Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) April 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa June 4 mpaka July 8, 2018.

Kodi Tingapeze Bwanji Ufulu Weniweni?

Anthu ena amalakalaka kuti asamaponderezedwe, kusankhidwa komanso kuti asakhale osauka. Koma ena amalakalaka atakhala ndi ufulu wolankhula kapena wosankha zimene amafuna. Kodi n’zotheka kukhala ndi ufulu weniweni?

Tizitumikira Yehova Mulungu Amene Amapereka Ufulu

Kodi mzimu wa Yehova umatithandiza bwanji kukhala ndi ufulu? Kodi tingatani kuti tisamagwiritse ntchito molakwika ufulu umene Mulungu amatipatsa?

Kodi Akulu ndi Atumiki Othandiza Angaphunzire Chiyani kwa Timoteyo?

Zikuoneka kuti Timoteyo ankadzikayikira pamene ankayamba kugwira ntchito ndi mtumwi Paulo. Kodi akulu ndi atumiki othandiza angaphunzire chiyani kwa Timoteyo?

Tizitsanzira Yehova pa Nkhani Yolimbikitsa Ena

Anthu a Yehova nthawi zonse akhala akufunika kulimbikitsidwa.

Tizilimbikitsana Ndipo “Tiwonjezere Kuchita Zimenezi”

Popeza tsiku la Yehova layandikira, tikuyenera kumachita chidwi ndi abale athu kuti tizitha kuwalimbikitsa pa nthawi yoyenera.

Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kukwaniritsa Zolinga Zauzimu?

Achinyamata akapatsidwa mwayi wochita zinthu zosiyanasiyana amafunika kusankha zochita. Kodi n’chiyani chingawathandize kusankha mwanzeru zinthu zoti adzachite m’tsogolo?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani si zololeka kuika pawebusaiti ina kapena pamalo ochezera a pa intaneti zinthu zimene a Mboni za Yehova amafalitsa?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani mawu a pa Salimo 144 asinthidwa mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso?