Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”

“Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”

“Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—AFIL. 1:10.

1, 2. Kodi ophunzira a Yesu ayenera kuti anachita chidwi ndi ulosi uti wonena za masiku otsiriza ndipo n’chifukwa chiyani?

YESU atauza ophunzira ake kuti kachisi adzawonongedwa, Petulo, Yakobo, Yohane ndiponso Andireya ankadera nkhawa. (Maliko 13:1-4) Choncho atakhala kwaokha ndi Yesu, anamufunsa kuti: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mat. 24:1-3) Yesu anayamba kuwauza zinthu zimene zidzachitike zomwe zidzasintha kwambiri moyo wa anthu ndiponso kusonyeza kuti dziko loipa la Satanali latsala pang’ono kutha. Ophunzira a Yesu ayenera kuti anachita chidwi kwambiri ndi chinthu chimodzi. Iye atanena za zinthu zovuta monga nkhondo, njala ndiponso kusamvera malamulo, anatchula chinthu chabwino chimene chidzachitike m’masiku otsiriza. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mat. 24:7-14.

2 Ophunzira a Yesu ankalalikira uthenga wabwino wa Ufumu limodzi ndi Khristu. (Luka 8:1; 9:1, 2) Komanso iwo ayenera kuti ankakumbukira mawu a Yesu akuti: “Zokolola n’zochulukadi, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokololazo kuti atumize antchito okam’kololera.” (Luka 10:2) Koma n’kutheka kuti ankadzifunsa kuti: ‘Tidzakwanitsa bwanji kulalikira “padziko lonse lapansi” ndiponso kupereka “umboni ku mitundu yonse”? Kodi anthu okwanira kuti alalikire padziko lonse adzachokera kuti?’ Ophunzirawo akanakhala ndi mwayi wooneratu zimene zikuchitika pokwaniritsa mawu a pa Mateyu 24:14, akanadabwa kwambiri.

3. Kodi lemba la Luka 21:34 likukwaniritsidwa bwanji masiku ano? Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

 3 Ulosi wa Yesu umenewu ukukwaniritsidwa masiku ano. Anthu mamiliyoni akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu mogwirizana padziko lonse. (Yes. 60:22) Koma Yesu anasonyezanso kuti m’masiku otsiriza anthu ena adzavutika kuti aike patsogolo ntchito yolalikira. Iye ananena kuti iwo adzasokonezedwa ndi zinthu zina ndipo mitima yawo ‘idzalemedwa.’ (Werengani Luka 21:34.) Mawu amenewa akukwaniritsidwanso masiku ano. Anthu a Mulungu ena akusokonezedwa ndi zinthu zina. Timaona zimenezi tikaganizira zimene iwo amasankha pa nkhani ya ntchito, maphunziro apamwamba, chuma ndiponso nthawi imene amachita masewera kapena zosangalatsa. Anthu ena akufooka chifukwa cha mavuto ndiponso nkhawa za tsiku ndi tsiku. Choncho muyenera kudzifunsa kuti: ‘Nanga ineyo ndikuchita bwanji pa nkhani imeneyi? Kodi zomwe ndimasankha zimasonyeza kuti ndikuika patsogolo zimene Mulungu amafuna?’

4. (a) Kodi Paulo anapempherera Akhristu oyambirira pa nkhani iti? Nanga iwo anachita chiyani? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino ndiponso yotsatira? Kodi kuchita zimenezi kutithandiza bwanji?

4 Akhristu a m’nthawi ya atumwi anayenera kuchita khama kuti apitirize kuika zinthu za Mulungu patsogolo. Mtumwi Paulo anaona kuti ndi bwino kupempherera Akhristu a ku Filipi kuti ‘azitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.’ (Werengani Afilipi 1:9-11.) Mofanana ndi mtumwi Paulo, Akhristu ambiri pa nthawiyo ankaonetsa “kulimba mtima kowonjezereka polankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.” (Afil. 1:12-14) Masiku anonso, Akhristu ambiri amalalikira Mawu a Mulungu molimba mtima. Komabe tiyeni tikambirane zimene gulu la Yehova likuchita masiku ano. Izi zitithandiza kuti tiziika patsogolo kwambiri ntchito yolalikira yomwe ndi yofunika koposa. Tikambirana zimene Yehova wakonza pofuna kukwaniritsa ulosi wa pa Mateyu 24:14. Tikambirananso zimene gulu la Yehova likuika patsogolo. Tionanso mmene kudziwa zimenezi kungatilimbikitsire ifeyo komanso mabanja athu. M’nkhani yotsatira tidzakambirana zimene zingatithandize kupirira komanso kutsatira bwinobwino gulu la Yehova.

