Poyamba mawu a pa Salimo 144:12-15 ankanena za anthu oipa amene atchulidwa muvesi 11. Koma m’Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi lokonzedwanso mu 2013, mawuwa akunena za anthu a Mulungu? N’chifukwa chiyani asinthidwa?

Malinga ndi mmene mavesiwa anawalembera m’Chiheberi, n’zotheka kuwamasulira m’njira ziwiri zonsezi. Ngakhale zili choncho, pokonzanso Baibuloli anaganiza zosintha pa zifukwa zotsatirazi:

  1. Kamasuliridwe katsopanoka n’kogwirizana ndi malamulo a chilankhulo. Munthu akhoza kuona mgwirizano wa pakati pa vesi 12 mpaka 15 ndi mavesi ena oyambirira, ngati atamvetsa tanthauzo la mawu oyambirira muvesi 12. M’chiheberi, mawu oyambirira a muvesi 12 ndi akuti asher ndipo akhoza kumasuliridwa m’njira zosiyanasiyana. Akhoza kumasuliridwa ngati mlowam’malo woimira munthu kapena anthu amene atchulidwa kale. Ndipo umu ndi mmene zinkamvekera m’Baibulo lathu lachingelezi lisanakonzedwenso mu 2013. Zotsatira zake zinali zakuti madalitso amene atchulidwa muvesi 12 mpaka 14 ankaoneka kuti ndi a anthu oipa amene atchulidwa kale. Koma mawu oti asher akhoza kumasuliridwanso kuti “n’cholinga choti,” “kuti” kapena “zikatero.” Ndiyeno pomasulira Baibulo lomwe linatuluka mu 2013, anagwiritsa ntchito mawu oti “zikatero” ndipo umu ndi mmenenso zilili m’Mabaibulo ena.

  2. Kamasuliridwe katsopanoka n’kogwirizana ndi mawu ena onse musalimoli. Kugwiritsa ntchito mawu oti “zikatero” muvesi 12 kukuthandiza anthu kuona kuti madalitso otchulidwa muvesi 12 mpaka 14 ndi a anthu olungama amene amapempha kuti apulumutsidwe kwa anthu oipa achilendo amene atchulidwa muvesi 11. Mfundo imeneyi ikuonekeranso muvesi 15 chifukwa chakuti mawu oti “odala” akutchulidwa mosonyeza kuti akunena za anthu abwinowo osati za anthu ena. Chifukwa cha zimenezi, malo awiri amene pali mawu oti “odala” amaonekeratu kuti akunena za anthu amene “Mulungu wawo ndi Yehova.” Mfundo ina yofunika kuikumbukira ndi yakuti m’Chiheberi, anthu sankalemba zizindikiro za m’kalembedwe monga zosonyeza kuti mawu enaake ananenedwa ndi winawake. Choncho omasulira amafunika kuzindikira tanthauzo la mawu amene akumasulira lomwe likugwirizana ndi kalembedwe ka Chiheberi, nkhani imene akumasulira komanso nkhani zina za m’Baibulo zimene n’zogwirizana ndi nkhaniyo.

  3. Kamasuliridwe katsopanoka kakugwirizana ndi nkhani zina za m’Baibulo zofotokoza madalitso amene Mulungu adzapatse anthu okhulupirika. Kamasuliridwe katsopanoka kakusonyeza kuti Davide sankakayikira mfundo yakuti Mulungu akadzapulumutsa mtundu wa Isiraeli kwa adani awo, Aisiraeliwo adzakhala osangalala ndiponso zinthu zizidzawayendera bwino. (Lev. 26:9, 10; Deut. 7:13; Sal. 128:1-6) Paja lemba la Deuteronomo 28:4 limanena kuti: “Chidzadalitsika chipatso cha mimba yako, chipatso cha m’dziko lanu, chipatso cha ziweto zako, ana a ng’ombe zako ndi ana a nkhosa zako.” Ndipo izi n’zimene zinachitika mu ulamuliro wa mwana wa Davide dzina lake Solomo. Aisiraeli anali pa mtendere ndipo zinthu zinkawayendera bwino. Tisaiwalenso kuti zinthu zina mu ulamuliro wa Solomo zinkasonyeza mmene zidzakhalire mu ulamuliro wa Mesiya.​—1 Maf. 4:20, 21; Sal. 72:1-20.

Pomaliza, tinganene kuti kusintha kamasuliridwe ka Salimo 144, sikukusintha zimene timakhulupirira m’Baibulo. M’malomwake kukungosonyeza bwino mfundo zimene atumiki a Yehova akhala akuzikhulupirira kwa nthawi yaitali zoti Yehova adzawononga oipa ndipo zikatero anthu olungama azidzakhala mwamtendere komanso mosangalala.​—Sal. 37:10, 11.