“Pamene munalandira mawu a Mulungu . . . simunawalandire monga mawu a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.”—1 ATES. 2:13.

NYIMBO: 114, 113

1-3. (a) Kodi mwina mavuto a Eodiya ndi Suntuke anayamba bwanji? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi mavuto oterewa tingawapewe bwanji?

ATUMIKI a Yehova amaona kuti Baibulo ndi buku lapadera kwambiri. Popeza tonsefe ndife ochimwa, nthawi zina timapatsidwa malangizo ochokera m’Malemba. Kodi inuyo mumatani mukapatsidwa malangizo? Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Eodiya ndi Suntuke. Alongo awiriwa anali mumpingo wachikhristu nthawi ya atumwi ndipo anali odzozedwa. Koma zikuoneka kuti anakhumudwitsana kwambiri. Baibulo silinena nkhani yake koma tiyeni tingoyerekezera zimene zinachitika.

2 Tiyerekeze kuti Eodiya anaitana abale ndi alongo kuti akadye komanso kucheza kunyumba kwake. Koma sanaitane Suntuke. Ndiyeno Suntukeyo anamva kuti anthuwo anasangalala kwambiri ndipo anakhumudwa. Anaganiza kuti: ‘Koma zoona Eodiya osandiitana? Ndinkamutenga ngati mnzangatu.’ Kuyambira pamenepo Suntuke anayamba kukayikira Eodiya. Ndiyeno nayenso anaitana abale ndi alongo kunyumba kwake. Koma sanaitane Eodiya. Nkhani  ya alongowa ikanatha kusokoneza mtendere mumpingo. Baibulo silinena mmene inathera koma n’kutheka kuti anatsatira malangizo amene mtumwi Paulo anawapatsa.—Afil. 4:2, 3.

3 Mavuto ngati amenewa akhoza kuchitikanso mumpingo masiku ano. Koma kutsatira malangizo a m’Baibulo kungatithandize kuti tiwathetse kapena kuwapewa. Zonsezi zingatheke ngati timaona kuti Baibulo ndi buku lapadera ndipo timatsatira malangizo ake.—Sal. 27:11.

BAIBULO LIMATITHANDIZA KUTI TISAMAFULUMIRE KUKWIYA

4, 5. Kodi m’Baibulo muli malangizo otani pa nkhani yougwira mtima?

4 Kunena zoona, si zapafupi kuugwira mtima munthu wina akatilakwira. Zimakhala zowawa ngati munthu watichitira zopanda chilungamo chifukwa choti timasiyana naye mtundu kapena chikhalidwe. Ndiyeno nkhaniyi imakhala yaikulu kwambiri ngati watilakwirayo ndi Mkhristu mnzathu. Koma m’Baibulo muli malangizo otithandiza zoterezi zikachitika.

5 Yehova amadziwa zimene munthu angachite chifukwa cholephera kuugwira mtima. Anthufe tikakhumudwa kapena kukwiya tikhoza kuchita zinthu zimene pambuyo pake tinganong’oneze nazo bondo. N’chifukwa chake Baibulo limatilangiza kuti tiziugwira mtima komanso tisamafulumire kukwiya. (Werengani Miyambo 16:32; Mlaliki 7:9.) Tikamatsatira malangizo amenewa tikhoza kupewa mavuto ambiri. Koma Baibulo limatilimbikitsanso kuti tikhale ndi mtima wokhululuka. Paja Yesu ananena kuti ngati sitikhululukira anzathu, ifenso Yehova sadzatikhululukira. (Mat. 6:14, 15) Kodi inuyo mumaona kuti zimakuvutani kuugwira mtima kapena kukhulululukira anzanu?

6. Kodi chingachitike n’chiyani tikalephera kuugwira mtima?

6 Anthu amene amalephera kuugwira mtima amakwiyakwiya ndipo akhoza kuyamba kudana ndi anzawo. Anthu oterewa akhoza kuyambitsa mavuto mumpingo. Mwina angayesetse kubisa mkwiyo wawo koma tsiku lina zinthu zoipa zimene zili mumtima mwawo “zidzaululika mumpingo.” (Miy. 26:24-26) Akulu amagwiritsa ntchito malemba pofuna kutithandiza kuti tisamakwiyire abale ndi alongo athu kapena kuwasungira chakukhosi. (Lev. 19:17, 18; Aroma 3:11-18) Ndiyeno kodi akatipatsa malangizowo, timawatsatira pokumbukira kuti ndi ochokera m’Mawu a Mulungu?

