Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  March 2016

Muziyesetsa kuthandiza komanso kulimbikitsa abale ndi alongo anu

Kodi Mungathandize Bwanji Mpingo Wanu?

Kodi Mungathandize Bwanji Mpingo Wanu?

YESU asanapite kumwamba anauza ophunzira ake kuti: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Koma kodi Akhristuwa akanakwanitsa bwanji kuchita zimenezi?

Pulofesa wina wa pa Oxford University, dzina lake Martin Goodman, ananena kuti: “M’nthawi ya ulamuliro wa Aroma, ntchito yolalikira inkachititsa kuti Akhristu azisiyana ndi anthu a zipembedzo zina kuphatikizapo Ayuda.” Yesu ankapita m’madera osiyanasiyana kukalalikira. Ndiyeno Akhristu oona ankayenera kutsatira chitsanzo chake n’kumalalikira “uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu” kwa anthu onse. Ankafunika kufufuza anthu amene akufuna kumva uthenga wa m’Baibulo. (Luka 4:43) N’chifukwa chake mumpingo wachikristu woyambirira munali “atumwi.” Mawuwa amanena za anthu amene atumizidwa kuti akalalikire. (Maliko 3:14) Yesu analamula otsatira ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.”—Mat. 28:18-20.

Ngakhale kuti atumwi 12 a Yesu anamwalira kale, atumiki ambiri a Yehova masiku ano amayesetsa kutsatira zimene atumwiwa ankachita. Tikutero chifukwa chakuti akapemphedwa kuti apite kumene kukufunika olalikira ambiri, iwo amayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6:8) Akhristu ena, kuphatikizapo amene anamaliza maphunziro a Sukulu ya Giliyadi, amasamukira kudziko lina kukalalikira. Ena amasamukira kudera lina m’dziko lawo lomwelo. Enanso amaphunzira chilankhulo china kuti azithandiza mpingo kapena kagulu ka anthu a chilankhulocho. Koma kuchita zonsezi sikophweka. Choncho abale ndi alongo amene amachita zimenezi amadzipereka kwambiri. Amasonyeza kuti amakonda Yehova komanso anthu anzawo. Iwo amakonzekera bwino ndipo amagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso ndalama zawo kuti athandize ena. (Luka  14:28-30) Zimene abale ndi alongo oterewa amachita zimathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira.

Koma mwina inuyo simungakwanitse kusamukira kudera kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri kapena kuphunzira chilankhulo china. Ngati ndi choncho, mukhoza kukhala mmishonale mumpingo wanu womwewo.

MUNGAKHALE MMISHONALE MUMPINGO WANU WOMWEWO

Kaya mwasamukira kudera lina kapena muli mumpingo wanu

Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankagwira ntchito yolalikira mwakhama. Koma ambiri sanali amishonale ndipo ankatumikira mumpingo wakwawo. Malangizo amene Paulo anauza Timoteyo anali ofunika kwa Akhristu onse oyambirira ndipo ndi ofunikanso kwa ifeyo. Iye anati: “Gwira ntchito ya mlaliki, ndipo ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.” (2 Tim. 4:5) Akhristu onse ayenera kumvera lamulo loti azilalikira uthenga wa Ufumu komanso azithandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Ndipotu munthu angathe kumachita zinthu ngati mmishonale ngakhale ali mumpingo wawo womwewo.

Mwachitsanzo, amishonale akasamukira kumayiko ena, amafunika kusintha kuti agwirizane ndi mmene zinthu zilili kumaloko. Nanga kodi ifeyo tingatani ngati sitingathe kusamukira kumene kukufunika ofalitsa Ufumu ambiri? Kodi ndi bwino kuganiza kuti tikudziwa kale chilichonse chokhudza anthu a m’gawo lathu? Kapena tingathe kupeza njira zatsopano zolalikirira? Mwachitsanzo, mu 1940 abale analimbikitsidwa kuti azichita ulaliki wamumsewu tsiku limodzi, mlungu uliwonse. Kodi inunso mumayesetsa kupeza tsiku lochita ulaliki wamumsewu? Nanga munayesapo kulalikira pogwiritsa ntchito katebulo kapena kashelefu kamatayala? Apa mfundo ndi yoti, muziyesetsa kugwiritsa ntchito njira zatsopano zolalikirira.

