Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”

“Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”

“Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?”​—YOH. 21:15.

NYIMBO: 128, 45

1, 2. Fotokozani zimene zinachitikira Petulo atachezera usiku wonse panyanja.

OPHUNZIRA 7 a Yesu anagwira ntchito yausodzi usiku wonse m’nyanja ya Galileya koma sanaphe nsomba ngakhale imodzi. Pa nthawiyi n’kuti Yesu ataukitsidwa ndipo m’mamawa iye anaima m’mbali mwa nyanja n’kuona zimene ankachita. Kenako anawauza kuti: “Ponyani ukonde kumbali ya kudzanja lamanja kwa ngalawayo ndipo mupeza kenakake.” Ophunzirawo “anaponyadi ukondewo, koma sanathenso kuukoka chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba.”​—Yoh. 21:1-6.

2 Yesu anawakonzera chakudya cham’mawa, kenako anayang’ana Simoni Petulo n’kumufunsa kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?” Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pofunsa funso limeneli? Petulo ankakonda usodzi. Ndiye zikuoneka kuti Yesu ankafuna kudziwa ngati iye amakonda kwambiri ntchito ya usodzi kuposa mmene amakondera Yesu ndi mfundo zimene ankaphunzitsa. Petulo anayankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.”  (Yoh. 21:15) Zimene Petulo ankachita kuyambira tsiku limenelo zinasonyeza kuti ankakondadi Yesu. Iye ankalalikira mwakhama ndipo anali munthu wodalirika kwambiri mumpingo.

3. Kodi Akhristu ayenera kusamala kwambiri ndi chiyani?

3 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anafunsa Petulo? Tiyenera kusamala kuti tisasiye kukonda Khristu komanso kuika zinthu za Ufumu pamalo oyamba. Yesu ankadziwa kuti munthu akhoza kusokonezeka chifukwa chodera nkhawa zinthu za m’dzikoli. Mufanizo lake la munthu wofesa mbewu, Yesu ananena kuti anthu ena akhoza kumva “mawu a ufumu” n’kuyamba kuwatsatira koma “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma” chimalepheretsa mawuwo kukula. (Mat. 13:19-22; Maliko 4:19) Choncho tikapanda kusamala, nkhawa za tsiku ndi tsiku zikhoza kusokoneza mtima wathu n’kuyamba kufooka. N’chifukwa chake Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo.”​—Luka 21:34.

4. N’chiyani chingatithandize kuti tisasiye kukonda Khristu? (Onani chithunzi choyambirira.)

4 Mofanana ndi Petulo, tingasonyeze kuti timakonda Khristu ngati tiika ntchito yolalikira pamalo oyamba. Koma kodi tingatani kuti tisasiye kuchita zimenezi? Nthawi zina tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimakonda chiyani kwenikweni? Kodi ndimasangalala kwambiri ndikamachita zinthu ziti, zokhudza kutumikira Yehova kapena zina?’ Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene tikapanda kusamala zikhoza kuchititsa kuti tisiye kukonda kwambiri Khristu. Zinthu zake ndi ntchito, zosangalatsa komanso chuma.

MUZIONA NTCHITO YANU MOYENERA

5. Kodi amuna ali ndi udindo wotani?

5 Petulo ankagwira ntchito ya usodzi kuti azipeza zofunika pa moyo. Masiku anonso amuna amadziwa kuti Malemba amanena kuti ali ndi udindo wopezera mabanja awo zofunika pa moyo. (1 Tim. 5:8) Iwo ayenera kugwira ntchito mwakhama kuti akwaniritse udindowu. Komabe m’masiku otsiriza ano kuchita zimenezi si kophweka.

6. Kodi anthu amakumana ndi mavuto ati pa nkhani ya ntchito?

6 Popeza ntchito zikusowa, anthu ambiri amalolera kugwira ntchito maola ambiri koma malipiro ake ali ochepa. Komanso mabwana amafuna kuti anthu azichita zambiri pa nthawi yochepa. Izi zimachititsa kuti anthuwo akhale otopa komanso akhale ndi nkhawa. Anthu amene amaona kuti sangakwanitse kuchita zimene abwana awo amafuna akhoza kuchotsedwa ntchito.