YEHOVA NDI AMENE AMATITSOGOLERA

7, 8. (a) Kodi Yehova amatsogolera bwanji anthu ake padzikoli? (b) Kodi malangizo ena amene timapeza m’Baibulo ndi ati, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuwamvera?

7 Yehova amatsogolera ndiponso kuphunzitsa anthu ake. Iye wasankha Yesu kuti akhale “mutu wa mpingo” ndipo Yesuyo amagwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47; Aef. 5:23) Mofanana ndi bungwe lolamulira la nthawi ya atumwi, kapolo wokhulupirika amaona kuti Baibulo ndi buku lapadera. (Werengani 1 Atesalonika 2:13.) Kodi m’Baibulo muli malangizo ati amene angatithandize?

8 Baibulo limatiuza kuti tiyenera kupezeka pamisonkhano nthawi zonse. (Aheb. 10:24, 25) Limatithandizanso kuti tizikhulupirira mfundo zofanana. (1 Akor. 1:10) Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba. (Mat. 6:33) Limatilimbikitsanso kuti tizilalikira kunyumba ndi nyumba, m’malo opezeka anthu ambiri komanso paliponse pamene mpata wapezeka. (Mat. 28:19, 20; Mac. 5:42; 17:17; 20:20) Mawu a Mulungu amalimbikitsanso akulu kuti azionetsetsa kuti mpingo ndi woyera. (1 Akor. 5:1-5, 13; 1 Tim. 5:19-21) Baibulo limanenanso  kuti tizikhala aukhondo komanso tizipewa chilichonse chimene chingakhumudwitse Yehova.—2 Akor. 7:1.

9. Kodi Yesu wasankha ndani kuti azithandiza anthu kumvetsa Mawu a Mulungu?

9 Anthu ena amaganiza kuti akhoza kumvetsa Baibulo paokha. Koma Yesu wasankha “kapolo wokhulupirika” kuti azipereka chakudya chauzimu. Kuyambira mu 1919, Yesu wakhala akugwiritsa ntchito kapoloyu kuti athandize anthu ake kumvetsa Mawu a Mulungu komanso kuwatsatira. Tikamachita zimenezi timakhala oyera, amtendere komanso ogwirizana. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine wokhulupirika kwa Yesu ndipo ndimatsatira malangizo a kapolo amene akumugwiritsa ntchito?’

GALETA LA YEHOVA LIKUYENDA MOTHAMANGA

10. Kodi buku la Ezekieli limafotokoza bwanji mbali yakumwamba ya gulu la Yehova?

10 Baibulo limatithandiza kudziwa bwino za mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. Mwachitsanzo, Ezekieli anaona m’masomphenya Yehova atakwera galeta limene linkayenda mothamanga kwambiri kulowera kulikonse kumene Yehovayo wafuna. (Ezek. 1:4-28) Galeta limeneli likuimira mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu ndipo limatsatira mwamsanga malangizo a Yehova. Ndiyeno mbali yakumwambayo imathandiza mbali yapadziko lapansi kuti izichitanso chimodzimodzi. Tangoganizirani mmene zinthu zasinthira m’gulu la Yehova zaka 10 zapitazi. Tisamaiwale mfundo yakuti Yehova ndi amene akuchititsa kusintha konseko. Posachedwapa, Yesu limodzi ndi angelo adzawononga dziko loipali. Izi zidzathandiza kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe ndipo aliyense atsimikizire kuti Yehova ndi woyenera kulamulira.

Timayamikira kwambiri abale ndi alongo amene amagwira mwakhama ntchito zomangamanga (Onani ndime 11)

11, 12. Tchulani zinthu zina zimene zachitika m’gulu la Yehova?

11 Kodi mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova yachita zinthu ziti m’masiku otsiriza ano? Zomangamanga. Abale ndi alongo ambirimbiri akhala akugwira nawo ntchito yomanga likulu latsopano ku Warwick m’dziko la United States. Ndiyeno pali abale ndi alongo ena amene amathandiza kumanga Nyumba za Ufumu ndi maofesi a nthambi. Abale amenewa amagwira ntchito moyang’aniridwa ndi Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga Padziko Lonse. Timayamikira kwambiri abale ndi alongo amene amagwira ntchito zonsezi mwakhama. Yehova akudalitsa atumiki ake odzichepetsa komanso okhulupirika amene amapereka ndalama zothandizira pa ntchito zimenezi.—Luka 21:1-4.

