Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  June 2017

“Udalitsike Chifukwa cha Kulingalira Bwino Kwako!”

“Udalitsike Chifukwa cha Kulingalira Bwino Kwako!”

MAWU ali pamwambawa anawalankhula ndi Davide pamene ankayamikira mzimayi wina dzina lake Abigayeli. Kodi n’chifukwa chiyani Davide anamuyamikira, nanga tingaphunzire chiyani pa zimene Abigayeli anachita?

Davide anakumana ndi mzimayiyu pa nthawi imene ankathawa Mfumu Sauli. Abigayeli anakwatiwa ndi munthu wachuma kwambiri dzina lake Nabala yemwe anali ndi nkhosa zambiri ndipo ankakhala kudera lamapiri kum’mwera kwa Yuda. Davide ndi amuna amene anali nawo “anali ngati khoma” loteteza abusa ndi nkhosa za Nabala. Kenako Davide anatuma amuna ena kwa Nabala kuti akapemphe kachakudya ‘kalikonse kamene dzanja lake lingapeze.’ (1 Sam. 25:8, 15, 16) Tikaganizira zimene Davide ndi anzake anachita, sitinganene kuti analakwitsa popempha zimenezi.

Koma Nabala anachita zinthu mogwirizana ndi dzina lake lomwe limatanthauza “Wopanda nzeru” kapena “Wopusa.” Iye anawayankha mwamwano ndipo anakana kupereka chakudyacho. Zitatero, Davide anakonzeka kuti akaphe Nabala ndi banja lake lonse chifukwa cha kupusa kwakeko.1 Sam. 25:2-13, 21, 22.

Abigayeli atazindikira kuti zimene mwamuna wakeyo anachita ziwabweretsera mavuto, anachita zinthu molimba mtima. Iye anapita kwa Davide mwaulemu n’kumudandaulira kuti aganizire mmene nkhaniyi ingakhudzire ubwenzi wake ndi Yehova. Abigayeli anapereka chakudya chambiri kwa Davide ndi anthu ake. Davide anazindikira kuti Yehova ndi amene anatuma Abigayeli kuti amuletse kupalamula mlandu wopha anthu. Iye anauza Abigayeli kuti: “Udalitsike chifukwa cha kulingalira bwino kwako. Udalitsike chifukwa cha kundigwira lero kuti ndisapalamule mlandu wamagazi.”1 Sam. 25:18, 19, 23-35.

Malinga ndi nkhaniyi, tiyenera kupewa kukhala ndi mtima wosayamika ngati wa Nabala. Taphunziranso kuti tikaona kuti vuto linalake likhoza kuchitika tiyenera kuchita zinthu mwanzeru kuti vutolo lisachitike. Mofanana ndi munthu wina amene analemba masalimo, tiyenera kupempha Mulungu kuti ‘atiphunzitse kulingalira bwino ndi kudziwa zinthu.’Sal. 119:66.

Tikatero, ena akhoza kuona kuti ndife anzeru. Kaya alankhula kapena ayi, mumtima mwawo akhoza kumva ngati Davide amene ananena kuti: “Udalitsike chifukwa cha kulingalira bwino kwako.”