Tsiku lina ndili ku Colorado ndinalandira foni yochokera ku Beteli ya ku Patterson. M’bale wina dzina lake Izak Marais ndi amene anaimba. Atandiuza zomwe ankafuna ndinamufunsa kuti: “Mukudziwa kuti ndili ndi zaka zingati?” Iye anayankha kuti: “Ee ndikudziwa bwinobwino.” Mwina ndikufotokozereni zimene zinachitika.

NDINABADWA pa December 10, 1936, ku Wichita m’dziko la United States. M’banja lathu tinalimo ana 4 ndipo ine ndine woyamba. Bambo anga anali a William ndipo mayi anga anali a Jean ndipo onse ankatumikira Yehova mokhulupirika. Bambo anga anali mtumiki wa mpingo. Mayi anaphunzitsidwa Baibulo ndi amayi awo dzina lawo a Emma Wagner. Agogowa anaphunzitsa choonadi anthu ambiri monga a Gertrude Steele amene anachita umishonale ku Puerto Rico kwa zaka zambiri. * Choncho panali anthu ambiri a zitsanzo zabwino oti nditengere.

ZITSANZO ZABWINO ZIMENE NDIKUKUMBUKIRA

Bambo anga akugawira magazini pamsewu

Loweruka lina, ine ndi abambo tinkagawira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pamsewu. Pa nthawiyi ndinali ndi zaka 5 ndipo n’kuti zinthu zisali bwino chifukwa cha nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Ndiyeno panafika dokotala woledzera n’kuyamba kulalatira bambo chifukwa choti sankalola kulowa usilikali. Anawayandikira kwambiri n’kunena kuti: “Sungandimenye iwe! Mantha ake amenewo?” Ndinachita mantha kwambiri koma ndinadabwa kuona zimene bambowo anachita. Ankangopereka magazini kwa anthu osamusamala. Ndiyeno patafika msilikali wina dokotalayo anamuuza kuti: “Uyutu musangomusiyasiya.” Msilikaliyo ataona kuti dokotalayo anali woledzera anangomuuza kuti: “Pita uko waledzera iwe!” Onse ananyamuka n’kumapita. Ndimayamikira kwambiri kuti Yehova anathandiza bambo anga kukhala olimba mtima. Bambowa anali ndi malo awiri ometera ku Wichita ndipo dokotalayo ankabwera kudzametetsa.

Ndikupita kumsonkhano wachigawo limodzi ndi makolo anga ku Wichita mu 1940

Ndili ndi zaka 8, makolo anga anagulitsa nyumba ndi mashopu awo n’kukonza kakalavani. Kenako tinasamukira ku Colorado chifukwa kunkafunika ofalitsa ambiri. Tinkakhala pafupi ndi misewu ina ndipo makolo anga ankachita upainiya kwinaku n’kumalima komanso kuweta ziweto. Yehova anawadalitsa chifukwa cha khama lawo ndipo  mpingo unakhazikitsidwa. Pa June 20, 1948 bambo anga anandibatiza ineyo, Billie ndi mkazi wake komanso anthu ena. Kenako Billie komanso mwana wake anakhala oyang’anira dera.

Tinkalimbikitsana kwambiri ndi abale ndi alongo ena amene ankalalikiranso mwakhama kumeneko. Ena mwa anthuwa anali Don ndi Earlene, Dave ndi Julia komanso Si ndi Martha ndipo onsewa anali a m’banja la Steele. Anthu amenewa anandithandiza kwambiri kudziwa kuti munthu akaika Ufumu pamalo oyamba, amakhala wosangalala kwambiri.

NDINASAMUKANSO

Ndili ndi zaka 19, mnzathu wina dzina lake Bud Hasty anandipempha kuti ndikalalikire naye kum’mwera kwa United States. Woyang’anira dera anatipempha kuti tipite ku Ruston, Louisiana chifukwa choti kumeneko kunali ofalitsa ambiri ofooka. Anatiuza kuti tizikachita misonkhano yonse mlungu uliwonse mosayang’ana kuti pafika anthu angati. Tinapeza malo abwino ochitira misonkhano ndipo tinawakonza bwinobwino. Kwa nthawi yaitali, pamisonkhano tinkangokhalapo anthu awiri basi moti wina akapita kupulatifomu, wina ankayankha mafunso onse. Ndiyeno mlongo wina wachikulire anayambanso kupezekapo. Kenako anthu ena amene tinkaphunzira nawo Baibulo komanso a Mboni ena amene anafooka anayamba kufika. Pasanapite nthawi unakhala mpingo wamphamvu.

