Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) October 2016

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira November 28 mpaka December 25, 2016.

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndimayesetsa Kutengera Anthu a Zitsanzo Zabwino

Anthu akalimbikitsidwa amakhala ndi zolinga zabwino n’kuzikwaniritsa. A Thomas McLain akusonyeza kuti anthu a zitsanzo zabwino anawathandiza ndipo nawonso akuyesetsa kuthandiza ena.

“Musaiwale Kuchereza Alendo”

Kodi Mulungu amawaona bwanji anthu ochokera m’mayiko ena? Kodi mungatani kuti anthu ochokera m’mayiko ena omwe ali mumpingo wanu azimasuka?

Mungatani Kuti Mukhalebe Olimba Mwauzimu mu Mpingo wa Chilankhulo China?

Akhristu onse ayenera kuonetsetsa kuti iwo komanso banja lawo ndi lolimba mwauzimu. Mukakhala mumpingo wa chilankhulo china mumakumana ndi mavuto ena.

Kodi ‘Mumasunga Nzeru Zopindulitsa’?

Kodi nzeru zopindulitsa zimasiyana bwanji ndi kudziwa komanso kumvetsa zinthu? Kudziwa kusiyana kwake kungakuthandizeni kwambiri.

Muzikhulupirira Kwambiri Zinthu Zimene Mukuyembekezera

Tingalimbikitsidwe kwambiri ndi zitsanzo za anthu okhulupirika, akale komanso a masiku ano. Kodi tingatani kuti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba?

Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Malonjezo a Yehova

Kodi chikhulupiriro n’chiyani? Nanga tingasonyeze bwanji kuti tili nacho?

Kodi Mukudziwa?

M’nthawi ya atumwi, kodi Aroma ankapereka ufulu wotani kwa Ayuda amene ankalamulira ku Yudeya? Kodi zinkachitikadi kuti munthu ankafesa namsongole m’munda umene mnzake wafesamo mbewu?