Mwina inuyo mutatsegula magazini yatsopano, munaonapo kuti zinthunzi zake n’zokongola kwambiri. Pamakhala chintchito kuti zithunzi zokongola zimenezi zijambulidwe ndipo zimakhala ndi cholinga chapadera. Zimathandiza kuti nkhanizo zitifike pa mtima ndiponso tiziganizire kwambiri. Zithunzi zingathandize kwambiri pokonzekera ndiponso poyankha pa Phunziro la Nsanja ya Olonda.

Mwachitsanzo, mungachite bwino kuganizira chithunzi chimene chimakhala kumayambiriro kwa nkhani yophunzira. Muzidzifunsa kuti, N’chifukwa chiyani anaika chithunzi chimenechi? Kodi chikusonyeza chiyani? Nanga chikugwirizana bwanji ndi mutu wa nkhani kapena lemba loyambirira? Mungachitenso bwino kuganizira zithunzi zina ndiponso kuona kugwirizana kwake ndi nkhaniyo komanso zochitika pa moyo wanu.

M’bale amene akuchititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda ayenera kupereka mpata kwa abale ndi alongo kuti afotokoze chithunzi chilichonse. Iwo afotokoze kugwirizana kwake ndi nkhaniyo komanso mmene chithunzicho chawathandizira. Nthawi zina, pachithunzi pamakhala mawu osonyeza ndime imene ikugwirizana nacho. Koma nthawi zina wochititsa amafunika kuona yekha kuti ndi pandime iti pamene angakambirane chithunzi. Kuchita zimenezi kungathandize kuti aliyense athandizidwe ndi zithunzi zomwe zajambulidwa n’cholinga choti timvetse bwino Mawu a Mulungu.

M’bale wina anati: “Nkhani zimalembedwa bwino koma zithunzi zimakometsera nkhanizo kuti zikhale zogwira mtima kwambiri.”