kuitamanda.

2 Nkhani ya mu salimoli ndi yosangalatsa komanso tikhoza kuphunziramo zambiri. Zimene zafotokozedwa m’nkhaniyi zikukhudza moyo wathu panopa komanso tsogolo lathu. Ndiye tiyeni tikambirane bwinobwino salimo limeneli.

“MTIMA WANGA WAGALAMUKA CHIFUKWA CHA NKHANI YOSANGALATSA”

3, 4. (a) Kodi ndi nkhani iti imene ‘imatisangalatsa,’ nanga ‘imagalamutsa’ bwanji mitima yathu? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ‘nyimbo yathu ikunena za mfumu’? (c) Kodi lilime lathu limafanana bwanji ndi “cholembera cha wokopera malemba waluso”?

3 Werengani Salimo 45:1. “Nkhani yosangalatsa” imene ‘yagalamutsa mtima’ wa wamasalimoyu ndi yokhudza mfumu. Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “wagalamuka” amatanthauza “kuwira.” Choncho nkhaniyi inachititsa mtima wa wamasalimoyu  kuwira chifukwa chofunitsitsa kuchita zinazake. Inachititsanso lilime lake kukhala ngati “cholembera cha wokopera malemba waluso.”

4 Ifenso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mesiya umatifika pamtima ndipo umatisangalatsa kwambiri. Uthengawu unayamba kukhala ‘wosangalatsa’ kwambiri mu 1914. Kuyambira m’chaka chimenechi, uthengawu sukunena za Ufumu wam’tsogolo koma za boma limene layamba kale kulamulira kumwamba. Umenewu ndi ‘uthenga wabwino wa ufumu’ umene timalalikira “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mat. 24:14) Ndiyeno funso ndi lakuti, Kodi uthenga wa Ufumuwu ‘umagalamutsa’ mitima yathu? Kodi timalalikira mwakhama uthenga wa Ufumuwu? Mofanana ndi wamasalimo, tikamalalikira timakhala ngati tikuimba ‘nyimbo yonena za mfumu’ ndipo Mfumu yathu ndi Yesu Khristu. Timalalikira zoti iye waikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya kumwamba. Timauzanso mafumu ndi anthu awo kuti azigonjera ulamuliro wake. (Sal. 2:1, 2, 4-12) Ifenso lilime lathu limakhala ngati “cholembera cha wokopera malemba waluso” chifukwa chakuti timagwiritsa ntchito kwambiri Baibulo tikamalalikira.

Timalalikira mosangalala uthenga wabwino wonena za Mfumu yathu, Yesu Khristu

‘MAWU OTULUKA M’KAMWA MWA MFUMUYI NDI OSANGALATSA’

5. (a) Kodi Yesu anali “wokongola” m’njira ziti? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ‘mawu otuluka m’kamwa mwa Yesu anali osangalatsa’? (c) Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo chake?

5 Werengani Salimo 45:2. Malemba sanena zambiri za mmene Yesu ankaonekera. Popeza kuti anali wangwiro, ayenera kuti anali “wokongola.” Koma chimene chinam’chititsa kukhala wokongola kwambiri chinali kukhulupirika kwake potumikira Yehova. Komanso mawu a Yesu anali “ogwira mtima” pamene ankalalikira uthenga wa Ufumu. (Luka 4:22; Yoh. 7:46) Kodi ifeyo timayesetsa kutsatira chitsanzo chake pogwiritsa ntchito mawu ogwira mtima pamene tikulalikira?—Akol. 4:6.

6. Kodi Mulungu anadalitsa bwanji Yesu “mpaka kalekale”?

6 Pamene Yesu anali padziko lapansi ankatumikira Mulungu ndi mtima wonse ndipo anapereka moyo wake monga nsembe. Choncho Yehova ankamudalitsa ndipo ataukitsidwa anam’patsa mphoto yaikulu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “[Yesu] atakhala munthu, anadzichepetsa ndi kukhala womvera mpaka imfa. Anakhala womvera mpaka imfa ya pamtengo wozunzikirapo. Pa chifukwa chimenechinso, Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse. Anachita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse akumwamba, apadziko lapansi, ndi apansi pa nthaka apinde mawondo awo. Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.” (Afil. 2:8-11) Yehova anamudalitsa “mpaka kalekale” pomupatsa moyo umene sungafe.—Aroma 6:9.