7, 8. (a) Kodi tiyenera kukhala okhulupirika kwambiri kwa ndani? (b) N’chiyani chinachitikira m’bale wina wa ku Thailand?

7 Koma Akhristufe tiyenera kukhala okhulupirika kwambiri kwa Yehova Mulungu osati kwa mabwana athu. (Luka 10:27) Ntchito imangotithandiza kuti tizipeza zofunika pa moyo n’cholinga choti tizitumikira bwino Mulungu. Koma tikapanda kusamala ntchito yathu ikhoza kutisokoneza potumikira Yehova. Mwachitsanzo, m’bale wina ku Thailand anati: “Ndinkasangalala kwambiri ndi ntchito yanga yokonza makompyuta koma sinkandipatsa mpata wopuma komanso wochita zinthu zokhudza kulambira. Ndinazindikira kuti ndiyenera kusintha ntchito kuti ndiziika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba.” Kodi m’baleyu anachita chiyani?

8 Iye anati: “Ndinayamba kukonza zinthu  kuti ndisinthe ntchito. Patapita chaka chimodzi, ndinasankha kuti ndiyambe kugulitsa ayisikilimu m’mbali mwa msewu. Poyamba, sindinkapeza ndalama zokwanira ndipo ndinayamba kutaya mtima. Ndikakumana ndi anthu amene ndinkagwira nawo ntchito, ankandiseka. Ankandifunsa chifukwa chake ndinasankha kugulitsa ayisikilimu padzuwa m’malo mogwira ntchito yokonza makompyuta mu ofesi yokhala ndi mashini obweretsa mpweya wozizira. Ndinkapempha Yehova kuti andithandize kupirira komanso kukwaniritsa cholinga changa chokhala ndi nthawi yambiri yomutumikira. Pasanapite nthawi yaitali, zinthu zinayamba kuyenda bwino. Ndinadziwa ayisikilimu amene anthu amakonda komanso kapangidwe kake moti tsiku lililonse palibe amene ankatsala. Kunena zoona, ndinayamba kupeza ndalama zambiri kuposa zimene ndinkapeza pa ntchito yokonza makompyuta. Ndimasangalalanso chifukwa sindikhala ndi nkhawa ngati mmene zinalili pa ntchito yakale ija. Koma chofunika kwambiri n’chakuti ndalimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova.”​—Werengani Mateyu 5:3, 6.

9. N’chiyani chingatithandize kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito?

9 Yehova amafuna kuti tizigwira ntchito mwakhama ndipo tikamachita zimenezi, timasangalala. (Miy. 12:14) Koma malinga ndi zimene zinachitikira m’bale uja, tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito. Paja Yesu anati: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi [zofunika pa moyo] zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mat. 6:33) Kuti tidziwe ngati tili ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito, tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimasangalala kwambiri ndikamagwira ntchito, kapena ndimasangalala ndikamachita zinthu zokhudza kulambira?’ Kuganizira kwambiri funsoli kungatithandize kuzindikira zimene timakonda kwambiri.

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu ananena kwa Marita?

10 Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Pa nthawi ina, iye anapita kunyumba ya Mariya ndi Marita. Marita anatanganidwa kwambiri ndi kukonza chakudya pomwe Mariya anakhala pansi n’kumamvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa. Marita atadandaula kuti Mariya sankamuthandiza, Yesu anamuuza kuti: “Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri, ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.” (Luka 10:38-42) Apatu Yesu anaphunzitsa Marita mfundo yofunika. Nafenso tiyenera kusankha “chinthu chabwino,” chomwe ndi kuika kutumikira Yehova pamalo oyamba. Tikatero tidzapewa kusokonezedwa ndi ntchito komanso tidzasonyeza kuti timakonda kwambiri Khristu.

