“Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri ndi kusonyeza kuti mulidi ophunzira anga.”​YOH. 15:8.

NYIMBO: 53, 60

1, 2. (a) Kodi Yesu anakambirana ndi atumwi ake mfundo ziti atatsala pang’ono kuphedwa? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira zifukwa zogwirira ntchito yolalikira? (c) Kodi tikambirana chiyani?

USIKU woti aphedwa mawa lake, Yesu anakambirana ndi atumwi ake kwa nthawi yaitali ndipo anawatsimikizira kuti amawakonda. Anawafotokozeranso fanizo la mtengo wa mpesa lomwe tinakambirana munkhani yapita ija. Mufanizoli, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti apitirize kubala zipatso kapena kuti azipirira polalikira uthenga wa Ufumu.​—Yoh. 15:8.

2 Sikuti Yesu anangowauza zimene ayenera kuchita koma anawauzanso chifukwa chake ayenera kuchita zimenezo. Iye anawauza zifukwa zogwirira ntchito yolalikira. Kodi kukambirana zifukwa zimenezi kungatithandize bwanji? Tikamakumbukira zifukwa zolalikirira, m’pamene timatha kupirira pochitira umboni kwa anthu a “mitundu yonse.” (Mat. 24:13, 14) Choncho tiyeni tsopano tikambirane zifukwa 4 za m’Malemba zotichititsa kulalikira. Tikambirananso mphatso 4 zimene Yehova watipatsa zomwe zimatithandiza kupirira pamene tikubala zipatso.

 TIMALEMEKEZA YEHOVA

3. (a) Kodi lemba la Yohane 15:8 limatchula zifukwa ziti zolalikirira? (b) Kodi mphesa za m’fanizo la Yesu zimaimira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi n’zomveka?

3 Chifukwa chachikulu chotichititsa kulalikira n’chakuti timalemekeza Yehova komanso kuyeretsa dzina lake. (Werengani Yohane 15:1, 8.) Yesu ananena kuti Atate wake Yehova ali ngati mlimi wa mphesa. Kenako ananena kuti iyeyo ali ngati mtengo wa mpesa pomwe otsatira ake ali ngati nthambi. (Yoh. 15:5) Choncho tinganene kuti mphesa zimaimira zipatso za Ufumu zimene otsatira a Khristu amabereka. Yesu anauza atumwi ake kuti: “Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri.” Mitengo ya mpesa imene imabala mphesa zabwino imachititsa kuti mlimi wake alemekezeke. N’chimodzimodzinso ndi ife. Timalemekeza Yehova tikamachita zonse zimene tingathe polalikira uthenga wa Ufumu.​—Mat. 25:20-23.

4. (a) Kodi timayeretsa bwanji dzina la Mulungu? (b) Kodi mumamva bwanji mukaganizira mwayi wanu woyeretsa dzina la Mulungu?

4 Kodi ntchito yathu yolalikira imayeretsa bwanji dzina la Mulungu? N’zosatheka kuti tichititse dzina la Mulungu kukhala loyera kuposa mmene lilili. Dzinalo ndi loyera kale kapena kuti lopatulika kwambiri. Koma taonani zimene mneneri Yesaya ananena. Iye anati: “Yehova wa makamu ndi amene muyenera kumuona kuti ndi woyera.” (Yes. 8:13) Choncho timayeretsa dzina la Mulungu tikamaliona kuti ndi lapamwamba kwambiri kuposa mayina ena onse komanso tikamathandiza anthu ena kuona kuti ndi loyera. (Mat. 6:9) Mwachitsanzo, tikamauza anthu za makhalidwe abwino a Yehova komanso cholinga chake chokhudza anthu chimene sangachisinthe, timasonyeza kuti zimene Satana ananena zokhudza Yehova ndi zabodza. (Gen. 3:1-5) Timayeretsanso dzina la Mulungu tikamathandiza anthu kuzindikira kuti Yehova ndi woyenera “kulandira ulemerero ndi ulemu.” (Chiv. 4:11) M’bale wina dzina lake Rune, yemwe wachita upainiya kwa zaka 16, anati: “Ndimathokoza kwambiri ndikaganizira kuti ndapatsidwa mwayi wochitira umboni Mlengi wa chilengedwe chonse. Zimenezi zimandichititsa kukhala ndi mtima wofuna kupitiriza kulalikira.”

TIMAKONDA YEHOVA NDI MWANA WAKE

5. (a) Kodi lemba la Yohane 15:9, 10 limatchula chifukwa chiti chotichititsa kulalikira? (b) Kodi Yesu anatsindika bwanji mfundo yoti kupirira n’kofunika?

5 Werengani Yohane 15:9, 10. Chifukwa china chofunika kwambiri chimene chimatichititsa kulalikira n’chakuti timakonda Yehova ndiponso Yesu ndi mtima wonse. (Maliko 12:30; Yoh. 14:15) N’zochititsa chidwi kuti Yesu sanangouza ophunzira ake kuti amukonde koma anati ‘akhalebe m’chikondi chake.’ Ananena zimenezi chifukwa chakuti munthu amafunika kupirira kuti chaka chilichonse moyo wake uzisonyeza kuti ndi wophunzira weniweni wa Khristu. Pa Yohane 15:4-10, Yesu anagwiritsa ntchito mobwerezabwereza mawu osonyeza kuchita zinthu mopitiriza pofuna kutsindika mfundo yoti kupirira n’kofunika.

6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikufuna kukhalabe m’chikondi cha Khristu?

6 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timafunitsitsa kusangalatsa Khristu komanso kukhalabe m’chikondi chake? Chofunika n’kutsatira malamulo ake. Mwachidule tingati Yesu akungotiuza kuti, ‘Muzindimvera.’ Chosangalatsa n’chakuti zimene Yesu anatiuza kuchita n’zimene iyenso amachita. Paja atauza ophunzira ake kuti azisunga malamulo ake anapitiriza kuti: “Monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.” Choncho tinganene kuti Yesu anatipatsa chitsanzo.​—Yoh. 13:15.

7. Kodi kukonda Mulungu ndi Yesu kumagwirizana bwanji ndi kuwamvera?

7 Zimene Yesu anauza atumwi ake pa nthawi ina zimasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa  kumukonda ndi kumumvera. Iye anati: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda.” (Yoh. 14:21) Koma tikamamvera lamulo la Yesu loti tizilalikira, timasonyezanso kuti timakonda Mulungu chifukwa malamulo a Yesu amakhala ogwirizana ndi maganizo a Atate wake. (Mat. 17:5; Yoh. 8:28) Tikamasonyeza kuti timakonda Yehova ndi Yesu, iwonso amapitiriza kutikonda.

TIMACHENJEZA ANTHU

8, 9. (a) Kodi chifukwa china chimene chimatichititsa kulalikira ndi chiti? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu a Yehova a pa Ezekieli 3:18, 19 ndi 18:23 amatilimbikitsa kupitiriza kulalikira?

8 Palinso chifukwa china chotichititsa kupitiriza kulalikira. Timalalikira n’cholinga choti tichenjeze anthu. Baibulo limanena kuti Nowa anali “mlaliki.” (Werengani 2 Petulo 2:5.) Zikuoneka kuti Chigumula chisanachitike, Nowa ankalalikira ndipo uthenga wake wina unali wochenjeza anthu. Tikutero chifukwa cha zimene Yesu ananena. Iye anati: “M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo. Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.” (Mat. 24:38, 39) Ngakhale kuti anthu sankamumvera, Nowa anapitiriza kuwauza uthengawo mokhulupirika.

9 Masiku anonso, timalalikira uthenga wa Ufumu kuti tithandize anthu kudziwa cholinga cha Mulungu chokhudza anthufe. Mofanana ndi Yehova, timafunitsitsa kuti anthu amvere uthengawo n’cholinga choti ‘akhalebe ndi moyo.’ (Ezek. 18:23) Tikamalalikira kunyumba ndi nyumba kapena m’malo opezeka anthu ambiri, timachenjezanso anthu kuti Ufumu wa Mulungu udzabwera ndipo udzawononga dziko loipali.​—Ezek. 3:18, 19; Dan. 2:44; Chiv. 14:6, 7.

TIMAKONDA ANTHU

10. (a) Kodi lemba la Mateyu 22:39 limatchula chifukwa chiti chotichititsa kulalikira? (b) Fotokozani zimene Paulo ndi Sila anachita pothandiza woyang’anira ndende ku Filipi.

10 Chifukwa china chofunika chotichititsa kupitiriza kugwira ntchito yathu yolalikira n’chakuti timakonda anthu. (Mat. 22:39) Zimenezi zimatilimbikitsa kupirira tikamalalikira pozindikira kuti anthu angayambe kumvetsera uthenga wathu zinthu zikasintha pa moyo wawo. Taganizirani zimene zinachitikira mtumwi Paulo ndi Sila. Mumzinda wa Filipi, anthu otsutsa anawatsekera mundende. Koma kenako usiku kunachitika chivomezi ndipo zitseko za ndende zinatseguka. Woyang’anira ndende anachita mantha poganiza kuti akaidi athawa ndipo ankafuna kudzipha. Koma Paulo anamuuza kuti: “Usadzivulaze.” Ndiyeno woyang’anira ndendeyo anafunsa kuti: “Ndichite chiyani kuti ndipulumuke?” Iwo anamuuza kuti: “Khulupirira mwa Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka.”​—Mac. 16:25-34.

Timalalikira chifukwa chokonda Yehova, Yesu ndiponso anthu (Onani ndime 5, 10)

11, 12. (a) Kodi nkhani ya woyang’anira ndende ikugwirizana bwanji ndi ntchito yathu yolalikira? (b) Kodi tiyenera kupitiriza kulalikira kuti tizitha kuchita chiyani?

11 Kodi nkhani ya woyang’anira ndendeyu ikugwirizana bwanji ndi ntchito yathu yolalikira? Taganizirani izi: Pambuyo poti chivomezi chachitika, woyang’anira ndendeyo  anasintha maganizo n’kupempha kuti amuthandize. Masiku anonso, anthu ena amene samvetsera uthenga wa m’Baibulo amasintha pambuyo pokumana ndi mavuto aakulu ndipo amafuna kuthandizidwa. Mwachitsanzo, anthu ena akhoza kuchotsedwa ntchito mwadzidzidzi ndipo amasowa mtengo wogwira. Pomwe ena akuvutika kwambiri chifukwa choti banja lawo lasokonekera. Ndipo ena ataya mtima chifukwa chopezeka ndi matenda aakulu kapena chifukwa mnzawo wamwalira. Anthu akakumana ndi mavuto oterewa akhoza kufunsa mafunso okhudza cholinga cha moyo omwe m’mbuyomo sankawaganizira. Mwina akhoza kumafunsa kuti, ‘Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumuke?’ Tikakumana nawo, mwina angayambe kumvetsera uthenga wathu wolimbikitsa.

12 Choncho chifukwa chopitiriza kulalikira timatha kulimbikitsa anthu pa nthawi imene akufuna thandizo. (Yes. 61:1) Mlongo wina dzina lake Charlotte, yemwe wachita upainiya kwa zaka 38, ananena kuti: “Masiku ano anthu ambiri akusowa mtengo wogwira. Iwo amafunika kukhala ndi mwayi womva uthenga wabwino.” Mlongo winanso dzina lake Ejvor, yemwe wachita upainiya kwa zaka 34, anati: “Masiku ano, anthu ambiri akuvutika maganizo. Ndimafunitsitsa kuwathandiza ndipo zimenezi zimandilimbikitsa kulalikira.” Kukonda anthu ndi chifukwa china chofunika kwambiri chotichititsa kulalikirabe.

MPHATSO ZIMENE ZIMATITHANDIZA KUPIRIRA

13, 14. (a) Kodi ndi mphatso iti imene yatchulidwa pa Yohane 15:11? (b) Kodi chimwemwe cha Yesu chingakhale bwanji chathu? (c) Kodi chimwemwe chimatithandiza bwanji?

13 Usiku woti aphedwa mawa lake uja, Yesu anauza atumwi ake za mphatso zingapo zomwe zingawathandize kupirira pobereka zipatso. Kodi anatchula mphatso ziti ndipo mphatsozi zingatithandize bwanji?

14 Mphatso ya chimwemwe. Kodi kumvera lamulo la Yesu loti tizilalikira n’kovuta kwambiri? Ayi. Tikutero chifuwa chakuti Yesu atafotokoza fanizo la mtengo wa mpesa ananena kuti olalikira za Ufumu adzapeza chimwemwe. (Werengani Yohane 15:11.) Iye anatitsimikizira kuti chimwemwe chake chidzakhalanso chathu. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Monga tanena kale, Yesu ananena kuti ali ngati mtengo wa mpesa ndipo ophunzira ake ali ngati nthambi. Mtengo ndi umene umathandiza nthambi kuti zizikhala ndi moyo. Nthambi zikakhala zolumikizidwabe ndi mtengo zimalandira madzi ndi chakudya. Ifenso tikakhalabe ogwirizana ndi Khristu potsatira mapazi ake, timakhala osangalala ngati mmene iye amasangalalira chifukwa chochita zofuna za Atate wake. (Yoh. 4:34; 17:13; 1 Pet. 2:21) Mlongo wina dzina lake Hanne, yemwe wachita upainiya kwa zaka zoposa 40, ananena kuti: “Ndimakhala wosangalala kwambiri ndikaweruka mu utumiki moti ndimafunitsitsa kugwirabe ntchito ya Yehova.” Kunena zoona, chimwemwe chimene timakhala nacho chimatithandiza kupitiriza kulalikira ngakhale m’magawo ovuta.​—Mat. 5:10-12.

15. (a) Kodi ndi mphatso iti imene yatchulidwa pa Yohane 14:27? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mtendere umatithandiza kupitiriza kubereka zipatso?