12 Maphunziro: Pali masukulu osiyanasiyana amene amathandiza anthu kudziwa bwino Mulungu ndi gulu lake. (Yes. 2:2, 3) Mwachitsanzo, pali Sukulu ya Utumiki wa Upainiya,  Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, Sukulu ya Giliyadi, Sukulu ya Otumikira pa Beteli Atsopano, Sukulu ya Oyang’anira Madera ndi Akazi Awo, Sukulu ya Akulu, Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ndiponso Sukulu ya Abale a m’Komiti ya Nthambi ndi Akazi Awo. Wonsewu ndi umboni wakuti Yehova amakonda kuphunzitsa anthu ake. Anthu ambiri amaphunziranso mfundo za m’Baibulo pa webusaiti yathu ya jw. org, yomwe imakhala ndi mabuku a zinenero zambirimbiri. Pa webusaitiyi pamapezeka nkhani za ana, mabanja komanso zinthu zatsopano zimene zatuluka. Kodi inuyo munagwiritsapo ntchito webusaitiyi mu utumiki komanso pa kulambira kwa pabanja?

TIKHALE OKHULUPIRIKA KWA YEHOVA NDIPO TIZITHANDIZA GULU LAKE

13. Kodi atumiki a Yehovafe tili ndi udindo wotani?

13 Ndi mwayi waukulu kukhala m’gulu la Yehova ndiponso kudziwa zimene amafuna kuti tizichita. Koma tilinso ndi udindo wochita zoyenera komanso kusonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake. Panopa makhalidwe a anthu akuipiraipirabe choncho tiyenera kuyesetsa ‘kudana ndi zoipa’ ngati mmene Yehova amachitira. (Sal. 97:10) Timapewa maganizo a anthu oipa amene amaona kuti “chabwino n’choipa ndipo choipa n’chabwino.” (Yes. 5:20) Popeza timafuna kusangalatsa Yehova, timayesetsa kukhala aukhondo, kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kupewa chilichonse chimene chingakhumudwitse Mulungu. (1 Akor. 6:9-11) Timakonda kwambiri Yehova komanso timamudalira ndi mtima wonse. Choncho timatsatira mfundo za m’Mawu ake n’cholinga choti tikhalebe okhulupirika kwa iye. Timayesetsa kutsatira mfundozi kulikonse kaya ndi kunyumba, mumpingo, kuntchito kapena kusukulu. (Miy. 15:3) Tiyeni tsopano tikambirane njira zina zimene tingasonyezere kuti ndife okhulupirika kwa Mulungu.

14. Kodi makolo achikhristu angasonyeze bwanji kuti ndi okhulupirika kwa Yehova?

14 Kulera ana. Makolo achikhristu amasonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Yehova akamaphunzitsa ana awo pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Iwo salera ana mongotengera chikhalidwe cha kumene amakhala. Amayesetsanso kuti mzimu wa dziko usasokoneze banja lawo. (Aef. 2:2) Mwamuna wachikhristu sangaganize kuti, ‘Kwathu kuno udindo wophunzitsa ana ndi wa azimayi.’ Amakumbukira malangizo a m’Baibulo akuti: ‘Inunso abambo, . . . muwalere [ana anu] m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Makolo achikhristu amafuna kuti ana awo akhale pa ubwenzi ndi Yehova ngati mmene Samueli anachitira ali wamng’ono.—1 Sam. 3:19.

15. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika kwa Yehova posankha zochita pa nkhani zikuluzikulu?

15 Posankha zochita. Tiyenera kufufuza malangizo a m’Mawu a Mulungu komanso gulu lake tisanasankhe zochita pa nkhani zikuluzikulu. Tikatero timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova. Mwachitsanzo, makolo ena amapita kudziko lina, ndipo akabereka ana amawatumiza kumudzi kuti achibale awo azikawalerera. Amachita izi kuti iwo azigwira bwino ntchito n’kumapeza ndalama kudziko linalo. N’zoona kuti aliyense angasankhe yekha zochita pa nkhaniyi. Koma tizikumbukira kuti aliyense adzayankhanso yekha kwa Mulungu pa zimene amasankha kuchita. (Werengani Aroma 14:12.) Si nzeru kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu zokhudza banja lathu popanda kufufuza malangizo a m’Baibulo. Paja anthufe sitingathe kuwongolera mapazi athu  choncho timafunika kutsogoleredwa ndi Atate wathu wakumwamba.—Yer. 10:23.

