“Tiyeni tiganizirane . . . tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.”​—AHEB. 10:24, 25.

NYIMBO: 90, 87

1. N’chifukwa chiyani Paulo anauza Akhristu achiheberi kuti awonjezere zimene ankachita pa nkhani yolimbikitsana?

N’CHIFUKWA chiyani tiyenera kuwonjezera zimene timachita pa nkhani yolimbikitsa ena? Mtumwi Paulo anafotokoza chifukwa chake m’kalata imene analembera Akhristu achiheberi. Iye anawauza kuti: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheb. 10:24, 25) Pasanathe zaka 5 kuchokera pamene Paulo anapereka malangizowa, Akhristu achiyuda anazindikira kuti tsiku la Yehova layandikira. Anaona chizindikiro chimene Yesu ananena kuti akadzachiona adzathawe mumzindawo. (Mac. 2:19, 20; Luka 21:20-22) Tsikuli linafika mu 70 C.E. pamene Yehova anawononga mzinda wa Yerusalemu pogwiritsa ntchito Aroma.

2. N’chifukwa chiyani masiku ano tiyenera kuganizirana kwambiri komanso kulimbikitsana?

2 Masiku anonso, umboni wakuti ‘tsiku la Yehova lalikulu komanso  lochititsa mantha’ layandikira uli paliponse. (Yow. 2:11) Mneneri Zefaniya analemba kuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.” (Zef. 1:14) Chenjezo limene anaperekali ndi lothandizanso masiku ano. Popeza tsiku la Yehova lili pafupi kwambiri, mtumwi Paulo akutiuza kuti: “Tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.” (Aheb. 10:24) Choncho tiyenera kuganizira kwambiri za abale ndi alongo athu n’cholinga choti tiziwalimbikitsa pa nthawi iliyonse yoyenera.

KODI NDANI AYENERA KULIMBIKITSIDWA?

3. Kodi mtumwi Paulo ananena chiyani pa nkhani yolimbikitsana? (Onani chithunzi choyambirira.)

3 Baibulo limanena kuti: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miy. 12:25) Zimene lembali likunena zimachitikira munthu aliyense. Choncho aliyense amafunika kulimbikitsidwa pafupipafupi. Paulo anasonyeza kuti ngakhale abale amene ali ndi udindo wolimbikitsa ena amafunikanso kulimbikitsidwa. Mwachitsanzo, m’kalata yake yopita kwa Aroma, analemba kuti: “Ndikulakalaka kukuonani kuti ndikugawireni mphatso inayake yauzimu kuti mukhale olimba, kapena kuti tidzalimbikitsane mwa chikhulupiriro, chanu ndi changa.” (Aroma 1:11, 12) Ngakhale kuti Paulo ankalimbikitsa kwambiri anthu ena, nayenso nthawi zina ankafunika kulimbikitsidwa.​—Werengani Aroma 15:30-32.

4, 5. Kodi ndi anthu ati amene amafunika kulimbikitsidwa masiku ano?

4 Abale ndi alongo amene amadzimana zinthu zina kuti atumikire Yehova ayenera kuyamikiridwa. Mwachitsanzo, anthu ambiri amalolera kuti asakhale ndi zinthu zina n’cholinga choti achite upainiya. N’chimodzimodzinso ndi amishonale, atumiki a pa Beteli, oyang’anira madera ndi akazi awo komanso anthu ogwira ntchito m’maofesi omasulira mabuku. Onsewa amadzimana zinthu zina n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Yehova, choncho amafunika kulimbikitsidwa. Anthu ena ofunika kuwalimbikitsa ndi amene amafunitsitsa kuchita utumiki wa nthawi zonse koma pa zifukwa zina sangakwanitse.

5 Tilinso ndi abale ndi alongo amene sali m’banja chifukwa choti sanapeze munthu woti angakwatirane naye “mwa Ambuye.” Anthu oterewa amafunika kuwalimbikitsa. (1 Akor. 7:39) Akazi achikhristu amene amagwira ntchito zapakhomo mwakhama amafunika kulimbikitsidwanso ndi amuna awo. (Miy. 31:28, 31) Akhristu amene amakhalabe okhulupirika pamene akuzunzidwa kapena kudwala amafunikanso kulimbikitsidwa. (2 Ates. 1:3-5) Yehova ndi Khristu amalimbikitsa atumiki okhulupirika onsewa.​—Werengani 2 Atesalonika 2:16, 17.

