“Uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.”—MIKA 6:8.

NYIMBO: 48, 95

1-3. Kodi mneneri wa ku Yuda analephera kuchita chiyani, nanga zotsatira zake zinali zotani? (Onani chithunzi pamwambapa.)

PA NTHAWI imene Yerobowamu ankalamulira ku Isiraeli, Yehova anatumiza mneneri wa ku Yuda kuti akamuuze uthenga wa chiweruzo. Anachita izi chifukwa chakuti Yerobowamuyo ankachita zoipa. Mneneriyo anachita zinthu modzichepetsa n’kupereka uthengawo. Yerobowamu anakwiya kwambiri koma Yehova anateteza mneneri wakeyo.—1 Maf. 13:1-10.

2 Mneneriyu akubwerera kwawo, anakumana ndi munthu wokalamba wochokera ku Beteli. Munthuyo ananena kuti nayenso ndi mneneri wa Yehova. Ndiyeno anapusitsa mneneriyo kuti asamvere malangizo a Yehova akuti: “Usakadye chakudya kapena kumwa madzi, ndipo pobwerera usakadzere njira imene udutse popita.” Yehova sanasangalale ndipo mneneriyu asanafike kwawo anaphedwa ndi mkango.—1 Maf. 13:11-24.

3 Koma n’chifukwa chiyani mneneriyu anadzikuza n’kutsatira zimene munthu wokalambayo ananena? Baibulo silinena chifukwa  chake. Koma n’kutheka kuti anaiwala mfundo yoti ankayenera ‘kuyenda modzichepetsa ndi Yehova.’ (Werengani Mika 6:8.) M’Baibulo, mawu oti kuyenda ndi Yehova amatanthauza kumukhulupirira, kukhala mbali ya ulamuliro wake komanso kulola kuti azititsogolera. Munthu wodzichepetsa amadziwa kuti ayenera kulankhulana ndi Yehova nthawi zonse. Mwachitsanzo, mneneriyu akanachita bwino kufunsa Yehova ngati anasintha malangizo ake. Koma Malemba sasonyeza kuti anachita zimenezi. Ifenso timafunika kusankha zochita pa nkhani zovuta. Koma tikadzichepetsa n’kuyamba tafufuza maganizo a Yehova, tikhoza kupewa kulakwitsa kwambiri zinthu.

4. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

4 M’nkhani yapita ija tinaona tanthauzo la kudzichepetsa komanso chifukwa chake tiyenera kukhala odzichepetsa masiku ano. Koma kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kukhala odzichepetsa? Nanga tingatani kuti nthawi zonse tizikhala odzichepetsa? Kuti tiyankhe mafunsowa, tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene zingachititse kuti kudzichepetsa kukhale kovuta. Tionanso zoyenera kuchita pa zochitika zonsezo.—Miy. 11:2.

ZINTHU ZIKASINTHA PA MOYO WATHU

5, 6. Kodi Barizilai anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa?

5 Zimene timachita zinthu zikasintha pa moyo wathu kapena tikapatsidwa utumiki watsopano zingasonyeze ngati tili odzichepetsa kapena ayi. Mwachitsanzo, Barizilai ali ndi zaka 80, Davide anamuuza kuti apite naye kunyumba yachifumu kuti azikakhala limodzi. Ngakhale kuti umenewu unali mwayi waukulu, Barizilai anakana. Iye anachita zimenezi poona kuti anali wokalamba ndipo sanafune kuti akakhale mtolo kwa Davide. Choncho anauza Davide kuti atenge Chimamu, yemwe mwina anali mwana wake.—2 Sam. 19:31-37.

6 Kudzichepetsa n’kumene kunathandiza Barizilai kuti asankhe bwino pa nkhaniyi. Sikuti iye anakana kupita ndi Davide chifukwa choti ankaona kuti ndi udindo woti sangaukwanitse. Si chifukwanso choti ankafuna moyo waphee osati wakunyumba yachifumu. Koma ndi chifukwa choti ankadziwa kuti zinthu zinali zitasintha pa moyo wake chifukwa cha ukalamba. Ankadziwanso kuti sakanatha kuchita zinthu zina choncho anaona kuti si bwino kudzikakamiza. (Werengani Agalatiya 6:4, 5.) Ifenso tiyenera kukhala odzichepetsa. Tisamadziyerekezere ndi ena komanso tisamangoganizira za udindo kapena kutchuka. Koma tizingoyesetsa kuchita zimene tingathe potumikira Yehova. (Agal. 5:26) Kudzichepetsa kungatithandize kuti tizigwira ntchito limodzi ndi abale athu polemekeza Yehova komanso kuthandiza ena.—1 Akor. 10:31.

