Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  February 2017

A George Rollston ndi a Arthur Willis aima pamalo enaake kuti athire madzi mu injini ya galimoto.—1933

 KALE LATHU

‘Kungatalike Bwanji Ndipo Msewu Ungaipe Bwanji Ankafikako’

‘Kungatalike Bwanji Ndipo Msewu Ungaipe Bwanji Ankafikako’

PA 26 MARCH, 1937, a Arthur Willis ndi a Bill Newlands anafika mumzinda wa Sydney ku Australia ali pa galimoto yawo yomwe inali fumbi lokhalokha. Iwo anali atatopa kwambiri ndipo panali patatha chaka kuchokera pamene anachoka mumzindawu. Anayenda mtunda wa makilomita 19,300 kuzungulira m’madera osiyanasiyana akumidzi m’dzikoli. Anthuwa sanali ofufuza zinthu kapena okaona malo. Koma anali apainiya akhama omwe ankafunitsitsa kulalikira uthenga wabwino m’madera akumidzi a ku Australia.

Mpaka chakumapeto kwa m’ma 1920 kagulu kochepa ka Ophunzira Baibulo * kankangolalikira m’mizinda ndi m’matauni a m’mbali mwa nyanja. Koma panalinso madera ena akumidzi ndipo anthu ake ankakhala motalikirana. Abale ankadziwa kuti otsatira a Yesu ayenera kulalikira “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Choncho kuti akwaniritse mawu a Yesuwa, ankafunika kulalikiranso m’madera akumidziwo. Koma kodi akanakwanitsa bwanji? Iwo ankakhulupirira kuti Yehova awathandiza ndipo anayesetsa kugwira ntchitoyi.

APAINIYA ANALI AKALAMBULA BWALO

Mu 1929, abale a m’mipingo ya ku Queensland ndi ku Western Australia anapanga makalavani oti azigwiritsa ntchito pokalalikira kumadera akutali. Apainiya amphamvu ndi amene anapita, omwe akanatha kupirira kumadera ovutawo komanso kukonza magalimoto akawonongeka. Apainiyawa anafika m’madera akutali oti anali asanalalikidwepo.

Apainiya omwe analibe magalimoto anapita pa njinga. Mwachitsanzo, mu 1932, m’bale wina wa zaka 23 dzina lake Bennett Brickell anachoka ku Queensland n’kupita kukalalikira kumadera a kumpoto. Iye analalikirako kwa miyezi 5. Ponyamuka, anamangirira panjinga yake mabulangete, zovala, chakudya komanso mabuku ambiri. Matayala a njinga yake atawonongeka iye anapitirizabe ntchito yake ndipo sankakayikira kuti Yehova amutsogolera. Anakoka njinga yakeyo ulendo wa makilomita 320 kudutsa m’dera limene anthu ena m’mbuyomo anafa ndi ludzu. Pa zaka 30  zotsatira, m’baleyu anayenda makilomita ambirimbiri kuzungulira mu Australia ndipo ankayenda pa njinga yopalasa, yamoto komanso pa galimoto. Iye analalikira kwa Aaborijini ndipo anathandiza kukhazikitsa mipingo moti anthu ambiri ankamudziwa komanso kumulemekeza.

MAVUTO AMENE ANAKUMANA NAWO

Chiwerengero cha anthu a ku Australia ndi chochepa, makamaka m’madera akumidzi. Koma a Mboni ayesetsa kuti afikire anthu onse a m’dzikoli, ngakhalenso akumidzi.

M’bale Stuart Keltie ndi M’bale William Torrington anasonyeza kuti anali akhama kwambiri. Mu 1933, anapita kulalalikira m’tauni ya Alice Springs. Iwo anadutsa m’chipululu chachikulu komanso cha mchenga wokhawokha chotchedwa Simpson. Galimoto yawo itawonongeka, anapitirizabe ulendo wawowu pa ngamira ngakhale kuti a Keltie ankayendera mwendo wa thabwa. Khama la apainiyawa linathandiza kwambiri. Mwachitsanzo, iwo anakumana ndi Charles Bernhardt yemwe anali mwiniwake wa hotelo ina yotchedwa William Creek yomwe inali pasiteshoni ya sitima. Patapita nthawi a Bernhardt anakhala a Mboni ndipo anagulitsa hotelo yawo n’kuyamba upainiya. Iwo ankalalikira okhaokha kwa zaka 15 kumadera akumidzi a ku Australia omwe ndi otentha kwambiri.

A Arthur Willis akukonzekera ulendo wokalalikira kumadera akumidzi a ku Australia.—1936

Apainiyawo anafunika kulimba mtima kuti apirire mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, a Arthur Willis ndi a Bill Newlands, amene tawatchula koyambirira aja, anayenda ulendo wa makilomita 32 kwa milungu iwiri chifukwa choti kunagwa chimvula ndipo paliponse panali matope okhaokha. Msewu womwe anadutsa pa ulendowu unali ndi mchenga wambiri, miyala komanso ankawoloka mitsinje. Nthawi zina ankafunika kukankha galimoto yawo chifukwa inkatitimira mumchenga. Komanso galimoto yawo ikawonongeka ankayenda wapansi kapena pa njinga masiku angapo kuti akafike patauni yapafupi. Akakafika ankadikira milungu ingapo kuti zipangizo za galimoto zifike. Ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto onsewa, iwo ankakhalabe osangalala. A Arthur Willis ananena mawu omwe ali mu Galamukani! ina akuti: “Kungatalike bwanji ndipo msewu ungaipe bwanji Mboni zake zinkafikako.”

M’bale Charles Harris anachita upainiya kwa nthawi yaitali n’kumalalikira kumadera akumidzi ndipo ankakumana ndi mavuto. Koma iye anati zimenezi zinamuthandiza kuti alimbitse ubwenzi wake ndi Yehova. M’baleyu anati: “Munthu akakhala wopanda katundu wambiri amakhala wosangalala. Ngati Yesu ankalolera kukhala opanda nyumba ndiye kuti nafenso tiyenera kuchita chimodzimodzi pakafunika kutero.” Chosangalatsa n’chakuti apainiya ambiri anachitadi zimenezi. Chifukwa cha khama lawo, uthenga wabwino unafika m’madera osiyanasiyana a ku Australia ndipo anthu ambiri anayamba kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu.

^ ndime 4 Ophunzira Baibulo anayamba kudziwika ndi dzina loti Mboni za Yehova mu 1931.—Yes. 43:10.