“Musamatengere nzeru za nthawi ino.”​—AROMA 12:2.

NYIMBO: 88, 45

1, 2. (a) Kodi Yesu anayankha bwanji Petulo atamuuza kuti adzikomere mtima? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) N’chifukwa chiyani Yesu anayankha choncho?

OPHUNZIRA a Yesu anadabwa kwambiri Yesu atawauza kuti pasanapite nthawi yaitali iye azunzidwa kenako aphedwa. Iwo anadabwa chifukwa ankayembekezera kuti Yesuyo ndi amene adzabwezeretse ufumu kwa Aisiraeli. Ndiyeno Petulo anauza Yesu kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” Koma iye anamuyankha kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”​—Mat. 16:21-23; Mac. 1:6.

2 Zimene Yesu ananenazi zikusonyeza kuti pali kusiyana pakati pa maganizo a Mulungu ndi maganizo a anthu m’dziko la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Mtumwi Petulo anafotokoza maganizo ofuna kudzikomera mtima amene afala m’dzikoli. Koma Yesu ankadziwa kuti maganizo a Atate wake ndi osiyana ndi maganizo a anthu. Iye ankadziwanso kuti Mulungu ankafuna kuti iye akonzekere m’maganizo mwake kuti avutika komanso kufa. Zimene Yesu anauza Petulo zinasonyeza  kuti anakana kuyendera maganizo a anthu koma a Yehova.

3. N’chifukwa chiyani zimakhala zovuta kuti tikane maganizo a m’dzikoli n’kumayendera maganizo a Yehova?

3 Nanga bwanji ifeyo? Kodi timayendera maganizo a Mulungu kapena a m’dzikoli? N’zoona kuti ambirife tinasintha khalidwe lathu n’kumatsatira zimene Mulungu amafuna. Koma kodi tinasinthanso maganizo athu? Kodi timayesetsa kuti tiziyendera maganizo a Yehova? Kuti zimenezi zitheke pamafunika khama ndithu. Koma munthu safunika kuchita khama kuti ayambe kuyendera maganizo a m’dzikoli. Zili choncho chifukwa chakuti mzimu wadziko uli paliponse m’dzikoli. (Aef. 2:2) Vuto lina ndi lakuti mtima wathu wodzikonda umafulumira kukopeka ndi maganizo a m’dzikoli. Mwachidule tingati pamafunika khama kuti tiziyendera maganizo a Yehova koma kuyendera maganizo a m’dzikoli n’kosavuta ngakhale pang’ono.

4. (a) Kodi chingachitike n’chiyani ngati titayamba kuyendera maganizo a m’dzikoli? (b) Kodi nkhaniyi itithandiza bwanji?

4 Munthu akamayendera maganizo a m’dzikoli amakhala wodzikonda komanso safuna kuuzidwa zochita ndi Mulungu. (Maliko 7:21, 22) Choncho ndi bwino kuyesetsa kukhala ndi “maganizo a Mulungu” osati “maganizo a anthu” ndipo nkhaniyi itithandiza kuchita zimenezi. Isonyeza kuti munthu akamayendera maganizo a Yehova zimamuthandiza osati kumuphwanyira ufulu. Ifotokozanso zimene tingachite kuti tipewe kutengera maganizo a m’dzikoli. Munkhani yotsatira, tidzaona zimene tingachite kuti tiziyendera maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana.

MAGANIZO A YEHOVA NDI ABWINO KOMANSO OTHANDIZA

5. N’chifukwa chiyani anthu ambiri safuna kuyendera maganizo a winawake?

5 Anthu ambiri amadana ndi zoti aziyendera maganizo a winawake. Iwo amaona kuti palibe angawauze zochita. Koma mwina izi zimatanthauza kuti amasankha okha zochita ndipo amaona kuti zimenezi n’zoyenera. Iwo amafuna kuti azikhala ndi ufulu wosankha zochita popanda kugonjera aliyense. *

6. (a) Kodi Yehova amatipatsa ufulu wotani? (b) Kodi ufulu umene Yehova amatipatsa ndi wopanda malire?

