NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) September 2019

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa October 28–December 1, 2019.

Yehova Amaona Kuti Atumiki Ake Odzichepetsa Ndi Amtengo Wapatali

Kudzichepetsa ndi khalidwe lofunika kwambiri. N’chifukwa chiyani tingavutike kukhala odzichepetsa zinthu zikasintha pa moyo wathu?

Uthenga Wokhudza Aramagedo Ndi Wosangalatsa

Kodi ndi zinthu zazikulu ziti zomwe zidzachitike Aramagedo isanayambe? Kodi tingatani kuti tikhalebe okhulupirika pamene mapeto akuyandikira?

Tizigonjera Yehova ndi Mtima Wonse

Akulu, abambo ndi amayi angaphunzire kugonjera kuchokera kwa Nehemiya, Mfumu Davide ndi Mariya, mayi ake a Yesu.

“Bwerani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”

Kodi tingapite bwanji kwa Yesu? Tingapitirize kutsitsimulidwa ndi goli la Yesu ngati titachita zinthu zitatu.

“Ndinaona Khamu Lalikulu la Anthu”

M’masomphenya amene Yohane anaona, Yehova anathandiza anthu kudziwa khamu lalikulu, kukula kwake komanso kuti anthu ake ndi ochokera m’mitundu yosiyanasiyana. Khamuli lidzapulumuka chisautso chachikulu n’kukhala padziko lapansi mpaka kalekale.