Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  January 2014

Lambirani Yehova, Mfumu Yamuyaya

Lambirani Yehova, Mfumu Yamuyaya

“Kwa Mfumu yamuyaya . . . kupite ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya.”—1 TIM. 1:17.

1, 2. (a) Kodi “Mfumu yamuyaya” ndi ndani nanga n’chifukwa chiyani dzinali ndi lomuyenera? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) N’chiyani chimatichititsa kukonda kwambiri Yehova?

KU SWAZILAND, Mfumu Sobhuza Yachiwiri inalamulira dzikolo kwa zaka pafupifupi 61. Si mafumu ambiri amene amalamulira kwa nthawi yaitali chonchi masiku ano. Komatu pali mfumu ina imene ulamuliro wake ndi wautali kuposa wa Mfumu Sobhuza chifukwa singafe. Baibulo limanena kuti mfumuyi ndi “Mfumu yamuyaya.” (1 Tim. 1:17) Wamasalimo anatchula dzina la Mfumuyi ponena kuti: “Yehova ndi Mfumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.”—Sal. 10:16.

2 Chifukwa cha zimenezi, ulamuliro wa Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi wa anthu. Koma timakonda kwambiri Yehova chifukwa chakuti amalamulira bwino. Mfumu ina imene inalamulira Aisiraeli kwa zaka 40 inatamanda Mulungu ponena kuti: “Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha. Yehova wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba. Ndipo ufumu wake ukulamulira chilichonse.” (Sal. 103:8, 19) Koma sikuti Yehova wangokhala Mfumu chabe. Iye ndi Atate wathu wakumwamba ndipo amatikonda kwambiri. Ndiyeno tingafunse mafunso awiri awa: Kodi Yehova amachita bwanji zinthu ngati Atate wathu? Kodi iye wasonyeza bwanji kuti ndi Mfumu kuchokera pamene zinthu zinasokonekera mu Edeni? Mayankho a mafunso amenewa akhoza kutilimbikitsa kukonda kwambiri Yehova komanso kumulambira ndi mtima wonse.

 BANJA LA MFUMU YAMUYAYA

3. Kodi mwana woyamba wa Yehova ndi ndani, nanga ndi “ana” ena ati amene analengedwa?

3 Yehova ayenera kuti anasangalala kwambiri atalenga Mwana wake wobadwa yekha ndipo sankamupondereza. M’malomwake, ankamukonda kwambiri ndipo anamupempha kuti amuthandize kulenga ana enanso angwiro. (Akol. 1:15-17) Ana ena amene analenga anali angelo mamiliyoni ambiri. Baibulo limanena kuti angelowo ndi ‘atumiki a Mulungu ochita chifuniro chake.’ Angelo amatumikira Mulungu mosangalala ndipo iye amawalemekeza powatchula kuti “ana” ake. Iwo ndi ana a Yehova akumwamba koma iye analenganso ana ena padziko lapansi.—Sal. 103:20-22; Yobu 38:7.

4. Kodi Mulungu anachita zotani polenga ana ake padzikoli?

4 Yehova atalenga kumwamba ndi dziko lapansi, analenganso ana ena. Poyamba, anakonza dziko lapansi kuti likhale lokongola kwambiri komanso malo abwino okhalamo. Kenako analenga mwamuna woyamba, Adamu. Anamulenga m’chifaniziro chake ndipo anali cholengedwa chapadera kwambiri padzikoli. (Gen. 1:26-28) Yehova ankayembekezera kuti Adamu azimumvera popeza iye anali Mlengi wake. Monga Atate, Yehova anapereka malangizo onse m’njira yachikondi ndiponso mokoma mtima. Malangizowa sanali owaphera ufulu ngakhale pang’ono.—Werengani Genesis 2:15-17.

5. Kodi Mulungu anachita chiyani kuti anthu adzaze dziko lapansi?

5 Mosiyana ndi mafumu ambiri a padzikoli, Yehova amapereka maudindo kwa atumiki ake ndipo amawaona ngati ana ake odalirika. Mwachitsanzo, anapatsa Adamu udindo woyang’anira zinyama ndiponso ntchito yosangalatsa yozipatsa mayina. (Gen. 1:26; 2:19, 20) Mulungu sanalenge anthu mamiliyoni ambiri kuti adzaze dzikoli. M’malomwake, analenga Hava n’kumupereka kwa Adamu kuti akhale mnzake womuyenerera. (Gen. 2:21, 22) Kenako anapatsa anthu awiriwa mwayi woti abereke ana n’kudzaza dziko. Popeza anali angwiro, akanafutukula munda wokongola wa Edeni mpaka dziko lonse likanakhala Paradaiso. Iwo akanalambira Yehova limodzi ndi angelo kumwamba monga banja limodzi mpaka muyaya. Zimenezitu zikanakhala zosangalatsa kwabasi. Powapatsa mwayi umenewu, Yehova anasonyeza kuti ndi Atate wachikondi kwambiri.

