“Muzilankhulana zoona zokhazokha.”​—ZEK. 8:16.

NYIMBO: 56, 124

1, 2. Kodi n’chiyani chakhala chikusokoneza anthu, nanga ndi ndani anachiyambitsa?

ZINTHU zina zimene anthu apanga zimatithandiza kwambiri. Chitsanzo ndi zinthu monga mafoni, magetsi, magalimoto ndi mafiriji. Koma zinthu zina zimene anthu apanga monga mfuti, ndudu komanso mabomba ndi zoopsa kwambiri. Palinso chinthu china chakalekale chimene chakhala chikusokoneza kwambiri anthu. Chinthu chake ndi bodza. Munthu amatha kulankhula zinthu zimene akudziwa kuti si zoona n’cholinga choti apusitse mnzake. Koma kodi ndi ndani amene anayambitsa bodza? Mdyerekezi ndi amene anayambitsa ndipo n’chifukwa chake Yesu Khristu anamunena kuti ndi “tate wake wa bodza.” (Werengani Yohane 8:44.) Kodi ndi liti pamene ananena bodza loyambirira?

2 Zimenezi zinachitika zaka masauzande angapo zapitazo m’munda wa Edeni. Adamu ndi Hava ankakhala mosangalala m’Paradaiso amene Mulungu anawapatsa. Mdyerekezi ankadziwa kuti Mulungu anali atawauza kuti asadye “zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa” ndipo akapanda kumvera adzafa. Ndiyeno iye anagwiritsa ntchito njoka n’kuuza Hava bodza loyambirira lakuti: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye  chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”​—Gen. 2:15-17; 3:1-5.

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti bodza la Satana linali loipa kwambiri, nanga labweretsa mavuto ati?

3 Bodza la Satanali linali loipa kwambiri chifukwa ankadziwa kuti Hava akakhulupirira zimene amuuze n’kudya chipatsocho adzafa. Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu ndipo patapita nthawi anafa. (Gen. 3:6; 5:5) Koma kuwonjezera pamenepo, uchimo wawo unachititsa kuti ‘imfa ifalikire kwa anthu onse.’ Ndipo Baibulo limanena kuti: “Imfa inalamulira monga mfumu . . . , ngakhalenso kwa anthu amene sanachimwe monga mmene anachimwira Adamu.” (Aroma 5:12, 14) Choncho m’malo mokhala ndi moyo wosatha ngati mmene Mulungu ankafunira poyamba, anthufe timangokhala ‘zaka 70, ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera zimakwana zaka 80.’ Chomvetsa chisoni n’chakuti masiku onsewa “amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.” (Sal. 90:10) Mavuto onsewatu anayamba chifukwa cha bodza la Satana.

4. (a) Kodi tikambirana mafunso ati? (b) Mogwirizana ndi Salimo 15:1, 2, kodi ndani angakhale mnzake wa Yehova?

4 Yesu ananena kuti Mdyerekezi “sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi.” Satana sanasinthe chifukwa akupitirizabe ‘kusocheretsa dziko lonse lapansi’ ndi mabodza ake. (Chiv. 12:9) Koma ife sitifuna kupusitsidwa ndi Mdyerekezi. Choncho tiyeni tikambirane mafunso atatu awa: Kodi Satana akupusitsa bwanji anthu? Kodi n’chifukwa chiyani anthu amakonda kunama? Nanga tingatani kuti ‘tizilankhula zoona’ zokhazokha? Funso lomalizali lingatithandize kuti tisasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova ngati mmene anachitira Adamu ndi Hava.​—Werengani Salimo 15:1, 2.

KODI SATANA AKUPUSITSA BWANJI ANTHU?

5. Kodi Satana akupusitsa bwanji anthu masiku ano?

5 Mtumwi Paulo ankadziwa kuti tikhoza kupewa kupusitsidwa ndi Satana chifukwa “tikudziwa bwino ziwembu zake.” (2 Akor. 2:11) Timadziwa kuti dziko lonse, kuphatikizapo ndale, zamalonda komanso chipembedzo chonyenga, zili m’manja mwa Mdyerekezi. (1 Yoh. 5:19) N’chifukwa chake sitidabwa kuti Satana ndi ziwanda amachititsa anthu amene ali ndi maudindo m’dzikoli kuti ‘azilankhula mabodza.’ (1 Tim. 4:1, 2) Zimenezi zimachitika kwambiri ndi anthu azamalonda amene amachita zachinyengo komanso amakokomeza zinthu potsatsa malonda awo.

