Kodi anthu Opereka zabwino amene Yesu anawatchula anali ndani, nanga n’chifukwa chiyani anapatsidwa dzina limeneli?

Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu analangiza atumwi ake kuti asamakhale ndi mtima wofuna kulamulira Akhristu anzawo. Iye anati: “Mafumu a mitundu ya anthu amachita ulamuliro pa anthu awo, ndipo amene ali ndi mphamvu pa anthuwo amatchedwa Opereka zabwino. Inu musakhale otero.”​—Luka 22:25, 26.

Kodi anthu Opereka zabwino amene Yesu anawatchula anali ndani? Agiriki ndi Aroma ankakonda kulemekeza anthu ndi mawu oti Euergetes omwe amatanthauza Opereka zabwino. Mawu amenewa ankalembedwa m’malo osiyanasiyana ngakhalenso pandalama. Anthu ankapatsidwa dzina limeneli ngati achita zinthu zina zothandiza anthu.

Mafumu ambiri ankatchedwa Opereka zabwino. Ena mwa mafumu amenewa anali a ku Iguputo ndipo ankadziwika kuti Ptolemy III Euergetes (c. 247-222 B.C.E.) ndi Ptolemy VIII Euergetes II (c. 147-117 B.C.E.). Komanso panali mafumu achiroma monga Julius Caesar (48-44 B.C.E.) ndi Augustus (31 B.C.E.–14 C.E.). Nayenso Herode Wamkulu amene ankalamulira ku Yudeya anapatsidwa dzina limeneli. Zikuoneka kuti Herode anapatsidwa dzina limeneli chifukwa choti anapereka tirigu kwa anthu ake pa nthawi ya njala komanso anapereka zovala kwa anthu osauka.

Katswiri wina wa ku Germany dzina lake Adolf Deissmann ananena kuti dzina lakuti Opereka zabwino linali lofala. Iye analemba kuti mawuwa ankapezeka atalembedwa m’zinthu zambiri zakale.

Ndiye kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anauza ophunzira ake kuti: “Inu musakhale otero”? Kodi ankatanthauza kuti ophunzira akewo asamaganizire zothandiza anthu? Ayi, apa nkhani si imeneyi. Yesu ankaganizira kwambiri zolinga zimene munthu ayenera kukhala nazo popereka zinthu zabwino.

Mu nthawi ya Yesu, anthu olemera ankafuna kukondedwa ndi anthu ndipo ankapereka ndalama zothandizira pa masewera osiyanasiyana komanso pa zomangamanga zimene anthu ambiri angazigwiritse ntchito. Koma ankachita zimenezi n’cholinga choti atchuke, azitamandidwa kapena avoteredwe. Pa nkhani imeneyi, munthu wina analemba kuti: “N’zoona kuti anthu ena ankapereka zinthu n’cholinga chothandiza anthu basi. Koma ambiri ankachita zimenezi n’cholinga choti zinthu ziziwayendera pa nkhani zandale.” Ndiyeno Yesu ankauza ophunzira ake kuti azipewa mtima umenewu.

Patapita zaka zingapo, mtumwi Paulo ananenanso mfundo yoti tizipereka ndi zolinga zoyenera. Iye analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”​—2 Akor. 9:7.