Pa nthawi ina, mfumu ya Siriya inkasakasaka mneneri Elisa ndipo inamva zoti ali kumzinda wa Dotana. Mzindawu unali paphiri ndipo unali ndi mpanda. Ndiyeno usiku, mfumuyi inatumiza mahatchi, magaleta ankhondo ndiponso asilikali kumzindawu. Pofika m’mawa, asilikaliwo anali atazungulira mzinda wonsewo.—2 Maf. 6:13, 14.

Mtumiki wa Elisa atadzuka, anaona gulu la asilikaliwo. Iye anadandaulira Elisa kuti: “Kalanga ine mbuyanga! Titani?” Koma Elisa anati: “Usaope, popeza ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.” Kenako mneneriyu anayamba kupemphera kuti: “Inu Yehova, m’tseguleni maso chonde kuti aone.” Ndiyeno nkhaniyi imapitiriza kuti: “Nthawi yomweyo Yehova anatsegula maso a mtumiki uja, moti anaona kuti dera lonse lamapiri kuzungulira Elisa linadzaza ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo oyaka moto.” (2 Maf. 6:15-17) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi komanso pa zinthu zina zimene zinachitika pa moyo wa Elisa?

Elisa atazunguliridwa ndi asilikali a ku Siriya, sanachite mantha chifukwa ankakhulupirira Yehova ndipo ankadziwa kuti amuteteza. Ifeyo sitiyembekezera kuti Yehova atiteteza mozizwitsa koma timadziwa kuti iye amateteza gulu la atumiki ake. Zili ngati tazunguliridwa ndi mahatchi komanso magaleta oyaka moto. Kukhulupirira zimenezi kungatithandize kuti tizidalira Mulungu ndipo ‘tidzakhala otetezeka’ komanso Yehova adzatidalitsa. (Sal. 4:8) Tiyeni tsopano tikambirane zimene tikuphunzira pa zinthu zina zomwe zinachitika pa moyo wa Elisa.

ELISA ANAYAMBA KUTUMIKIRA ELIYA

Nthawi ina Elisa akulima, kunafika mneneri Eliya ndipo anam’ponyera chovala chake chauneneri. Elisa anadziwa tanthauzo la zimenezi. Choncho anakonza phwando potsanzikana ndi makolo ake ndipo kenako anapita kukatumikira Eliya. (1 Maf. 19:16, 19-21) Elisa anadzipereka kuchita zonse zimene akanatha potumikira Mulungu. Choncho Yehova anamugwiritsa ntchito kwambiri ndipo anadzakhala mneneri m’malo mwa Eliya.

Elisa anatumikira Eliya kwa zaka pafupifupi 6. Iye ndi “amene anali kuthirira Eliya madzi osamba m’manja.”  (2 Maf. 3:11) Pa nthawiyo, anthu akamaliza kudya, wantchito ndi amene ankathirira madzi mbuye wake posamba m’manja. Choncho nthawi zina Elisa ankagwira ntchito zooneka zonyozeka. Komabe ankaona kuti kutumikira Eliya unali mwayi waukulu.

Mofanana ndi Elisa, Akhristu ambiri masiku ano akuchita utumiki wa nthawi zonse. Iwo akuchita zimenezi chifukwa chokhulupirira Yehova ndiponso pofuna kuchita zonse zimene angathe pomutumikira. Ena amachoka kwawo n’kumakatumikira ku Beteli, kukagwira ntchito zomangamanga kapena kuchita utumiki wina. Anthu ena amaona kuti ntchito zina zimene atumiki amenewa amagwira ndi zonyozeka. Koma Akhristu sayenera kuziona choncho. Tikutero chifukwa Yehova amaona kuti ntchitozi ndi zofunika kwambiri.—Aheb. 6:10.

ELISA SANASIYE UTUMIKI WAKE

Mulungu ‘asanatenge Eliya mumphepo yamkuntho kupita naye kumwamba,’ anamuuza kuti achoke ku Giligala kupita ku Beteli. Asananyamuke, Eliya anauza Elisa kuti asapite naye, koma Elisa anati: “Sindikusiyani.” Ali pa ulendowu, Eliya anamuuzanso Elisa kawiri kuti asapite naye koma Elisa sanalole. (2 Maf. 2:1-6) Mofanana ndi Rute amene anakana kusiya Naomi, Elisa anakakamira Eliya. (Rute 1:8, 16, 17) Iye sanamusiye chifukwa ankayamikira kwambiri ntchito imene Mulungu anamupatsa yotumikira Eliya.

Elisa ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Tikapatsidwa utumiki wina m’gulu la Mulungu, tizikumbukira kuti tikutumikira Yehova. Kuchita zimenezi kungatithandize kuona kuti utumikiwo ndi wofunika kwambiri ndiponso ndi mwayi waukulu.—Sal. 65:4; 84:10.

“PEMPHA CHIMENE UKUFUNA KUTI NDIKUCHITIRE”

Ndiyeno akuyenda, Eliya anauza Elisa kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikuchitire ndisanakuchokere.” Mofanana ndi Solomo, Elisa anapempha zinthu zomuthandiza kutumikira Mulungu. Iye anapempha kuti alandire “magawo awiri a mzimu” wa Eliya. (1 Maf. 3:5, 9; 2 Maf. 2:9) Ku Isiraeli, mwana woyamba kubadwa ndi amene ankalandira magawo awiri a zinthu za bambo ake monga cholowa. (Deut. 21:15-17) Choncho tingati Elisa anapempha kuti adzalowe m’malo mwa Eliya pa ntchito yauneneri. Koma ankafunanso kuti adzakhale wolimba mtima ngati Eliya amene ankafunitsitsa kuti anthu azilambira Yehova yekha.—1 Maf. 19:13, 14.