6 Chimene tiyenera kukumbukira n’chakuti kuyendera maganizo a Yehova sikutanthauza kuti munthu sakhala ndi ufulu uliwonse woganiza kapena wosankha yekha zochita. Malinga ndi lemba la 2 Akorinto 3:17, “pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.” Munthu amakhala ndi ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi mmene iyeyo alili. Angasankhe yekha zochita pa zinthu zimene zimamusangalatsa. Ndipo Yehova anatilenga m’njira yoti tizigwiritsa ntchito ufulu umenewu. Chimene amangofuna n’chakuti tizidziwa malire athu pogwiritsa ntchito ufuluwo. (Werengani 1 Petulo 2:16.) Posankha kuti ichi n’choyenera ichi n’cholakwika, Yehova amafuna kuti tiziyendera maganizo ake omwe amapezeka m’Baibulo. Kodi mfundo imeneyi ndi yopanikiza kwambiri kapena yothandiza?

7, 8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuyendera maganizo a Yehova si kopanikiza? Perekani chitsanzo.

7 Kuti timvetse mfundoyi tiyeni tikambirane chitsanzo. Makolo amayesetsa kuthandiza ana awo kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Angawaphunzitse kuti akhale oona mtima, akhama komanso oganizira anzawo. Zimenezi sizingapanikize anawo. Koma zingawathandize kuti m’tsogolo adzakhale anthu abwino. Anawo akadzakula n’kuchoka pakhomo adzakhala ndi ufulu wosankha zimene akufuna kuchita.  Akatsatira mfundo zimene anaphunzitsidwa ndi makolo awo, akhoza kumasankha komanso kuchita zinthu zimene sanganong’oneze nazo bondo. Izi zingawathandize kuti apewe mavuto komanso zinthu zodetsa nkhawa.

8 Yehova ali ngati kholo labwino chifukwa amafuna kuti ana akefe tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. (Yes. 48:17, 18) Choncho amatiphunzitsa kuti tikhale ndi makhalidwe abwino komanso tiziganizira anzathu. Ndiye amafuna kuti tiziyendera maganizo ake pa nkhani imeneyi. Zimenezi sizitipanikiza ayi, koma zimangotithandiza kuti tikhale ndi maganizo abwino komanso apamwamba. (Sal. 92:5; Miy. 2:1-5; Yes. 55:9) Zimatithandiza kusankha zinthu zimene tingasangalale nazo koma pa nthawi imodzimodziyo tikugwiritsa ntchito ufulu wathu. (Sal. 1:2, 3) Kunena zoona, kuyendera maganizo a Yehova n’kwabwino komanso kothandiza.

MAGANIZO A YEHOVA NDI APAMWAMBA

9, 10. N’chiyani chikusonyeza kuti maganizo a Yehova ndi apamwamba kuposa a m’dzikoli?

9 Anthu a Yehova amafunanso kuyendera maganizo ake chifukwa chakuti maganizo akewo ndi apamwamba kwambiri kuposa a m’dzikoli. Anthu m’dzikoli akhala akupereka malangizo pa nkhani ya makhalidwe abwino, mabanja, ntchito komanso zinthu zina. Koma nthawi zambiri malangizo awo amakhala osiyana ndi maganizo a Yehova. Mwachitsanzo, anthu amalimbikitsa mtima wodzikonda ndipo amaona kuti kuchita chiwerewere si vuto. Ena amalangiza anzawo kuti ngati banja silikuyenda bwino kupatukana, kapena kungolithetsa kungathandize kuti munthu asangalale. Malangizo amenewa ndi osemphana kwambiri ndi Malemba. Kodi inuyo mukuona kuti malangizo ena amene anthu amaperekawa ndi othandiza masiku ano?

10 Yesu ananena kuti: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mat. 11:19) Anthu m’dzikoli apita patsogolo kwambiri pa nkhani ya zipangizo zamakono koma akulephera kuthetsa mavuto amene amatisowetsa mtendere monga nkhondo, kusankhana mitundu ndi ziwawa. Nanga kodi mtima wolekerera makhalidwe oipa wabweretsa mavuto otani? Ambiri amavomereza kuti mtima umenewu ndi umene ukuchititsa kuti mabanja azisokonekera, matenda azifala komanso kuti pakhale mavuto ena osiyanasiyana. Koma Akhristu amene amayendera maganizo a Mulungu amasangalala m’banja, amakhala ndi moyo wathanzi chifukwa chopewa makhalidwe oipa komanso amagwirizana ndi Akhristu anzawo padziko lonse. (Yes. 2:4; Mac. 10:34, 35; 1 Akor. 6:9-11) Kodi umenewu si umboni wakuti maganizo a Yehova ndi apamwamba kuposa a m’dzikoli?

