Malinga ndi Yohane 11:35, n’chifukwa chiyani Yesu anagwetsa misozi asanaukitse Lazaro?

Munthu amene timamukonda akamwalira timagwetsa misozi chifukwa chodziwa kuti timusowa kwa nthawi yaitali. N’zoona kuti Yesu ankakonda kwambiri Lazaro. Koma Lazaroyo atamwalira, Yesu sanalire chifukwa choti amusowa. Zikuoneka kuti analira chifukwa chomvera chisoni achibale komanso anzake a Lazaro.—Yoh. 11:36.

Yesu atamva kuti Lazaro akudwala, sanapite nthawi yomweyo kukamuchiritsa. Yohane anati: “[Yesu] atamva kuti Lazaro akudwala, anakhalabe masiku awiri kumalo kumene iye anali.” (Yoh. 11:6) N’chifukwa chiyani Yesu sanapiteko mwamsanga? Anachita dala zimenezi. Iye anati: “Kudwala kumeneku si kwa imfa chabe, koma n’kopatsa Mulungu ulemerero, kuti mwa kudwalako, Mwana wa Mulungu alemekezeke.” (Yoh. 11:4) Kodi Yesu ankatanthauza chiyani ponena kuti matenda a Lazaro sanali a imfa chabe? Ankatanthauza kuti imfa ya Lazaro idzathandiza kuti ‘Mulungu alandire ulemerero.’ Yesu ankadziwa kuti adzachita chozizwitsa poukitsa mnzakeyo.

Pokambirana ndi ophunzira ake, Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. N’chifukwa chake anawauza kuti: “Ndikupita kumeneko kukamudzutsa [Lazaro] ku tulo take.” (Yoh. 11:11) Yesu ankadziwa kuti atha kuukitsa Lazaro ngati mmene mayi amadzutsira mwana amene wagona. Choncho imfa ya Lazaro payokha sikanam’chititsa kuti alire.

Nanga n’chiyani chinam’chititsa kuti agwetse misozi? Tikhoza kupeza yankho la funsoli tikaona nkhani yonseyi. Yesu ataona Mariya, yemwe anali mchemwali wake wa Lazaro, limodzi ndi anthu ena akulira, “anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni.” Yesu anapwetekedwa mtima kwambiri ataona chisoni chimene anzakewo anali nacho. N’chifukwa chake “anadzuma povutika mumtima” ndiponso ‘kugwetsa misozi.’—Yoh. 11:33, 35.

Nkhaniyi imasonyeza kuti Yesu ali ndi mphamvu zoukitsa anzathu amene anamwalira kuti adzasangalale ndi moyo m’dziko latsopano. Ikutithandizanso kuona kuti Yesu amamvera chisoni anthu amene akulira chifukwa choferedwa. Nkhaniyi ikutiphunzitsanso kuti tiyenera kumvera chisoni anthu amene akulira chifukwa choti mnzawo wamwalira.

Yesu ankadziwa kuti aukitsa Lazaro. Koma analirabe chifukwa chokonda kwambiri anzake ndiponso kuwamvera chisoni. Ifenso tikhoza ‘kulira ndi anthu amene akulira’ chifukwa chowamvera chisoni. (Aroma 12:15) Sikuti munthu akamalira ndiye kuti sakhulupirira zoti akufa adzauka. Yesu ankadziwa kuti Lazaro auka, koma anapereka chitsanzo chabwino kwambiri polira chifukwa chomvera chisoni anthu amene anaferedwa.