MBALI YAKUMWAMBA YA GULU LA YEHOVA

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anaonetsa anthu masomphenya a mbali yakumwamba ya gulu lake? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa masomphenya a Ezekieli?

5 Pali zinthu zambiri zimene Yehova anasankha kusalemba m’Baibulo. Mwachitsanzo, iye sanalembemo mmene ubongo umagwirira ntchito ndiponso mmene zinthu zonse zimayendera m’chilengedwe. Koma watipatsa mfundo zofunika zimene zingatithandize kumvetsa zolinga zake komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi zolingazo. (2 Tim. 3:16, 17) N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limatiuzanso zinthu zina zokhudza mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. Timasangalala kwambiri kuwerenga zinthu zokhudza mbali yakumwambayi zimene zili m’mabuku a Yesaya, Ezekieli, Danieli komanso Chivumbulutso. (Yes. 6:1-4; Ezek. 1:4-14, 22-24; Dan. 7:9-14; Chiv. 4:1-11) Zili ngati Yehova anangotsegula katani kuti tione zakumwamba. N’chifukwa chiyani analemba zimenezi m’Baibulo?

6 Yehova amafuna kuti tizikumbukira kuti sitili m’gulu limene lili padziko lapansi lokhali. Mbali ina ya gululi ili kumwamba ndipo ikuchita zambiri pokwaniritsa zolinga zake. Mwachitsanzo, Ezekieli anaona galeta lalikulu kwambiri limene likuimira mbali yakumwambayi. Galetali limayenda pa liwiro loopsa ndipo limatha kusintha kolowera mofulumira kwambiri. (Ezek. 1:15-21) Mawilo  ake akangozungulira kamodzi, galetali limakhala kuti lapita patali kwambiri. M’masomphenyawo, Ezekieli anaonanso Wokwera pa galetalo. Iye anati: “Ndinaona chinachake chowala ngati siliva wosakanikirana ndi golide, chooneka ngati kuti mkati mwake monse mukuyaka moto . . . Zinali kuoneka ngati ulemerero wa Yehova.” (Ezek. 1:25-28) Kodi mukuganiza kuti Ezekieli anamva bwanji ataona zimenezi? Masomphenyawo anathandiza Ezekieli kuona kuti Yehova akutsogoleradi gulu lake n’kumaliyendetsa pogwiritsa ntchito mzimu woyera. Kunena zoona, galeta limeneli likusonyeza bwino kwambiri mmene mbali yakumwamba ya gulu la Yehova imachitira zinthu.

7. Kodi masomphenya amene Danieli anaona amalimbitsa bwanji chikhulupiriro chathu?

7 Nayenso Danieli anaona masomphenya amene amalimbitsa chikhulupiriro chathu. Iye anaona Yehova, yemwe ankaoneka ngati “Wamasiku Ambiri,” atakhala pampando wachifumu umene unali kuyaka moto walawilawi. Mpandowo unali ndi mawilo. (Dan. 7:9) Yehova ankafuna kuti Danieli adziwe kuti gulu Lake likuyenda, kapena kuti likuchita zambiri pokwaniritsa chifuniro Chake. Danieli anaonanso Yesu yemwe ankaoneka “ngati mwana wa munthu.” Yesuyo ankapatsidwa ufumu kuti azilamulira mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova. Ulamuliro wake si wazaka zochepa ayi koma “udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.” (Dan. 7:13, 14) Masomphenya amenewa amatilimbikitsa kukhulupirira Yehova ndiponso zimene akuchita. Iye anapereka “ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu” kwa Yesu yemwe ndi Mwana wake  wokhulupirika. Popeza Yehova amakhulupirira Mwana wakeyu, ifenso tiyenera kukhulupirira kuti Yesu ndi Mfumu yabwino.