15 Mphatso ya mtendere. (Werengani Yohane 14:27.) Usiku umene Yesu ankakambirana ndi atumwi ake uja, anawauzanso kuti: “Ndikupatsani mtendere wanga.” Kodi mtendere umenewo umatithandiza bwanji kubereka zipatso? Tikamapirira, timamva mtendere wamumtima chifukwa chodziwa kuti tikusangalatsa Yehova ndiponso Yesu. (Sal. 149:4; Aroma 5:3, 4; Akol. 3:15) M’bale wina dzina lake Ulf, yemwe wachita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 45, anati: “Ndimatopa ndikagwira ntchito yolalikira koma ntchitoyi imandithandiza kukhala wosangalala.” Kunena zoona, timayamikira kwambiri kuti timatha  kukhala ndi mtendere weniweni wamumtima.

16. (a) Kodi ndi mphatso iti imene yatchulidwa pa Yohane 15:15? (b) Kodi atumwi ankayenera kuchita chiyani kuti akhalebe anzake a Yesu?

16 Mphatso ya kukhala anzake a Yesu. Yesu atauza atumwi ake kuti akufuna kuti ‘chimwemwe chawo chisefukire,’ anawafotokozera kufunika kosonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. (Yoh. 15:11-13) Kenako ananena kuti: “Ndakutchani mabwenzi.” Kukhala anzake a Yesu ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri. Koma kodi atumwi ankayenera kuchita chiyani kuti akhalebe anzake? Iwo ankayenera ‘kupitiriza kubala zipatso.’ (Werengani Yohane 15:14-16.) Zaka pafupifupi ziwiri asananene zimenezi, Yesu anauza atumwi ake kuti: “Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’” (Mat. 10:7) Choncho usiku woti aphedwa mawa lake anawalimbikitsa kuti apirire pochita ntchito imene anali atayamba kale. (Mat. 24:13; Maliko 3:14) Kumvera lamulo la Yesuli sikunali kophweka koma akanatha kukwanitsa n’kumakhalabe anzake. Tikutero chifukwa chakuti pali mphatso inanso imene ikanawathandiza kuti akwanitse kuchita zimenezi.

17, 18. (a) Kodi ndi mphatso iti imene yatchulidwa pa Yohane 15:16? (b) Kodi mphatsoyi inathandiza bwanji ophunzira a Yesu? (c) Kodi ndi mphatso ziti zimene zimatithandiza masiku ano?

17 Mphatso ya kuyankhidwa mapemphero. Yesu anati: “Chilichonse chimene mungapemphe Atate m’dzina langa [akupatsani].” (Yoh. 15:16) Lonjezo limeneli liyenera kuti linalimbikitsa kwambiri atumwi. * N’zoona kuti atumwiwo sanamvetse bwinobwino zimene zichitike. Pa nthawiyo, Mtsogoleri wawo anali atatsala pang’ono kuphedwa koma iwo sakanasiyidwa popanda thandizo. Yehova ankafunitsitsa kuyankha mapemphero awo opempha kuti aziwathandiza kumvera lamulo loti azilalikira uthenga wa Ufumu. Ndiyeno patangopita nthawi yochepa, anaonadi Yehova akuyankha mapemphero awo oti awathandize.​—Mac. 4:29, 31.

Sitiyenera kukayikira kuti Yehova azitiyankha tikamupempha kuti atithandize (Onani ndime 18)

18 Ndi mmene zililinso masiku ano. Tikamapirira pobereka zipatso timakhala anzake a Yesu. Ndipo sitiyenera kukayikira kuti Yehova amafunitsitsa kuti aziyankha mapemphero athu n’kumatithandiza kuthetsa vuto lililonse lomwe tingakumane nalo polalikira. (Afil. 4:13) Timayamikira kwambiri kuti mapemphero athu amayankhidwa komanso kuti ndife anzake a Yesu. Mphatso zochokera kwa Mulungu zimenezi zimatithandiza kupitiriza kubereka zipatso.​—Yak. 1:17.

19. (a) N’chifukwa chiyani timapitiriza kugwira ntchito yolalikira? (b) N’chiyani chingatithandize kumaliza ntchito imene Mulungu watipatsa?

19 Munkhaniyi taona kuti timapitiriza kulalikira n’cholinga choti tizilemekeza Yehova ndi kuyeretsa dzina lake, tizisonyeza kuti timakonda Yehova ndi Yesu, tizichenjeza anthu komanso kuti tizisonyeza kuti timakonda anthu. Taonanso kuti mphatso monga chimwemwe, mtendere, kukhala anzake a Yesu komanso kuyankhidwa mapemphero athu zimatithandiza kumaliza ntchito imene Mulungu watipatsa. Yehova amasangalala kwambiri akaona kuti tikuyesetsa ndi mtima wonse ‘kupitiriza kubala zipatso zambiri.’

^ ndime 17 Polankhula ndi atumwi ake, Yesu anawatsimikizira mobwerezabwereza kuti mapemphero awo aziyankhidwa.​—Yoh. 14:13; 15:7, 16; 16:23.