“Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo, chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.”​—MAT. 24:12.

NYIMBO: 60, 135

1, 2. (a) Kodi ndi ndani amene analola kuti chikondi chawo chizirale m’nthawi ya atumwi? (b) Kodi buku la Machitidwe limasonyeza bwanji kuti Akhristu ambiri oyambirira ankasonyezabe chikondi? (Onani chithunzi choyambirira.)

POFOTOKOZA chizindikiro cha “mapeto a nthawi ino,” Yesu ananena kuti “chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.” (Mat. 24:3, 12) M’nthawi ya atumwi, Ayuda omwe ankati ndi anthu a Mulungu analola kuti chikondi chawo chizirale ndipo anasiya kukonda kwambiri Mulungu.

2 Koma Akhristu ambiri ankakonda kwambiri Mulungu, Akhristu anzawo komanso anthu ena ndipo ankalalikira mwakhama “uthenga wabwino wonena za Khristu.” (Mac. 2:44-47; 5:42) Ngakhale zinali choncho, panalinso Akhristu ena amene analola kuti chikondi chawo chizirale.

3. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti chikondi cha Akhristu ena chizirale?

3 Yesu Khristu ataukitsidwa anauza mpingo wa ku Efeso kuti: “Ndakupeza ndi mlandu wakuti wasiya chikondi chimene unali nacho poyamba.” (Chiv. 2:4) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti  asinthe? Mwina anasokonezedwa ndi anthu okonda zinthu za m’dziko. (Aef. 2:2, 3) Mofanana ndi mizinda yambiri ya masiku ano, mumzinda wa Efeso munkachitika zinthu zambiri zoipa. Mzindawu unali wotukuka kwambiri ndipo anthu ankakonda kwambiri chuma ndi zosangalatsa. Zikuoneka kuti izi zinachititsa kuti asiye kukonda Mulungu ndiponso anzawo. Anthu ambiri amumzindawu analinso otayirira komanso achiwerewere.

4. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti chikondi cha anthu masiku ano chazirala? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Zimene Yesu ananena pa nkhani ya chikondi zikuchitikanso masiku ano. Masiku ano anthu ambiri asiya kukonda Mulungu. Ambiri asiya kumukhulupirira ndipo amaganiza kuti mabungwe a anthu ndi amene angathetse mavuto awo. Chikondi cha anthu amene salambira Mulungu chikunka chichepa. Ndipo zimene zinkachitika mumpingo wa ku Efeso zikusonyeza kuti chikondi cha Akhristu masiku ano chikhozanso kuzirala. Tiyeni tsopano tikambirane zimene tingachite kuti tisasiye kukonda (1) Yehova (2) choonadi ndiponso (3) abale ndi alongo athu.

MUZIKONDA YEHOVA

5. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukonda Mulungu?

5 Tsiku limene Yesu ananena zoti chikondi cha ena chidzazirala, anali atanenanso za chikondi chofunika kwambiri. Iye anati: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba.” (Mat. 22:37, 38) Zimenezi zikusonyeza kuti kukonda kwambiri Yehova kungatichititse kuti tizikonda malamulo ake, tikhale opirira ndiponso kuti tizidana ndi zinthu zoipa. (Werengani Salimo 97:10.) Komabe, dziko loipali ndiponso zochita za Satana zikhoza kutichititsa kuti tisiye kukonda Mulungu.

6. Kodi anthu akasiya kukonda Mulungu zotsatira zake zimakhala zotani?

6 Anthu a m’dzikoli amakonda zinthu zolakwika. M’malo mokonda Mlengi wawo, ‘amadzikonda’ okha. (2 Tim. 3:2) Dziko lolamulidwa ndi Satanali limalimbikitsa “chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yoh. 2:16) Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu anzake za kuopsa komangochita zimene thupi lawo likufuna. Iye anati: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa . . . chifukwa kuika maganizo pa zinthu za thupi ndiko udani ndi Mulungu.” (Aroma 8:6, 7) Ndipotu anthu amene moyo wawo wonse amangokhalira kufunafuna chuma kapena kuchita dama, pa mapeto pake amaona kuti sanapindule chilichonse ndipo amakhumudwa.​—1 Akor. 6:18; 1 Tim. 6:9, 10.

7. N’chiyani chingatisokoneze tikapanda kusamala?

7 Anthu amene sakhulupirira Mulungu amachititsa anthu ena kuti asiye kukonda Mulungu komanso kukhulupirira zoti aliko. Amachititsanso anthu ambiri kuganiza kuti munthu wanzeru zake sangakhulupirire zoti kuli Mulungu. Komanso anthu ambiri amalemekeza kwambiri asayansi, zomwe zimachititsa kuti asamalemekeze Mulungu yemwe anatilenga. (Aroma 1:25) Ngati titamamvetsera zonena za anthu amenewa, tikhoza kusiya kukonda Yehova.​—Aheb. 3:12.