AKULU AMAYESETSA KUTILIMBIKITSA

6. Mogwirizana Yesaya 32:1, 2, kodi udindo wa akulu ndi wotani?

6 Werengani Yesaya 32:1, 2Yesu Khristu amagwiritsa ntchito “akalonga” omwe ndi akulu odzozedwa komanso a nkhosa zina kuti alimbikitse komanso kutsogolera abale ndi alongo amene akusowa mtendere chifukwa cha mavuto. N’chifukwa chake akuluwa amayesetsa kuti ‘asakhale olamulira chikhulupiriro chathu koma antchito anzathu kuti tikhale ndi chimwemwe.’​—2 Akor. 1:24.

7, 8. Kodi akulu angachitenso zinthu ziti kuti alimbikitse anthu ena?

7 Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Pa nthawi imene Akhristu a ku Tesalonika ankazunzidwa, iye anawalembera kuti: “Popeza timakukondani kwambiri, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeniyeniyo, chifukwa tinakukondani kwambiri.”​—1 Ates. 2:8.

 8 Pozindikira kuti mawu olimbikitsa okha si okwanira, Paulo anauza Akhristu a ku Efeso kuti: “Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.’” (Mac. 20:35) Paulo ankalimbikitsa abale ake koma ankayesetsanso ‘kugwiritsa ntchito zinthu zake zonse ndiponso kudzipereka ndi moyo wake wonse’ pofuna kuwathandiza. (2 Akor. 12:15) Nawonso akulu ayenera kulimbikitsa abale ndi alongo ndiponso kupeza njira zodziwira mavuto awo n’kumawathandiza.​—1 Akor. 14:3.

9. Kodi akulu angatani kuti azipereka malangizo m’njira yolimbikitsa?

9 Kupereka malangizo ndi njira inanso imene akulu angalimbikitsire anthu. Koma pochita zimenezi, akulu ayenera kutsatira zitsanzo zabwino za m’Baibulo n’cholinga choti malangizo awo akhale olimbikitsa. Chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi ndi Yesu. Iye ataukitsidwa anafunika kupereka malangizo amphamvu kumipingo ina ya ku Asia Minor. Koma asanapereke malangizo aliwonse anayamba ndi kuyamikira mpingo wa Efeso, Pegamo ndi Tiyatira. (Chiv. 2:1-5, 12, 13, 18, 19) Yesu anauza mpingo wa ku Laodikaya kuti: “Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho, khala wodzipereka ndipo ulape.” (Chiv. 3:19) Akulu ayenera kutengera chitsanzo cha Yesu popereka malangizo.

ALIYENSE ALI NDI UDINDO WOLIMBIKITSA ENA

Ngati ndinu makolo, kodi mumathandiza ana anu kuti azilimbikitsa ena? (Onani ndime 10)

10. Kodi tonsefe tingatani kuti tizilimbikitsa anzathu?

10 Udindo wolimbikitsa ena si wa akulu okha. Paja Paulo anauza Akhristu onse kuti azilankhula mawu “alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.” (Aef. 4:29) Choncho aliyense ayenera kukhala tcheru kuti azindikire mavuto amene anthu ena akukumana nawo. Paja Paulo analangiza Akhristu achiheberi kuti: “Limbitsani manja amene ali lende ndi mawondo olobodoka, ndipo pitirizani kuwongola njira zimene mapazi anu akuyendamo, kuti chiwalo chimene chavulala  chisaguluke polumikizira, koma chichiritsidwe.” (Aheb. 12:12, 13) Kaya ndife achikulire kapena achinyamata, tikhoza kuuza anzathu mawu olimbikitsa.

11. Kodi mlongo wina analimbikitsidwa bwanji pa nthawi imene ankavutika maganizo?

11 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Marthe. * Pa nthawi ina mlongoyu ankavutika maganizo ndipo analemba kuti: “Tsiku lina ndinapempha Yehova kuti andilimbikitse ndipo ndinakumana ndi mlongo wachikulire amene anasonyeza kuti amandikonda kwambiri komanso amandiganizira ndipo izi n’zimene ndinkafunika pa nthawiyo. Iye anandifotokozera kuti nayenso anakumana ndi mavuto amene ndinkavutika nawo moti ndinamva kuti sindili ndekha.” N’kutheka kuti mlongo wachikulireyo sanazindikire mmene mawu ake analimbikitsira Marthe.

12, 13. Kodi tingachite zinthu ziti potsatira malangizo a pa Afilipi 2:1-4?

12 Paulo anapereka malangizo awa kwa Akhristu onse amumpingo wa Filipi: “Chotero, ngati pakati panu pali kulimbikitsana kulikonse mwa Khristu, kaya kutonthozana kulikonse kwa chikondi, kaya mzimu woganizirana, kaya chikondi chachikulu chilichonse ndi chifundo, chititsani chimwemwe changa kusefukira pokhala ndi maganizo amodzi, ndi chikondi chofanana. Mukhalenso ogwirizana mu mzimu umodzi, ndi mtima umodzi. Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afil. 2:1-4.

