“Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo . . . kudziletsa.”—AGAL. 5:22, 23.

NYIMBO: 83, 52

1, 2. (a) Kodi munthu wosadziletsa angakumane ndi zotani? (b) Kodi nkhani ya kudziletsa ndi yofunika bwanji masiku ano?

KUDZILETSA ndi limodzi mwa makhalidwe amene Mulungu ali nawo. (Agal. 5:22, 23) Yehova amatha kusonyeza bwino kwambiri khalidwe limeneli. Koma anthufe zimativuta kudziletsa chifukwa si ife angwiro. Zimenezi zimachititsa kuti tizikumana ndi mavuto ambiri. Munthu amene sadziletsa angamavutike kuchita zinthu pa nthawi yake, kugwira bwino ntchito komanso kukhoza bwino kusukulu. Mwina angachitenso zinthu monga kulalatira ena, kuledzera, kuchita chiwawa, kutenga ngongole yosafunika ndiponso kuthetsa banja. Angakumanenso ndi mavuto monga kuvutika maganizo, matenda opatsirana pogonana, mimba yapathengo komanso kumangidwa.​—Sal. 34:11-14.

2 Apa zikuonekeratu kuti anthu amene sadziletsa amakumana ndi mavuto komanso amabweretsera anzawo mavuto. Vuto la kusadziletsa lafala kwambiri masiku ano. M’ma 1940, anthu anachita kafukufuku yemwe anasonyeza kuti anthu amavutika kudziletsa. Koma kafukufuku wina amene wachitika posachedwapa amasonyeza kuti masiku ano zinthu zafika poipa kwambiri pa nkhaniyi. Mfundo imeneyi ndi yosadabwitsa kwa anthu amene amadziwa Baibulo chifukwa linaneneratu kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu adzakhala “osadziletsa.”​—2 Tim. 3:1-3.

3. Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kukhala odziletsa?

 3 Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala odziletsa? Tiyeni tikambirane zifukwa ziwiri. Choyamba, anthu odziletsa sakumana ndi mavuto ambiri poyerekezera ndi amene sadziletsa. Komanso amakhala ndi anzawo odalirika, sakhala okwiya, sada nkhawa kwambiri komanso sakhumudwa mofanana ndi anthu osadziletsa. Chachiwiri, Mulungu amasangalala ndi anthu amene amatha kudziletsa komanso amene sagonja akamayesedwa. Nkhani ya Adamu ndi Hava imasonyeza kuti mfundo imeneyi ndi yoona. (Gen. 3:6) Tangoganiziraninso za mavuto amene anthu ambirimbiri akhala akukumana nawo kuchokera nthawi ya Adamu ndi Hava chifukwa cholephera kudziletsa.

4. N’chiyani chingalimbikitse anthu amene amavutika kudziletsa?

4 Popeza anthufe si angwiro nthawi zina timalephera kudziletsa. Yehova amadziwa zimenezi ndipo amafunitsitsa kutithandiza kuti tisamachite zinthu zoipa zimene timalakalaka. (1 Maf. 8:46-50) Popeza Mulungu ndi wachikondi, amalimbikitsa anthu amene akufunitsitsa kumutumikira omwe amavutika kudziletsa. Tiyeni tikambirane chitsanzo chabwino kwambiri cha Yehova pa nkhani yodziletsa. Kenako tikambirana zitsanzo zina za m’Baibulo za anthu amene anadziletsa komanso amene sanadziletse. Tionanso zinthu zina zimene zingatithandize kuti tikhale odziletsa.

YEHOVA NDI CHITSANZO CHABWINO

5, 6. Kodi Yehova wapereka chitsanzo chotani pa nkhani yodziletsa?

5 Popeza kuti Yehova ndi wangwiro, amatha kudziletsa bwinobwino. (Deut. 32:4) Koma anthufe si angwiro. Choncho kuti timvetse nkhani yodziletsayi tiyenera kuona chitsanzo cha Yehova n’kumayesetsa kumutsanzira. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti ndi wodziletsa?

