Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) July 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa August 28 mpaka September 24, 2017.

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Turkey

Mu 2014, kunali ntchito yapadera yolalikira ku Turkey. N’chifukwa chiyani ntchito yapaderayi inachitika? Kodi zotsatirapo zake zinali zotani?

Muzifunafuna Chuma Chenicheni

Kodi tingagwiritse ntchito bwanji chuma chathu kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Mulungu?

“Lirani ndi Anthu Amene Akulira”

Kodi n’chiyani chingalimbikitse munthu amene waferedwa? Nanga inuyo mungamuthandize bwanji?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutamanda Yehova?

Salimo 147 limatikumbutsa kuti tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyamikira ndiponso kuthokoza Mlengi wathu.

‘Mulungu Akwaniritse Zofuna Zanu’

Achinyamata ayenera kusankhiratu zimene adzachite m’tsogolo. Kuchita zimenezi kungakhale kovuta koma Yehova amadalitsa anthu amene amatsatira malangizo ake.

Tetezani Maganizo Anu

Satana amagwiritsa ntchito mfundo za bodza pofuna kutisokoneza. Kodi inuyo mungadziteteze bwanji?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi ndi nzeru kuti Mkhristu azisunga mfuti pofuna kudziteteza kwa anthu?