Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzisankha Zochita Mwanzeru

Muzisankha Zochita Mwanzeru

“Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.”—MIY. 3:5.

1, 2. (a) Kodi mumamva bwanji ngati mukufunika kusankha zochita? (b) Kodi mumaona kuti mumasankha mwanzeru nthawi zonse?

TSIKU lililonse timafunika kusankha zochita pa nkhani zosiyanasiyana. Kodi mumamva bwanji ngati mukufunika kusankha zochita? Anthu ena amakonda kusankha okha zochita. Iwo amaona kuti ndi ufulu wawo ndipo amadana ndi zoti wina awauze nzeru. Koma ena amaopa kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Ndipo ena amafufuza malangizo m’mabuku kapena kwa alangizi, moti nthawi zina amawononga ndalama zambiri kuti apeze malangizowo.

2 Koma ambirife sitili choncho. Timadziwa kuti pa zinthu zina tilibe ufulu wosankha. Komabe pali zinthu zambiri zimene tingasankhe malinga ndi zimene tikufuna. (Agal. 6:5) Ngakhale kuti tili ndi ufulu umenewu, tikudziwa kuti nthawi zina timalephera kusankha mwanzeru.

3. Kodi ndani angatithandize kusankha zochita mwanzeru, koma kodi tingavutike kusankha zochita pa nkhani zotani?

3 Timayamikira kuti Yehova amatipatsa malangizo omveka bwino pa nkhani zambiri zofunika pa moyo wathu. Tikudziwa kuti tikamatsatira malangizo amenewo, tidzasankha zochita zomwe zingasangalatse Yehova komanso kutithandiza. Koma nthawi zina timafunika kusankha zochita pa nkhani zimene Mawu a Mulungu safotokoza zambiri. Kodi n’chiyani chingatithandize kusankha mwanzeru pa nkhani zimenezo? Mwachitsanzo, tikudziwa kuti sitiyenera kuba. (Aef. 4:28) Koma kodi tinganene kuti munthu ndi wakuba ngati wachita chiyani? Kodi timanena kuti munthu waba tikaona mtengo wa chinthu chimene watenga kapena cholinga chake potenga chinthucho? Kodi n’chiyani chingatithandize kusankha bwino pa zinthu zimene Baibulo silifotokoza zambiri?

 TIKHALE OGANIZA BWINO

4. Kodi anthu amakonda kupereka malangizo ati tikafuna kusankha zochita?

4 Mwina nthawi ina pamene tinkafuna kusankha zochita, Mkhristu mnzathu anatiuza kuti tiyenera kuganiza bwino. Malangizo amenewa ndi abwino ndithu. Paja Baibulo limachenjeza kuti: “Aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miy. 21:5) Koma kodi kuganiza bwino n’kutani? Kodi kumangotanthauza kuganizira kwambiri nkhaniyo n’kuyesetsa kuimvetsa bwino tisanasankhe zochita? Zinthu zimenezi n’zofunika koma si zokhazi.—Aroma 12:3; 1 Pet. 4:7.

5. N’chifukwa chiyani anthufe mwachibadwa sitiganiza bwinobwino?

5 Tiyenera kuvomereza kuti tonsefe mwachibadwa sitiganiza bwinobwino. N’chifukwa chiyani zili choncho? Tonsefe tinabadwa ochimwa, choncho maganizo athu ndiponso matupi athu si angwiro. (Sal. 51:5; Aroma 3:23) Chinanso n’chakuti ambirife pa nthawi inayake tinali m’gulu la anthu ochititsidwa “khungu” ndi Satana ndipo sitinkadziwa Yehova kapena mfundo zake zolungama. (2 Akor. 4:4; Tito 3:3) Choncho ngati tidalira nzeru zathu zokha posankha zochita, tikhoza kudzipusitsa. Izi zingachitike ngakhale nkhaniyo titaiganizira kwa nthawi yaitali.—Miy. 14:12.

