NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) July 2019

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa September 2-29, 2019

Tizikonzekera Kuti Tidzathe Kupirira Pozunzidwa

Kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima pokumana ndi anthu amene amadana nafe?

Tizilambirabe Yehova Ngakhale Boma Litatiletsa

Kodi tizitani ngati boma latiletsa kulambira Yehova?

‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga’

N’chifukwa chiyani ntchito yothandiza anthu kukhala ophunzira a Khristu ndi yofunika kwambiri, nanga ndi zinthu ziti zimene zingatithandize pogwira ntchitoyi?

Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Amene Sakonda Zachipembedzo?

Kodi tingathandize bwanji anthu amene sakonda zachipembedzo kuti azikonda Mulungu komanso kukhala ophunzira a Khristu?

MBIRI YA MOYO WANGA

Yehova Wandidalitsa Kuposa Mmene Ndinkaganizira

Kuchita umishonale ku Africa kunathandiza Manfred Tonak kuti akhale ndi makhalidwe abwino ambiri monga kuleza mtima komanso moyo wosalira zambiri.

Kodi N’zoona Kuti Yesu Anandifera Ineyo?

Kodi mumadziona ngati wachabechabe? Kodi mungathetse bwanji maganizo amenewa?