Tsiku lina, ine ndi Bud tinakumana ndi m’busa wa Mpingo wa Khristu. Iye anatchula malemba amene ine sindinkawadziwa bwino. Izi zinandidabwitsa moti ndinayamba kuganizira kwambiri zimene ndimakhulupirira. Kwa mlungu wathunthu, ndinkafika pakati pa usiku ndikufufuza mayankho a mafunso amene anafunsa. Izi zinandithandiza kuti ndiyambe kukonda kwambiri choonadi ndipo ndinkalakalaka kukumana ndi m’busa wina.

Kenako woyang’anira dera anandipempha kuti ndipite kukathandiza mpingo wina wa ku El Dorado ku Arkansas. Ndili kumeneko ndinkapitapita ku Colorado kukaonekera kwa anthu amene ankalemba asilikali. Pa ulendo wina, ndili ndi apainiya angapo, tinachita ngozi ku Texas ndipo galimoto yanga inathera pomwepo. Tinaimbira foni m’bale wina amene anatitengera kunyumba kwawo ndipo kenako tinapita kumisonkhano. Misonkhano itatha, analengeza kuti tinachita ngozi ndipo abale ndi alongo anatithandiza potipatsa ndalama. Komanso m’bale uja anandigulitsira chiphapha cha galimoto yangayo ndalama zokwana madola 25.

 Ndiyeno tinapita ku Wichita kumene mnzathu wina dzina lake Doc ankachita upainiya. Anali ndi ana awiri amapasa ndipo mayina awo ndi Frank ndi Francis. Ndinkagwirizana nawo kwambiri ndipo mpaka pano timagwirizanabe. Iwo anali ndi galimoto yakale ndipo anandigulitsa pa mtengo wa madola 25. Nditaona kuti ndi ndendende ndalama zimene ndinagulitsira chiphapha chija, ndinadziwa kuti Yehova akundithandiza chifukwa choika Ufumu pamalo oyamba. Pa ulendowu, anzangawa anandisonyeza mlongo wina wokongola komanso wokonda Yehova dzina lake Bethel Crane. Mayi ake anali a Ruth ndipo ankalalikira mwakhama ku Wellington. Iwo ankachitabe upainiya ali ndi zaka za m’ma 90. Pasanathe chaka, ine ndi Bethel tinakwatirana mu 1958. Nayenso anayamba upainiya ndipo tinkalalikira limodzi ku El Dorado.

TINASANGALALA TITAITANIDWA KUSUKULU YA GILIYADI

Chifukwa choganizira kwambiri anthu a zitsanzo zabwino aja, tinali okonzeka kuchita chilichonse chimene gulu la Yehova lingatipemphe. Ndiyeno tinapemphedwa kuti tikachite upainiya wapadera ku Walnut Ridge ku Arkansas. Mu 1962, tinasangalala kwambiri titaitanidwa kuti tikalowe kalasi ya nambala 37 ya Sukulu ya Giliyadi. Tinasangalalanso kukaphunzira limodzi ndi a Don Steele. Titamaliza maphunziro, ine ndi Bethel anatitumiza ku Nairobi m’dziko la Kenya. Pamene tinkachoka ku New York tinadandaula kwambiri. Koma titangofika pabwalo la ndege ku Nairobi n’kulandiridwa ndi abale, tinasangalala kwambiri.

Tili mu utumiki ku Nairobi limodzi ndi a Mary ndi a Chris Kanaiya

Tinayamba kusangalala kwambiri ku Kenya ndipo utumiki unkayenda bwino kwabasi. Tinayamba kuphunzira Baibulo ndi Chris Kanaiya ndi mkazi wake Mary. Phunzirolo linkayenda bwino kwambiri ndipo banjali likuchitabe utumiki wa nthawi zonse ku Kenya. Chaka chotsatira, tinapemphedwa kuti tipite ku Kampala m’dziko la Uganda ndipo tinali amishonale oyambirira m’dzikoli. Utumiki unkasangalatsa kwabasi chifukwa anthu ambiri ankaphunzira Baibulo ndipo anakhala a Mboni za Yehova. Koma titakhala zaka zitatu ndi hafu ku Africa, tinaganiza zobwerera ku United States kuti tikakhale ndi ana. Tsiku limene tinkachoka ku Africa tinadandaula kwambiri kuposa tsiku limene tinkachoka ku New York lija. Zinali choncho chifukwa tinkagwirizana kwambiri ndi anthu a ku Africa ndipo tinkayembekezera kuti tidzabwererako.

UDINDO WOLERA ANA

Tinapita kukakhala pafupi ndi makolo anga ku Colorado. Pasanapite nthawi yaitali, mwana wathu woyamba dzina lake Kimberly anabadwa. Patadutsa miyezi 17, tinakhalanso ndi mwana wina dzina lake Stephany. Tinkaona kuti udindo wolera ana ndi waukulu kwambiri ndipo tinkayesetsa kuwathandiza kuti azikonda kwambiri Yehova. Pa nkhani imeneyi, tinkafunanso kutengera anthu a zitsanzo zabwino. Tinkadziwa kuti chitsanzo chathu chikhoza kuwathandiza kwambiri. Koma tinkadziwanso kuti munthu amasankha yekha kuti azitumikira Yehova kapena ayi. Mng’ono wanga komanso mchemwali wanga anasiya choonadi. Tikukhulupirira kuti adzatengeranso anthu a zitsanzo zabwino kuphatikizapo ifeyo.

