“Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.”—AHEB. 11:1.

NYIMBO: 81, 134

1, 2. (a) Kodi zimene Akhristufe tikuyembekezera zikusiyana bwanji ndi zimene anthu a m’dzikoli amayembekezera? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

AKHRISTUFE tikuyembekezera zinthu zofunika komanso zabwino kwabasi. Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” tikuyembekezera nthawi imene cholinga cha Mulungu choyambirira chidzakwaniritsidwe, dzina lake n’kuyeretsedwa. (Yoh. 10:16; Mat. 6:9, 10) Yehova watilonjezanso moyo wosatha moti Akhristu ena adzapita kumwamba pomwe ena adzakhala padziko lapansi. (2 Pet. 3:13) Panopa, tikudziwa kuti Yehova apitiriza kutitsogolera komanso kutithandiza m’masiku otsirizawa.

2 Anthu a m’dzikoli amayembekezeranso zinthu zosiyanasiyana koma sakhala otsimikiza ngati zingachitikedi. Mwachitsanzo, amene amatchova juga amayembekezera kuti awina koma sangatsimikize zoti awinadi. Koma Akhristufe timatsimikizira ndi mtima wonse kuti zimene tikuyembekezera zidzachitikadi. (Aheb. 11:1) Koma kodi tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri zinthu zimene tikuyembekezera? Nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji?

3. N’chifukwa chiyani timakhulupirira kwambiri zimene Mulungu watilonjeza?

3 Munthu sabadwa ndi chikhulupiriro ndipo sichibwera chokha. Mkhristu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa choti mzimu  woyera ukumuthandiza. (Agal. 5:22) Baibulo silinena kuti Yehova ali ndi chikhulupiriro kapena kuti amafunika chikhulupiriro. Iye ndi Wamphamvuyonse ndipo ali ndi nzeru zopanda malire choncho sangalephere kukwaniritsa cholinga chake. Sakayikira zoti adzakwaniritsa lonjezo lakuti adzadalitsa anthu ake. Kwa iye zili ngati “zakwaniritsidwa” kale. (Werengani Chivumbulutso 21:3-6.) Akhristufe timakhala ndi chikhulupiriro chifukwa chodziwa kuti Yehova ndi Mulungu wokhulupirika ndipo amakwaniritsa chilichonse chimene walonjeza.—Deut. 7:9.

TIZITSANZIRA CHIKHULUPIRIRO CHA ANTHU AKALE

4. Kodi anthu amene anamwalira Yesu asanabwere padzikoli akuyembekezera chiyani?

4 Chaputala 11 cha buku la Aheberi chimatchula za amuna ndi akazi okwana 16 amene anali ndi chikhulupiriro. Paulo anatchula za anthuwa komanso za ena ambiri amene “anachitiridwa umboni chifukwa cha chikhulupiriro chawo.” (Aheb. 11:39) Onsewa anali ndi “chiyembekezo chotsimikizika” choti Mulungu adzatumiza “mbewu” imene idzaphwanye mutu wa Satana n’kukwaniritsa cholinga cha Mulungu choyambirira. (Gen. 3:15) Koma anthu okhulupirika amenewa anamwalira Yesu Khristu yemwe ndi “mbewu,” asanatsegule njira yoti anthu ena adzapite kumwamba. (Agal. 3:16) Komabe popeza Yehova amakwaniritsa malonjezo ake, anthuwa adzaukitsidwa ndipo adzakhala m’paradaiso.—Sal. 37:11; Yes. 26:19; Hos. 13:14.

5, 6. Kodi Abulahamu ndi banja lake ankachita zotani kuti chikhulupiriro chawo chikhalebe cholimba? (Onani chithunzi patsamba 21.)

