Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) February 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa April 2 mpaka 29, 2018.

Tizikhala Okhulupirika Komanso Omvera Ngati Nowa, Danieli ndi Yobu

Anthu okhulupirikawa anakumana ndi mavuto ngati amene timakumana nawo. Kodi n’chiyani chinawathandiza kukhalabe okhulupirika?

Kodi Mumadziwa Yehova Ngati Mmene Nowa, Danieli ndi Yobu Ankamudziwira?

Kodi anthu amenewa anadziwa bwanji Wamphamvuyonse? Kodi kudziwa Mulungu kunawathandiza bwanji? Nanga tingatsanzire bwanji chikhulupiriro chawo?

MBIRI YA MOYO WANGA

Zinthu Zonse N’zotheka ndi Yehova

Mawu ochepa amene mayi wina anamva m’basi anathandiza kuti moyo wa banja lake usinthiretu.

Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauza Chiyani?

Baibulo limafotokoza kusiyana pakati pa munthu wauzimu ndi munthu wakuthupi

Pitirizani Kukula Mwauzimu

Kungophunzira Baibulo si kokwanira kuti tikhale auzimu. Kodi chimafunikanso n’chiyani?

Chimwemwe Ndi Khalidwe Limene Mulungu Amapereka

Kodi mungatani ngati mavuto amene mukukumana nawo pa moyo wanu akukulepheretsani kukhala achimwemwe?

KALE LATHU

Nkhani za Onse Zinathandiza Kufalitsa Uthenga Wabwino ku Ireland

N’chiyani chinathandiza C. T. Russell kuona kuti “m’munda mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola”?