6, 7. (a) N’chifukwa chiyani atsogoleri achipembedzo ali ndi mlandu waukulu? (b) Kodi inuyo mwamvapo atsogoleri achipembedzo akunena mabodza ati?

6 Atsogoleri achipembedzo amene amalankhula mabodza ali ndi mlandu waukulu kwambiri chifukwa amawononga tsogolo la anthu amene amawakhulupirira. Zili choncho chifukwa munthu amene amakhulupirira mabodza awo n’kumachita zinthu zimene Mulungu amadana nazo, sadzalandira moyo wosatha. (Hos. 4:9) Yesu ankadziwa kuti atsogoleri a munthawi yake ankanamiza anthu. Paja anawauza kuti: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumatha mitunda kuti mukatembenuze munthu mmodzi, koma akatembenuka mumam’sandutsa woyenera kuponyedwa m’Gehena [kapena kuti kuwonongedweratu] kuposa inuyo.” (Mat. 23:15, mawu am’munsi) Apatu Yesu anadzudzula atsogoleriwo mwamphamvu kwambiri. Iwo anachokeradi ‘kwa atate wawo Mdyerekezi, yemwe ndi wopha anthu.’​—Yoh. 8:44.

7 Kaya amadziwika kuti abusa, ansembe, arabi kapena ndi mayina ena, atsogoleri achipembedzo chonyenga ali paliponse. Mofanana ndi atsogoleri akale aja, iwo “akupondereza  choonadi” chochokera m’Mawu a Mulungu ndipo “anasinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza.” (Aroma 1:18, 25) Iwo amaphunzitsa mabodza monga akuti munthu akangolandira Khristu ndiye kuti wapulumutsidwa basi, mzimu sufa, munthu akamwalira amabadwanso kwinakwake komanso kuti Mulungu amavomereza kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.

8. Kodi posachedwapa andale adzanena bodza liti, nanga tiyenera kuchita chiyani?

8 Nawonso andale amanamiza anthu. Koma iwo adzanena bodza lalikulu kwambiri pamene azidzati “bata ndi mtendere!” Baibulo limanena kuti akadzangonena bodzali “chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo.” Tisadzapusitsidwe n’kuyamba kuganiza kuti zinthu zayamba kuyenda bwino m’dzikoli. Paja timadziwa kuti “tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.”​—1 Ates. 5:1-4.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU AMAKONDA KUNAMA?

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani anthu amakonda kunama, nanga zotsatira zake n’zotani? (b) Kodi tiyenera kukumbukira mfundo iti yokhudza Yehova?

9 Anthu akatulukira chinthu chatsopano chimafala kwambiri. Ndi mmene zililinso ndi bodza. Anthu masiku ano amakonda kufalitsa mabodza ndipo si anthu otchuka okha amene amanamiza anzawo. Munkhani ina yofotokoza chifukwa chake anthu amakonda kunama, munthu wina (Y. Bhattacharjee) analemba kuti “bodza linalowerera m’mitima ya anthu.” Anthu amakonda kunama pofuna kudziteteza kapena kudzitchukitsa. Amanama pofuna kuti anthu asadziwe zimene alakwitsa kapena pofuna kuti apeze kenakake. Munkhani imene tanena ija, analembanso kuti anthu ena “amanama mosavuta pa nkhani zikuluzikulu komanso zing’onozing’ono kwa anthu achilendo, anzawo akuntchito, anzawo apamtima ngakhalenso kwa anthu a m’banja lawo.”