MUZIONA ZOSANGALATSA M’NJIRA YOYENERA

11. Kodi Malemba amati bwanji pa nkhani yopuma ndi kusangalala?

11 Anthufe timafunika nthawi yopuma komanso yosangalala. Paja Mawu a Mulungu amati: “Kwa munthu, palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake.” (Mlal. 2:24) Yesu anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Tsiku lina atalalikira kwa nthawi yaitali, anauza ophunzira ake kuti: “Bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”​—Maliko 6:31, 32.

12. Kodi tiyenera kupewa chiyani pa nkhani ya zosangalatsa? Perekani chitsanzo.

12 Kupeza nthawi yopuma komanso yosangalala kumatithandiza. Koma pamakhala  mavuto ngati munthu amangoganizira zosangalala basi. M’nthawi ya atumwi, anthu ambiri ankayendera mfundo yoti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.” (1 Akor. 15:32) Masiku anonso, anthu ambiri ali ndi maganizo amenewa. Mwachitsanzo, zaka zingapo zapitazo, mnyamata wina wa ku Europe anayamba kupezeka pamisonkhano. Koma iye ankakonda kwambiri zosangalatsa moti anasiya kusonkhana. Koma kenako anazindikira kuti mtima umene anali nawowo unkamubweretsera mavuto. Choncho anayambiranso kuphunzira Baibulo ndipo anayenerera kukhala wofalitsa. Iye atabatizidwa ananena kuti: “Ndazindikira kuti kutumikira Yehova n’kumene kumasangalatsa kwambiri osati kumangotanganidwa ndi zosangalatsa za m’dzikoli. Ndikungodandaula kuti sindinazindikire zimenezi mwamsanga.”

13. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kumangochita zosangalatsa zokhazokha n’koopsa. (b) N’chiyani chingatithandize kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya zosangalatsa?

13 Cholinga cha zosangalatsa n’choti zititsitsimule komanso kutipatsa mphamvu. Koma kodi tiyenera kuchita zosangalatsazo kwa nthawi yaitali bwanji? Kuti tiyankhe funsoli, taganizirani chitsanzo ichi. Anthu ambiri amakonda maswiti koma tonse timadziwa kuti zinthu sizingayende bwino ngati tikungodya maswiti okhaokha. Timafunika kudya zakudya zina zopatsa thanzi. Mofanana ndi zimenezi, munthu amene amangokhalira kuchita zosangalatsa akhoza kufooka potumikira Mulungu. Kuti zimenezi zisatichitikire, tiyenera kuchita mwakhama zinthu zokhudza kulambira. Koma kodi tingadziwe bwanji ngati tili ndi maganizo oyenera pa nkhani ya zosangalatsa? Tingachite bwino kuona zimene tachita mlungu umenewowo. Kodi ndi maola angati amene tinkachita zinthu monga kusonkhana, kulalikira komanso kuphunzira Mawu a Mulungu patokha kapena ndi banja lathu? Nanga ndi maola angati amene tinkangocheza, kuchita masewera enaake kapena kuonera TV? Kodi zimene tapezazo zikusonyeza chiyani? Kodi tikufunikira kusintha zinthu zina kuti tisakhale ngati munthu wodya maswiti okhaokha?​—Werengani Aefeso 5:15, 16.

14. N’chiyani chingatithandize kuti tizisankha bwino pa nkhani ya zosangalatsa?

14 Mabanja, komanso munthu aliyense payekha ali ndi ufulu wosankha zosangalatsa zimene amakonda, bola ngati sizikusemphana ndi mfundo za m’Baibulo. * Zosangalatsa zabwino “ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlal. 3:12, 13) N’zoona kuti anthufe tingasankhe mosiyana pa nkhani imeneyi. (Agal. 6:4, 5) Koma kaya tasankha zosangalatsa zotani, tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera. Paja Yesu ananena kuti: “Kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.” (Mat. 6:21) Choncho chifukwa chokonda Yesu, timayesetsa kuganizira, kulankhula komanso kuchita zinthu zosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri kwa ife kuposa zinthu zina.​—Afil. 1:9, 10.