ANA ENA ANAKANA ULAMULIRO WA MULUNGU

6. (a) Kodi ana a Mulungu anayamba bwanji kumupandukira? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova sanasiye kukhala Mfumu?

6 Koma n’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava sanafune kuti Yehova aziwalamulira. M’malomwake anasankha kutsatira Satana, amene ndi mwana wopanduka wa Mulungu. (Gen. 3:1-6) Chifukwa chosamvera Mulungu, iwo ndiponso ana awo anakumana ndi mavuto ambiri kuphatikizapo imfa. (Gen. 3:16-19; Aroma 5:12) Choncho pa nthawiyo padziko lapansi panalibe ana omvera Mulungu. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti iye anasiya kukhala Mfumu ya anthu padzikoli? Ayi. Mulungu anasonyeza kuti ali ndi mphamvube pothamangitsa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni. Iye anaika akerubi panjira yolowera m’mundawo kuti anthuwo asabwereremo. (Gen. 3:23, 24) Koma Mulungu anasonyezanso kuti ndi bambo wachikondi potsimikizira kuti cholinga chake chokhala ndi ana omvera kumwamba ndiponso padziko lapansi chidzakwaniritsidwa. Iye analonjeza za mbewu imene idzawononge Satana n’kuthetsa mavuto onse obwera chifukwa cha uchimo wa Adamu.—Werengani Genesis 3:15.

7, 8. (a) Kodi zinthu zinali bwanji pofika m’nthawi ya Nowa? (b) Kodi Yehova anachita chiyani kuti ayeretse dziko lapansi komanso kupulumutsa anthu?

 7 Patapita zaka zambiri, anthu ena anakhala okhulupirika kwa Yehova. Ena mwa iwo anali Abele ndi Inoki. Koma anthu ambiri sanafune kuti Yehova akhale Atate komanso Mfumu yawo. Pofika m’nthawi ya Nowa, dziko lapansi linali ‘litadzaza ndi chiwawa.’ (Gen. 6:11) Kodi izi zikutanthauza kuti Yehova analibenso mphamvu pa zochitika zapadzikoli? Tikhoza kupeza yankho tikaona zimene zinadzachitika pambuyo pake.

8 Poyamba, tiyeni tikambirane za Nowa. Yehova anamupatsa malangizo komanso mapulani omangira chingalawa n’cholinga choti iye ndi banja lake apulumuke. Koma Mulungu anasonyeza kuti amakonda anthu onse padzikoli popatsa Nowa ntchito yoti akhale “mlaliki wa chilungamo.” (2 Pet. 2:5) Mosakayikira, Nowa ankauza anthu kuti alape komanso ankawachenjeza kuti Mulungu awononga dziko, koma anthuwo sanamvere. Kwa zaka zambiri, Nowa ndi banja lake ankakhala pakati pa anthu achiwawa ndiponso amakhalidwe oipa kwambiri. Koma monga Atate wachikondi, Yehova anateteza ndi kudalitsa Nowa ndi banja lake. Pamene Yehova anabweretsa Chigumula, anasonyeza anthu ndiponso angelo opandukawo kuti iye adakali Mfumu yaikulu.—Gen. 7:17-24.

Yehova wakhala akusonyeza kuti ndi Mfumu (Onani ndime 6, 8, 10, 12, 17)

ULAMULIRO WA YEHOVA PAMBUYO PA CHIGUMULA

9. Kodi Yehova anapatsanso anthu mwayi uti pambuyo pa Chigumula?

9 Nowa ndi banja lake atatuluka m’chingalawa anayamba kukhala padziko loyeretsedwa komanso kupuma mpweya wabwino. Iwo ayenera kuti anayamikira kwambiri Yehova chifukwa chowasamalira komanso kuwateteza. Nthawi yomweyo Nowa anamanga guwa n’kupereka nsembe kwa Yehova. Mulungu anadalitsa Nowa ndi banja lake n’kuwauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Gen. 8:20-22; 9:1) Apatu anthu anapatsidwa mwayi winanso woti azilambira Mulungu mogwirizana komanso adzaze dziko lapansi.

10. (a) Kodi anthu anayambanso bwanji kupandukira Yehova pambuyo pa Chigumula, nanga zinayambira kuti? (b) Kodi Yehova anachita zotani kuti cholinga chake chithekebe?