11. Kodi Mose ankayendera maganizo a ndani, nanga zotsatira zake zinali zotani?

11 Atumiki a Mulungu otchulidwa m’Baibulo ankazindikira zoti maganizo a Yehova ndi apamwamba. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Mose. Ngakhale kuti “anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo,” iye ankadalira Yehova kuti amupatse “mtima wanzeru.” (Mac. 7:22; Sal. 90:12) Iye anapemphanso Yehova kuti: “Ndidziwitseni njira zanu.” (Eks. 33:13) Popeza ankayendera maganizo a Yehova, iye anathandiza pokwaniritsa cholinga cha Mulungu ndipo Malemba amasonyeza kuti iye anali ndi chikhulupiriro cholimba.​—Aheb. 11:24-27.

12. Kodi Paulo ankayendera maganizo a ndani?

12 Chitsanzo china ndi cha mtumwi Paulo. Iye anali wanzeru, wophunzira komanso ankadziwa zilankhulo ziwiri kapena kuposerapo. (Mac. 5:34; 21:37, 39; 22:2, 3) Koma sanalole kuti aziyendera maganizo a m’dzikoli pa nkhani  yoti izi ndi zoyenera izi ndi zosayenera. M’malomwake ankayendera maganizo a Yehova. (Werengani Machitidwe 17:2; 1 Akorinto 2:6, 7, 13.) Zotsatira zake n’zakuti zinthu zinkamuyendera bwino pa utumiki wake ndipo ankayembekezera mphoto yamuyaya.​—2 Tim. 4:8.

13. Kodi udindo wosintha kuti tiziyendera maganizo a Yehova ndi wa ndani?

13 Zikuonekeratu kuti maganizo a Yehova ndi apamwamba kwambiri kuposa a anthu. Munthu akamayendera maganizo a Mulungu amakhala wosangalala ndipo zinthu zimamuyendera bwino. Koma Yehova satikakamiza kuti tiziyendera maganizo ake. Akulu komanso “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” salamulira maganizo a anthu. (Mat. 24:45; 2 Akor. 1:24) M’malomwake, Mkhristu aliyense ali ndi udindo wosintha kuti aziyendera maganizo a Yehova. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

TISAMATENGERE MAGANIZO A M’DZIKOLI

14, 15. (a) Ngati tikufuna kukhala ndi maganizo a Yehova, kodi tiyenera kuganizira kwambiri za chiyani? (b) Malinga ndi lemba la Aroma 12:2, n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kutengera nzeru za m’dzikoli? Perekani chitsanzo.

14 Lemba la Aroma 12:2 limanena kuti: “Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” Malinga ndi lembali, kaya tisanaphunzire choonadi tinkayendera maganizo otani, n’zotheka ndithu kusintha n’kumayendera maganizo a Yehova. N’zoona kuti zinthu ngati chibadwa chathu komanso zimene takumana nazo pa moyo wathu zimakhudza maganizo athu. Koma maganizo athu amatha kusintha. Zimene timalola kuti zilowe m’maganizo mwathu n’kumaziganizira zimatha kusintha kaganizidwe kathu. Choncho tikamaganizira kwambiri maganizo a Yehova tingayambe kuona kuti ndi olondola. Tikatero tidzakhala ndi mtima wofuna kumayendera maganizo akewo.

15 Komabe, kuti munthu ayambe kukhala ndi maganizo a Yehova amafunika kusiya ‘kutengera nzeru za nthawi ino.’ Tiyenera kupewa maganizo kapena mfundo zotsutsana ndi maganizo a Mulungu. Zimenezi tingaziyerekezere ndi zakudya. Munthu amene akufuna kukhala wathanzi akhoza kuganiza kuti asinthe n’kumadya zakudya zopatsa thanzi. Koma kodi munthuyo angakhale wathanzi ngati amadyanso zakudya zoipa? Mofanana ndi zimenezi, kuphunzira maganizo a Yehova sikungatithandize kwenikweni ngati timasokonezanso maganizo athu ndi nzeru za m’dzikoli.

16. Kodi tiyenera kudziteteza ku chiyani?

16 Koma kodi n’zotheka kupeweratu maganizo a m’dzikoli? Ayi, chifukwa tidakali m’dziko lomweli. Nthawi zina maganizo a m’dzikoli amakhala osapeweka. (1 Akor. 5:9, 10) Paja tikamalalikira timakumana ndi anthu amene ali ndi maganizo olakwika. Koma ngati tamva maganizo osemphana ndi a Yehova, tiyenera kuyesetsa kuti tisayambe kutengera maganizowo. Tiyenera kutsanzira Yesu amene ankakana mwamsanga maganizo amene akanamuchititsa kukhala kumbali ya Satana. Ndipo tiyenera kudziteteza kuti tisamachite dala zinthu zimene zingachititse kuti tisokonezedwe ndi maganizo olakwika.​—Werengani Miyambo 4:23.

17. Kodi tingapewe bwanji kusokonezedwa ndi maganizo olakwika?

17 Mwachitsanzo, tiyenera kusamala posankha anthu ocheza nawo. Baibulo limatichenjeza kuti tikamacheza kwambiri ndi anthu amene salambira Mulungu, tikhoza  kutengera maganizo awo. (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:12, 32, 33) Tiyeneranso kusamala posankha zosangalatsa. Tikamapewa zinthu zolimbikitsa chiwerewere, chiwawa kapena maganizo oti zamoyo sizinachite kulengedwa, zidzatithandiza kuti tisasokonezedwe ndi “chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu.”​—2 Akor. 10:5.

Kodi timathandiza ana athu kupewa zosangalatsa zimene zingawasokoneze? (Onani ndime 18, 19)

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kuti tisatengere maganizo a m’dzikoli obwera mosaonekera kwambiri? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati, nanga n’chifukwa chiyani?

18 Tiyenera kukhalanso osamala kuti tisayambe kutengera maganizo olakwika m’njira zovuta kuzizindikira. Mwachitsanzo, nkhani za pa wailesi kapena munyuzi zingafotokozedwe m’njira yokomera maganizo enaake pa nkhani ya ndale. Nkhani zina zimatilimbikitsa kuchita zimene anthu a m’dzikoli amaona kuti n’zabwino. Mabuku ndi mafilimu ena amalimbikitsa mtima wongodziganizira kapena woganizira kwambiri za banja lako kuposa chilichonse. Zimenezi ndi zosiyana ndi mfundo ya m’Malemba yakuti munthu komanso mabanja amakhala osangalala ngati amakonda Yehova kuposa chilichonse. (Mat. 22:36-39) Palinso tinthano tina ta ana tooneka ngati tabwinobwino koma timachititsa kuti anawo aziona kuti kuchita chiwerewere si kolakwika.

19 Apatu sitikunena kuti zosangalatsa n’zolakwika. Koma ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi timatha kuzindikira maganizo a m’dzikoli ngakhale atabwera m’njira yosaonekera kwambiri? Kodi timakhala ndi malire pa nkhani ya zosangalatsa zimene ana athu kapena ifeyo timakonda? Kodi timayesetsa kuchotsa maganizo olakwika amene ana athu akumana nawo n’kuwasinthanitsa ndi maganizo a Mulungu?’ Tikamazindikira kusiyana pakati pa maganizo a Yehova ndi maganizo a m’dzikoli, zidzakhala zosavuta kuti tipewe ‘kutengera maganizo a m’dzikoli.’

KODI PANOPA MUMAYENDERA MAGANIZO A NDANI?

20. Kodi tingadziwe bwanji ngati timayendera nzeru za Mulungu kapena za dzikoli?

20 Tizikumbukira nthawi zonse kuti maganizo amachokera mbali ziwiri. Mbali yoyamba ndi kwa Yehova ndipo mbali yachiwiri ndi kudziko lolamulidwa ndi Satanali. Ndiye kodi ifeyo timayendera maganizo ati? Kuti tipeze yankho tiyenera kudzifunsa kuti, Kodi mfundo zimene ndimamva kwambiri zimachokera kuti? Tikamamva kwambiri mfundo za m’dzikoli, timayamba kuganiza ndiponso kuchita zinthu ngati anthu ake. N’chifukwa chake tiyenera kusamala kwambiri ndi zimene timalola kuti tiziziganizira.

21. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

21 Monga tanena kale, pamafunika khama kuti munthu aziyendera maganizo a Yehova osati kungopewa zinthu zimene zingamusokoneze maganizo. Munthu amafunika kuphunzira maganizo a Yehovawo n’kuyamba kuwayendera. Munkhani yotsatira tidzaona mmene tingachitire zimenezi.

^ ndime 5 Koma chimene anthuwa sadziwa n’chakuti ngakhale munthu amene amayendera maganizo akeake amakhala akutsatira winawake. Kaya munthu akuganizira nkhani zikuluzikulu monga mmene moyo unayambira kapena zing’onozing’ono monga kavalidwe, sangapeweretu kuyendera maganizo a anthu ena. Koma aliyense akhoza kusankha kuti aziyendera maganizo a ndani.