Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi abale monga oyang’anira madera ndi akulu ayenera kuchita chiyani akalandira malangizo amene gulu la Yehova limapereka?

Ayenera kutsatira mwamsanga malangizowo. Angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimalimbikitsa abale ndi alongo kuti akhale okhulupirika kwa Yehova? Nanga kodi ndimatsatira mwamsanga malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa?’w16.11, tsa. 11.

Kodi Akhristu oona analowa liti mu ukapolo wa Babulo Wamkulu?

Analowa mu ukapolowu pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene atumwi onse anamwalira. Pa nthawiyo m’pamene atsogoleri achipembedzo anayamba kukhala osiyana kwambiri ndi anthu ena. Matchalitchi anayambanso kugwira ntchito ndi boma ndipo ankalimbikitsa ziphunzitso zampatuko. Izi zinachititsa kuti anthu asamamvetsere zimene Akhristu okhulupirika ankaphunzitsa. Koma pofika chaka cha 1914, odzozedwa anali atayamba kutuluka mu ukapolowu.w16.11, tsa. 23-25.

Kodi ntchito ya Lefèvre d’Étaples inali yofunika bwanji?

Cha m’ma 1520 Lefèvre anamasulira Baibulo m’Chifulenchi n’cholinga choti anthu wamba aziliwerenga. Kafotokozedwe kake ka Malemba kanathandiza kwambiri Martin Luther, William Tyndale ndi John Calvin.wp16.6, tsa. 10-12.

Kodi “kuika maganizo pa zinthu za thupi” kumasiyana bwanji ndi “kuika maganizo pa zinthu za mzimu”? (Aroma 8:6)

Munthu amene amaika maganizo pa zinthu za thupi amangoganizira zilakolako za thupi, amakonda kulankhula za zinthuzo ndipo amasangalala akamazichita. Koma munthu amene amaika maganizo pa zinthu za mzimu amaona kuti chofunika kwambiri ndi zinthu zokhudza Mulungu ndipo amalola kuti mzimu woyera uzimutsogolera. Mapeto a kuika maganizo pa zinthu za thupi ndi imfa, pomwe mapeto a kuika maganizo pa zinthu za mzimu ndi moyo komanso mtendere.w16.12, tsa. 15-17.

Kodi mungatani kuti muchepetse nkhawa?

Muziona kuti zofunika kwambiri ndi ziti, musamayembekezere zinthu zosatheka, tsiku lililonse muzipeza nthawi yokhala panokha, muzisangalala ndi chilengedwe, muzichita tinthabwala, muzichita masewera olimbitsa thupi komanso muzigona mokwanira.w16.12, tsa. 22-23.

Kodi mawu oti “Inoki anasamutsidwa kuti asafe mozunzika” akutanthauza chiyani? (Aheb. 11:5)

Zikuoneka kuti Yehova anachititsa kuti Inoki amwalire popanda Inokiyo kudziwa kuti akufa.wp17.1, tsa. 12-13.

Kodi kudzichepetsa n’kofunika bwanji?

Munthu wodzichepetsa amazindikira kuti pali zinthu zina zimene sangakwanitse kuchita ndipo amadziwanso zinthu zimene si udindo wake kuchita. Tiyenera kuzindikira kuti zimene timachita zikhoza kukhudza anthu ena komanso tiyenera kupewa kudziona kuti ndife ofunika kwambiri.w17.01, tsa. 18.

Kodi pali umboni wotani woti Mulungu ankatsogolera bungwe lolamulira nthawi ya atumwi ngati mmene akuchitira ndi Bungwe Lolamulira masiku ano?

Mzimu woyera unkathandiza bungwe lolamulira la nthawi ya atumwi kuti lizimvetsa mfundo za m’Malemba. Angelo ankalithandiza kuti lizitsogolera bwino ntchito yolalikira. Komanso linkadalira Mawu a Mulungu kuti lizipereka malangizo abwino. Umu ndi mmene Yehova akuchitiranso ndi Bungwe Lolamulira la masiku ano.w17.02, tsa. 26-28.

N’chifukwa chiyani timaona kuti dipo ndi lamtengo wapatali kwambiri?

Timatero chifukwa cha zinthu 4 izi: Amene anapereka dipolo, chifukwa chimene analiperekera, zimene anadzimana kuti alipereke komanso chifukwa chakuti tinkafunikira kwambiri dipolo. Tiyenera kuganizira kwambiri zinthu zimenezi.wp17.2, tsa. 4-6.

Kodi Mkhristu akasankha zochita, akhoza kusintha zimene wasankhazo?

N’zoona kuti tiyenera kuchita zimene talonjeza. Koma nthawi zina tiyenera kuganiziranso zimene tasankha ndipo mwina tingafunike kuzisintha. Anthu a ku Nineve atalapa, Mulungu anasintha zimene ankafuna kuchita. Nthawi zina tiyenera kusintha zimene tasankha chifukwa cha mfundo zatsopano zimene tadziwa.w17.03, tsa. 16-17.

N’chifukwa chiyani miseche ndi yoopsa kwambiri?

Chifukwa chakuti ikhoza kukulitsa nkhani n’kufika poipa kwambiri. Kaya zimene tikuganizazo n’zoona kapena ayi, kulankhula zoipa za munthu wina kumangowonjezera mavuto.w17.04, tsa. 21.