10 Komabe anthu amene anapulumuka Chigumula sanali angwiro ndipo Satana komanso angelo opanduka aja ankayesetsabe kuwasokoneza. Pasanapite nthawi yaitali, anthu ena anayambanso kupandukira ulamuliro wabwino wa Yehova. Mwachitsanzo, Nimurodi, yemwe anali chidzukulu cha mwana wa Nowa, anachita zinthu zoipa kwambiri zotsutsana ndi ulamuliro wa Yehova. Baibulo limanena kuti Nimurodi anali “mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.” Iye anamanga mizinda ikuluikulu, monga Babele, ndipo anadzipatsa ufumu “m’dziko la Sinara.” (Gen. 10:8-12) Kodi Mfumu yamuyaya inachita zotani itaona kuti Nimurodi akuchita zinthu zosemphana ndi cholinga  chake choti anthu ‘adzaze dziko lapansi’? Mulungu anangosokoneza chilankhulo cha anthuwo. Izi zinachititsa kuti mapulani a Nimurodi athere pomwepo ndipo anthuwo ‘anabalalika padziko lonse lapansi.’ Koma iwo anapitiriza kulambira konyenga m’madera amene anabalalikirawo ndipo anapitiriza kukhala ndi mafumu.—Gen. 11:1-9.

11. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika kwa Abulahamu?

11 Ngakhale kuti anthu ambiri ankalambira milungu yonyenga pambuyo pa Chigumula, panali anthu ena amene ankatumikira Yehova mokhulupirika. Mmodzi mwa iwo anali Abulahamu. Iye anamvera Mulungu n’kuchoka mumzinda wotukuka wa Uri n’kumakakhala m’mahema kwa zaka zambiri. (Gen. 11:31; Aheb. 11:8, 9) Pa moyo wake wam’mahema, Abulahamu ankakhala pakati pa mafumu osiyanasiyana ndipo ena ankakhala m’mizinda yokhala ndi mipanda. Koma Yehova anateteza Abulahamu ndi banja lake. Pofotokoza mmene Yehova ankawatetezera monga Atate wawo, wamasalimo anati: “Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awachitire zachinyengo, koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.” (Sal. 105:13, 14) Yehova anali wokhulupirika kwa Abulahamu ndipo anamulonjeza kuti: ‘Mwa iwe mudzatuluka mafumu.’—Gen. 17:6; Yak. 2:23.

12. (a) Kodi Yehova anasonyeza bwanji mphamvu zake ku Iguputo? (b) Kodi zimenezi zinathandiza bwanji anthu ake?

12 Lonjezo limeneli anauzanso Isaki, yemwe anali mwana wa Abulahamu, komanso Yakobo, yemwe anali mdzukulu wake. Anawauza kuti adzawadalitsa komanso kuti mwa iwo mudzatuluka mafumu. (Gen. 26:3-5; 35:11) Koma izi zisanachitike, ana a Yakobo anakhala akapolo ku Iguputo. Kodi izi zinasonyeza kuti Yehova sadzakwaniritsa lonjezo lake kapena kuti wasiya kusonyeza mphamvu zake padzikoli monga mfumu? Ayi ndithu. Nthawi yake itakwana, Yehova anasonyeza kuti ndi wamphamvu polanga Farao yemwe anali waliuma. Aisiraeliwo anakhulupirira Yehova ndipo iye anawapulumutsa m’njira yodabwitsa kwambiri pa Nyanja Yofiira. Apatu Yehova anasonyeza kuti ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. Monga Atate wachikondi, anagwiritsa ntchito mphamvu zake poteteza anthu ake.—Werengani Ekisodo 14:13, 14.

YEHOVA ANAKHALA MFUMU YA AISIRAELI

13, 14. (a) Kodi m’nyimbo ya Aisiraeli munali mawu ati onena za Yehova monga mfumu? (b) Kodi Mulungu analonjeza Davide za chiyani pa nkhani ya ufumu?

13 Aisiraeli atangopulumutsidwa ku Iguputo, anaimba nyimbo yotamanda Yehova. Nyimboyi ili mu chaputala 15 cha Ekisodo ndipo pavesi 18 pali mawu akuti: “Yehova adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale. Adzalamulira mpaka muyaya.” Yehova anakhaladi Mfumu ya mtundu watsopano wa Aisiraeli. (Deut. 33:5) Koma Aisiraeliwo ankafunanso kukhala ndi mfumu yoti aziiona. Patadutsa zaka 400 kuchokera pamene anatulutsidwa mu Iguputo, iwo anapempha Mulungu kuti awapatse munthu woti akhale mfumu yawo kuti azifanana ndi mitundu ina yowazungulira. (1 Sam. 8:5) Ngakhale zinali choncho, Yehova anakhalabe Mfumu ndipo umboni wake unaonekera pa nthawi ya ulamuliro wa Davide amene anali mfumu yachiwiri ya Aisiraeli.