7, 8. Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kuti tizipewa kudzidalira?

7 Nthawi zambiri munthu akapatsidwa udindo waukulu, amakhalanso ndi mphamvu zambiri. Kupanda kusamala, zimenezi zingachititse kuti asakhale wodzichepetsa. Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi Nehemiya. Iye atamva kuti ku Yerusalemu kuli mavuto ambiri, anapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. (Neh. 1:4, 11) Yehova anayankha pemphero la Nehemiya ndipo Mfumu Aritasasita anamuika kuti akhale bwanamkubwa. Ngakhale kuti Nehemiya anali ndi udindo waukulu komanso chuma, sanayambe kudalira nzeru zake. Koma anapitiriza kuyenda ndi Mulungu ndipo nthawi zonse ankawerenga Chilamulo kuti adziwe malangizo a Yehova. (Neh. 8:1, 8, 9) Komanso iye sankagwiritsa ntchito udindo wake kuti apeze phindu. M’malomwake  ankagwiritsa ntchito zinthu zake pothandiza ena.—Neh. 5:14-19.

8 Nafenso utumiki wathu ukasintha kapena tikapatsidwa udindo wina, tisamayambe kudzidalira. Kodi munthu angasonyeze bwanji kuti wayamba kudzidalira? Mwachitsanzo, mkulu angayambe kugwira ntchito zina zampingo asanapemphe kaye Yehova kuti amuthandize. Komanso m’bale kapena mlongo angasankhe kuchita zinazake kenako n’kupempha Yehova kuti adalitse zimene wasankhazo. Kodi kumeneku tingati n’kudzichepetsa? Munthu wodzichepetsa sadalira nzeru zake ngakhale zitakhala kuti zimene akufuna kuchitazo si koyamba kuzichita. Amakumbukira kuti nzeru zake n’zochepa kwambiri poyerekeza ndi za Yehova ndipo amadziwa malo ake m’gulu la Yehova. (Werengani Miyambo 3:5, 6.) Anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda ndipo amafuna kukhala oposa ena. Koma atumiki a Yehovafe sitichita zimenezi. Timachita zinthu mogwirizana ndipo sitiganiza kuti udindo m’banja kapena mumpingo umapangitsa kuti munthu akhale wapamwamba kuposa ena.—1 Tim. 3:15.

ENA AKATICHITIRA ZOLAKWIKA KAPENA AKAMATITAMANDA

9, 10. Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji anthu akatiganizira kapena kutichitira zolakwika?

9 Munthu akhoza kukhumudwa kwambiri ngati ena amuganizira molakwika. Zoterezi zikanatha kuchitikira Hana. Mwamuna wake ankamukonda kwambiri koma iye sankasangalala chifukwa choti anali wosabereka. Ndiyeno mkazi mnzake dzina lake Penina ankamunyoza kwambiri. Tsiku lina Hana akupemphera kukachisi, Mkulu wa Ansembe dzina lake Eli anamudzudzula poganiza kuti waledzera. Apatu Hana akanatha kukwiya kwambiri. Koma iye anadzichepetsa n’kudziletsa ndipo anayankha mwaulemu. Pemphero lake lochokera mumtima linalembedwa m’Baibulo ndipo limasonyeza kuti iye ankakhulupirira kwambiri Mulungu, ankamutamanda komanso ankamuyamikira.—1 Sam. 1:5-7, 12-16; 2:1-10.

10 Mtima wodzichepetsa ungatithandizenso kuti ‘tigonjetse choipa mwa kuchita chabwino.’ (Aroma 12:21) M’dziko la Satanali, zinthu  zambiri sizikuyenda bwino ndipo tiyenera kusamala kuti tisamapse mtima kwambiri anthu akatichitira zoipa. (Sal. 37:1) Zimakhala zopweteka kwambiri ngati amene watilakwira ndi m’bale kapena mlongo. Koma munthu wodzichepetsa akalakwiridwa amatsanzira Yesu. Paja Baibulo limati: “Pamene anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe . . . koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” (1 Pet. 2:23) Yesu ankadziwa kuti udindo wobwezera ndi wa Yehova. (Aroma 12:19) Akhristufe timalangizidwanso kuti tiyenera kukhala odzichepetsa ndipo tizipewa kubwezera “choipa pa choipa.”—1 Pet. 3:8, 9.