8. Kodi Ezekieli ndi Yesaya anamva bwanji Yehova atawaonetsa masomphenya? Nanga masomphenyawa ayenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?

8 Kodi masomphenya a mbali yakumwamba ya gulu la Yehova ayenera kutilimbikitsa kuchita chiyani? Mofanana ndi Ezekieli, ifenso timagoma kwambiri tikaona zimene Yehova akuchita. (Ezek. 1:28) Kuganizira kwambiri za gulu la Yehova kukhoza kutilimbikitsa kuchita zambiri ngati mmene anachitira Yesaya. Iye ataona masomphenyawo kenako n’kumva Yehova akufuna munthu woti amutume, anayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Werengani Yesaya 6:5, 8.) Yesaya ankadziwa kuti Yehova amuthandiza kuthana ndi vuto lililonse. Masomphenya amenewa ayenera kutilimbikitsanso kutumikira Yehova mwakhama. N’zolimbikitsa kudziwa kuti tili m’gulu limene likugwira ntchito nthawi zonse pokwaniritsa zolinga za Yehova.

MBALI YAPADZIKO LAPANSI YA GULU LA YEHOVA

9, 10. Kodi mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ndi yofunika bwanji?

9 Kudzera mwa Mwana wake, Yehova wakhazikitsa mbali yapadziko lapansi ya gulu lake yomwe imagwira ntchito limodzi ndi mbali yakumwamba. Kodi mbali yapadzikoyi ndi yofunika bwanji pokwaniritsa ntchito yotchulidwa pa Mateyu 24:14? Ndi yofunika pa zifukwa zitatu.

10 Choyamba, Yesu ananena kuti ophunzira ake adzalalikira “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Chachiwiri, panafunika kuti anthu ogwira ntchito imeneyi aziphunzitsidwa Baibulo ndiponso kulimbikitsidwa. (Yoh. 21:15-17) Chachitatu, panafunikanso kuti anthu ogwira ntchito yolalikira azisonkhana kuti azilambira Yehova ndiponso kuphunzitsidwa mmene angagwirire ntchitoyo. (Aheb. 10:24, 25) Kuti zinthu zimenezi zitheke, panafunika gulu lochita zinthu mwadongosolo.

11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona gulu la Yehova kukhala lofunika?

11 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona gulu la Yehova kukhala lofunika? Njira imodzi ndi kukhulupirira anthu amene akutitsogolera pa ntchito yolalikira. Yehova ndi Yesu akuwakhulupirira choncho ifenso tiyenera kuwakhulupirira. Abale amene akutitsogolera akhoza kugwiritsa ntchito nthawi yawo pochita zinthu zambirimbiri m’dzikoli. Koma salola kutanganidwa ndi zimenezo. Tiyeni tione zimene mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ikuika patsogolo nthawi zonse.

“ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI” ZIMAKHALA PATSOGOLO

12, 13. Kodi akulu amatsogolera bwanji pa ntchito yolalikira? Kodi zimenezi zimakulimbikitsani bwanji?

12 Padziko lonse, akulu oyenerera amaikidwa kuti ayang’anire ndiponso kutsogolera ntchito yolalikira Ufumu m’mayiko amene akutumikira. Iwo asanasankhe zochita, amafufuza kaye m’Mawu a Mulungu kuti Mawuwo akhale ngati ‘nyale younikira kumapazi awo komanso kuwala kounikira njira yawo.’ Abalewa amapempheranso kuti Yehova awatsogolere.—Sal. 119:105; Mat. 7:7, 8.

13 Mofanana ndi oyang’anira mu nthawi ya atumwi, akulu amene amayang’anira ntchito yolalikira masiku ano amadzipereka kwambiri “pa utumiki wokhudza mawu a Mulungu.” (Mac. 6:4) Iwo amasangalala kwambiri akaona kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino ikuyenda bwino m’dziko lawo komanso padziko lonse. (Mac. 21:19, 20) M’malo mopanga malamulo ambirimbiri, iwo amatsatira Malemba ndipo amalola mzimu  woyera kuwatsogolera akamasankha zimene zingathandize pa ntchito yolalikira. (Werengani Machitidwe 15:28.) Akamachita zimenezi, amapereka chitsanzo chabwino kwa abale ndi alongo m’mipingo.—Aef. 4:11, 12.