8. (a) Kodi anthu a Yehova ambiri amakumana ndi mavuto ati? (b) Kodi lemba la Salimo 136 limatitsimikizira za chiyani?

8 Kukhumudwa kungachititsenso kuti chikhulupiriro  chathu chifooke ndipo tingasiye kukonda Mulungu. M’dziko la Satanali, tonsefe timakumana ndi zinthu zokhumudwitsa. (1 Yoh. 5:19) Mwina panopa tikuvutika chifukwa cha ukalamba, matenda kapena mavuto azachuma. Mwinanso tikuvutika chifukwa choti timadziona ngati olephera, timadziimba mlandu pa zimene tinalakwitsa, apo ayi chifukwa choti zimene tinkayembekezera sizikuchitika. M’malo mochita zimenezi, tiyenera kuganizira kwambiri mawu olimbikitsa osonyeza kuti Yehova sangasiye kutikonda. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 136:23 limati: “Anatikumbukira pamene adani anatinyazitsa: Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amakonda atumiki ake nthawi zonse. Choncho sitiyenera kukayikira kuti amamva ‘madandaulo athu’ ndipo amatithandiza.​—Sal. 116:1; 136:24-26.

9. N’chiyani chinathandiza Paulo kuti asasiye kukonda Mulungu?

9 Mofanana ndi amene analemba Salimoli, Paulo ankalimbikitsidwa kwambiri akaganizira zoti Yehova ankamuthandiza nthawi zonse. Iye analemba kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?” (Aheb. 13:6) Paulo ankatha kulimbana ndi mavuto ake chifukwa ankadziwa kuti Yehova amamukonda komanso kumuthandiza. Sankalola kuti mavuto amukhumudwitse kapena kumutayitsa mtima. Ndipotu atamangidwa, Paulo analemba makalata ambiri olimbikitsa Akhristu anzake. (Aef. 4:1; Afil. 1:7; Filim. 1) Ngakhale atakumana ndi mayesero aakulu, Paulo sanasiye kukonda Mulungu. Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Nthawi zonse ankadalira “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akor. 1:3, 4) Kodi tingatsanzire bwanji Paulo n’kumakondabe kwambiri Yehova?

Muzikonda Yehova (Onani ndime 10)

10. Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri Yehova?

10 Paulo anatchula mfundo imene ingatithandize kuti tizikondabe Yehova. Iye analemba kuti: “Muzipemphera mosalekeza.” Komanso nthawi ina analemba kuti: “Limbikirani kupemphera.” (1 Ates. 5:17; Aroma 12:12) Popanda kulankhula ndi Mulungu m’pemphero sitingakhale naye pa ubwenzi wabwino. (Sal. 86:3) Tikamafotokozera Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” zimene zili mumtima mwathu komanso mmene tikumvera, timayamba kumukonda kwambiri. (Sal. 65:2) Ndiyeno tikaona kuti Yehova akuyankha mapemphero athu, chikondicho chimakula. Timafikanso pozindikira kuti “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.” (Sal. 145:18) Munthu akadziwa kuti Yehova amamuthandiza amatha kupirira mayesero aakulu kwambiri.

MUZIKONDA CHOONADI

11, 12. Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri choonadi?

11 Akhristufe timakonda kwambiri choonadi ndipo timadziwa kuti chimapezeka m’Mawu a Mulungu. Paja popemphera kwa Atate wake, Yesu anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yoh. 17:17) Choncho kuti munthu akonde choonadi, ayenera kudziwa kaye Mawu a Mulungu. (Akol. 1:10) Komabe kungodziwa Mawuwo si kokwanira. Munthu yemwe analemba Salimo 119 anatithandiza kumvetsa tanthauzo la kukonda choonadi. (Werengani Salimo 119:97-100.) Tsiku lililonse tiyenera kupeza mpata woganizira kwambiri  zimene tawerenga m’Baibulo. Tikhoza kukonda kwambiri choonadi tikamaganiziranso mmene mfundo za m’Baibulo zimatithandizira.

12 Salimo 119 limanenanso kuti: “Mawu anu amatsekemera m’kamwa mwanga, kuposa mmene uchi umakomera!” (Sal. 119:103) Mfundo za m’Baibulo zimene timaphunzira m’gulu la Mulungu zingakhale zokoma ngati uchi. Tikamaziganizira kwambiri zingakhale ngati tikumva kutsekemera kwa “mawu okoma” m’kamwa mwathu. Ndipo izi zingathandize kuti tizikumbukira mfundozo komanso kuzigwiritsa ntchito.​—Mlal. 12:10.

13. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza Yeremiya kuti azikonda choonadi? (b) Kodi zotsatira zake zinali zotani?

13 Mneneri Yeremiya ankakonda choonadi ndi mtima wonse. Iye anati: “Mawu anu anandipeza ndipo ndinawadya. Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu wa makamu.” (Yer. 15:16) Yeremiya ankaganizira kwambiri mawu a Mulungu ndipo zinali ngati anawadya. Zimenezi zinamuthandiza kuyamikira kwambiri mwayi wake wodziwika ndi dzina la Yehova. Kodi nafenso timakonda kwambiri choonadi komanso kuyamikira mwayi wathu wapadera wodziwika ndi dzina la Mulungu ndiponso wolengeza za Ufumu wake?

Muzikonda choonadi (Onani ndime 14)

14. Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri choonadi?

14 Kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo komanso mabuku athu, kodi tingachitenso chiyani kuti tizikonda kwambiri choonadi? Tiyenera kupezeka pamisonkhano yonse yampingo. Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi njira yaikulu imene Yehova amatiphunzitsira. Koma kuti tizimvetsa bwino nkhani zake tiyenera kukonzekera bwino phunziro lililonse. Pokonzekera tiyenera kuwerenga malemba onse amunkhaniyo. Masiku ano, tikhoza kuchita dawunilodi Nsanja ya Olonda m’zilankhulo zosiyanasiyana pawebusaiti ya jw.org kapena kuiwerenga pogwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Library. Tikamawerenga pogwiritsa zipangizo zamakono timatha kutsegula malemba amene ali munkhaniyo mosavuta. Koma kaya tikugwiritsa njira iti powerenga  magazini, tikamawerenga ndiponso kuganizira kwambiri malembawa timayamba kukonda kwambiri choonadi.​—Werengani Salimo 1:2.

TIZIKONDA ABALE NDI ALONGO ATHU

15, 16. (a) Kodi Yesu anapereka lamulo liti pa Yohane 13:34, 35? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kukonda abale athu kumayendera limodzi ndi kukonda Mulungu ndiponso Baibulo?

15 Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”​—Yoh. 13:34, 35.

16 Kukonda Yehova kumayendera limodzi ndi kukonda abale ndi alongo athu. Ndipotu sizingatheke kukonda Mulungu koma osakonda abale athu. Komanso n’zosatheka kukonda abale athu koma osakonda Mulungu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:20) Komanso kukonda Yehova ndi abale athu kumayendera limodzi ndi kukonda Mawu a Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti kukonda Mawu a Mulungu kumatilimbikitsa kuti tizimvera lamulo la m’Baibulo lakuti tizikonda Mulungu ndiponso abale athu.​—1 Pet. 1:22; 1 Yoh. 4:21.

Muzikonda abale ndi alongo (Onani ndime 17)

17. Tchulani njira zina zimene tingasonyezere kuti timakonda abale ndi alongo athu.

17 Werengani 1 Atesalonika 4:9, 10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu? Tikhoza kuthandiza m’bale kapena mlongo wachikulire amene akufunika kumuthandiza kuti azitha kufika kumisonkhano. Kapena tikhoza kuthandiza mlongo wamasiye amene nyumba yake ikufunikira kukonzedwa. (Yak. 1:27) Abale ndi alongo athu onse, kaya achikulire kapena ana, amafunika kulimbikitsidwa akakhala ndi nkhawa, akakhumudwa kapena akakumana ndi mavuto ena. (Miy. 12:25; Akol. 4:11) Zimene timalankhula komanso kuchita zingasonyeze kuti timakonda kwambiri “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.”​—Agal. 6:10.

18. Kodi n’chiyani chingatithandize kuthetsa mikangano ndi Akhristu anzathu?

18 Baibulo linaneneratu kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu adzakhala odzikonda komanso adyera. (2 Tim. 3:1, 2) Choncho, Akhristufe tiyenera kuyesetsa kuti tizikonda kwambiri Mulungu, choonadi komanso abale ndi alongo athu. N’zoona kuti nthawi zina tikhoza kusemphana maganizo ndi Akhristu anzathu. Koma chifukwa chakuti timakondana, tonse timayesetsa kuthetsa kusemphana maganizo mwamsanga komanso mwachikondi. (Aef. 4:32; Akol. 3:14) Choncho, tisalole kuti chikondi chathu chizirale. M’malomwake tiyeni tipitirize kukonda kwambiri Yehova, Mawu ake ndiponso abale ndi alongo athu.