5 Ponena za anthu ena amene anakhalako Chikhristu chisanayambe, lemba la Aheberi 11:13 limati: “Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro, ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo. Koma anawaona ali patali ndi kuwalandira.” Anthuwa ankayembekezera dziko latsopano ndipo ankaganizira mmene angasangalalire atakhala m’dzikolo. Mmodzi mwa anthu amenewa anali Abulahamu. Yesu ananena kuti Abulahamu ‘ankasangalala’ akaganizira mmene zinthu zidzakhalire pa nthawi imeneyo. (Yoh. 8:56) N’chimodzimodzinso ndi Sara, Isaki, Yakobo ndi ena ambiri amene ankaganizira kwambiri za madalitso amene adzapeze mu Ufumu. Ufumuwu uli ngati “mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.”—Aheb. 11:8-11.

6 Kodi Abulahamu ndi banja lake ankachita zotani kuti chikhulupiriro chawo chikhalebe cholimba? Iwo ankapitiriza kuphunzira za Mulungu. Mulunguyo ankalankhula nawo pogwiritsa ntchito angelo, masomphenya kapena maloto. Koma n’kuthekanso kuti ankamva zinthu zina kuchokera kwa anthu ena akuluakulu okhulupirika ndiponso m’zolemba zakale. Chofunika kwambiri n’chakuti iwo ankaganizira malonjezo a Mulungu ndipo sankakayikira zoti adzakwaniritsidwa. Izi zinawathandiza kuti akhalebe okhulupirika ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto.

7. Kodi Yehova watipatsa zinthu ziti kuti tikhalebe ndi chikhulupiriro cholimba, nanga ifeyo tiyenera kuchita chiyani?

7 Yehova watipatsa Baibulo lathunthu kuti litithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. M’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kuti tizisangalala. Choncho ndi bwino kuyesetsa kuti tiziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. (Sal. 1:1-3; werengani Machitidwe 17:11.) Mofanana ndi atumiki a Mulungu akale, tiyenera kuganizira kwambiri malonjezo a Yehova komanso kumvera malangizo ake. Yehova amagwiritsanso ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitipatsa chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera. (Mat. 24:45) Tiyeni tizigwiritsa ntchito zinthu zonse zimene Yehova  amatipatsa. Tikatero tidzafanana ndi atumiki akale okhulupirika omwe ankayembekezera Ufumu wa Mulungu ndipo sankakayikira malonjezo ake.

8. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba?

8 Pemphero linkathandizanso atumiki a Yehova akale kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Akazindikira kuti Yehova wayankha mapemphero awo, iwo ankayamba kumukhulupirira kwambiri. (Neh. 1:4, 11; Sal. 34:4, 15, 17; Dan. 9:19-21) Nafenso tiyenera kupemphera kuchokera mumtima. Tisamakayikire zoti adzatiyankha komanso kutithandiza kuti tizisangalala ngakhale kuti timakumana ndi mavuto. Ndipo tikazindikira kuti Yehova watiyankha, chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri. (Werengani 1 Yohane 5:14, 15.) Koma tizikumbukiranso kuti mzimu wa Mulungu ndi umene umatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro. Choncho tiyeni tizitsatira malangizo a Yesu oti tipitirize kupempha Mulungu kuti azitipatsa mzimu wake.—Luka 11:9, 13.

9. Kodi tiyenera kupemphereranso ndani?

9 Koma si bwino kumangopemphera kwa Yehova tikafuna thandizo. Tiyeneranso kumuyamika komanso kumutamanda chifukwa cha zinthu zambiri zimene wachita. (Sal. 40:5) Mapemphero athu ayenera kusonyeza kuti timaganiziranso ‘amene ali m’ndende ngati kuti tamangidwa nawo limodzi.’ Tiyeneranso kupempherera abale athu padziko lonse makamaka amene ‘akutitsogolera.’ Ndipotu timayamikira kwambiri tikaona kuti Yehova wayankha mapemphero athu.—Aheb. 13:3, 7.

ANAKHALABE OKHULUPIRIKA

10. (a) Tchulani zitsanzo za atumiki a Mulungu amene anakhalabe okhulupirika. (b) Kodi n’chiyani chinawathandiza kuti asagonje?