6 Choyamba tiyeni tione mmene iye anasonyezera khalidweli atagalukiridwa ndi Satana. N’zosachita kufunsa kuti angelo okhulupirika anakwiya kwambiri ndi zimene Satana anachita. N’kutheka kuti inunso zimakupwetekani mukaganizira mavuto ambirimbiri amene Satana anayambitsa. Yehova anafunika kuthetsa nkhani imeneyi koma sanachite zinthu mopupuluma. Iye anaiganizira bwinobwino n’kuchita zinthu moyenera. Sanakwiye msanga ndipo njira imene wasankha kuti athetsere nkhaniyi ndi yachilungamo. (Eks. 34:6; Yobu 2:2-6) Yehova walola kuti nthawi yaitali idutse chifukwa choti safuna kuti munthu aliyense awonongedwe koma kuti “anthu onse alape.”​—2 Pet. 3:9.

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anachita?

7 Zimene Yehova anachita zikusonyeza kuti nafenso sitiyenera kuchita zinthu mopupuluma koma tiyenera kuganiza bwino tisanalankhule kapena kuchita chilichonse. Pakakhala nkhani yofunika kwambiri, tiyenera kudzipatsa nthawi yoti tiiganizire bwinobwino n’kuchita zinthu mwanzeru. Tiyeneranso kupempha Yehova kuti atipatse nzeru n’cholinga choti tilankhule komanso kuchita zinthu zoyenera. (Sal. 141:3) Munthu akachita zinthu asanaganize bwinobwino akhoza kulakwitsa kwambiri n’kudzadandaula pambuyo pake.​—Miy. 14:29; 15:28; 19:2.

ZITSANZO ZA M’BAIBULO ZABWINO KOMANSO ZOIPA

8. (a) Kodi tingapeze kuti zitsanzo za anthu amene anasonyeza kudziletsa? (b) N’chiyani chinathandiza Yosefe kuti adziletse pamene mkazi wa Potifara ankamukopa? (Onani chithunzi choyambirira.)

8 M’Baibulo muli zitsanzo zosonyeza kuti kudziletsa n’kofunika. Muyenera kuti mumakumbukira anthu ambiri otchulidwa m’Baibulo amene anasonyeza khalidweli. Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi Yosefe yemwe anali mwana wa  Yakobo. Iye anasonyeza kudziletsa pamene ankagwira ntchito kunyumba ya Potifara, yemwe anali mkulu wa alonda a Farao. Mkazi wa Potifara anayamba kukopa Yosefe chifukwa iye anali “wokongola m’maonekedwe ndi wa thupi loumbika bwino.” Kodi n’chiyani chinathandiza Yosefe kuti asakopeke naye? Iye ayenera kuti anaganizira mofatsa zimene zingachitike akapanda kudziletsa. Zimenezi zinamuthandiza kuti athawe zinthu zitafika poipa. Iye ananena kuti: “Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”​—Gen. 39:6, 9; werengani Miyambo 1:10.

9. Kodi mungakonzekere bwanji kuti musagonje poyesedwa?

9 Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yosefe? Tikuphunzira kuti nthawi zina tiyenera kuthawa zinthu zina n’cholinga choti tisaphwanye lamulo la Mulungu. Anthu ena asanakhale a Mboni ankachita zinthu monga kudya mopitirira malire, kuledzera, kusuta, kumwa mankhwala osokoneza bongo komanso chiwerewere. Ngakhale atabatizidwa mwina ankavutika kuti asayambirenso kuchita zimenezi. Koma mukamayesedwa kuti muphwanye lamulo la Mulungu muyenera kuganizira mavuto amene angabwere chifukwa cholephera kudziletsa. Muyenera kuganiziranso zimene zingakubweretsereni mayesero n’kuoneratu mmene mungapewere zinthuzo. (Sal. 26:4, 5; Miy. 22:3) Ndiyeno mayeserowo akafika, muzipempha Yehova kuti akupatseni nzeru komanso akuthandizeni kukhala odziletsa.

10, 11. (a) Kodi achinyamata ambiri amakumana ndi zotani kusukulu? (b) N’chiyani chingathandize achinyamata kuti asakopeke ndi zinthu zosayenera?