14 Davide anabweretsa ku Yerusalemu likasa la pangano lomwe linali lopatulika. Pa nthawiyi anthu anasangalala kwambiri ndipo Alevi anaimba nyimbo yotamanda Mulungu. M’nyimboyo munali mawu amene ali pa 1 Mbiri 16:31 akuti: “Anene pakati pa anthu a mitundu ina kuti: ‘Yehova wakhala mfumu!’” Apatu ena angadabwe kuti, ‘Popeza Yehova ndi Mfumu yamuyaya, zikutheka bwanji kuti anakhala Mfumu pa nthawiyo?’ Yehova amakhala Mfumu akachita zinthu zosonyeza kuti iye ndi amene akulamulira kapena akasankha wina kuti amuimire pa nthawi inayake kapena pothana ndi vuto linalake.  Mfundo imeneyi ingatithandize kumvetsa mfundo zina zokhudza ulamuliro wake. Davide asanamwalire, Yehova anamulonjeza kuti ufumu wake sudzatha. Ananena kuti: “Ndidzautsa mbewu yako yobwera pambuyo pako, imene idzatuluka m’chiuno mwako. Ndipo ndidzakhazikitsadi ufumu wake.” (2 Sam. 7:12, 13) Ndiyeno mawuwa anadzakwaniritsidwa patadutsa zaka zoposa 1,000. Kodi ndani anadzakhala “mbewu” yolonjezedwayo, nanga anayamba liti kulamulira?

YEHOVA ANASANKHA MFUMU YATSOPANO

15, 16. (a) Kodi Yesu anadzozedwa liti kuti akhale Mfumu? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene Yesu anachita padzikoli zokhudza Ufumu wake?

15 M’chaka cha 29 C.E., Yohane M’batizi anayamba kulalikira kuti “ufumu wakumwamba wayandikira.” (Mat. 3:2) Pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane, Yehova anamudzoza kukhala Mesiya komanso kuti adzakhale Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Yehova anasonyeza kuti amakonda Yesu monga Mwana wake ponena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.”—Mat. 3:17.

16 Pa utumiki wake wonse, Yesu ankalemekeza Atate wake. (Yoh. 17:4) Iye anachita zimenezi polalikira za Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43) Anauzanso ophunzira ake kuti azipempherera Ufumuwo kuti ubwere. (Mat. 6:10) Popeza iye anasankhidwa kukhala Mfumu, Yesu anauza anthu amene ankamutsutsa kuti: “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.” (Luka 17:21) Ndiyeno madzulo oti aphedwa mawa lake, Yesu anachita “pangano la ufumu” ndi atumwi ake. Apa anapatsa ophunzira ake okhulupirika mwayi wokalamulira naye mu Ufumu wa Mulungu.—Werengani Luka 22:28-30.

17. Kodi Yesu anayamba kulamulira mu ufumu uti nthawi ya atumwi, nanga anafunika kudikirabe chiyani?

17 Kodi Yesu anayamba liti kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu? Sikuti anayamba pa nthawi imene anali padzikoli. Atangochita pangano ndi atumwi aja, Yesu anaphedwa tsiku lotsatira ndipo atumwiwo anabalalika. (Yoh. 16:32) Koma monga mwa nthawi zonse, Yehova anasonyezabe kuti adakali Mfumu. Tikutero chifukwa chakuti pa tsiku lachitatu, iye anaukitsa Mwana wakeyo. Ndiyeno pa Pentekosite mu 33 C.E., Yesu anakhazikitsa ufumu kuti azilamulira mpingo wa Akhristu odzozedwa. (Akol. 1:13) Koma iye anafunika kudikirabe kuti adzayambe kulamulira padziko lonse lapansi monga “mbewu” yolonjezedwa. Paja Yehova anauza Mwana wakeyu kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”—Sal. 110:1.

LAMBIRANI MFUMU YAMUYAYA

18, 19. (a) Kodi timalimbikitsidwa kuchita chiyani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

18 Kwa zaka masauzande ambiri, ulamuliro wa Yehova wakhala ukutsutsidwa kumwamba komanso padziko lapansi. Koma Yehova wakhala akusonyezabe kuti ndi Mfumu ya chilengedwe chonse. Iye ndi Atate wachikondi ndipo ankateteza komanso kusamalira atumiki ake okhulupirika monga Nowa, Abulahamu ndiponso Davide. Mosakayikira, zimenezi zimatilimbikitsa kugonjera Mfumu yathu ndiponso kuyesetsa kukhala naye pa ubwenzi wabwino.

19 Koma tikhoza kudzifunsa kuti: Kodi Yehova wakhala bwanji Mfumu masiku ano? Kodi tingatani kuti tigonjere mokhulupirika Ufumu wa Yehova ndiponso kuti tikhale ana angwiro a m’banja lake? Kodi tikamapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere, timakhala tikupempha chiyani kwenikweni? Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.