10 Muchaputala 11 cha Aheberi, mtumwi Paulo anafotokoza za mayesero amene atumiki ena a Mulungu anakumana nawo. Mwachitsanzo, iye anati akazi ena ana awo anamwalira koma anawalandiranso ataukitsidwa. Kenako anatchula za anthu enanso amene “sanalole kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe. Iwo anachita zimenezi kuti adzauke kwa akufa, komwe ndi kuuka kwabwino kwambiri.” (Aheb. 11:35) Sitikudziwa kuti apa Paulo ankanena za ndani. Koma pali anthu monga Naboti komanso Zekariya amene anaponyedwa miyala mpaka kufa chifukwa choti anamvera Mulungu komanso ankachita chifuniro chake. (1 Maf. 21:3, 15; 2 Mbiri 24:20, 21) Nayenso Danieli ndi anzake akanatha ‘kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe.’ Koma chifukwa choti anali ndi chikhulupiriro cholimba, sanachite zimenezi ndipo tingati “anatseka mikango pakamwa” komanso “anagonjetsa mphamvu ya moto.”—Aheb. 11:33, 34; Dan. 3:16-18, 20, 28; 6:13, 16, 21-23.

11. Fotokozani mavuto amene aneneri ena anakumana nawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo.

11 Chifukwa cha chikhulupiriro, aneneri monga Mikaya ndi Yeremiya ‘analandira mayesero awo mwa kutonzedwa komanso kuikidwa m’ndende.’ Ena monga Eliya “anayenda uku ndi uku m’zipululu, m’mapiri, m’mapanga, ndi m’maenje a dziko lapansi.” Onsewa anakhalabe okhulupirika chifukwa anali ndi “chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.”—Aheb. 11:1, 36-38; 1 Maf. 18:13; 22:24-27; Yer. 20:1, 2; 28:10, 11; 32:2.

12. Kodi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kupirira ndi ndani, nanga n’chiyani chinamuthandiza?

12 Paulo atafotokoza za anthu amene anali ndi chikhulupiriro, anatchula za Yesu Khristu yemwe ndi chitsanzo choposa zonse. Lemba la Aheberi 12:2 limati: “Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake, anapirira mtengo wozunzikirapo. Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando  wachifumu wa Mulungu.” Tiyenera ‘kuganizira mozama’ chitsanzo cha Yesu chifukwa anakhalabe wokhulupirika atakumana ndi mayesero aakulu kwambiri. (Werengani Aheberi 12:3.) Akhristu enanso oyambirira monga Antipa anaphedwa chifukwa chakuti anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu. (Chiv. 2:13) Mosiyana ndi anthu akale okhulupirika, Akhristu amenewa analandira kale mphoto. (Aheb. 11:35) Patangopita nthawi kuchokera pamene Yesu anakhala Mfumu mu 1914, Akhristu odzozedwa amene anali atamwalira anaukitsidwa n’kupita kumwamba ndipo adzalamulira limodzi ndi Yesu.—Chiv. 20:4.

ANTHU A MASIKU ANO AMENE ANASONYEZA CHIKHULUPIRIRO

13, 14. Kodi M’bale Rudolf anakumana ndi mavuto ati, nanga n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire?

13 Atumiki ambiri a Mulungu masiku ano akutsanzira Yesu. Iwo amaganizira kwambiri malonjezo a Yehova ndipo amakhalabe okhulupirika akakumana ndi mavuto. Chitsanzo ndi M’bale Rudolf Graichen wa ku Germany amene anabadwa mu 1925. M’baleyu ankakumbukira zithunzi za nkhani za m’Baibulo zimene zinaikidwa m’makoma a nyumba yawo. Iye anati: “Chithunzi china chinkasonyeza mmbulu uli ndi mwana wa nkhosa, mwana wa mbuzi ali ndi kambuku  komanso mwana wa ng’ombe ali ndi mkango. Zonse zinkakhala mwamtendere ndipo zinkatsogoleredwa ndi mwana wamng’ono. . . . Sindiiwala zithunzi ngati zimenezi.” (Yes. 11:6-9) Kuganizira mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso kunathandiza m’baleyu kukhalabe wokhulupirika pamene ankazunzidwa ndi chipani cha Nazi komanso cha chikomyunizimu.