MFUMUYI YAKWEZEDWA KUPOSA “MAFUMU ENA”

7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu anadzoza Yesu ndi mafuta a chikondwerero chachikulu kuposa “mafumu ena”?

7 Werengani Salimo 45:6, 7Yesu amakonda kwambiri chilungamo ndipo amadana ndi chilichonse chimene chinganyozetse Atate wake. Chifukwa cha zimenezi, Yehova anamudzoza kuti akhale Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. Yesu anadzozedwa ndi “mafuta achikondwerero chachikulu”  kuposa cha “mafumu ena” a Yuda, omwe anali mu mzere wa Davide. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Choyamba, Yesu anadzozedwa ndi Yehova weniweniyo. Anamudzoza kuti akhale Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe. (Sal. 2:2; Aheb. 5:5, 6) Chinanso n’chakuti Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera osati mafuta ndipo ufumu wake ndi wakumwamba osati padziko lapansi.

8. (a) Kodi mawu akuti ‘Mulungu ndiye mpando wachifumu’ wa Yesu akutanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti Yesu ndi wolamulira wachilungamo?

8 Yehova anaika Mwana wakeyu kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya kumwamba mu 1914. ‘Ndodo yake yachifumu ndi ndodo yachilungamo’ choncho n’zosachita kufunsa kuti iye ndi wolamulira wachilungamo komanso wosakondera. Mawu akuti ‘Mulungu ndiye mpando wake wachifumu’ akusonyeza kuti ulamuliro wake ndi wovomerezeka chifukwa chakuti Mulungu ndi amene wamupatsa. Ulamuliro wa Yesu udzakhalapo “mpaka muyaya.” Kodi inuyo simunyadira kutumikira Yehova motsogoleredwa ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulunguyi?

MFUMUYI ‘YAMANGIRIRA LUPANGA LAKE’

9, 10. (a) Kodi ndi liti pamene Khristu anamangirira lupanga lake, nanga anayamba bwanji kuligwiritsa ntchito? (b) Kodi posachedwapa iye adzaligwiritsa ntchito bwanji?

9 Werengani Salimo 45:3. Yehova analangiza Mfumuyi kuti: “Mangirira lupanga lako m’chiuno mwako wamphamvu iwe.” Izi zikutanthauza kuti Yehova anapatsa Yesu mphamvu kuti amenye nkhondo yolimbana ndi aliyense wotsutsa ulamuliro wa Mulungu ndi kupereka chiweruzo. (Sal. 110:2) Mawu akuti “wamphamvu iwe” akusonyeza kuti Yesu ndi Mfumu Yankhondo imene singagonje. Yesu anamangirira lupanga m’chiuno mwake mu 1914. Pa nthawiyo, iye anagonjetsa Satana ndi ziwanda zake n’kuwaponyera padziko lapansi.—Chiv. 12:7-9.

10 Ichi chinali chiyambi chabe, chifukwa akufunika kupitiriza kulimbana ndi adaniwo mpaka atawagonjetsa. (Chiv. 6:2) Iye adzapereka chiweruzo cha Yehova pa dziko la Satanali ndipo Satana ndi ziwanda zake adzafooledwa. Choyamba, adzawononga Babulo wamkulu yemwe akuimira zipembedzo zonse zonyenga. Yehova adzagwiritsa ntchito atsogoleri andale kuti awononge ‘huleli.’ (Chiv. 17:16, 17) Kenako Mfumu Yankhondoyi idzawonongeratu mabungwe onse andale. Ndiyeno Khristu, yemwe amatchedwa “mngelo wa phompho,” adzamaliza kugonjetsa adani ake poponya Satana ndi ziwanda zake m’phompho. (Chiv. 9:1, 11; 20:1-3) Tiyeni tsopano tione zimene ulosi wa pa Salimo 45 ukunena pa nkhani yochititsa chidwiyi.

MFUMUYI YAKWERA PAHATCHI “CHIFUKWA CHA CHOONADI”

11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Khristu ‘wakwera pahatchi chifukwa cha choonadi’?

