Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  April 2016

Kodi Utumiki Wanu Uli Ngati Mame?

Kodi Utumiki Wanu Uli Ngati Mame?

UTUMIKI wathu ndi wofunika kwambiri. Koma anthu ena amene timawalalikira sadziwa zimenezi. Palinso ena amene amachita chidwi ndi Mawu a Mulungu, koma savomera kuti tiziphunzira nawo Baibulo.

Mwachitsanzo, munthu wina dzina lake Gavin anayamba kusonkhana koma ankakana kuphunzira Baibulo. Iye anati: “Sindinkadziwa zambiri zokhudza Baibulo koma sindinkafuna kuti anthu adziwe zimenezi. Komanso sindinkafuna kukhala membala wa chipembedzo chilichonse chifukwa ndinkaopa kupusitsidwa.” Kodi inuyo mukanaganiza chiyani za Gavin? Kodi iye ndi wokanika? Ayi. Taganizirani mmene Baibulo limathandizira kuti munthu asinthe. Yehova anauza anthu ake kuti: “Mawu anga adzatsika ngati mame, ngati mvula yowaza pa udzu.” (Deut. 31:19, 30; 32:2) Ndiye kodi tingatani kuti utumiki wathu uzifanana ndi mame, n’cholinga choti tizithandiza anthu a mitundu yonse?—1 Tim. 2:3, 4.

 KODI UTUMIKI WATHU UNGAFANANE BWANJI NDI MAME?

Mame amagwa pang’onopang’ono. Mpweya wozizira umasintha mwapang’onopang’ono n’kupanga timadontho ta mame. Tinganene kuti mawu a Yehova ankatsika ngati mame chifukwa chakuti ankalankhula mokoma mtima, modekha komanso moganizira anthu ake. Ifenso tingatsanzire Yehova ngati timalemekeza maganizo a anthu amene timawalalikira. Sitikakamiza anthu kukhulupirira zimene akuphunzira koma timawalimbikitsa kuti aziganizire n’kuona okha ngati zili zolondola kapena ayi. Tikatero zimakhala zosavuta kuti amvetsere mfundo zimene tikuwaphunzitsa komanso ayambe kuzitsatira.

Mame amasangalatsa. Kuti anthu asangalale ndi mfundo zimene timawaphunzitsa, tiyenera kuganizira njira zabwino zowaphunzitsira. Gavin amene tamutchula poyamba uja sanakakamizidwe kuti aziphunzira Baibulo. Koma m’bale wina dzina lake Chris, amene anacheza naye poyamba, anayesetsa kupeza njira yabwino yoti azikambirana naye mfundo za m’Baibulo. Anamuuza kuti Baibulo lonse limakamba za nkhani inayake ndipo akaimvetsa nkhaniyo, zidzakhala zosavuta kumvetsanso zimene amaphunzira pamisonkhano. Kenako anamuuza kuti pali ulosi wina umene unamuthandiza iyeyo kukhulupirira kuti Baibulo ndi lolondola. Izi zinachititsa kuti anthuwa akambirane maulosi osiyanasiyana amene anakwaniritsidwa. Gavin anasangalala kwambiri ndi zimene anakambiranazi ndipo pamapeto pake anavomera kuti aziphunzira Baibulo.

Mame amathandiza kuti zomera zisafe. Ku Israel ndi kotentha kwambiri ndipo nthawi zina kumatha miyezi yambiri kusanagwe mvula. Popanda mame, zomera zimafota n’kufa. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limanena kuti masiku ano padzakhala “ludzu lofuna kumva mawu a Yehova.” (Amosi 8:11) Koma limanenanso kuti Akhristu odzozedwa adzakhala ngati “mame ochokera kwa Yehova” ndipo azidzalalikira uthenga wa Ufumu limodzi ndi a “nkhosa zina.” (Mika 5:7; Yoh. 10:16) Kodi ifeyo timaona kuti uthenga umene timalalikira ndi wochokera kwa Yehova ndipo ungathandize anthu ngati mmene mame amachitira?

Mame ndi madalitso ochokera kwa Yehova. (Deut. 33:13) Anthu amene amamvetsera uthenga wathu amadalitsidwa. Izi ndi zimene zinachitikira Gavin. Atayamba kuphunzira Baibulo anapeza mayankho a mafunso ake onse. Kenako iye ndi mkazi wake Joyce anabatizidwa ndipo panopa amalalikira limodzi uthenga wa Ufumu.

A Mboni za Yehova akulalikira uthenga wa Ufumu padziko lonse

MUZIONA KUTI UTUMIKI WANU NDI WOFUNIKA KWAMBIRI

Kuganizira zimene mame amachita, kungatithandize kuona kuti utumiki wathu ndi wofunika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti dontho limodzi la mame silingathandize chilichonse. Koma madonthowa akakhalapo ambiri amathandiza kuti nthaka inyowe. Mofanana ndi zimenezi, zimene Mkhristu mmodzi amachita polalikira zingaoneke ngati zazing’ono. Koma zimene tonse timachita, zimathandiza kuti uthenga ulalikidwe “ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Choncho tiyeni tiziyesetsa kuti utumiki wathu uzikhala ngati mame, omwe amagwa pang’onopang’ono, amasangalatsa komanso amathandiza kuti zomera zisafe. Tikatero anthu amene timawalalikira adzaona kuti Yehova wawadalitsa powalola kuti aphunzire za iye.