Tinkasangalala kwambiri kulera ana athu ndipo tinkayesetsa kuchitira nawo limodzi zinthu. Popeza tinkakhala pafupi ndi kumapiri, tinkapita limodzi kukachita masewera otsetsereka pa sinowo. Tikamasewera, tinkakhala ndi mpata wokambirana nawo zinthu zambiri. Nthawi zina tinkapita kumalo ena ndi tenti n’kukagona komweko ndipo  tinkacheza, uku tikuwotha moto. Ngakhale kuti anawo anali ang’onoang’ono, ankatifunsa mafunso monga akuti: “Kodi ndikadzakula ndidzachita chiyani?” “Kodi ndidzakwatiwe ndi munthu wotani?” Tinkayesetsa kuthandiza ana athuwa kuti azikonda kwambiri Yehova. Tinawathandiza kuzindikira ubwino wa utumiki wa nthawi zonse komanso wokwatirana ndi munthu wokonda utumiki. Tinkawalimbikitsanso kuti asathamangire kukwatiwa adakali aang’ono. Tinkakonda kunena kuti: “Ndi bwino kukhala osakwatiwa mpaka mutafika zaka 23.”

Tinkayesetsanso kutsanzira makolo athu. Tinkapita limodzi ndi ana athu kumisonkhano komanso mu utumiki. Nthawi zina tinkaitana anthu amene ankachita utumiki wa nthawi zonse kuti adzakhale kwathu. Tinkakondanso kufotokoza zinthu zosangalatsa zimene zinachitika tili amishonale. Tinkanena kuti mwina tsiku lina tonse tidzapita limodzi ku Africa. Ana athu ankafunitsitsa zimenezi zitatheka.

Tinkaphunzira Baibulo limodzi ndipo tinkayesezera zimene zingachitike kusukulu. Tinkauza ana athuwo kuti aziyerekezera kuyankha mafunso a anzawo a kusukulu. Ankasangalala kwambiri kuphunzira m’njira imeneyi ndipo zinkawathandiza kukhala olimba mtima. Atayamba kukula nthawi zina ankadandaula tikanena kuti tichite phunziro la banja. Tsiku lina ndinawauza kuti basi sitiphunzira. Koma izi zinawakhudzanso ndipo anayamba kulira. Apa m’pamene ndinazindikira kuti tikuwathandiza kukonda kwambiri Mulungu. Ndiyeno atakula ankakonda kwambiri kuphunzira ndipo ankafotokoza maganizo awo momasuka. Nthawi zina zinkatipweteka tikawamva akunena kuti sakugwirizana ndi mfundo ina imene timakhulupirira. Komabe zinkatithandiza kudziwa zimene zili mumtima mwawo. Ndiyeno tikakambirana nawo mwachifatse, ankayamba kukhala ndi maganizo a Yehova pa nkhaniyo.

TINAFUNIKA KUSINTHA ZAMBIRI

Timaona kuti ntchito yolera ana athu inayenda mofulumira kuposa mmene tinkaganizira. Tinayesetsa kuwathandiza kuti azikonda Yehova ndipo malangizo a gulu la Yehova ndi amene atithandiza kwambiri. Tinasangalala kwambiri kuona kuti ana athuwo atangomaliza sukulu anayamba upainiya ndipo anapeza zochita kuti azipeza kangachepe. Atsikanawa limodzi ndi anzawo awiri, anasamukira ku Cleveland ku Tennessee kukachita upainiya. Tinkawasowa kwambiri koma tinkasangalala kudziwa kuti akuchita utumiki wa nthawi zonse. Ine ndi mkazi wanga tinayambiranso upainiya ndipo izi zinatithandiza kuti tipezenso mwayi wina. Ndinkatumikira ngati woyang’anira dera wogwirizira komanso ndinkathandiza pamisonkhano yachigawo.

Ana athuwa asanasamukire ku Tennessee, anapita ku London ku England ndipo anakafika kunthambi. Pa nthawiyo, Stephany anali ndi zaka 19 ndipo anakumana ndi m’bale wina wachinyamata dzina lake Paul Norton, yemwe ankatumikira pa Beteli. Pa ulendo wachiwiri, Kimberly anakumana ndi mnzake wa Paul, dzina lake Brian Llewellyn. Paul ndi Stephany anakwatirana ndipo pa nthawiyi n’kuti Stephany atakwanitsa zaka 23. Chaka chotsatira, Brian ndi Kimberly nawonso anakwatirana ndipo pa nthawiyi n’kuti Kimberly ali ndi zaka 25. Tingati anawa anamvera mawu athu aja oti: “Ndi bwino kukhala osakwatiwa mpaka mutafika zaka 23.” Timayamikira kuti ana athu anasankha bwino anthu oti akwatirane nawo.

