“Kupusa kwa munthu wochokera kufumbi n’kumene kumapotoza njira yake, choncho mtima wake umakwiyira Yehova.”—MIY. 19:3.

1, 2. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuimba mlandu Yehova pa mavuto amene ali m’dzikoli? Perekani chitsanzo.

TIYEREKEZE kuti ndinu bambo ndipo mwakhala m’banja mosangalala kwa zaka zambiri. Ndiye tsiku lina pofika kunyumba mukupeza kuti zinthu zasokonekereratu. Mipando yonse yaphwasulidwa ndiponso mbale ndi mawindo zaswedwa. Kodi mungafikire kunena kuti: “Mkazi wanga wachitiranji zimenezi?” Kapena mungafunse kuti: “Ndani wachita zimenezi?” N’zosakayikitsa kuti mungafunse funso lachiwirili chifukwa chakuti mukudziwiratu kuti mkazi wanu amene mumamukonda kwambiri sangachite zimenezo.

2 Nalonso dzikoli lasokonekera kwambiri. Chilengedwe chikuwonongedwa komanso chiwawa ndi chiwerewere zili ponseponse. Zimene taphunzira m’Baibulo zatithandiza kudziwa kuti si Yehova amene akuchititsa mavutowa. Iye analenga dzikoli kuti likhale paradaiso wokongola kwambiri. (Gen. 2:8, 15) Yehova ndi Mulungu wachikondi. (1 Yoh. 4:8) Kuphunzira Malemba kwatithandiza kudziwa kuti amene anayambitsa mavuto ambiri si winanso ayi koma Satana Mdyerekezi. Iye ndi “wolamulira wa dziko.”—Yoh. 14:30; 2 Akor. 4:4.

3. Kodi tingayambe bwanji kuganiza molakwika?

3 Komabe sitinganene kuti Satana ndi amene amachititsa mavuto athu onse. Tikutero chifukwa chakuti mavuto ena amabwera ngati ifeyo tinalakwitsa zinazake. (Werengani Deuteronomo 32:4-6.) N’kutheka kuti timadziwa zimenezi koma popeza ndife ochimwa tingayambe kuganiza m’njira yolakwika kwambiri n’kukumana ndi mavuto. (Miy. 14:12) Kodi tingachite bwanji zimenezi? M’malo modziimba mlandu kapena kuimba mlandu Satana pa mavuto amene tikukumana nawo, tikhoza kuyamba kuimba mlandu Yehova. Tikhoza kufika mpaka ‘pokwiyira Yehova.’—Miy. 19:3.

4, 5. Kodi Mkhristu ‘angakwiyire bwanji Yehova’?

 4 Koma kodi n’zothekadi ‘kukwiyira Yehova’? Ee n’zotheka, koma n’zosathandiza. (Yes. 41:11) Kodi munthu amene wakwiyira Yehova zinthu zingamuyendere bwino? Wandakatulo wina anati: “Mikono yako ndi yaifupi kwambiri moti sungamenyane ndi Mulungu.” Mwina sitingafike polankhula zinthu zosonyeza kuti takwiyira Yehova. Koma lemba la Miyambo 19:3 limanena kuti kupusa kwa munthu “n’kumene kumapotoza njira yake, choncho mtima wake umakwiyira Yehova.” Izi zikusonyeza kuti munthu akhoza kukwiyira Mulungu mumtima mwake. Zimenezi zikhoza kuonekera m’njira zina. Munthu wotereyu amakhala ngati wasungira Yehova chakukhosi. Kenako angasiye kusonkhana kapena kuchita zinthu zina zokhudza kulambira Yehova.

5 N’chiyani chingatichititse ‘kukwiyira Yehova’? Nanga tingapewe bwanji msampha umenewu? Kudziwa mayankho a mafunso amenewa n’kofunika kwambiri chifukwa akukhudza ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu.

N’CHIYANI CHINGATICHITITSE ‘KUKWIYIRA YEHOVA’?

6, 7. N’chifukwa chiyani Aisiraeli anayamba kuimba mlandu Yehova m’nthawi ya Mose?

6 N’chiyani chingachititse munthu amene wakhala akutumikira Yehova mokhulupirika kuti ayambe kuimba mlandu Mulungu wake? Tiyeni tikambirane mfundo zisanu ndiponso tione zitsanzo za m’Baibulo zosonyeza zimene zinachititsa anthu ena akale kukwiyira Yehova.—1 Akor. 10:11, 12.