10 Kodi zotsatira za mabodza onsewa n’zotani? Anthu amasiya kukhulupirirana komanso kugwirizana. Mwachitsanzo, kodi mukuganiza kuti mwamuna wokhulupirika angamve bwanji atazindikira kuti mkazi wake anachita chigololo n’kumunamiza kuti asadziwe? Nanga mkazi komanso ana angamve bwanji ngati mwamuna amawachitira nkhanza kunyumba koma akakhala pagulu n’kumanamizira kuti ndi mwamuna wabwino kwambiri. Koma choyenera kudziwa n’chakuti anthu oterewa sangabisire kanthu Yehova chifukwa “kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino.”​—Aheb. 4:13.

11. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Hananiya ndi Safira? (Onani chithunzi choyambirira.)

11 Mwachitsanzo, Baibulo limasonyeza kuti munthawi ya atumwi, Satana ‘analimbitsa mtima’ banja lina kuti linamize Mulungu. Hananiya ndi mkazi wake Safira anapangana kuti anamize atumwi. Iwo anagulitsa munda wawo koma sanapereke kwa atumwi ndalama zonse zimene anapeza. Pofuna kuoneka banja labwino mumpingo, banjali linanama kuti lapereka ndalama zonse. Koma Yehova anaona zimene anachita ndipo anawapatsa chilango choyenerera.​—Mac. 5:1-10.

12. N’chiyani chidzachitikire anthu onse abodza, nanga n’chifukwa chiyani?

12 Kodi Yehova amakuona bwanji kunama? Satana komanso anthu onse amene amamutsanzira ponena mabodza koma osalapa, “adzaponyedwa m’nyanja ya moto.” (Chiv. 20:10; 21:8; Sal. 5:6) Zili choncho chifukwa choti Yehova amaona kuti munthu wabodza akufanana ndi munthu aliyense amene amachita zinthu zomunyansa.​—Chiv. 22:15.

13. Kodi timadziwa mfundo iti yokhudza Yehova, nanga mfundo imeneyi imatilimbikitsa kuchita chiyani?

13 Timadziwa kuti Yehova “si munthu, woti  anganene mabodza” moti “n’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Num. 23:19; Aheb. 6:18) Baibulo limanena kuti ‘Yehova amadana ndi lilime lonama.’ (Miy. 6:16, 17) Choncho kuti timusangalatse, tiyenera kuyendera mfundo zake pa nkhani yonena zoona zokhazokha. N’chifukwa chake timapewa ‘kunamizana.’​—Akol. 3:9.

TIMALANKHULA “ZOONA ZOKHAZOKHA”

14. (a) Kodi timasiyana bwanji ndi anthu azipembedzo zonyenga? (b) Kodi mfundo ya pa Luka 6:45 imatanthauza chiyani?

14 Kodi Akhristu enieni amasiyana ndi anthu azipembedzo zina m’njira iti? Ifeyo timalankhula zoona zokhazokha. (Werengani Zekariya 8:16, 17.) Paulo anafotokoza kuti: ‘Timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu tikamalankhula zoona.’ (2 Akor. 6:4, 7) Yesu ananena kuti ‘pakamwa pa munthu pamalankhula zosefukira mumtima.’ (Luka 6:45) Choncho munthu wabwino amene alibe chinyengo mumtima mwake amalankhula zoona zokhazokha. Iye amalankhula zoona pa nkhani zikuluzikulu komanso zing’onozing’ono kwa anthu achilendo, anzake akuntchito, anzake apamtima komanso kwa anthu a m’banja lake. Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene tingachite posonyeza kuti timayesetsa kulankhula zoona zokhazokha.

Kodi mukuona vuto limene mlongoyu ali nalo? (Onani ndime 15, 16)

15. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuchita zinthu mwachiphamaso? (b) N’chiyani chingakuthandizeni kuti musamatengere zinthu zoipa zimene anzanu amachita? (Onani mawu am’munsi.)

