Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) October 2013

M’magazini ino muli nkhani imene ikufotokoza mmene tingathandizire anthu kumvetsa kuti Mlengi wathu ndi wamphamvu ndiponso wanzeru. Komanso tiphunzira mmene tingachitire zinthu mogwirizana ndi pemphero la Yesu.

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Philippines

Onani zimene zinalimbikitsa anthu ena kuti asiye ntchito yawo komanso kugulitsa katundu wawo n’kukakhala kumadera akumidzi ku Philippines.

Chilengedwe Chimatithandiza Kukhulupirira Kwambiri Mulungu

Nkhaniyi itithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Mlengi komanso kuti tithandize ena kumudziwa bwino.

“Tumikirani Yehova Monga Akapolo”

Kodi tingapewe bwanji kukhala akapolo a Satana? Kodi Yehova amadalitsa bwanji akapolo ake okhulupirika?

MBIRI YA MOYO WANGA

Tadalitsidwa Chifukwa Chodalira Yehova

Malcolm ndi Grace Allen atumikira Yehova zaka zoposa 75 aliyense. Zimene zawachitikira pa moyo wawo zikusonyeza kuti aona kuti Yehova amadalitsa anthu amene amamudalira.

Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Pemphero Limene Linakonzedwa Bwino?

Kodi tikuphunzira chiyani pa pemphero la Alevi? Kodi tingatani kuti tizipereka mapemphero okonzedwa bwino?

Muzichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Yesu

M’pemphero lake, Yesu anayamba kutchula zinthu zokhudza chifuniro cha Yehova kenako zofuna zake. Kodi tingatani kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lakeli?

Kodi Mungatani Kuti Muchenjeze Anthu Ambiri?

Onani zimene anthu ena akuchita kuti agwiritse ntchito mpata uliwonse kuti alalikire anthu amene angakumane nawo tsiku lililonse.