Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  February 2014

 KALE LATHU

Padutsa Zaka 100 Tsopano

Padutsa Zaka 100 Tsopano

“Zikungokhala ngati tikuona M’bale Russell pamasom’pamaso!”—Anatero mmodzi wa anthu amene anaonera filimuyo mu 1914.

PADUTSA zaka 100 tsopano kuchokera pamene “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” linayamba kuonetsedwa. Filimuyi inakonzedwa n’cholinga choti ithandize anthu kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Inathandizanso anthu kukhulupirira kuti Yehova ndi amene analenga zinthu. Pa nthawiyo, anthu ambiri sankakhulupirira zimenezi chifukwa chosokonezedwa ndi maphunziro apamwamba komanso chikhulupiriro chakuti zamoyo zinangokhalako zokha.

M’bale Charles T. Russell, amene ankatsogolera gulu la Ophunzira Baibulo, ankafufuzafufuza njira yabwino komanso yachangu kwambiri yophunzitsira anthu choonadi cha m’Baibulo. Pa nthawiyo, gululi linali litafalitsa mabuku ndi magazini kwa zaka zoposa 30. Ndiyeno anatulukira njira yatsopano yogwiritsira ntchito filimu.

ANAFALITSA UTHENGA POGWIRITSA NTCHITO FILIMU

Cha m’ma 1890 mafilimu opanda mawu anayamba kuonetsedwa. Komanso mu 1903, filimu yachipembedzo inaonetsedwa m’tchalitchi chinachake mumzinda wa New York. Choncho pamene M’bale Russell ankayamba kupanga “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” mu 1912, anthu anali atangoyamba kumene kupanga mafilimu. Iye anazindikira kuti mafilimu angaphunzitse uthenga wa m’Baibulo m’njira yapadera kuposa mabuku.

Filimu ya “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” inali ya maola 8 ndipo ankaionetsa m’zigawo zinayi. Inali ndi nkhani 96 zokambidwa ndi munthu wina wodziwika, yemwe anali ndi mawu abwino kwambiri. M’filimuyi munalinso nyimbo zambiri. Akatswiri oonetsa mafilimu ankaika mawu ndi nyimbo pogwiritsa ntchito galamafoni ndipo pa nthawi imodzimodziyo ankasonyeza zithunzi ndi filimu za nkhani zodziwika za m’Baibulo.

“Filimuyi inkasonyeza zinthu kuyambira pa kulengedwa kwa nyenyezi mpaka zochitika za mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu.”—F. Stuart Barnes ndi amene ananena zimenezi ndipo mu 1914 anali ndi zaka 14

Zinthu zambiri za filimuyi anazigula ku makampani opanga mafilimu. Akatswiri ochokera m’mizinda ya Philadelphia, New York, Paris ndi London ndi amene anajambula zithunzi za filimuyi. Nawonso anthu ogwira ntchito ku Beteli anathandiza pojambula  zinthunzi ndiponso kukonza zinthu zimene zinawonongeka. Kuwonjezera pa mbali za filimu zimene anagula, anajambulanso mbali zina mumzinda wa Yonkers ku New York. Ndipo abale ena anasewera mbali ya Abulahamu, Isaki ndiponso mngelo amene analetsa Abulahamu kuti asapereke mwana wake nsembe.—Gen. 22:9-12.

Anthu ophunzitsidwa bwino ankaonetsa filimu yaitaliyi m’njira yoti zithunzi zambirimbiri zizigwirizana ndi mawu komanso nyimbo zake

Mnzake wina wa M’bale Russell anauza atolankhani a nyuzipepala kuti kugwiritsa ntchito filimu “kuthandiza anthu ambiri kuti ayambe kuchita chidwi ndi Malemba kuposa njira ina iliyonse imene inagwiritsidwapo ntchito.” Kodi atsogoleri a matchalitchi anasangalala ndi njira yapadera yothandiza anthu kuphunzira Baibulo imeneyi? Ayi. Ambiri anatsutsa kwambiri filimuyi moti ena anayesa m’njira zosiyanasiyana kuti alepheretse anthu kuionera. Kumalo ena amene anthu ankaonera filimuyi, abusa ena anakonza zoti magetsi azimitsidwe kumeneko.

Alongo ena ochokera m’mipingo yapafupi ankasankhidwa kuti azipereka mapepala okhala ndi zithunzi za mu filimuyi

Anthu ankapatsidwa mabaji olembedwa kuti “Pax,” omwe ankakhala ndi chithunzi cha Yesu ali mnyamata. Mawu akuti “Pax” amatanthauza kuti “mtendere.” Zimenezi zinkakumbutsa anthu ovala mabajiwo kuti ayenera kukhala “ana a mtendere”

Ngakhale zinali choncho, anthu ambirimbiri ankasonkhana kuti aonere filimu yaulereyi. M’dziko la United States, filimuyi inkaonetsedwa m’mizinda 80 tsiku lililonse. Kwa anthu ambiri kanali koyamba kuonera filimu yokhala ndi mawu. Filimuyi inasonyeza mwanapiye akutuluka m’dzira komanso duwa lokongola likutseguka. Inalinso ndi nkhani zokhudza chilengedwe zimene asayansi anali atatulukira pa nthawiyo ndipo zinkasonyeza bwino nzeru za Yehova. Monga tanenera kumayambiriro kwa nkhaniyi, munthu wina ataona M’bale Russell m’filimuyi anati: “Zikungokhala ngati tikuona M’bale Russell pamasom’pamaso!”

NJIRA YOSAIWALIKA YOPHUNZITSIRA ANTHU BAIBULO

“Sewero la Pakanema la Chilengedwe” linayamba kuonetsedwa pa January 11, 1914 mumzinda wa New York m’chinyumba ichi cha Ophunzira Baibulo

Katswiri wina wa zamafilimu dzina lake Tim Dirks ananena kuti “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” inali “filimu yoyamba kukhala ndi mawu komanso zithunzi zapadera.” Mafilimu ena amene anatulutsidwa pa nthawiyo ankakhala ndi zina mwa zinthuzi koma osati zonse. Komanso ambiri mwa mafilimuwo sanali onena za Baibulo. Palibenso filimu imene inaoneredwa ndi anthu ambiri kuposa imeneyi. M’chaka choyamba chokha, anthu okwana 9 miliyoni anaionera ku North America, ku Ulaya, ku Australia, ndi ku New Zealand.

Filimuyi anayamba kuionetsa pa January 11, 1914 mumzinda wa New York. Patangopita miyezi 7, nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayamba. Koma anthu ambiri m’mayiko osiyanasiyana ankasonkhanabe kuti aionere ndipo ankalimbikitsidwa kwambiri akaona madalitso amene Ufumu udzabweretse. Kunena zoona, kupanga filimu ya “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” mu 1914, chinali chinthu chapadera kwambiri.

Ku North America kunali maseti 20 a zipangizo kuti azionetsa filimuyi malo osiyanasiyana