11, 12. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa zinthu zikayamba kutiyendera bwino? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa pa nkhani ya zovala, kudzikongoletsa komanso khalidwe lathu?

11 Kudzichepetsa kumakhalanso kovuta ngati tikutamandidwa. Taganizirani zimene zinachitikira Esitere. Iye anali wokongola kwambiri. Ndiyeno anatengedwa kuti akakhale m’gulu la atsikana oti asamaliridwe bwino kwa chaka chathunthu. Kumeneko ankakhala ndi atsikana ambiri ochokera m’madera osiyanasiyana amene ankalamuliridwa ndi ufumu wa Perisiya. Pa nthawiyo anthu ankafuna kupeza mkazi amene angasangalatse mfumu. Koma Esitere anakhalabe waulemu komanso wodzichepetsa. Anapitiriza kuchita zimenezi ngakhale pamene anasankhidwa kuti akhale mfumukazi.—Esitere 2:9, 12, 15, 17.

Kodi timavala komanso kudzikongoletsa mosonyeza kuti timalemekeza Yehova ndi anzathu kapena mosonyeza kuti ndife odzikuza? (Onani ndime 12)

12 Kudzichepetsa kumathandizanso kuti tizivala komanso kudzikongoletsa mwaulemu. Munthu wodzichepetsa amapewa kudzionetsera kapena kudzitama koma amasonyeza “mzimu wabata ndi wofatsa.” (Werengani 1 Petulo 3:3, 4; Yer. 9:23, 24) Zimene timachita komanso kulankhula zimasonyeza zimene zili mumtima mwathu. Mwachitsanzo, anthu ena amakonda kulankhula zosonyeza kuti akusangalala chifukwa choti ali ndi udindo winawake, akudziwa zinsinsi zina kapena chifukwa choti amagwirizana ndi abale ena audindo. Ena amakonda kulankhula zosonyeza kuti zinthu zina zinayenda bwino chifukwa cha iwowo kuiwala kuti ena anathandizaponso. Koma Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani ya kudzichepetsa. Mfundo zambiri zimene ankalankhula zinali zochokera m’Malemba Achiheberi kapena zokhudza Malembawo. Iye ankachita zimenezi n’cholinga choti anthu adziwe kuti zimene ankalankhula zinali zochokera kwa Yehova osati nzeru zake.—Yoh. 8:28.

TIKAFUNA KUSANKHA ZOCHITA

13, 14. Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kusankha bwino zochita?

13 Tiyeneranso kukhala odzichepetsa tikafuna kusankha zochita. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ali ku Kaisareya, mneneri Agabo anamuuza kuti akapita ku Yerusalemu akamangidwa mwinanso kuphedwa kumene. Abale atamva zimenezi anachita mantha ndipo anauza Paulo kuti asapite. Koma Paulo anasankha kuti apitebe. Sikuti iye anachita zimenezi chifukwa chodzidalira. Kungoti sanalole kuti izi zimulepheretse kugwira ntchito imene Mulungu anamupatsa. Choncho anadalira Yehova. Abalewo ataona zimenezi anadzichepetsa ndipo anasiya kumuletsa.—Mac. 21:10-14.

14 Nafenso kudzichepetsa kungatithandize kuti tisankhe bwino ngakhale pa nkhani zimene sitikudziwa zonse. Mwachitsanzo, tingamaganize kuti, tikayamba utumiki winawake wa nthawi zonse, kodi zidzatithera bwanji tikadzadwala? Nanga tidzatani makolo athu okalamba akamadzafunika kuwasamalira? Kodi tikadzakalamba tizidzapeza kuti thandizo? Ngakhale munthu atapemphera kwambiri  kapena kufufuza sangapeze mayankho a mafunso ngati amenewa. (Mlal. 8:16, 17) Koma tikamakhulupirira kwambiri Yehova, tidzavomereza kuti zinthu zina sitingazimvetse patokha. Chofunika n’choti tisanasankhe zochita tizifufuza kaye, tizifunsa ena kuti atithandize komanso tizipemphera kwa Yehova. Kenako tiyenera kutsatira malangizo a Yehova. (Werengani Mlaliki 11:4-6.) Tikatero Yehova angadalitse zimene tasankha kapenanso angatithandize kuti tidziwe zoyenera kuchita.—Miy. 16:3, 9.