Kumvetsera zinthu zoipa zimene ena akunena kungakusokonezeni (Onani ndime 7)

7 Zinthu zoipa zimene anthu ena amanena. (Werengani Deuteronomo 1:26-28.) Taganizirani zimene Aisiraeli anachita atangomasulidwa ku ukapolo m’dziko la Iguputo. Yehova anali atabweretsa miliri 10 pa Aiguputo omwe ankapondereza anthu akewo. Kenako anawononga Farao pamodzi ndi asilikali ake pa Nyanja Yofiira. (Eks. 12:29-32, 51; 14:29-31; Sal. 136:15) Tsopano anthu a Mulungu anali atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Koma pa nthawi yapadera kwambiriyo, Aisiraeli anayamba kuimba mlandu Yehova. N’chiyani chinachititsa kuti chikhulupiriro chawo chichepe chonchi? Iwo anachita mantha kwambiri atamva zimene anthu ena omwe anapita kukazonda dzikolo ananena. (Num. 14:1-4) Kodi zotsatira zake zinali zotani? M’badwo wonsewo sunaloledwe kulowa ‘m’dziko labwinolo.’ (Deut. 1:34, 35) Kodi nafenso nthawi zina tingafooketsedwe ndi zolankhula za ena n’kuyamba kuimba mlandu Yehova?

8. N’chifukwa chiyani anthu a Mulungu anayamba kuimba mlandu Yehova m’nthawi ya Yesaya?

8 Tingakhumudwe chifukwa chokumana ndi mavuto. (Werengani Yesaya 8:21, 22.) M’nthawi ya Yesaya, Ayuda anali m’mavuto aakulu. Mwachitsanzo, iwo anazunguliridwa ndi adani, chakudya chinali chosowa ndipo ambiri anali ndi njala. Koma vuto lalikulu linali njala yauzimu. (Amosi 8:11) M’malo modalira Yehova kuti awathandize pa mavuto awo, anayamba ‘kutukwana’ mfumu yawo ndi Mulungu wawo. Apatu iwo ankaimba mlandu Yehova chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawo. Kodi nafenso tikakumana ndi mavuto, tingayambe kunena mumtima mwathu kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova sakundithandiza?’

9. N’chifukwa chiyani Aisiraeli a m’nthawi ya Ezekieli anayamba kuona zinthu molakwika?

9 Sitidziwa zonse. Aisiraeli a m’nthawi ya Ezekieli sankadziwa zonse ndipo anayamba kuona ngati njira za Yehova “n’zopanda chilungamo.” (Ezek. 18:29) Zinali ngati iwowo akuweruza Mulungu n’kumaona kuti mfundo zawo n’zolungama kuposa za Yehova. Iwo ankachita zimenezi ngakhale kuti sankadziwa zonse. Mwina ifenso nthawi zina tingalephere kumvetsa bwino nkhani inayake ya m’Baibulo kapena chifukwa chake zinthu zina zatichitikira. Zoterezi zikachitika, kodi tingayambe  kuona mumtima mwathu kuti zimene Yehova akuchita “n’zopanda chilungamo”?—Yobu 35:2.

10. Kodi anthu amachita zotani mofanana ndi Adamu?

10 Timakonda kuimba mlandu ena pa zimene talakwitsa tokha. Ngakhale Adamu, yemwe anali munthu woyamba kulengedwa, anaimba mlandu Mulungu pa zimene analakwitsa yekha. (Gen. 3:12) Adamu ankadziwa bwino zimene zingachitike akaphwanya lamulo la Mulungu. Komabe iye anasankha mwadala kusamvera lamulolo ndipo kenako anaimba mlandu Yehova. Tingati iye anaimba mlandu Yehova kuti mkazi amene anam’patsa sanali wabwino. Kuyambira nthawi imeneyo, anthu amaimba mlandu Mulungu pa zinthu zimene alakwitsa okha. Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikakhumudwa chifukwa cha zinthu zimene ndalakwitsa ndekha, ndimayamba kuona kuti njira za Yehova n’zopanda chilungamo?’

11. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yona?

11 Timaganizira zathu zokha. Yehova atakomera mtima anthu a ku Nineve, mneneri Yona sanasangalale. (Yona 4:1-3) Mwina iye ankaona kuti adzanyozeka ngati zimene ankalengeza, zoti mzindawo uwonongedwa, sizichitika. Chifukwa choganizira kwambiri zimenezi, Yona sanachitire chifundo anthu a ku Nineve omwe analapa. Kodi ifenso timaganizira zathu zokha n’kumakwiyira Yehova chifukwa choti sakuwononga dzikoli mwamsanga? Mwina inuyo mwakhala mukulalikira kwa zaka zambiri kuti tsiku la Yehova layandikira. Kodi mungayambe kukwiyira Yehova ngati anthu ena akukunyozani chifukwa cholalikira uthenga wa m’Baibulo?—2 Pet. 3:3, 4, 9.