11 Werengani Salimo 45:4. Cholinga cha nkhondo imene Mfumuyi idzamenye si kungogonjetsa anthu kuti aziwalamulira. Nkhondo yake ndi yachilungamo ndipo zolinga zake ndi zabwino kwambiri. Yesu wakwera pahatchi “chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo.” Mfundo ya choonadi yofunika kwambiri imene ikumuchititsa kumenya nkhondo ndi yakuti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Satana anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira ndipo anamupandukira. Kungoyambira nthawi imeneyo, ziwanda ndiponso anthu ena amatsutsanso ulamuliro wa Yehova. Ndiyeno nthawi idzafika yoti Mfumu yoikidwa ndi Mulungu isonyeze kuti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndipo sipadzakhalanso wotsutsa.

12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu wakwera pahatchi “chifukwa cha kudzichepetsa”?

12 Mfumuyi yakweranso ‘pahatchi chifukwa cha kudzichepetsa.’ Yesu, yemwe ndi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, wapereka  chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yodzichepetsa komanso kugonjera ulamuliro wa Atate wake. (Yes. 50:4, 5; Yoh. 5:19) Anthu onse amene akumvera Mfumuyi mokhulupirika ayeneranso kukhala odzichepetsa n’kumagonjera ulamuliro wa Yehova pa moyo wawo wonse. Anthu oterowo ndi amene adzaloledwe kulowa m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.—Zek. 14:16, 17.

13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Khristu wakwera pahatchi ‘chifukwa cha chilungamo’?

13 Khristu wakweranso pahatchi yake ‘chifukwa cha chilungamo.’ Iye akumenya nkhondo pofuna kuti chilungamo cha Mulungu chichitike. Ponena kuti chilungamo cha Mulungu, tikutanthauza mfundo za Yehova zothandiza kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika. (Aroma 3:21; Deut. 32:4) Yesaya analosera za Mfumu Yesu Khristu kuti: “Mfumu idzalamulira mwachilungamo.” (Yes. 32:1) Ulamuliro wa Yesu udzabweretsa “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano” ndipo “mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Pet. 3:13) Munthu aliyense amene adzalowe m’dziko latsopano adzayenera kutsatira mfundo za Yehova.—Yes. 11:1-5.

MFUMUYI IDZACHITA “ZINTHU ZOCHITITSA MANTHA”

14. Kodi dzanja lamanja la Khristu lidzachita bwanji “zinthu zochititsa mantha”? (Onani chithunzi patsamba 3.)

14 Mfumuyi yamangirira lupanga m’chiuno mwake. (Sal. 45:3) Koma nthawi idzakwana yoti isolole lupangali n’kuligwira m’dzanja lake lamanja. Wamasalimo analosera kuti: “Dzanja lako lamanja lidzakulangiza mu zinthu zochititsa mantha.” (Sal. 45:4) Yesu Khristu akadzakwera pahatchi yake kuti adzapereke chiweruzo cha Yehova pa Aramagedo, adzachitira adani ake “zinthu zochititsa mantha.” Sitikudziwa zimene adzachite powononga dziko la Satanali. Koma zimene adzachitezo zidzachititsa mantha kwambiri anthu onse okhala padziko lapansi, amene sanamvere chenjezo la Mulungu ndi kugonjera ulamuliro wa Mfumuyi. (Werengani Salimo 2:11, 12.) Polosera za masiku otsiriza, Yesu ananena kuti anthu “adzakomoka chifukwa cha mantha ndi kuyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi kumene kuli anthu, pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.” Ananenanso kuti: “Kenako adzaona Mwana wa munthu akubwera mumtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.”—Luka 21:26, 27.

15, 16. Kodi ndani ali ‘m’magulu ankhondo’ amene adzatsatire Khristu?

15 Buku la Chivumbulutso limanena zimene zidzachitike Mfumuyi ikadzabwera “ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu” kudzapereka chiweruzo. Limati: “Ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera. Wokwerapo wake dzina lake linali Wokhulupirika ndi Woona. Iyeyo anali kuweruza ndi kumenya nkhondo mwachilungamo. Komanso magulu ankhondo amene anali kumwamba, anali kumutsatira pamahatchi oyera, atavala zovala zapamwamba, zoyera bwino, za mbee! M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo. Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa cha mkwiyo waukulu wa Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chiv. 19:11, 14, 15.

16 Kodi ndani ali ‘m’magulu ankhondo’ amene adzatsatire Khristu? Pa nthawi imene Yesu ankamangirira lupanga lake n’kuthamangitsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba, anali limodzi ndi “angelo ake.” (Chiv. 12:7-9) Choncho tikhoza kunena kuti pa nkhondo ya Aramagedo, angelo oyera adzakhala m’magulu ankhondo a Khristu. Koma kodi pali enanso amene adzamenye nawo? Yesu analonjeza abale ake odzozedwa kuti: “Amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatira zochita zanga kufikira mapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu. Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo, ngati imenenso ine ndailandira kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa  ngati mbiya zadothi.” (Chiv. 2:26, 27) Choncho odzozedwa, amene pa nthawiyo adzakhala atapita kale kumwamba, adzakhalanso m’magulu ankhondo a Khristu. Odzozedwawa adzakhala limodzi ndi Yesu pamene azidzachita “zinthu zochititsa mantha” pokusa mitundu ya anthu ndi ndodo yachitsulo.

MFUMUYI IDZAPAMBANA PA NKHONDO

17. Kodi hatchi yoyera imene Khristu wakwera ikuimira chiyani? (b) Kodi lupanga ndi uta zikuimira chiyani?

17 Werengani Salimo 45:5. Mfumuyi yakwera pahatchi yoyera. Hatchiyi ikuimira nkhondo yoyera komanso yolungama pamaso pa Yehova. (Chiv. 6:2; 19:11) Kuwonjezera pa lupanga, Mfumuyi yatenganso uta. Baibulo limanena kuti: “Nditayang’ana, ndinaona hatchi yoyera. Wokwerapo wake ananyamula uta. Iye anapatsidwa chisoti chachifumu, ndi kupita kukagonjetsa adani ake ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nawo.” Lupanga ndi uta zikuimira zinthu zimene Khristu adzagwiritse ntchito popereka chiweruzo kwa adani ake.

Mbalame zidzaitanidwa kuti ziyeretse dziko(Onani ndime 18)

18. Kodi ‘kuthwa’ kwa “mivi” ya Khristu kudzaonekera bwanji?

18 Wamasalimo anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa polosera kuti ‘mivi ya Mfumuyi ndi yakuthwa ndipo idzalasa mitima ya adani ake’ komanso idzachititsa kuti ‘mitundu ya anthu igwe pamapazi ake.’ Nkhondoyi idzamenyedwa padziko lonse lapansi. Paja Yeremiya analosera kuti: “Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi.” (Yer. 25:33) Ulosi winanso wofanana ndi umenewu umanena kuti: “Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zouluka chapafupi m’mlengalenga, kuti: ‘Bwerani kuno, dzasonkhaneni ku phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo, kuti mudzadye minofu ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu, ya mahatchi ndi ya okwerapo ake, ndi minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.’”—Chiv. 19:17, 18.

19. Kodi Khristu ‘adzapambana’ bwanji nkhondo yake?

19 Khristu atawononga dziko loipa la Satanali adzapitiriza kumenya nkhondo yake ndipo ‘adzapambana mu ulemerero wake.’ (Sal. 45:4) Iye adzamaliza kugonjetsa adani akewo poponya Satana ndi ziwanda zake m’phompho ndipo adzakhala mmenemo pa nthawi yonse ya Ulamuliro wa Zaka 1,000. (Chiv. 20:2, 3) Satana ndi ziwanda zake akadzatsekeredwa, adzangokhala ngati afa ndipo sadzasokonezanso anthu padzikoli. Anthuwo azidzamvera Mfumu yawo ya ulemerero popanda vuto lililonse. Koma nthawi yosintha dzikoli kuti likhale paradaiso isanafike, anthu onse adzasangalalanso ndi zinthu zina limodzi ndi Mfumuyi komanso olamulira anzake. M’nkhani yotsatira tikambirana zinthu zosangalatsa zimenezi.