Tili ndi Paul ndi Stephany komanso Kimberly ndi Brian kunthambi ya ku Malawi mu 2002

Kimberly ndi Stephany amanena kuti chitsanzo chathu komanso cha agogo awo chawathandiza kutsatira malangizo a Yesu akuti: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba.” (Mat. 6:33) Iwo akhala akutsatira malangizowa ngakhale atakumana ndi mavuto azachuma. Mu April 1998, Paul ndi Stephany anaitanidwa kuti akalowe kalasi ya nambala 105 ya Giliyadi. Kenako anatumizidwa ku Africa m’dziko la Malawi. Pa nthawi yomweyinso, Brian ndi Kimberly anaitanidwa kuti azikatumikira ku Beteli ya ku London ndipo kenako anatumizidwanso ku Malawi. Timasangalala kwambiri kuti ana athuwa asankha kutumikira Yehova.

TINAITANIDWANSO KUTI TIKACHITE UTUMIKI WINA

Mu January 2001, ndinalandira foni imene ndaitchula kumayambiriro ija. M’bale Marais, amene amayang’anira ntchito yomasulira padziko lonse ndi amene anaimba. Anati pakufunika abale oti akaphunzitse Chingelezi kwa abale ndi alongo  omasulira mabuku. Pa nthawiyo n’kuti ndili ndi zaka 64 ndipo ndinasankhidwa kuti ndikhale m’gulu lokaphunzitsalo. Ine ndi mkazi wanga tinaipempherera kwambiri nkhaniyi ndipo tinakambirana ndi amayi anga komanso apongozi anga. Onse anatilimbikitsa kuti tipite ngakhale kuti ankafunika thandizo lathu. Ndiyeno ndinaimbira M’bale Marais n’kumuuza kuti tipita.

Kenako mayi anga anapezeka ndi khansa. Ndiyeno ndinawauza kuti sitipita n’cholinga choti tiziwasamalira mothandizana ndi mchemwali wanga dzina lake Linda. Mayiwo anayankha kuti: “Zimenezotu sizitheka. Ngati simupita ine sindimva bwino.” Nayenso Linda ankafuna kuti tipite basi. Tinasangalala kwambiri chifukwa cha mtima umene mayi ndi Linda anasonyeza komanso mmene abale ndi alongo ankawathandizira. Titapita ku Patterson tsiku lotsatira, Linda anatiimbira foni yonena kuti mayi anga amwalira. Tinkadziwa kuti akanakhala moyo akanatilimbikitsa kuti tizingochita utumiki wathuwo mwakhama, choncho tinachita zomwezo.

Chosangalatsa kwambiri chinali chakuti dziko loyamba kupitako kunali ku Malawi komwe ana athu aja ankatumikira. Tinasangalala kwambiri kukumananso. Pambuyo pake anatiuza kuti tipite ku Zimbabwe ndipo kenako tinapita ku Zambia. Titachita utumikiwu kwa zaka zitatu ndi hafu tinapemphedwa kuti tipitenso ku Malawi. Apa tsopano tinakathandiza kulemba zimene abale ndi alongo a m’dzikoli anakumana nazo pa nthawi ya chizunzo. *

Tikulalikira ndi zidzukulu zathu

Ndiyeno mu 2005, ine ndi mkazi wanga tinabwereranso ku Colorado n’kumakapitiriza upainiya. Mu 2006, Brian ndi Kimberly anabwera kudzakhala nafe ndipo nawonso ali ndi ana awiri. Woyamba dzina lake ndi Mackenzie ndipo wachiwiri ndi Elizabeth. Paul ndi Stephany adakali ku Malawi ndipo Paul ali mu Komiti ya Nthambi. Panopa ndili ndi zaka pafupifupi 80 ndipo ndimasangalala kuona achinyamata amene ndatumikira nawo akugwira ntchito zimene ndinkachita. Zitsanzo zabwino zimene anthu ena anatisonyeza n’zimene zatithandiza kuti titumikire Yehova mosangalala kwa zaka zonsezi. Ifenso tayesetsa kupereka chitsanzo chabwino kwa ana athu komanso zidzukulu zathu.

^ ndime 5 Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 1, 1956, tsamba 269 mpaka 272, ndi ya March 15, 1971, tsamba 186 mpaka 190 kuti mumve za anthu a m’banja la a Steele.

^ ndime 30 Mwachitsanzo, onani mbiri ya moyo wa a Trophim Nsomba mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2015 tsamba 14 mpaka 18.