6. N’chiyani chingatithandize kuti tiziganiza bwino?

6 Mosiyana ndi anthufe, Yehova, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, ndi wangwiro. (Deut. 32:4) Ndipo chosangalatsa n’chakuti watipatsa zinthu zimene zingatithandize kuganiza bwino. (Werengani 2 Timoteyo 1:7.) Akhristufe timafunika kuganiza bwino n’kumachita zinthu mwanzeru. Choncho tiyenera kukhala odziletsa kuti tizipewa maganizo oipa. Komanso tiziyesetsa kutsanzira Yehova ndiponso kuona zinthu mmene iye amazionera.

7, 8. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti munthu akhoza kusankha zinthu mwanzeru ngakhale atapanikizika.

7 Tiyeni tione chitsanzo. Anthu ena amene anasamukira kudziko lina kukagwira ntchito amakonda kutumiza ana awo ang’onoang’ono kwa achibale awo kuti azikawalera. Iwo amachita zimenezi n’cholinga choti apitirize kugwira ntchito. * Mayi wina wogwira ntchito kudziko lina anabereka mwana wamwamuna wokongola. Pa nthawi imeneyo, anayamba kuphunzira Baibulo ndiponso kusintha moyo wake. Anzake ndi achibale ake anayamba kukakamiza mayiyo ndi mwamuna wake kuti atumize mwanayo kwa agogo ake. Komabe kuphunzira Baibulo kunathandiza mayiyo kuzindikira kuti Mulungu anapatsa makolo udindo wolera ana. (Sal. 127:3; Aef. 6:4) Kodi iye anayenera kutsatira zimene anthu ambiri ankamuuzazo? Kapena kodi anayenera kutsatira zimene ankaphunzira m’Baibulo ngakhale kuti zikanasokoneza ntchito yake komanso akananyozedwa ndi anthu ena? Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?

8 Mayiyo atapanikizika kwambiri, anapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kuti amutsogolere. Atakambirana ndi mlongo amene ankamuphunzitsa komanso anthu ena mumpingo, anayamba kuona nkhaniyi mmene Yehova amaionera. Anaganiziranso mfundo yakuti ana ang’onoang’ono amene sakhala ndi makolo awo amatha kusokonezedwa. Ataganizira zimene Malemba amanena pa nkhaniyi, anazindikira kuti si bwino kutumiza mwanayo kwa agogo ake. Mwamuna wakeyo anaona kuti abale ndi alongo ankawathandiza ndipo mwanayo ankasangalala komanso kukula bwino. Kenako nayenso anayamba kuphunzira Baibulo  ndiponso kupezeka pa misonkhano limodzi ndi mkazi wake.

9, 10. Kodi munthu woganiza bwino amatani?

9 Apa tangokambirana chitsanzo chimodzi chokha chosonyeza kuti munthu woganiza bwino samangotsatira zimene iyeyo kapena anthu ena akuona kuti n’zoyenera. Popeza si ife angwiro, maganizo athu ali ngati wotchi yotaya. Tikhoza kukumana ndi mavuto oopsa ngati timangotsatira maganizowo. (Yer. 17:9) Choncho tiyenera kuyesetsa kuti maganizo athu azigwirizana ndi mfundo za Mulungu zomwe n’zodalirika.—Werengani Yesaya 55:8, 9.

10 M’pake kuti Baibulo limatilangiza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.” (Miy. 3:5, 6) Onani kuti palembali pali mawu akuti “usadalire luso lako lomvetsa zinthu” kenako akuti “uzim’kumbukira [Yehova].” Iye ndi amene amaganiza bwino kwambiri. Choncho tisanasankhe zochita, tiziyamba tafufuza m’Baibulo kuti tidziwe maganizo a Mulungu pa nkhaniyo. Ndiyeno tizisankha zinthu mogwirizana ndi maganizo akewo. Choncho tinganene kuti munthu woganiza bwino amatsatira maganizo a Yehova nthawi zonse.

