Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Josephus Analembadi Zimenezi?

Kodi Josephus Analembadi Zimenezi?

Flavius Josephus, yemwe ndi wolemba mbiri wa m’nthawi ya atumwi, analemba m’buku lake lina za imfa ya “Yakobo m’bale wake wa Yesu amene ankadziwikanso kuti Khristu.” Akatswiri ambiri amanena kuti nkhaniyi ndi yoona. Komabe ena amakayikira ngati mawu ena a m’nkhaniyi analembedwadi ndi Josephus. M’nkhani yakeyo analemba kuti:

“Tsopano pa nthawi imeneyi, panali munthu wanzeru dzina lake Yesu. Kaya n’zoyenera n’komwe kumutchula kuti munthu, chifukwa ankachita zinthu zodabwitsa kwambiri ndipo anthu ankakonda kumvetsera iye akamaphunzitsa. Iye anakopa Ayuda ambiri komanso anthu a mitundu ina. Anali Khristu ndipo Pilato anamuweruza kuti apachikidwe pamtanda. Anatero chifukwa chomvera amuna ena audindo omwe analinso Ayuda anzathu. Poyamba anthu amene ankamukonda sanamusiye ndipo atauka pambuyo pa masiku atatu anaonekera kwa anthuwo. Izi zinali zogwirizana ndi zimene Mulungu anauzira aneneri kuti alembe. Palinso zinthu zina zodabwitsa zokhudza Yesuyo zokwana 10,000 zimene aneneriwo analemba. Anthu omutsatira amatchedwa Akhristu ndipo alipobe mpaka pano.”—Josephus—The Complete Works, lomasuliridwa ndi William Whiston.

Kungoyambira kumapeto kwa zaka za m’ma 1500, anthu akhala akukangana za nkhani imeneyi. Ena amakhulupirira kuti Josephus analemba zimenezi koma ena amakayikira. Serge Bardet wa ku France, amene anali katswiri wa mbiri yakale komanso wolemba mabuku, anachita kafukufuku kuti apeze zoona zenizeni pa nkhaniyi yomwe yakhala ikuvuta kwa zaka zoposa 400. Zomwe anapeza anazilemba m’buku lake.

Josephus sankalemba mabuku achikhristu. Iye anali Myuda wolemba mbiri basi. N’chifukwa chake anthu amakayikira zoti iye analembadi kuti Yesu anali “Khristu.” Bardet analemba kuti mmene dzina lakuti Khristu analilembera n’zogwirizana kwambiri ndi mmene Agiriki amalembera mayina a anthu. Iye anawonjezera kuti n’zotheka kuti Josephus alembe choncho dzina lakuti Khristu ndipo umenewu ndi umboni wakuti Yesu analikodi. Ananenanso kuti anthu otsutsawo anafunika kuganizira mfundo imeneyi.

Kodi tinene kuti pali munthu wina amene anatengera kalembedwe ka Josephus yemwe anasintha zinthu zina? Bardet ataona maumboni ochokera m’mbiri komanso kalembedwe ka nkhaniyo, ananena kuti zimenezi n’zosatheka m’pang’ono pomwe. Iye anapitiriza kuti zimenezi zingatheke pokhapokha munthuyo atakhala ndi luso lotha kulemba ndendende ngati Josephus chifukwa kalembedwe ka Josephus kanali kakekake.

Komano n’chifukwa chiyani akatswiri ena amakayikira kuti amene analemba zimenezi ndi Josephus? Bardet anatchula pamene pagona vuto. Iye anati iwo amakayikira zimenezi kuposa nkhani zina zambirimbiri chifukwa chakuti safuna kukhulupirira kuti Yesu ndi Khristu.

Sitikudziwa ngati zimene anapeza Bardet zingasinthe maganizo a akatswiriwo. Komabe zinachititsa katswiri wina wodziwa bwino za Chiyuda ndi Chikhristu, dzina lake Pierre Geoltrain, kusintha maganizo. Poyamba iye ankakhulupirira kuti pali munthu wina amene anasintha nkhaniyi ndipo ankanyoza anthu onse amene ankaikhulupirira. Iye ananena kuti chimene chinachititsa kuti asinthe ndi kafukufuku wa Bardet. Geoltrain ananena kuti “aliyense ayenera kukhulupirira kuti nkhaniyo inalembedwadi ndi Josephus.”

A Mboni za Yehova ali ndi zifukwa zambiri zimene zimawapangitsa kukhulupirira kuti Yesu ndi Khristu. Zifukwazo zili m’Baibulo.—2 Tim. 3:16.