Muzilimbikitsa ena kuti ‘azigwira ntchito ya mlaliki’

Chinanso chofunika ndi kukhala ndi maganizo oyenera. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzichita utumiki wanu mwakhama komanso muzisangalala potumikira ena. Nthawi zambiri abale ndi alongo amene amasamukira kudera lina kapena mumpingo wa chilankhulo china, amakhala kuti ndi ofalitsa aluso. Choncho amathandiza kwambiri mumpingo komanso pa ntchito yolalikira. Komanso, amishonale amatsogolera mumpingo umene asamukira mpaka patapezeka abale ena oyenerera. Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, kodi ‘mukuyesetsa’ kuti muyenerere kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu n’cholinga  choti muzithandiza mumpingo wanu?—1 Tim. 3:1.

‘MUZITHANDIZA KOMANSO KULIMBIKITSA’ ANTHU A MUMPINGO WANU

Muzithandiza ena

Monga taonera, mungathandize mpingo wanu ngati mutamachita khama pa ntchito yolalikira komanso kuyesetsa kuti muyenerere udindo mumpingo. Koma pali zinanso zimene mungachite. Kaya ndinu wachinyamata kapena wachikulire, m’bale kapena mlongo, mukhoza ‘kuthandiza komanso kulimbikitsa’ anthu a mumpingo wanu.—Akol. 4:11.

Kuti tithe kuchita zimenezi tiyenera kuwadziwa bwino anthu a mumpingo wathu. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tiziganizirana’. (Aheb. 10:24) Izi sizikutanthauza kuti tiyenera kulowerera nkhani za ena. Koma mfundo ndi yakuti, tikakumana ndi abale athu kumisonkhano tiyenera kupeza nthawi yocheza nawo kuti tiwadziwe bwino komanso tidziwe mavuto amene akukumana nawo. Tikamachita zimenezi tingathe kuwathandiza kapena kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo. Umenewu si udindo wa akulu ndi atumiki othandiza okha. N’zoona kuti pali mavuto ena amene abale amenewa okha ndi omwe angathandize. (Agal. 6:1) Komabe pali zambiri zimene tonsefe tingachite. Mwachitsanzo, tingathandize abale ndi alongo achikulire komanso mabanja amene akukumana ndi mavuto.

Muzilimbikitsa anthu amene ali ndi nkhawa

Chitsanzo ndi zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Salvatore. Chifukwa cha mavuto a zachuma, m’baleyu anagulitsa bizinezi yake, nyumba yake komanso katundu wambiri wa banja lake. A Salvatore analibenso pogwira ndipo ankada nkhawa kuti azisamalira bwanji banja lawo. Koma kenako banja lina mumpingo wawo linadziwa za nkhaniyi ndipo linaona kuti m’pofunika kuwathandiza. Choncho anawapatsa ndalama ndiponso anawathandiza iwowo ndi akazi awo kupeza ntchito. Banjali linkapezanso nthawi yocheza komanso kulimbikitsa banja lonse la a Salvatore. Panopa mabanja awiriwa amasangalala kwambiri akakumbukira zinthu zosangalatsa zimene ankachitira limodzi pa nthawi yovutayo.

Akhristufe timatsanzira Yesu ndipo timauza ena zomwe timakhulupirira komanso zimene Mulungu walonjeza. Choncho, kaya tingathe kusamuka kapena ayi, tiziyesetsa kuchitira zabwino anthu onse. Ndipotu tingathe kuchita izi mumpingo wathu womwewo. (Agal. 6:10) Tikamachita zimenezi timasangalala komanso ‘timapitiriza kubala zipatso m’ntchito iliyonse yabwino.’—Akol. 1:10; Mac. 20:35.