PHUNZITSANI MPHAMVU ZANU ZA KUZINDIKIRA

11. Kodi chofunika n’chiyani kuti munthu aphunzire kusankha zochita mwanzeru?

11 Kusankha zochita mwanzeru ndiponso kuchita zimene mwasankhazo si kophweka. Makamaka anthu amene angoyamba kumene kutumikira Yehova angavutike kwambiri kuchita zimenezi. Baibulo limanena kuti anthu amenewa ali ngati tiana koma akhoza kuphunzira kusankha zinthu mwanzeru. Taganizirani mmene mwana amaphunzirira kuyenda. Iye amaphunzira poyenda timayadi ting’onoting’ono mobwerezabwereza. N’chimodzimodzi ndi munthu amene wangoyamba kumene kutumikira Yehova. Kumbukirani kuti mtumwi Paulo ananena kuti anthu okhwima mwauzimu ‘aphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikira kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera pogwiritsa ntchito mphamvuzo.’ Mawu akuti ‘kuphunzitsa’ ndiponso “pogwiritsa ntchito” amasonyeza kuti munthuyo  amachita zimenezi mwakhama ndiponso mobwerezabwereza. Izi n’zimene anthu atsopano ayenera kuchita.—Werengani Aheberi 5:13, 14.

Tikamasankha mwanzeru pa zinthu za tsiku ndi tsiku, timaphunzitsa mphamvu zathu za kuzindikira (Onani ndime 11)

12. Kodi tingatani kuti tizisankha zochita mwanzeru?

12 Monga tanenera kale, tsiku lililonse timafunika kusankha zochita pa nkhani zing’onozing’ono ndiponso zikuluzikulu. Pa kafukufuku wina, anthu anapeza kuti pafupifupi hafu ya zinthu zimene timachita, timangozichita mwachizolowezi popanda kuziganizira. Mwachitsanzo, tsiku lililonse timasankha zovala zoti tivale. Mukhoza kuona kuti nkhaniyi ndi yaing’ono ndipo mwina mumasankha popanda kuganizira kwambiri, makamaka ngati mukufulumira. Koma ndi bwino kudzifunsa kuti, Kodi zovalazi ndi zoyenera mtumiki wa Yehova? (2 Akor. 6:3, 4) Tikamagula zovala tisamangoganizira za mafashoni amakono koma tiziganiziranso mtengo wake ndiponso ngati ndi zaulemu. Kusankha bwino pa nkhani zoterezi kungatithandize kuphunzitsa mphamvu zathu za kuzindikira. Zimenezi zidzatithandiza kusankhanso mwanzeru pa nkhani zikuluzikulu.—Luka 16:10; 1 Akor. 10:31.

KHALANI NDI MTIMA WOFUNITSITSA KUCHITA ZOYENERA

13. Kodi n’chiyani chimafunika kuti munthu achitedi zimene wasankha?

13 Munthu akhoza kusankha bwino zochita koma nthawi zina chimene chimavuta ndi kutsatira zimene wasankhazo. Mwachitsanzo, anthu ena amafuna atasiya kusuta fodya koma amalephera chifukwa choti palibe chowalimbikitsa kusiya fodyayo. Munthu amafunika kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuchita zimene wasankha. Ndipo kuti achitedi zimene akufunazo pamafunika khama. Koma pali chinthu chinanso chimene chingatithandize pa nkhaniyi. Tiyenera kupemphera kwa Yehova nthawi zonse.—Werengani Afilipi 2:13.

14. N’chiyani chinathandiza Paulo kuchita zinthu zoyenera?

14 Paulo anazindikira mfundo imeneyi chifukwa cha zimene zinkamuchitikira. Pa nthawi ina, iye anadandaula kuti: “Pakuti ndimafuna kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita.” Iye ankadziwa zimene ankafuna kuchita kapena zimene ankayenera kuchita koma nthawi zina panali chinachake chimene chinkamulepheretsa kuchita zimenezi. Iye anati: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu, koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo chimene chili m’ziwalo zanga.” Koma kodi analibiretu mtengo wogwira? Ayi. Paja ananena kuti Mulungu adzamuthandiza kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. (Aroma 7:18, 22-25) M’kalata ina iye analembanso kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afil. 4:13.

