Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) December 2013

Magaziniyi ikufotokoza zinthu zimene zingatithandize kuti chikhulupiriro chathu chisafooke. Ikufotokozanso tsiku limene tiyenera kuchita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye komanso kufunika kwa mwambowu.

Yehova Anawateteza Pamene Ankazemba M’mapiri

Kodi a Mboni za Yehova ku Germany ankalandira bwanji mabuku ofotokoza Baibulo pa nthawi imene Hitler ndi chipani cha Nazi ankalamulira? Kodi kuzembetsa mabuku kunali koopsa bwanji?

“Musafulumire Kugwedezeka pa Maganizo Anu”

Kodi kalata yachiwiri imene Paulo analembera Atesalonika inali ndi machenjezo a pa nthawi yake ati? N’chiyani chingatithandize kuti tisapusitsidwe?

Kodi Mungapereke Chiyani pa Ntchito ya Ufumu?

Onani zimene tingachite kuti tigwiritse ntchito nthawi, ndalama, mphamvu ndiponso luso lathu pa ntchito ya Ufumu.

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunsowa kuti muone ngati mukukumbukira.

‘Tsikuli Lidzakhala Chikumbutso Chanu’

Kodi Akhristu ayenera kudziwa zinthu ziti zokhudza Pasika? Kodi mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndi wofunika bwanji kwa tonsefe?

“Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”

Kodi deti la Chakudya Chamadzulo cha Ambuye limadziwika bwanji? Kodi mkate ndi vinyo zimaimira chiyani?

Musataye Mtima Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Wamwalira

Munthu amavutika kwambiri ngati mwamuna kapena mkazi wake wamwalira ndipo chisoni chake chimatenga nthawi. Koma chiyembekezo chakuti akufa adzauka chimatilimbikitsa.

Mlozera Nkhani wa Magazini a Nsanja ya Olonda a 2013

Onani mlozera nkhani kuti mudziwe nkhani zimene zafalitsidwa m’magazini a Nsanja ya Olonda mu 2013.