14 Koma M’bale Rudolf anakumananso ndi mavuto ena. Mayi ake anamwalira kundende ndi matenda enaake. Bambo ake anafooka n’kusaina chikalata chonena kuti asiya kukhala wa Mboni za Yehova. Koma m’baleyu anakhalabe wokhulupirika ndipo atatuluka kundende, anakhala woyang’anira dera. Kenako anapita ku Sukulu ya Giliyadi. Atamaliza maphunziro anatumizidwa ku Chile kumene anakakhalanso woyang’anira dera. Komatu anakumananso ndi mavuto ena. Iye anakwatira mmishonale wina dzina lake Patsy ndipo patatha chaka anakhala ndi mwana. Koma mwana wawoyo anamwalira. Kenako mkazi wake anamwaliranso. Mkaziyo anamwalira ali ndi zaka 43 zokha. M’bale Rudolf anapirira mavuto onsewa. Mbiri ya moyo wake inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1997 tsamba 20 mpaka 25. Pa nthawiyi n’kuti iye ali mpainiya wokhazikika komanso mkulu ngakhale kuti anali wokalamba ndipo ankadwaladwala. [1]

15. Perekani zitsanzo za Akhristu amene akukhalabe osangalala ngakhale kuti akuzunzidwa?

15 A Mboni za Yehova amasangalalabe akaganizira zimene akuyembekezera ngakhale kuti amazunzidwa kwambiri. Mwachitsanzo, pali abale ndi alongo amene ali m’ndende ku Eritrea, ku Singapore ndi ku South Korea. Ambiri mwa anthuwa anamangidwa chifukwa chomvera mawu a Yesu akuti tisamamenye nkhondo. (Mat. 26:52) Ena mwa abalewa ndi a Isaac, a Negede ndi a Paulos amene akhala m’ndende ku Eritrea kwa zaka zoposa 20. Iwo akuzunzidwa kwambiri ndipo alibe mwayi wokwatira kapena wosamalira makolo awo okalamba koma ndi okhulupirikabe mpaka pano. Mmene nkhope zawo zikuonekera pawebusaiti ya jw.org, zikungosonyezeratu kuti chikhulupiriro chawo n’cholimba kwabasi. Ngakhale asilikali owalondera kundendeko amawalemekeza kwambiri.

Kodi mumalola kuti anthu okhulupirika a mumpingo wanu akuthandizeni? (Onani ndime 15 ndi 16)

16. Kodi kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kungakuthandizeni bwanji?

16 Sikuti atumiki a Yehova onse akukumana ndi mavuto ngati amene tawatchulawa. Ena amakumana ndi mayesero a mtundu wina. Mwachitsanzo, ena amavutika ndi umphawi, nkhondo kapena ngozi zadzidzidzi. Ena ali ngati atumiki a Mulungu akale monga Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi Mose. Iwo alolera kusiya moyo wawofuwofu n’cholinga choti atumikire Mulungu ndipo amapewa mtima wodzikonda komanso wokonda chuma. Kodi amatha bwanji kuchita zonsezi? Iwo amakonda kwambiri Yehova ndipo sakayikira lonjezo lake loti adzathetsa mavuto onse ndiponso loti anthu okhulupirika adzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lachilungamo.—Werengani Salimo 37:5, 7, 9, 29.

17. Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani, nanga m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

17 M’nkhaniyi taona kuti kupemphera komanso kuganizira kwambiri malonjezo a Mulungu kungatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Tikamachita zimenezi, tikhoza kupirira mayesero alionse ndipo sitingakayikire ‘zinthu zimene tikuyembekezera.’ Koma Baibulo likamanena za chikhulupiriro limatanthauza zambiri. Choncho m’nkhani yotsatira tidzakambirana zimenezi.

^ [1] (ndime 14) Onani mbiri ya moyo wa M’bale Andrej Hanák wa ku Slovakia mu Galamukani! yachingelezi ya April 22, 2002.