15. Kodi kusankha zochita mwanzeru n’kuzitsatira kungatithandize bwanji?

15 Apa taona kuti tiyenera kusankha zochita mwanzeru n’kuzitsatira kuti tisangalatse Mulungu. Kumbukirani zimene Eliya ananena paphiri la Karimeli polankhula ndi anthu olambira Baala komanso Aisiraeli amene anasiya Yehova. Iye anati: “Kodi mukayikakayika mpaka liti? Ngati Yehova ali Mulungu woona m’tsateni, koma ngati Baala ndiye Mulungu woona tsatirani ameneyo.” (1 Maf. 18:21) Aisiraeli ankadziwa zoyenera kuchita koma sanachite zinthuzo chifukwa chokayikakayika. Zaka zambiri izi zisanachitike, Yoswa anapereka chitsanzo chabwino kwambiri. Iye anauza Aisiraeli kuti: “Ngati  kutumikira Yehova kukukuipirani, sankhani lero amene mukufuna kum’tumikira . . . Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.” (Yos. 24:15) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Yoswa ndi anthu amene ankamutsatira anadalitsidwa kwambiri. Iwo analowa m’Dziko Lolonjezedwa, lomwe linali “loyenda mkaka ndi uchi.”—Yos. 5:6.

MUZISANKHA ZOCHITA MWANZERU KUTI MUDALITSIDWE

16, 17. Perekani chitsanzo chosonyeza ubwino wosankha kuchita zinthu zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna.

16 Tiyeni tione chitsanzo cha m’bale amene wangobatizidwa kumene. M’baleyu ndi mkazi wake ali ndi ana atatu ang’onoang’ono. Tsiku lina munthu wina anauza m’baleyu kuti iwo angachite bwino kukayamba ntchito m’kampani ina imene malipiro ake ndi abwino kwambiri. M’baleyo anaganizira za nkhaniyi ndi kuipempherera. Pa nthawiyi m’baleyu anali pa ntchito imene malipiro ake sanali abwino kwenikweni. Iye analowa ntchitoyi n’cholinga choti azipeza mpata wopita ku misonkhano komanso kulowa mu utumiki ndi banja lake. Ankadziwa kuti akayamba ntchito kukampani inayo, zidzatenga nthawi yaitali kuti ayambe kupeza mpata wochita zimenezi. Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?

17 M’baleyu anakana kukalowa ntchitoyo ngakhale kuti inali yamalipiro ambiri. Iye anaona kuti ingamulepheretse kutumikira bwino Yehova. Kodi ananong’oneza bondo chifukwa cha zimene anasankhazo? Ayi sanatero, chifukwa ankaona kuti chofunika kwambiri kwa iye ndi banja lake n’kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu osati malipiro ambiri. M’baleyu ndi mkazi wake anasangalala kwambiri mwana wawo wamkazi wa zaka 10 atawauza kuti amawakonda, amakonda abale ndi alongo komanso amakonda kwambiri Yehova. Ananenanso kuti akufuna kudzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa. Mwanayu ayenera kuti anatengera chitsanzo cha bambo ake omwe ankaona kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wawo ndi kulambira Yehova.

Muzisankha zochita mwanzeru kuti muzisangalala ndi anthu a Mulungu (Onani ndime 18)

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kusankha zochita mwanzeru tsiku ndi tsiku?

18 Kwa zaka zambiri, Yesu Khristu, yemwe ndi Mose Wamkulu, wakhala akutsogolera atumiki a Yehova m’dziko la Satanali, lomwe lili ngati chipululu. Yesu amatchedwanso Yoswa Wamkulu chifukwa posachedwapa awononga dziko loipali ndi kulowetsa otsatira ake m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. (2 Pet. 3:13) Choncho ino si nthawi yoti tiyambirenso kuganizira zinthu zakale, kuzilakalaka kapena kuzichita. Ino ndi nthawi yoti timvetsetse zimene Mulungu akufuna kuti tizichita. (Aroma 12:2; 2 Akor. 13:5) Choncho zimene timasankha kuchita tsiku ndi tsiku zizisonyeza kuti ndifedi oyenera kudzalandira madalitso osatha a Mulungu.—Werengani Aheberi 10:38, 39.

^ ndime 7 Anthu amachitanso zimenezi pofuna kuti agogo azinyaditsa anzawo kuti ali ndi zidzukulu.