16. (a) Kodi mayi wina anafunika kusankha zochita pa nkhani iti? (b) Kodi n’chiyani chinamuthandiza kusankha mwanzeru?

16 Mayi wina ali kudziko lina anabereka mwana wamwamuna. Ndiyeno anaganiza zotumiza mwanayo kwawo kuti azikaleredwa ndi agogo ake. Koma pa nthawiyo, panali wa Mboni za Yehova wina amene anayamba kuphunzira naye Baibulo. Phunzirolo linkayenda bwino kwambiri ndipo anazindikira kuti Mulungu anapatsa makolo udindo wothandiza ana awo kuti azimutumikira. (Sal. 127:3; Miy. 22:6) Mayiyo anatsatira malangizo a m’Malemba oti tizipemphera kuchokera mumtima tisanasankhe zochita. (Sal. 62:7, 8) Iye anakambirananso nkhaniyi ndi amene ankamuphunzitsa Baibulo komanso anthu ena mumpingo. Ngakhale kuti anzake ndi achibale ake ankamuuza kuti atumize mwanayo kwawo, iye anaona kuti si bwino kuchita zimenezo. Mwamuna wake anachita chidwi kuona kuti abale ndi alongo ankathandiza kwambiri mkazi wakeyo komanso mwana wake. Izi zinachititsa kuti nayenso ayambe kuphunzira Baibulo komanso kupezeka pamisonkhano limodzi ndi banja lake. Mayiyu ayenera kuti anasangalala kwambiri kuona kuti Yehova wayankha pemphero lake lochokera pansi pa mtima.

17. Kodi gulu la Yehova latipatsa malangizo ati okhudza anthu amene timaphunzira nawo?

17 Kutsatira malangizo. Munthu wokhulupirika kwa Mulungu amatsatira malangizo amene gulu limatipatsa. Mwachitsanzo, gulu latipatsa malangizo abwino okhudza anthu amene timaphunzira nawo. Lanena kuti tikangoyamba kuphunzira ndi munthu buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? tizipeza nthawi yochepa yokambirana naye mfundo zokhudza gulu lathu. Tingachite zimenezi pogwiritsa ntchito vidiyo yakuti, Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? kapena kabuku kakuti, Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano? Ndiyeno tikamaliza buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? timalimbikitsidwa kuti tiziphunzira naye buku lakuti, Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani?’ Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale munthuyo atabatizidwa. Gulu lapereka malangizo amenewa n’cholinga choti anthu atsopano ‘akhazikike m’chikhulupiriro.’ (Akol. 2:7) Ndiye kodi inuyo mumatsatira malangizo ngati amenewa, omwe gulu la Yehova limatipatsa?

18, 19. Kodi ndi zifukwa zina ziti zotipangitsa kuyamikira kwambiri Yehova?

18 Pali zinthu zambiri zotichititsa kuyamikira Yehova. Iye ndi amene anatipatsa moyo ndipo pakanapanda iye si bwenzi tiliko. (Mac. 17:27, 28) Watipatsanso Baibulo, lomwe ndi mphatso yapadera kwambiri. Mofanana ndi Akhristu a ku Tesalonika, timaona kuti Baibulo ndi lofunika kwambiri chifukwa muli uthenga wochokera kwa Mulungu.—1 Ates. 2:13.

19 Baibulo latithandiza kuti tiyandikire Mulungu komanso kuti iye atiyandikire. (Yak. 4:8) Atate wathu wakumwamba watipatsa mwayi wapadera wokhala m’gulu lake. Tiyenera kuyamikira kwambiri mwayi umenewu. Wamasalimo anasonyeza kuyamikira pamene anaimba kuti: “Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino: Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” (Sal. 136:1) Mu Salimo 136, timapeza mawu akuti “kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale” maulendo 26. Tikakhala okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake, tidzaona kukwaniritsidwa kwa mawu amenewa chifukwa tidzakhala ndi moyo mpaka kalekale.