KODI TINGAPEWE BWANJI ‘KUKWIYIRA YEHOVA’?

12, 13. Ngati tayamba kukayikira njira zina za Yehova mumtima mwathu, Kodi tiyenera kuchita chiyani?

12 Kodi tingatani ngati tayamba kukayikira njira zina za Yehova mumtima mwathu? Tizikumbukira kuti kuchita zimenezi si nzeru. Paja lemba la Miyambo 19:3 limati: “Kupusa kwa munthu wochokera kufumbi n’kumene kumapotoza njira yake, choncho mtima wake umakwiyira Yehova.” Tiyeni tsopano tikambirane  mfundo 5 zimene zingatithandize kuti tisayambe kuimba Yehova mlandu chifukwa chokhumudwa ndi zinthu zina pa moyo wathu.

13 Yesetsani kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Kuchita zimenezi kungatithandize kwambiri kupewa mtima wokwiyira Mulungu. (Werengani Miyambo 3:5, 6.) Tiyenera kukhulupirira Yehova. Tisamadzione kuti ndife anzeru ndipo tizipewa kuganizira zathu zokha. (Miy. 3:7; Mlal. 7:16) Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tisaimbe mlandu Yehova zinthu zoipa zikatichitikira.

14, 15. N’chiyani chingatithandize kuti tisasokonezedwe ndi zinthu zoipa zimene ena anganene?

14 Musasokonezedwe ndi zinthu zoipa zimene ena anganene. Aisiraeli a m’nthawi ya Mose anali ndi zifukwa zambiri zowathandiza kukhulupirira kuti Yehova adzawatsogolera ku Dziko Lolonjezedwa. (Sal. 78:43-53) Koma atamva zinthu zoipa zimene azondi 10 osakhulupirika ananena, iwo anaiwala zimene Yehova anawachitira. Baibulo limati: “Iwo sanakumbukire dzanja la Mulungu.” (Sal. 78:42) Kuganizira kwambiri zinthu zabwino zimene Yehova watichitira kungatithandize kukhalabe naye pa ubwenzi wabwino. Tikatero, sitidzalola kuti zinthu zoipa zimene ena anganene zisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.—Sal. 77:11, 12.

15 Ubwenzi wathu ndi Yehova ukhoza kusokonekeranso ngati sitigwirizana ndi Akhristu anzathu. (1 Yoh. 4:20) Yehova anaona kuti Aisiraeli akutsutsana naye pamene anayamba kung’ung’udza chifukwa chakuti Aroni anasankhidwa kukhala wansembe. (Num. 17:10) Yehova angaonenso kuti tikutsutsana naye ngati titayamba kung’ung’udza chifukwa cha anthu amene iye akuwagwiritsira ntchito kuti azitsogolera m’gulu lake.—Aheb. 13:7, 17.

16, 17. Kodi tizikumbukira chiyani tikakhala pa mavuto?

16 Kumbukirani kuti si Yehova amene amayambitsa mavuto athu. Yehova ankafunabe kuthandiza Aisiraeli m’masiku a Yesaya ngakhale kuti iwo anamusiya. (Yes. 1:16-19) N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amatikonda ndipo amafunitsitsa kutithandiza pa vuto lililonse limene tingakumane nalo. (1 Pet. 5:7) Ndipotu analonjeza kuti azitipatsa mphamvu kuti tipirire.—1 Akor. 10:13.

17 Anthu ena akatichitira zinthu zopanda chilungamo, ngati mmene zinalili ndi Yobu, tizikumbukira kuti si Yehova amene wayambitsa vutolo. Yehova amakonda chilungamo ndipo amadana ndi chinyengo. (Sal. 33:5) Tiyeni tikhale ngati Elihu, yemwe anali mnzake wa Yobu. Iye ananena kuti: “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.” (Yobu 34:10) Yehova sayambitsa mavuto athu koma amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.”—Yak. 1:13, 17.

18, 19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira Yehova? Perekani chitsanzo.