YESETSANI KUKHALA ODZICHEPETSA KWAMBIRI

15. Kodi kuganizira za Yehova kungatithandize bwanji kukhala odzichepetsa?

15 Pofika pano taona kuti kudzichepetsa n’kofunika kwabasi. Ndiye kodi tingatani kuti tikhale odzichepetsa kwambiri? Tiyeni tikambirane mfundo 4. Choyamba, tiziganizira kwambiri za Yehova chifukwa zingatithandize kuzindikira kuti iye ndi wapamwamba kwambiri kuposa ifeyo. (Yes. 8:13) Tisaiwale kuti tikuyenda ndi Mulungu Wamphamvuyonse osati mngelo kapena munthu. Kukumbukira mfundo imeneyi kungatithandize kuti ‘tizidzichepetsa pansi pa dzanja lake lamphamvu.’—1 Pet. 5:6.

16. Kodi kuganizira chikondi cha Yehova kungatithandize bwanji kukhala odzichepetsa?

16 Chachiwiri, tiyenera kuganizira chikondi cha Yehova. Mtumwi Paulo anayerekezera mpingo ndi thupi ndipo ananena kuti Yehova amachititsa kuti chiwalo chilichonse chikhale chofunika kwambiri. (1 Akor. 12:23, 24) Izi zikusonyeza kuti Yehova amasamalira munthu aliyense ngakhale kuti timalephera kuchita zinthu zina. Iye samatiyerekezera ndi anthu ena ndipo tikalakwitsa zinazake sasiya kutikonda. Popeza timadziwa kuti Yehova amatikonda, timaona kuti ndife otetezeka m’gulu lake.

17. Kodi kuganizira zimene ena amachita bwino kungatithandize bwanji?

17 Chachitatu, tiyenera kuganizira kwambiri zimene ena amachita bwino. M’malo mofuna kuti anthu azimvera ifeyo nthawi zonse, tizifunsa maganizo awo kapena kutsatira zimene ena anena. (Miy. 13:10) Abale athu akapatsidwa udindo tizisangalala nawo. Komanso tizitamanda Yehova poona kuti akudalitsa ‘gulu lonse la abale m’dzikoli.’—1 Pet. 5:9.

18. Kodi tingaphunzitse bwanji chikumbumtima chathu kuti chiziyendera maganizo a Yehova?

18 Chinthu cha 4 chimene chingatithandize kukhala odzichepetsa kwambiri ndi kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pophunzitsa chikumbumtima chathu. Tikamaona zinthu mmene Mulungu amazionera, timakhala anthu ozindikira. Chikumbumtima chathu chikhoza kumagwira bwino ntchito ngati timakonda kupemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kutsatira zimene tikuphunzirazo. (1 Tim. 1:5) Tikamachita zimenezi timaphunziranso kuika patsogolo zofuna za anzathu. Ndiyeno ifeyo tikachita mbali yathu, Yehova ‘adzamalizitsa kutiphuzitsa’ kuti tikhale ndi makhalidwe abwino monga kudzichepetsa.—1 Pet. 5:10.

19. N’chiyani chingatithandize kukhala odzichepetsa mpaka kalekale?

19 Kudzikuza kamodzi kokha kunasokoneza ubwenzi wa mneneri wa ku Yuda uja ndi Yehova. Kunachititsanso kuti mneneriyu aphedwe. Koma taona kuti n’zotheka ndithu kukhala odzichepetsa. Tili ndi zitsanzo za atumiki a Yehova okhulupirika akale komanso a masiku ano amene asonyeza kudzichepetsa. Ngati tayenda ndi Yehova kwa nthawi yaitali tiyenera kukhalanso odzichepetsa kwambiri. (Miy. 8:13) Kaya panopa tikuchita zotani m’gulu la Yehova, tizikumbukira kuti kuyenda naye ndi mwayi wamtengo wapatali. Tiyeni tisalole chilichonse kutilepheretsa kuyenda modzichepetsa ndi Yehova mpaka kalekale.