Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  June 2016

Masiku ano munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi akuimira Yesu Khristu ndipo adzalemba chizindikiro anthu oyenera kupulumuka

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera komanso amuna 6 okhala ndi zida zophwanyira, omwe Ezekieli anaona akuimira ndani?

Akuimira Yesu komanso gulu lankhondo lakumwamba limene anagwira nalo ntchito yowononga Yerusalemu komanso limene adzagwire nalo ntchito yowononga dziko la Satanali pa Aramagedo. N’chifukwa chiyani tasintha mmene tinkafotokozera mfundo imeneyi?

Yerusalemu asanawonongedwe mu 607 B.C.E., Ezekieli anaona masomphenya a zoipa zimene zinkachitika mumzindawo komanso mmene mzindawo udzawonongedwere. Iye anaona amuna 6 atanyamula zida zophwanyira. Anaonanso munthu “wovala zovala zansalu” yemwe anali ndi “kachikwama ka mlembi, konyamuliramo inki ndi zolembera.” (Ezek. 8:6-12; 9:2, 3) Munthuyu anauzidwa kuti: “Uyendeyende mumzinda wonse ndipo ulembe . . . chizindikiro pamphumi za anthu amene akuusa moyo ndi kubuula chifukwa cha zonyansa zonse zimene zikuchitika mumzindawu.” (Ezek. 9:4-7) Kodi tikuphunzira chiyani pa masomphenyawa nanga munthu wonyamula kachikwamayu akuimira ndani?

Ezekieli anaona masomphenya amenewa mu 612 B.C.E., ndipo patangodutsa zaka 5 masomphenyawa anakwaniritsidwa koyamba pamene Ababulo anawononga Yerusalemu. Yehova ndi amene anagwiritsa ntchito Ababulowa popereka chilango kwa anthu ake osamvera. (Yer. 25:9, 15-18) Koma sikuti Ababulo anapha anthu onse. Yehova sanalole kuti olungama aphedwe limodzi ndi oipa. Iye anakonza njira yoti Ayuda amene sankagwirizana ndi zoipa zimene zinkachitikazo apulumuke.

Ezekieli sanagwire nawo ntchito yolemba chizindikiro kapena yakupha. Amene anagwira ntchito imeneyi ndi angelo. Choncho ulosiwu umatithandiza kudziwa zimene zinkachitika kumwamba. Yehova anatuma angelo kuti akawononge anthu oipa n’kupulumutsa anthu olungama. *

M’mbuyomu tinkafotokoza kuti munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi akuimira odzozedwa amene atsala padzikoli. Tinkanena kuti anthu amene akumvetsera uthenga umene timalalikira akulembedwa chizindikiro kuti adzapulumuke. Koma taona kuti m’pofunika kusintha mmene tinkamvera mfundo imeneyi. Malinga ndi zimene zili pa Mateyu 25:31-33 udindo woweruza anthu ndi wa Yesu. Pa chisautso chachikulu, iye adzasiyanitsa anthu kuti amene ali ngati nkhosa apulumuke koma amene ali ngati mbuzi awonongedwe.

Ndiyeno malinga ndi zimene tafotokozazi kodi tikuphunzira chiyani pa masomphenya a Ezekieli? Pali mfundo 5 zimene tikuphunzirapo.

  1.  Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa, Ezekieli anali ngati mlonda limodzi ndi Yeremiya. Ntchito imeneyi ndi imenenso anagwira Yesaya m’mbuyomo. Masiku ano, Yehova akugwiritsa ntchito kagulu ka odzozedwa kuti azidyetsa anthu ake komanso kuchenjeza ena za chisautso chachikulu. Ndipo antchito apakhomo onse a Khristu akugwira nawo ntchito yochenjeza anthuyi.—Mat. 24:45-47.

  2.  Ezekieli sanagwire nawo ntchito yolemba chizindikiro anthu opulumuka ndipo n’chimodzimodzinso ndi anthu a Mulungu masiku ano. Iwo amangolengeza uthenga wa Yehova pogwira  nawo ntchito yolalikira yomwe ikutsogoleredwa ndi angelo.—Chiv. 14:6.

  3.  M’masiku a Ezekieli, anthu sanalembedwe chizindikiro chenicheni pamphumi pawo. N’chimodzimodzinso masiku ano. Komano kodi iwo amafunika kuchita chiyani kuti mophiphiritsa adzalembedwe chizindikiro choti adzapulumuke? Ayenera kumvetsera uthenga umene ukulalikidwa padziko lonse, kusonyeza makhalidwe achikhristu, kudzipereka kwa Yehova komanso kuthandiza mokhulupirika abale ake a Khristu. (Mat. 25:35-40) Anthu amene amachita zimenezi adzalandira chizindikiro choti ndi oyenera kupulumuka chisautso chachikulu.

  4.  Munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi akuimira Yesu Khristu. Pa chisautso chachikulu, iye adzalemba chizindikiro anthu a khamu lalikulu akadzawaweruza kuti ndi nkhosa. Ndiyeno anthuwa adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.—Mat. 25:34, 46. *

  5.  Masiku ano, amuna 6 onyamula zida zophwanyira, akuimira gulu lankhondo lakumwamba la Yesu lotsogoleredwa ndi Yesuyo. Posachedwapa iwo awononga maboma a anthu n’kuthetsa zoipa zonse.—Ezek. 9:2, 6, 7; Chiv. 19:11-21.

Mfundo zimene tikuphunzira m’masomphenya a Ezekieliwa zikutithandiza kukhulupirira kuti Yehova sadzawononga anthu olungama limodzi ndi oipa. (2 Pet. 2:9; 3:9) Zikutikumbutsanso kufunika kogwira nawo mwakhama ntchito yolalikira chifukwa anthu onse akufunika kuchenjezedwa mapeto asanafike.—Mat. 24:14.

^ ndime 6 Anthu monga Baruki (mlembi wa Yeremiya), Ebedi-meleki Mwitiyopiya komanso Arekabu anapulumuka ngakhale kuti sanalembedwe chizindikiro chooneka. (Yer. 35:1-19; 39:15-18; 45:1-5) Iwo analembedwa chizindikiro chophiphiritsa pamphumi zawo.

^ ndime 12 Akhristu odzozedwa okhulupirika sadzafunika kulandira nawo chizindikirochi. M’malomwake iwo amadindidwa chidindo komaliza akatsala pang’ono kumwalira kapena adzadindidwa chisautso chachikulu chitatsala pang’ono kuyamba.—Chiv. 7:1, 3.