Kodi Eliya anayankha bwanji pempho la mtumiki wakeyu? Iye anati: “Wapempha chinthu chovuta. Ukandiona ndikutengedwa, zimene wapemphazi zikuchitikiradi, koma ukapanda kundiona, sizichitika.” (2 Maf. 2:10) Zikuoneka kuti yankho la Eliya linali ndi mfundo ziwiri. Choyamba, likusonyeza kuti Mulungu yekha ndi amene akanasankha zoti Elisa alandire zimene wapemphazo kapena ayi. Chachiwiri, likusonyeza kuti Elisa akanalandira zinthuzo ngati akanakhalabe ndi Eliya zivute zitani.

ZIMENE ELISA ANAONA

Kodi Mulungu anayankha bwanji pempho la Elisa loti apatsidwe magawo awiri a mzimu wa Eliya? Nkhaniyi imati: “Pamene anali kuyenda n’kumalankhulana, anangoona galeta lankhondo lowala ngati moto ndi mahatchi owala ngati moto. Galeta ndi mahatchiwo zinadutsa pakati pawo n’kuwalekanitsa, ndipo Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho n’kukwera kumwamba. Nthawi yonseyi Elisa anali kuona zimene zinali kuchitikazo.” * Iye anaona Eliya akutengedwa, analandira magawo awiri a mzimu wake komanso analowa m’malo mwake monga mneneri. Umu ndi mmene Yehova anayankhira pempho la Elisa.—2 Maf. 2:11-14.

Elisa anatenga chovala chauneneri chimene Eliya anagwetsa n’kuchivala. Chovala chimenecho chinkasonyeza kuti tsopano Elisa ndi mneneri wa Mulungu. Umboni wina wosonyeza kuti Elisa anaikidwa kukhala mneneri unaoneka pamene anagawa madzi a mtsinje wa Yorodano mozizwitsa.

Mosakayikira Elisa analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene anaona pamene Eliya ankakwera kumwamba. Ndipo zimenezi n’zomveka chifukwa palibe amene anaonapo galeta lankhondo loyaka moto ndi mahatchi owala ngati moto. Zinthu zimenezi zinangopereka umboni woti Yehova wayankha pempho lake. Mulungu akamayankha mapemphero athu, sikuti timaona masomphenya a galeta lankhondo loyaka moto kapena mahatchi owala ngati moto. Koma timadziwa kuti Mulungu akugwiritsa ntchito mphamvu  zake zazikulu poonetsetsa kuti chifuniro chake chichitike. Ndipotu tikamaona kuti Yehova akudalitsa mbali ya padziko lapansi ya gulu lake, zimakhala ngati tikuona galeta lake lakumwamba likuyenda.—Ezek. 10:9-13.

Elisa anaona zinthu zambiri zimene zinam’thandiza kukhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zambiri. Ndipo mzimu wa Mulungu unathandiza mneneriyu kuchita zozizwitsa zokwana 16, pomwe Eliya anangochita 8 zokha. * Nthawi yachiwiri imene Elisa anaona mahatchi ndiponso magaleta ankhondo oyaka moto ndi pamene asilikali a ku Siriya anazungulira mzinda wa Dotana.

ELISA ANKAKHULUPIRIRA YEHOVA

Elisa sanachite mantha pamene anazunguliridwa ndi adani ku Dotana. Iye sanaope chifukwa chakuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Ifenso tiyenera kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse. Choncho tizipempha mzimu woyera wa Mulungu kuti tikhale ndi chikhulupiriro ndiponso makhalidwe ena amene mzimuwu umatulutsa.—Luka 11:13; Agal. 5:22, 23.

Zimene zinachitika ku Dotana zinathandiza Elisa kuti azidalira Yehova ndiponso magulu ake ankhondo akumwamba. Mneneriyu anazindikira kuti Yehova anatumiza angelo ambirimbiri kuti akazungulire mzindawu ndiponso adani ake. Mulungu anachititsa khungu adaniwo ndipo anapulumutsa Elisa ndi mtumiki wake. (2 Maf. 6:17-23) Mofanana ndi mmene ankachitira nthawi zonse, apanso Elisa anakhulupirira Yehova ndiponso kumudalira ndi mtima wonse.

Nafenso tizikhulupirira kwambiri Yehova Mulungu. (Miy. 3:5, 6) Tikatero, “Mulungu adzatiyanja ndi kutidalitsa.” (Sal. 67:1) N’zoona kuti sitinazunguliridwe ndi magaleta oyaka moto ndi mahatchi. Koma pa “chisautso chachikulu” Yehova adzateteza gulu lake la padziko lonse. (Mat. 24:21; Chiv. 7:9, 14) Mpaka nthawi imeneyo, tiyeni tizikumbukira kuti “Mulungu ndiye pothawirapo pathu.”—Sal. 62:8.

^ ndime 16 Eliya sanapite kumwamba kumene Yehova ndi angelo amakhala. Onani Nsanja ya Olonda ya September 15, 1997, tsamba 15.

^ ndime 19 Onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 2005, tsamba 10.