MUZIPEWA MTIMA WOKONDA CHUMA

15, 16. (a) Kodi Mkhristu angasokonezedwe bwanji ndi kukonda chuma? (b) Kodi Yesu anapereka malangizo ati pa nkhani ya chuma?

15 Masiku ano anthu ambiri amangokhalira kuganizira zinthu monga zovala ndiponso zipangizo zamakono zomwe zangotuluka kumene. N’chifukwa chake Mkhristu aliyense ayenera kudzifufuza pa nkhaniyi.  Akhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona kuti zinthu za m’dzikoli ndi zofunika kwambiri? Kodi nthawi yambiri ndimakhala ndikufufuza ndiponso kuganizira zinthu monga mafoni kapena zovala kuposa nthawi imene ndimakhala ndikukonzekera misonkhano? Kodi ndimatanganidwa kwambiri ndi zinthu za tsiku ndi tsiku moti sindikhala ndi nthawi yambiri yoti ndizipemphera kapena kuwerenga Baibulo?’ Tikaona kuti tikuyamba kukonda zinthu za m’dzikoli kuposa Khristu, tingachite bwino kuganizira mawu a Yesu akuti: “Chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse.” (Luka 12:15) N’chifukwa chiyani Yesu anapereka chenjezo limeneli?

16 Yesu ananena kuti “kapolo sangatumikire ambuye awiri.” Iye ananenanso kuti: “Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” Zili choncho chifukwa “ambuye” onse sangafune kuti tizitumikiranso wina. Komanso Yesu ananena kuti tikamatumikira onse awiri ‘tidzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena tidzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo.’ (Mat. 6:24) Tonsefe ndife ochimwa choncho tiyenera kulimbana ndi “zilakolako za thupi lathu,” kuphatikizapo mtima wokonda chuma.​—Aef. 2:3.

17. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena amavutika kuti akhale ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chuma? (b) N’chiyani chingatithandize kupewa mtima wokonda chuma?

17 Anthu amene amakonda zinthu za m’dzikoli amavutika kuti azikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chuma. (Werengani 1 Akorinto 2:14.) Popeza kuti saganiza bwino, zimawavuta kuti asiyanitse choyenera ndi chosayenera. (Aheb. 5:11-14) N’chifukwa chake amangokhalira kufunafuna chuma ndipo sakhutira. (Mlal. 5:10) Komabe tikhoza kupewa zimenezi tikamawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse. (1 Pet. 2:2) Yesu anatha kukana mayesero chifukwa choganizira Mawu a Mulungu. Nafenso tikamatsatira mfundo za m’Baibulo tikhoza kupewa mtima wokonda chuma. (Mat. 4:8-10) Tikamachita zimenezi, Yesu amaona kuti timamukonda kwambiri kuposa chuma.

Kodi mumaika zinthu ziti pamalo oyamba? (Onani ndime 18)

18. Kodi mukufunitsitsa kuchita chiyani?

18 Pamene Yesu anafunsa Petulo kuti, “Kodi umandikonda ine kuposa izi?” ankamukumbutsa kuti ayenera kuika zinthu zokhudza Mulungu pamalo oyamba. Dzina lakuti Petulo limatanthauza kuti “mwala” ndipo dzinali linkamuyenera chifukwa Petulo anali wolimba komanso wodalirika potumikira Yehova. (Mac. 4:5-20) Ifenso tiyenera kukhala osasunthika pa nkhani yokonda Khristu ndipo tisalole kuti ntchito, zosangalatsa kapena chuma zitisokoneze. Tiyeni nthawi zonse tizisankha zinthu zomwe zimasonyeza kuti timagwirizana ndi mawu amene Petulo anauza Yesu akuti: “Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.”

^ ndime 14 Onani nkhani yakuti “Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2011, tsamba 9-12, ndime 6-15.