Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muzolowere Mpingo Wanu Watsopano?

Kodi Mungatani Kuti Muzolowere Mpingo Wanu Watsopano?

M’BALE wina dzina lake Allen * atasamukira mumpingo wina ananena kuti: “Poyamba ndinkaopa kwambiri kusamukira kuno. Sindinkadziwa ngati anthu angandilandire bwino komanso ngati ndingapeze anzanga.” Allen akuyesetsa kuti azolowere mpingo wake watsopano umene uli pa mtunda wa makilomita 1,400 kuchokera kwawo.

Ngati nanunso mwangosamukira kumene mumpingo wina, mukhoza kukhala ndi maganizo ofanana ndi a Allen. Koma kodi mungatani kuti muzolowere mpingo watsopanowo? Nanga mungatani ngati zikukuvutani kuzolowera? Mwina inuyo simunasamukire mumpingo wina, koma kodi mungathandize bwanji anthu amene asamukira mumpingo wanu?

KODI MUNGATANI KUTI MUZOLOWERE?

Kuti timvetse nkhaniyi, tiyeni tiganizire zimene zimachitika posamutsa mtengo kuti ukabzalidwe pena. Pozula mtengowo mizu yambiri imadulidwa kuti usavute kunyamula. Choncho ukabzalidwa malo ena, nthawi yomweyo umafunika kumeranso mizu ina. N’chimodzimodzinso ndi kusamukira mumpingo wina. Mumpingo wanu wakale munali mutazolowera zinthu komanso munali mutapeza anzanu ambiri ndipo zinali ngati mwazika mizu. Koma panopa muyenera kumeranso mizu ina kuti muzisangalala mumpingo wanu watsopanowo. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuchita zimenezi? Muyenera kutsatira mfundo za m’Baibulo. Tiyeni tikambirane mfundo zina zomwe zingakuthandizeni.

Munthu amene amawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse amakhala “ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi, umene umabala zipatso m’nyengo yake, umenenso masamba ake safota, ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”​Sal. 1:1-3.

Mofanana ndi mtengo umene umafunika kupeza madzi nthawi zonse kuti ukhalebe wolimba, Mkhristu ayenera kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse kuti azikhala wolimba mwauzimu. Choncho muyenera kumawerenga Baibulo tsiku lililonse komanso kupezeka pamisonkhano. Muyeneranso kupitiriza kuchita kulambira kwa pabanja komanso kuphunzira Baibulo panokha. Zinthu zimene zinkakuthandizani kale kuti muzitumikira bwino Mulungu n’zimene zingakuthandizeninso mumpingo wanu watsopano.

“Wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.”​Miy. 11:25.

Mukamachita khama mu utumiki mudzalimbikitsidwa komanso kuzolowera mwamsanga mpingo wanu watsopano. Mkulu wina dzina lake Kevin ananena kuti: “Ine ndi mkazi wanga titangosamukira mumpingo watsopano, tinachita upainiya wothandiza. Zimenezi zinatithandiza kwambiri chifukwa tinayamba kudziwana bwino ndi abale, apainiya komanso kudziwa deralo.” M’bale wina dzina lake Roger anasamukira kudera limene linali pa mtunda wa makilomita 1,600 kuchokera kumene ankakhala. Iye anati: “Njira yothandiza kwambiri kuti muzolowere mpingo watsopano ndi kulowa nawo mu utumiki pafupipafupi. Mungachitenso bwino kuuza akulu kuti mukhoza kuthandiza pa ntchito zosiyanasiyana monga kuyeretsa Nyumba ya Ufumu, kukamba nkhani kapena kuthandiza ena kuti afike kumisonkhano. Abale ndi alongo akaona kuti muli ndi mtima wodzipereka, adzakulandirani bwino.”

“Futukulani mtima wanu.”​—2 Akor. 6:13.

Muziyesetsa kudziwana ndi abale ndi alongo osiyanasiyana. Melissa ndi banja lake atasamukira mumpingo watsopano, anayesetsa kuti apeze anzawo. Iye anati: “Tinkacheza ndi anthu ku Nyumba ya Ufumu  misonkhano isanayambe komanso ikatha. Zimenezi zinatithandiza kuti tisamangopatsana moni ndi anthu koma tizilankhula nawo nkhani zina.” Zinawathandizanso kuti adziwe msanga mayina a abale ndi alongo. Ankakondanso kuitana anthu kuti adzacheze kwawo ndipo zimenezi zinawathandiza kuti ayambe kugwirizana ndi anthu ambiri. Melissa ananenanso kuti: “Tinapatsana manambala a foni n’cholinga choti azitiuza ngati pali zinthu zina zimene anthu amumpingo akuchitira limodzi.”

Ngati zimakuvutani kulankhula ndi anthu amene simukuwadziwa, pali zinthu zing’onozing’ono zimene mungachite. Mwachitsanzo, muziyesetsa kumwetulira ngakhale pa nthawi imene simukufuna, chifukwa zimathandiza kuti anthu ena azifuna kucheza nanu. Paja Baibulo limati: “Maso owala amapangitsa mtima kusangalala.” (Miy. 15:30) Mlongo wina dzina lake Rachel anasamukira kutali ndi kumene anakulira. Iye ananena kuti: “Ndine wamanyazi choncho nthawi zina ndimachita kudzikakamiza kuti ndilankhule ndi abale ndi alongo mumpingo wanga watsopano. Ndikalowa mu Nyumba ya Ufumu ndimayang’ana munthu amene wakhala pampando koma sakulankhula ndi aliyense ndipo ndimayamba kulankhula naye. Ndimaganiza kuti mwina nayenso ndi wamanyazi.” Misonkhano isanayambe kapena ikatha muziyesetsa kulankhula ndi munthu amene simunachezepo naye.