13 Malinga ndi lembali, tonsefe tiyenera kusonyeza mzimu woganizira abale ndi alongo athu, kuwatonthoza mwachikondi komanso kuwachitira chifundo n’cholinga choti tiwalimbikitse.

ZINTHU ZIMENE ZINGATILIMBIKITSE

14. Kodi ndi nkhani ziti zimene zingatilimbikitse?

14 Anthufe timalimbikitsidwa tikamva kuti anthu amene tinawathandiza m’mbuyomu akupitirizabe kutumikira Mulungu mokhulupirika. Umu ndi mmene anamveranso mtumwi Yohane pamene analemba kuti: “Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.” (3 Yoh. 4) Apainiya ambiri akhoza kuvomereza kuti amasangalala kwambiri akamva kuti anthu amene anawaphunzitsa choonadi adakali okhulupirika ndipo mwinanso ayamba upainiya. Choncho kukumbutsa mpainiya amene wakhumudwa zinthu zosangalatsa zimene anachita m’mbuyomo, kungamulimbikitse kwambiri.

15. Kodi tingayamikire bwanji anthu amene akutumikira Yehova mokhulupirika?

15 Oyang’anira madera ndi akazi awo amayamikiranso kwambiri akalandira kakalata kowayamikira pambuyo pochezera mpingo. Ndi mmenenso amamvera akulu, amishonale, apainiya komanso atumiki a pa Beteli akalandira uthenga woyamikira zimene akuchita potumikira Mulungu.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZILIMBIKITSA ENA

16. Kodi chimafunika n’chiyani kuti tilimbikitse munthu?

16 Si nzeru kuganiza kuti ifeyo sitingalimbikitse munthu chifukwa choti timasowa chonena pocheza ndi anthu. Tikutero chifukwa chakuti kulimbikitsa munthu sikufuna zambiri. Ngakhale tikangomwetulira popereka moni kwa munthu timakhala titamulimbikitsa. Ngati munthu winayo wayankha moniyo popanda kumwetuliranso zingasonyeze kuti mwina pali vuto linalake. Ndiyeno kumumvetsera munthu woteroyo kungamulimbikitse kwambiri.​—Yak. 1:19.

17. Kodi m’bale wina anathandizidwa bwanji pa nthawi imene anali wokhumudwa?

17 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wachinyamata dzina lake Henri. Iye anakhumudwa  kwambiri abale ake ena komanso bambo ake, omwe anali mkulu, atasiya choonadi. Henri anasangalala kwambiri pamene woyang’anira dera anamutengera kumalo enaake kukamugulira kachakudya kenako n’kuyamba kucheza naye kuti adziwe zimene zili mumtima mwake. Henri anazindikira kuti akhoza kuthandiza abale akewo kubwerera m’choonadi ngati iyeyo angakhalebe wokhulupirika. Analimbikitsidwa kwambiri atawerenga lemba la Salimo 46; Zefaniya 3:17 ndiponso Maliko 10:29, 30.

Udindo wolimbikitsa ena ndi wa tonse (Onani ndime 18)

18. (a) Kodi Solomo anasonyeza kuti n’chiyaninso chimene chingalimbikitse munthu? (b) Kodi Paulo anatchulanso chinthu china chiti chimene chingatilimbikitse?

18 Nkhani ya Marthe komanso ya Henri zikusonyeza kuti n’zotheka kulimbikitsa munthu amene akuda nkhawa. Paja Mfumu Solomo analemba kuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri. Maso owala amapangitsa mtima kusangalala. Uthenga wabwino umanenepetsa mafupa.” (Miy. 15:23, 30) Kuwerenga magazini a Nsanja ya Olonda komanso nkhani zapawebusaiti yathu kukhoza kulimbikitsa munthu amene ali ndi nkhawa. Paulo anasonyeza kuti kuimba nyimbo za Ufumu limodzi kumalimbikitsanso. Iye analemba kuti: “Pitirizani kuphunzitsana ndi kulangizana [kapena kuti “kulimbikitsana” *] mwa masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu zogwira mtima. Pitirizani kuimbira Yehova m’mitima yanu.”​—Akol. 3:16; Mac. 16:25.

19. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kulimbikitsana kudzakhala kofunika kwambiri m’tsogolomu, ndipo tiyenera kuchita chiyani?

19 Pamene tsiku la Yehova “likuyandikira,” anthufe tizifunika kulimbikitsana kwambiri. (Aheb. 10:25) Paja Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukuchitira.”​—1 Ates. 5:11.

^ ndime 11 Mayina asinthidwa.

^ ndime 18 Mogwirizana ndi Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi lokonzedwanso mu 2013.