Kodi Aisiraeli ankapha anthu oipa powapachika pamtengo?

Kale anthu a mitundu yambiri ankapha anthu opalamula milandu ina powapachika pamtengo. Mwachitsanzo, Aroma ankamangirira kapena kukhomera anthu pamtengo. Nthawi zina munthuyo ankakhalabe moyo kwa masiku angapo kenako n’kufa chifukwa cha ululu, ludzu, njala apo ayi chifukwa cha nyengo yoipa. Aroma ankapha anthu opalamula milandu ikuluikulu m’njira imeneyi chifukwa ankaona kuti chilango chimenechi n’chochititsa manyazi kwambiri.

Kodi Aisiraeli ankaphanso anthu powapachika pamtengo? Chilamulo cha Mose chinati: “Pakakhala munthu amene wachita tchimo loyenera chiweruzo choti aphedwe, ndiyeno munthuyo waphedwa, ndipo wam’pachika pamtengo, mtembo wake usakhale pamtengopo usiku wonse, koma uzionetsetsa kuti wamuika m’manda tsiku lomwelo.” (Deut. 21:22, 23) Choncho, zikuoneka kuti pa nthawi imene Malemba Achiheberi ankalembedwa, munthu amene waweruzidwa kuti aphedwe, ankaphedwa kaye kenako n’kupachikidwa pamtengo.

Pa nkhani imeneyi, lemba la Levitiko 20:2 limati: “Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli, ndiponso mlendo aliyense wokhala mu Isiraeli, wopereka mwana wake aliyense kwa Moleki, aziphedwa ndithu. Nzika za m’dziko lanu zizimupha mwa kum’ponya miyala.” Anthu ‘olankhula ndi mizimu kapena olosera zam’tsogolo’ ankaphedwanso. Koma ankawapha ‘powaponya miyala.’—Lev. 20:27.

Lemba la Deuteronomo 22:23, 24 limati: “Pakakhala namwali wolonjezedwa kukwatiwa, ndipo mwamuna wina wam’peza mumzinda ndi kugona naye, onsewo muziwabweretsa kuchipata cha mzindawo ndi kuwaponya miyala kuti afe. Mtsikanayo afe chifukwa chakuti sanakuwe mumzindawo ndipo mwamunayo afe chifukwa waipitsa mkazi wa mnzake. Motero muzichotsa oipawo pakati panu.” Choncho tingati Aisiraeli ankapha anthu amene apalamula milandu ikuluikulu powaponya miyala. *

Zikuoneka kuti pa nthawi imene Malemba Achiheberi ankalembedwa, munthu amene waweruzidwa kuti aphedwe, ankaphedwa kaye kenako n’kupachikidwa pamtengo

Lemba la Deuteronomo 21:23 limanena kuti: “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu.” Aisiraeli ayenera kuti ankaphunzirapo kanthu akaona mtembo wa munthu woipa komanso “wotembereredwa ndi Mulungu,” utapachikidwa pamtengo. Izi zinkakhala ngati chenjezo kwa Aisiraeli onse.

^ ndime 6 Akatswiri ambiri amavomereza kuti malinga ndi Chilamulo, munthu wopalamula milandu ikuluikulu ankaphedwa kaye kenako n’kupachika thupi lake. Koma pali umboni wakuti m’nthawi ya atumwi, Ayuda ankapachika anthu ena ali moyo moti ankafera pamtengo pompo.