Mwina milungu yoyambirira mukhoza kumasangalala kwambiri kukumana ndi anthu atsopano. Koma pakapita nthawi mungayambe kutopa nazo. Ngati zili choncho, muyenera kuyesetsa kuti mupitirize kupeza anzanu atsopano.

Mitengo imene yasamutsidwa n’kukabzalidwa pena imafunika kumera mizu yatsopano

MUZIKUMBUKIRA KUTI ZIMATENGA NTHAWI

Mitengo ina imatenga nthawi yaitali kuposa ina kuti izike mizu m’malo atsopano. Chimodzimodzinso ndi anthu amene asamukira mumpingo watsopano. Ena amazolowera msanga koma ena amachedwa. Ngati mukuvutikabe kuzolowera ngakhale kuti papita nthawi yaitali, mfundo za m’Baibulo izi zingakuthandizeni:

“Choncho tisaleke kuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.”​Agal. 6:9.

Muyenera kuleza mtima. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi anthu amene anapita ku Giliyadi n’kutumizidwa kumayiko ena monga amishonale. Ambiri amakhala m’dziko limene asamukira kwa zaka zingapo asanapite kwawo kukacheza. Zimenezi zimawathandiza kugwirizana kwambiri ndi abale a m’dzikolo komanso kuzolowera chikhalidwe cha kumeneko.

Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi Alejandro. Iye wasamuka kangapo ndipo amadziwa kuti kuzolowera malo atsopano kumatenga nthawi. Iye anati: “Ulendo womaliza umene tinasamuka, mkazi wanga ananena kuti, ‘Anzanga onse ali mumpingo wathu wakale.’” Alejandro anamukumbutsa kuti ananena zomwezo zaka ziwiri zapitazo pamene anasamukanso. Koma pa zaka ziwiri zimene anakhala mumpingo umene asamuka kumenewo ankayesetsa kudziwana ndi anthu ambiri ndipo ena anakhala anzake apamtima.

“Usanene kuti: ‘N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?’ Pakuti si nzeru kufunsa funso lotere.”​Mlal. 7:10.

Muzipewa kuyerekeza mpingo wanu watsopano ndi wakale. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti abale ambiri amumpingo watsopanowu sakonda kulankhula kapena sabisa chichewa kuposa amumpingo wanu wakale. Koma muziyesetsa kuona zinthu zabwino zimene amachita chifukwa inunso mungafune kuti iwowo aziona zabwino zimene mumachita. Anthu ena amene anasamukira mumpingo wina anadabwa ndi mmene anavutikira ndipo anadzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimakondadi “gulu lonse la abale”?’​—1 Pet. 2:17.

 “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.”​Luka 11:9.

Muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni. Mkulu wina dzina lake David ananena kuti: “Musamangoyesetsa kupirira nokha. Pali zinthu zambiri zimene sitingachite patokha koma pokhapokha Yehova atatithandiza. Choncho muzikonda kupempha Yehova kuti akuthandizeni.” Rachel yemwe tamutchula kale uja anati: “Ngati ine ndi mwamuna wanga sitikusangalala kwenikweni mumpingo wathu, timapemphera kwa Yehova n’kumamupempha kuti atithandize kudziwa ngati pali zinthu zina zimene ifeyo tikuchita zomwe zikuchititsa kuti anthu ena asamamasuke nafe. Kenako timayesetsa kupeza mpata wocheza ndi abale ndi alongo.”

Ngati ndinu makolo ndipo ana anu akuvutika kuti azolowere mpingo wanu, muzipemphera nawo limodzi. Muziwathandiza kupeza anzawo pokonza zoti azicheza ndi abale ndi alongo.

TIZILANDIRA BWINO ANTHU ATSOPANO

Kodi mungatani kuti muthandize anthu amene asamukira mumpingo wanu? Muziyambiratu kuwathandiza. Kuti muchite zimenezi, ganizirani zimene inuyo mungafune kuti ena akuchitireni ngati mwasamukira mumpingo wina. Ndiyeno muzichita zinthu zimene mwaganizirazo. (Mat. 7:12) Mwina mukhoza kuwaitana kuti akhale nanu pa kulambira kwa pabanja kapena kuti aonere nanu pulogalamu ya JW Broadcasting. Apo ayi mukhoza kuwapempha kuti alowe nanu mu utumiki. Ngati mungawaitane kuti adzadye kunyumba kwanu, adzayamikira kwambiri. Koma kodi ndi zinthu zina ziti zimene mungachite kuti muthandize anthu atsopano?

M’bale wina dzina lake Carlos ananena kuti: “Titafika mumpingo wathu watsopano, mlongo wina anatilembera mayina a mashopu amene amagulitsa zinthu pa mtengo wabwino. Zimenezi zinatithandiza kwambiri.” Nthawi zina dera limene anthu asamukira limakhala ndi nyengo yosiyana kwambiri ndi kumene achokera. Choncho mungawathandize kudziwa mmene angavalire m’dera latsopanoli, kaya ndi lotentha, lozizira kapena limene kumagwa mvula kwambiri. Mungawathandizenso mu utumiki mukamawafotokozera mmene anthu alili m’deralo komanso zimene amakhulupirira.

UBWINO WOYESETSA KUTI MUZOLOWERE

Allen, yemwe tamutchula kumayambiriro uja, wakhala mumpingo wake watsopano kwa nthawi yoposa chaka chimodzi. Iye anati: “Poyamba ndinkachita kudzikakamiza kuti ndilankhule ndi abale ndi alongo. Koma panopa ali ngati achibale anga ndipo ndine wosangalala.” Iye wazindikira kuti sanataye anzake pamene anasamuka. M’malomwake wapeza anzake atsopano omwe akhoza kugwirizana nawo mpaka kalekale.

^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa.