Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) January 2014

Magaziniyi ikutitsimikizira kuti kuyambira kale Yehova wakhala Mfumu. Ikutithandizanso kudziwa zambiri zokhudza Ufumu wa Mesiya ndiponso zimene Ufumuwo wachita.

Anadzipereka ndi Mtima Wonse Kumadzulo kwa Africa

Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Akhristu ena ku Ulaya kuti asamukire kumadzulo kwa Africa, nanga zinthu zikuwayendera bwanji kumeneko?

Lambirani Yehova, Mfumu Yamuyaya

Kuphunzira zimene Yehova wachita monga Atate wathu komanso monga Mfumu kungakuthandizeni kuti muzimukonda kwambiri.

Kodi Ufumu Umene Walamulira kwa Zaka 100 Umakukhudzani Bwanji?

Kodi Ufumu wa Mulungu ungatithandize bwanji? Werengani kuti mudziwe zimene Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ikuchita poyeretsa ndiponso kuphunzitsa anthu ake. Muonanso mmene Mfumuyo yasinthira zinthu m’gulu la Mulungu.

Achinyamata, Muzisankha Zochita Mwanzeru

Achinyamata ambiri amene ndi odzipereka kwa Mulungu akusangalala kwambiri pothandiza anthu ena. Kodi mungatani kuti muchite zambiri potumikira Yehova?

Tumikirani Yehova Masiku Oipa Asanafike

Kodi Akhristu achikulire ali ndi mwayi wapadera uti wowonjezera utumiki wawo?

Kodi Ufumu wa Mulungu Ubwera Liti?

N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti posachedwapa Mfumu yoikidwa ndi Mulungu idzaonetsetsa kuti chifuniro cha Mulungu chachitika?

Zimene Ndinasankha Ndili Mwana

Mnyamata wina wa ku Columbus, Ohio, U.S.A. anaganiza zophunzira Chikambodiya. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Kodi zimenezi zinakhudza bwanji zimene anadzachita m’tsogolo?