10 Zimene Yosefe anakumana nazo n’zimenenso achinyamata ambiri amakumana nazo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtsikana wina dzina lake Kim. Anzake ambiri akusukulu ankachita chiwerewere ndipo ankakonda kufotokoza monyadira zimene ankachitazo. Koma Kim sankachita nawo zimenezi. Iye ananena kuti nthawi zina ankasalidwa chifukwa chakuti anali wosiyana kwambiri ndi anzake. Anzakewo ankaonanso kuti iye ndi wotsalira chifukwa choti analibe chibwenzi. Kim ankadziwa kuti munthu akakhala wachinyamata zimamuvuta kudziletsa pa nkhaniyi. (2 Tim. 2:22) Nthawi zambiri anzakewo ankamufunsa ngati n’zoona kuti sanagonepo ndi munthu. Zimenezi zinathandiza kuti Kim akhale ndi mpata wowafotokozera chifukwa chake amadzisunga. Timanyadira kwambiri achinyamata amene amayesetsa kupewa chiwerewere ndipo Yehova amawanyadiranso.

11 M’Baibulo muli zitsanzo zina za anthu amene analephera kudziletsa pa nkhani ya chiwerewere. Baibulo limasonyezanso mavuto amene munthu angakumane nawo chifukwa cholephera kudziletsa pa nkhaniyi. Tikamayesedwa kuti tichite chiwerewere tingachite bwino kuganizira za mnyamata wopanda nzeru amene watchulidwa m’chaputala 7 cha buku la Miyambo. Tingaganizirenso zimene Aminoni anachita komanso mavuto amene anakumana nawo. (2 Sam. 13:1, 2, 10-15, 28-32) Makolo angathandize ana awo kuti akhale odziletsa komanso azichita zinthu mwanzeru pa nkhani imeneyi. Angachite zimenezi akamakambirana nawo nkhani za m’Baibulo zimene tatchulazi pa kulambira kwa pabanja.

12. (a) Kodi Yosefe anasonyeza bwanji kudziletsa pochita zinthu ndi abale ake? (b) Kodi tingafunike kudziletsa pa nkhani ziti?

12 Pa nthawi ina, Yosefe anasonyezanso kudziletsa. Pamene abale ake anabwera ku Iguputo kudzagula chakudya, Yosefe anadzibisa n’cholinga choti adziwe zimene zinali mumtima mwa abale akewo. Pamene anakhudzidwa kwambiri anachoka n’kupita kwayekha kuti abale akewo asaone kuti akulira.  (Gen. 43:30, 31; 45:1) Ngati Mkhristu mnzanu kapena wachibale wanu wachita zinthu mosaganiza bwino, muyenera kutsanzira Yosefe n’kumapewa kuchita zinthu mopupuluma. (Miy. 16:32; 17:27) Ngati muli ndi achibale amene anachotsedwa mungafunike kudziletsa kuti musamalankhule nawo popanda chifukwa chomveka. N’zoona kuti kudziletsa pa nkhani zoterezi si kophweka. Koma kukumbukira kuti tikuchita zimenezi chifukwa chomvera malangizo a Mulungu komanso kutsatira chitsanzo chake kungatithandize kwambiri.

13. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Davide?

13 Chitsanzo china cha m’Baibulo ndi Mfumu Davide. Ngakhale kuti anali ndi mphamvu, sanachite zinthu mopupuluma kuti abwezere zimene Sauli ndi Simeyi anamuchitira. (1 Sam. 26:9-11; 2 Sam. 16:5-10) Koma sikuti Davide ankadziletsa nthawi zonse. Paja anachita chigololo ndi Batiseba komanso atanyozedwa ndi Nabala anatsala pang’ono kupha anthu. (1 Sam. 25:10-13; 2 Sam. 11:2-4) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Davide? Choyamba, oyang’anira m’gulu la Mulungu ayenera kusamala kwambiri kuti asamagwiritse ntchito molakwika udindo wawo. Chachiwiri, palibe munthu amene sangayesedwe.​—1 Akor. 10:12.

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUKHALA ODZILETSA

14. (a) Fotokozani zimene zinachitikira m’bale wina. (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira m’baleyu anthu akatilakwira?

14 Kodi mungatani kuti mukhale munthu wodziletsa? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Luigi. Tsiku lina, galimoto ina inagunda galimoto yake kumbuyo. Dalaiva winayo ndi amene analakwitsa koma anayamba kulalatira Luigi ndipo ankafuna kuti amenyane naye. M’baleyu anapempha Yehova kuti amuthandize kuugwira mtima ndipo anayesetsa kukambirana ndi dalaivayo koma sizinatheke. Luigi anangolemba zinthu zina zokhudza galimoto ya munthuyo n’kusiya munthuyo akulalatabe. Patapita mlungu umodzi, m’baleyu anapita kukachita ulendo wobwereza kwa mayi wina ndipo anapeza kuti mwamuna wake anali dalaivala uja. Munthuyo anachita manyazi kwambiri ndipo anapepesa. Iye analonjeza kuti ayesetsa kuti galimoto ya Luigi ikonzedwe mofulumira. Iye anamvetseranso uthenga umene Luigi ankafotokoza ndipo anayamikira kwambiri. Luigi amaona kuti anachita bwino kudziletsa chifukwa akanapanda kutero zotsatira zake zikanakhala zoipa kwambiri.​—Werengani 2 Akorinto 6:3, 4.

Zimene timachita tikalakwiridwa zingachititse kuti anthu amvetsere uthenga wathu kapena ayi (Onani ndime 14)

15, 16. Kodi kuphunzira Baibulo kungathandize bwanji inuyo ndi banja lanu kuti mukhale odziletsa?

15 Kuphunzira Baibulo mwakhama nthawi zonse kungatithandize kuti tikhale odziletsa. Kumbukirani kuti Mulungu anauza Yoswa kuti: “Buku la malamulo ili lisachoke pakamwa pako, uziliwerenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatira zonse zolembedwamo. Pakuti ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.” (Yos. 1:8) Koma kodi kuphunzira Baibulo kungatithandize bwanji kuti tikhale odziletsa?

16 Monga taonera kale, m’Baibulo muli nkhani zosonyeza ubwino wa kudziletsa komanso mavuto amene angabwere chifukwa cholephera kuchita zimenezi. Yehova anakonza zoti nkhani zimenezi zilembedwe m’Baibulo n’cholinga choti zitithandize. (Aroma 15:4) Choncho ndi bwino kuziwerenga, kuziganizira kwambiri ndiponso kuona zimene tikuphunzirapo. Tiziganizira mmene zingatithandizire ifeyo komanso banja lathu. Tizipemphanso Yehova kuti atithandize kutsatira Mawu ake. Muzivomerezanso ngati muli ndi vuto linalake pa  nkhani yodziletsayi. Ndiyeno muziipempherera nkhaniyo ndiponso kuona zimene mungachite kuti musinthe. (Yak. 1:5) Mungachite bwino kufufuza nkhani zimene gulu lathu lafalitsa zomwe zingakuthandizeni kuthana ndi vuto lililonse limene muli nalo.

17. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhale odziletsa?

17 Ngati ndinu makolo, kodi mungathandize bwanji ana anu kuti akhale odziletsa? Muyenera kudziwa kuti ana sabadwa ndi mtima wodziletsa. Pophunzitsa ana anu makhalidwe abwino, muyenera kupereka chitsanzo chabwino. (Aef. 6:4) Choncho mukaona kuti ana anu akuvutika kudziletsa, ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikupereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi?’ Dziwaninso kuti chitsanzo chanu chabwino pa nkhani yolalikira, kusonkhana komanso kuchititsa kulambira kwa pabanja chingathandize kwambiri ana anu. Mwana wanu akapempha zinthu zimene mukuona kuti sizingamuthandize musamaope kumukaniza. Paja nayenso Yehova analetsa Adamu ndi Hava kuchita zinthu zina n’cholinga choti azizindikira komanso kulemekeza ulamuliro wake. Makolo akamalangiza ana awo komanso kupereka chitsanzo chabwino akhoza kuthandiza anawo kuti akhale odziletsa. Kukonda Mulungu komanso kulemekeza malamulo ake ndi zinthu zofunika kwambiri zimene makolo ayenera kuphunzitsa ana awo.​—Werengani Miyambo 1:5, 7, 8.

18. Kodi kusankha bwino anthu ocheza nawo kungakuthandizeni bwanji?

18 Kaya ndinu makolo kapena ayi, muyenera kusankha bwino anthu ocheza nawo. Ndi bwino kugwirizana ndi anthu amene angatilimbikitse kuchita zabwino n’kumapewa mavuto. (Miy. 13:20) Mukamacheza kwambiri ndi anthu amene amakonda Mulungu mudzayamba kutengera chitsanzo chawo ndipo mudzakhala odziletsa. Nawonso adzalimbikitsidwa chifukwa cha khalidwe lanu labwino. Mukamayesetsa kukhala odziletsa tsiku lililonse mumasangalatsa Yehova, mumakhala osangalala komanso mumathandiza anzanu.