15 Ngati ndinu wachinyamata mwina mumafuna kuti anzanu asamakusaleni. Komabe muyenera kuyesetsa kuti musamachite zinthu mwachiphamaso ngati mmene achinyamata ena amachitira. Iwo amaoneka abwino akakhala ndi anthu a m’banja lawo kapena amumpingo koma amasintha akakhala ndi achinyamata a m’dzikoli kapena akamacheza pa intaneti. Achinyamatawa akhoza kumachita zinthu zoipa monga kutukwana, kuvala mosayenera, kumvetsera nyimbo zoipa, kuledzera, kumwa mankhwala osokoneza bongo kapena kuchita chibwenzi mobisa. Iwo amakhala achinyengo ndipo amanamiza makolo awo, Akhristu anzawo komanso Mulungu. (Sal. 26:4, 5) Yehova amadziwa ‘tikamamulemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yathu ili kutali ndi iye.’ (Maliko 7:6) Tingachite bwino kwambiri kutsatira mawu akuti: “Mtima wako usamasirire anthu ochimwa, koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.”​—Miy. 23:17. *

16. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timanena zoona pofunsira utumiki winawake?

 16 N’kutheka kuti mukufuna kuchita utumiki winawake monga upainiya wokhazikika kapena utumiki wa pa Beteli. Mukamalemba fomu, muyenera kulemba zoona zokhazokha pa funso lililonse lokhudza thanzi lanu, zosangalatsa zimene mumakonda komanso makhalidwe anu. (Aheb. 13:18) Koma kodi mungatani ngati mwachita zinthu zina zoipa zomwe akulu sakudziwa? Muyenera kuwapempha kuti akuthandizeni n’cholinga choti muzitumikira Yehova ndi chikumbumtima choyera.​—Aroma 9:1; Agal. 6:1.

17. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati anthu odana ndi ntchito yathu akutifunsa za abale athu?

17 Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati ntchito yathu yaletsedwa m’dziko limene tikukhala ndipo akuluakulu a boma akutifunsa za Akhristu anzathu? Kodi tiyenera kuwauza zonse zimene tikudziwa? Chitsanzo chabwino ndi zimene Yesu anachita pamene bwanamkubwa wa Aroma ankamufunsa mafunso. Mogwirizana ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti pali “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula,” pa nthawi ina, Yesu sankayankha chilichonse. (Mlal. 3:1, 7; Mat. 27:11-14) Choncho zimenezi zikatichitikira, tiyenera kukhala osamala kwambiri kuti tisabweretsere mavuto abale ndi alongo athu.​—Miy. 10:19; 11:12.

Kodi tingadziwe bwanji nthawi yoyenera kukhala chete ndi nthawi yoyenera kufotokoza chilichonse? (Onani ndime 17, 18)

18. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikamauza akulu nkhani inayake yokhudza abale athu?

18 Kodi muyenera kuchita chiyani ngati munthu wina mumpingo wachita tchimo lalikulu ndipo mukudziwa zimene zinachitika? Mwina akulu, omwe ali ndi udindo woonetsetsa kuti mpingo ndi woyera, angakufunseni za nkhaniyo. Kodi inuyo mungachite chiyani, makamaka ngati amene wachimwa ndi mnzanu wapamtima kapena wachibale wanu? Baibulo limanena kuti: “Wotulutsa mawu okhulupirika amanena zolungama.” (Miy. 12:17; 21:28) Choncho muli ndi udindo wouza akulu zinthu zonse zimene mukudziwa ndipo simuyenera kusintha mfundo zina. Iwo ayenera kudziwa nkhani yonse n’cholinga choti adziwe njira yabwino yothandizira munthuyo kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova.​—Yak. 5:14, 15.

19. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

19 Davide anapemphera kwa Yehova kuti: “Mumakondwera ndi choonadi chochokera pansi pa mtima.” (Sal. 51:6) Davide ankadziwa kuti kukhala wopanda chinyengo kumayambira mumtima. Nthawi zonse Akhristu oona ‘amalankhula zoona zokhazokha.’ Koma atumiki a Yehova amasiyananso ndi anthu a m’dzikoli chifukwa choti amaphunzitsa anthu mfundo za choonadi. Munkhani yotsatira tidzakambirana mmene tingachitire zimenezi.

^ ndime 15 Onani buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri pamutu 15 wakuti “Kodi Ndingapewe Bwanji Kutengera Zochita za Anzanga?” ndiponso mutu 16 wakuti “N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kuulula Zimene Ndimachita Mseri?