18 Musamakayikire Yehova. Yehova ndi wangwiro ndipo maganizo ake ndi apamwamba kwambiri kuposa maganizo athu. (Yes. 55:8, 9) Choncho tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumazindikira kuti pali zinthu zina zimene sitidziwa. (Aroma 9:20) Nthawi zambiri sitidziwa zonse zokhudza vuto limene lachitika. N’zosakayikitsa kuti inuyo mwaonapo umboni wakuti mawu a pa Miyambo 18:17 ndi oona. Lembali limati: “Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola, koma mnzake amabwera n’kumufufuzafufuza.”

19 Tiyerekeze kuti mnzanu amene mumam’khulupirira wachita zinthu zina zimene mukuona kuti ndi zachilendo ndipo simukuzimvetsa. Kodi nthawi yomweyo mungaganize kuti walakwa? Kapena kodi mungadikire kaye kuti mumvetse, podziwa kuti mwakhala naye bwinobwino kwa nthawi yaitali? Ngati timachita zimenezo ndi anzathu omwe ndi opanda  ungwiro, kuli bwanji ndi Atate wathu wakumwamba? Pajatu maganizo ake ndiponso njira zake n’zapamwamba kwambiri kuposa zathu.

20, 21. Kodi kudziwa zimene zayambitsa mavuto athu n’kofunika bwanji?

20 Dziwani zimene zayambitsa mavuto anu. Kudziwa zimenezi n’kofunika chifukwa chakuti nthawi zina timadzibweretsera tokha mavuto. Ngati izi zitachitika, ndi bwino kungovomereza. (Agal. 6:7) Si bwino kuimba Mulungu mlandu pa mavuto athu. N’chifukwa chiyani si nzeru kuimba Mulungu mlandu? Tiyerekeze kuti munthu wina akuyendetsa galimoto yothamanga kwambiri. Ndiye atafika pakona, sakuchepetsa liwiro ndipo akuchita ngozi. Kodi munthuyo angaimbe mlandu kampani imene inakonza galimotoyo? Ayi. N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Potilenga, iye anatipatsa ufulu wosankha. Komanso watipatsa malangizo othandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Choncho, palibe chifukwa choimbira mlandu Mlengi wathu ngati ifeyo talakwitsa zinazake n’kukumana ndi mavuto.

21 Sikuti mavuto onse amabwera chifukwa choti ifeyo talakwitsa zinazake. Mavuto ena amangobwera chifukwa cha “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka.” (Mlal. 9:11) Tisamaiwalenso kuti mavuto anayamba chifukwa cha Satana Mdyerekezi. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:9) Mdani wathu ndi Satanayo osati Yehova.—1 Pet. 5:8.

MUZIONA KUTI UBWENZI WANU NDI YEHOVA NDI WAMTENGO WAPATALI

Yoswa ndi Kalebe anadalitsidwa chifukwa chokhulupirira Yehova (Onani ndime 22)

22, 23. Kodi tizikumbukira chiyani tikakhumudwa chifukwa chokumana ndi mavuto?

22 Mukakumana ndi mavuto, muzikumbukira chitsanzo cha Yoswa ndi Kalebe. Mosiyana ndi anzawo 10 aja, amuna okhulupirikawa anabweretsa lipoti lolimbikitsa. (Num. 14:6-9) Iwo ankakhulupirira Yehova. Ngakhale zinali choncho, anthu awiriwa anayendabe m’chipululu kwa zaka 40 pamodzi ndi Aisiraeli ena onse. Kodi Yoswa ndi Kalebe anakwiya kapena kuyamba kudandaula n’kumaganiza kuti Mulungu sakuwachitira chilungamo? Ayi ndithu. Iwo ankadalira Yehova ndipo anadalitsidwa kwambiri. M’badwo wawo wonse unafera m’chipululu koma amuna awiriwa analowa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 14:30) Ifenso Yehova adzatidalitsa “tikapanda kutopa” pochita zimene amafuna.—Agal. 6:9; Aheb. 6:10.

23 Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwakhumudwa chifukwa chokumana ndi mavuto mwinanso chifukwa cha zimene anthu ena kapena inuyo mwalakwitsa? Muziganizira kwambiri makhalidwe a Yehova omwe ndi abwino kwambiri. Muziganiziranso madalitso amene Yehova wakulonjezani. Komanso muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndikanapanda kudziwa Yehova, zinthu zikanakhala bwanji pa moyo wanga?’ Nthawi zonse muziyesetsa kuti ubwenzi wanu ndi iye ukhale wolimba ndipo musalole ngakhale pang’ono kumukwiyira mumtima mwanu.