14, 15. (a) Kodi Akhristu akugwira ntchito ziti zothandiza kuti ntchito yolalikira padziko lonse iziyenda bwino? (b) Kodi inuyo mumamva bwanji mukamathandiza kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino?

14 Abale ambiri amagwira ntchito tsiku lililonse kuti akonze mabuku ndiponso mapulogalamu a misonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu. Palinso abale ndi alongo masauzande ambiri amene amagwira ntchito mwakhama kwambiri kuti amasulire mabuku m’zinenero zoposa 600. Izi zikuthandiza kuti anthu ambiri aphunzire “zinthu zazikulu za Mulungu” m’zinenero zawo. (Mac. 2:7-11) Abale ndi alongo achinyamata amagwiranso ntchito yosindikiza mabuku pogwiritsa ntchito makina apamwamba kwambiri. Mabuku amenewa amatumizidwa kumipingo ngakhale imene ili kutali kwambiri.

15 Gulu la Yehova likuchitanso zinthu zina n’cholinga choti litithandize kuika patsogolo ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, pali abale ndi alongo ambiri amene amadzipereka kumanga Nyumba za Ufumu komanso malo a misonkhano. Ena amathandiza kukachitika masoka achilengedwe kapena kuthandiza abale ndi alongo m’zipatala. Enanso amathandiza pokonzekera misonkhano ikuluikulu ndipo ena amakhala alangizi m’sukulu zophunzitsa Baibulo. Kodi cholinga cha ntchito zonsezi n’chiyani? Choyamba, zimathandiza kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino. Zimathandizanso kuti Akhristu amene akugwira ntchitoyi aphunzitsidwe ndiponso kulimbikitsidwa. Komanso zikuthandiza kuti anthu ena ayambe kulambira Yehova. Kunena zoona, mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ikuikadi patsogolo zinthu zofunika kwambiri.

TSANZIRANI GULU LA YEHOVA

16. Kodi mungafufuze zinthu ziti pa Kulambira kwa Pabanja kapena pophunzira panokha?

16 Kodi ifeyo nthawi zina timafatsa n’kuganizira zimene gulu la Yehova lakhala likuchita? Anthu ena asankha kuti pa Kulambira kwa Pabanja kapena pamene akuphunzira paokha azifufuza ndiponso kusinkhasinkha nkhani ngati zimenezi. Mukhoza kusangalala kwambiri kuphunzira masomphenya amene Yehova anaonetsa Yesaya, Ezekieli, Danieli ndiponso Yohane. Palinso mabuku ena (monga buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom) ndiponso ma DVD omwe angakuthandizeni kudziwa zambiri zokhudza gulu la Yehova.

17, 18. (a) Kodi nkhani imeneyi yakuthandizani bwanji? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

17 Kusinkhasinkha zimene Yehova akuchita pogwiritsa ntchito gulu lake kumatithandiza. Mofanana ndi gulu lake lochititsa chidwi, nthawi zonse tiziika patsogolo zinthu zofunika kwambiri. Tikamachita zimenezi, timafunitsitsa kutsanzira mtumwi Paulo, yemwe analemba kuti: “Popeza tili ndi utumiki umenewu malinga ndi chifundo chimene tinasonyezedwa, sitikubwerera m’mbuyo.” (2 Akor. 4:1) Iye analimbikitsanso Akhristu anzake kuti: “Tisaleke kuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.”—Agal. 6:9.

18 Kodi pali zinthu zimene inuyo kapena banja lanu muyenera kusintha kuti tsiku lililonse muziika patsogolo zinthu zofunika kwambiri? Kodi mungachepetse zinthu ziti pa moyo wanu kuti mukhale ndi nthawi yambiri yogwira ntchito yolalikira? M’nkhani yotsatira tidzakambirana zinthu zisanu zimene zingatithandize kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova.