Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  February 2016

Tsanzirani Anthu Amene Anali pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova

Tsanzirani Anthu Amene Anali pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova

“Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa.”—Sal. 25:14.

NYIMBO: 106, 118

1-3. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti tikhoza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu? (b) Kodi m’nkhaniyi tikambirana zitsanzo za anthu ati?

BAIBULO limasonyeza kuti Abulahamu anali bwenzi la Mulungu. (2 Mbiri 20:7; Yes. 41:8; Yak. 2:23) Ndipotu m’Baibulo ndi Abulahamu yekha amene amatchedwa bwenzi la Mulungu. Koma kodi izi zikutanthauza kuti Abulahamu yekha ndi amene anali bwenzi la Yehova? Ayi. Baibulo limasonyeza kuti tonsefe tikhoza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.

2 M’Mawu a Mulungu muli nkhani zambiri zokhudza amuna ndi akazi amene ankakhulupirira kwambiri Yehova. (Werengani Salimo 25:14.) Mtumwi Paulo analemba kuti anthu amenewa ali m’gulu la “mtambo wa mboni waukulu.” (Aheb. 12:1) Anthu onsewa anali ndi makhalidwe abwino osiyanasiyana ndipo anali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.

3 M’nkhaniyi tikambirana za (1) Rute yemwe anali mkazi wamasiye wa ku Moabu, (2) Hezekiya amene anali mfumu ya Yuda ndiponso (3) Mariya yemwe anali mayi ake a Yesu. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene anthuwa anachita kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu?

 ANASONYEZA CHIKONDI KOMANSO KUKHULUPIRIKA

4, 5. (a) Kodi Rute anafunika kusankha zochita pa nkhani iti? (b) N’chifukwa chiyani zinali zovuta kusankha pa nkhaniyi? (Onani chithunzi patsamba 13.)

4 Yerekezani kuti mukuona Naomi ali m’chigwa cha Mowabu pa ulendo wopita kwawo ku Isiraeli. Pa ulendowu ali limodzi ndi apongozi ake awiri, Rute ndi Olipa. Kenako Olipa akutembenuka n’kuyamba kubwerera kwawo ku Mowabu. Rute nayenso ndi wa ku Mowabu ndipo akufunika kusankha kumene angapite. Kodi asankha kubwerera kwawo, kapena apita ku Betelehemu limodzi ndi apongozi ake?—Rute 1:1-8, 14.

5 Makolo komanso achibale ake a Rute ankakhala ku Mowabu. Choncho iye akanaona kuti ndi bwino kubwerera kwawoko kuti achibale ake azikamusamalira. Komanso ankadziwa bwino anthu a ku Mowabu ndiponso chikhalidwe ndi chilankhulo chawo. Koma akanapita ku Betelehemu zonse zikanakhala zachilendo. Naomi ankaonanso kuti Rute akapita ku Betelehemu sakapeza mwamuna wokhala naye pa banja. Choncho anauza Rute kuti abwerere ku Mowabu. Ndiye kodi Rute anatani? Iye anasankha mosiyana ndi Olipa. Paja Olipa anabwerera “kwa anthu a kwawo ndi kwa milungu yake.” (Rute 1:9-15) Koma Rute sanafune kubwerera kwawo kuti akayambirenso kulambira milungu yonyenga.

6. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Rute anasankha bwino? (b) Kodi Boazi ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti Rute anathawira m’mapiko a Yehova?

6 N’kutheka kuti Rute anaphunzira za Yehova kuchokera kwa apongozi ake a Naomi kapena kwa malemu mwamuna wake. Anaphunzira kuti Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi milungu ya ku Mowabu. Ndiyeno anayamba kukonda Yehova ndipo anazindikira kuti ndiye Mulungu woyenera kumulambira. Choncho Rute anauza apongozi ake kuti: “Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Izi zikusonyeza kuti Rute ankakonda Naomi komanso ankakonda kwambiri Yehova. N’chifukwa chake pa nthawi ina Boazi anamuyamikira kuti zimene anachita zinali ngati anathawira m’mapiko a Yehova kuti amuteteze. (Werengani Rute 2:12.) Mawu a Boaziwa akutikumbutsa za kamwana ka mbalame kamene kamabisala m’mapiko a mayi ake kuti katetezeke. (Sal. 36:7; 91:1-4) Choncho mawuwa akusonyeza kuti Yehova anateteza Rute ndiponso kumudalitsa. Ndipotu Rute sananong’oneze bondo chifukwa cha zimene anasankhazi.

7. Kodi n’chiyani chingathandize anthu amene akuzengereza kudzipereka kwa Yehova?

7 Pali anthu ambiri amene anaphunzira za Yehova koma sanasankhebe kudzipereka kwa iye ndiponso kubatizidwa. Ngati inuyo muli m’gulu la anthu amenewa, dzifunseni kuti, ‘N’chifukwa chiyani ndikuzengereza kudzipereka kwa Yehova?’ Dziwani kuti ngati munthu sakutumikira Yehova ndiye kuti akutumikira mulungu winawake. (Yos. 24:15) Choncho ndi bwino kusankha kutumikira Yehova yemwe ndi Mulungu woona. Mukadzipereka kwa Yehova mumasonyeza kuti mukumukhulupirira kuti angakutetezeni. Iye adzakuthandizani kuti mupitirize kumutumikira ngakhale pamene mukukumana ndi mavuto ngati mmene anachitira ndi Rute.

ANKAMVERA YEHOVA NGAKHALE KUTI BAMBO AKE ANKACHITA ZOIPA

8. Kodi Hezekiya anaona zotani ali mwana?

8 Mosiyana ndi Rute, Hezekiya anabadwira mu mtundu wa Aisiraeli omwe anadzipereka kwa Yehova. Koma si Aisiraeli onse amene ankamvera Mulungu. Mwachitsanzo Ahazi, yemwe anali bambo ake a Hezekiya, anali mfumu  yoipa kwambiri. Iye anachititsa kuti anthu a ku Yuda ayambe kulambira mafano ndipo sankalemekeza kachisi wa Yehova wa ku Yerusalemu. Ahazi anafika mpaka powotcha ana ake ena ali moyo n’kuwapereka nsembe kwa mulungu wonyenga. Choncho Hezekiya ali mwana, ankaona bambo ake akuchita zinthu zambiri zoipa.—2 Maf. 16:2-4, 10-17; 2 Mbiri 28:1-3.

9, 10. (a) N’chiyani chikanachititsa kuti Hezekiya akwiyire Yehova? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukwiyira Yehova? (c) Kodi munthu amene anakulira m’banja loipa sangakhale wabwino? Fotokozani.

9 Zinthu zoipa zimene Hezekiya anaona bambo ake akuchita, zikanamukhumudwitsa kwambiri moti akanatha kukwiyira Yehova. Masiku ano, anthu ena amene anakumanapo ndi mavuto amaona kuti ali ndi zifukwa zomveka zoti ‘azikwiyira Yehova’ kapena gulu lake. (Miy. 19:3) Amachita zimenezi ngakhale kuti mavuto awo sakhala aakulu ngati a Hezekiya. Enanso amachita zinthu zoipa poganiza kuti sangachitire mwina chifukwa anakulira m’banja limene munkachitika zinthu zoipa. (Ezek. 18:2, 3) Koma kodi zimenezi ndi zoona?

10 Chitsanzo cha Hezekiya chimasonyeza kuti zimenezi si zoona. Palibe chifukwa chomveka chotichititsa kukwiyira Yehova popeza iye si amene amachititsa zinthu zoipa zimene timakumana nazo. (Yobu 34:10) N’zoona kuti zochita za makolo, zikhoza kuchititsa kuti ana awo azichita zabwino kapena zoipa. (Miy. 22:6; Akol. 3:21) Koma izi sizikutanthauza kuti munthu amene anakulira m’banja limene munkachitika zinthu zoipa sangakhale wabwino. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anatipatsa ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa. (Deut. 30:19) Kodi Hezekiya anagwiritsa ntchito bwanji ufulu umenewu?

Pali achinyamata ambiri amene anasankha kutumikira Mulungu ngakhale kuti makolo awo sakonda Yehova (Onani ndime 9 ndi 10)

11. N’chiyani chinachititsa kuti Hezekiya akhale mfumu yabwino kwambiri?

11 Ngakhale kuti Hezekiya anali mwana wa mfumu yoipa kwambiri, atakula anakhala mfumu yabwino. (Werengani 2 Mafumu 18:5, 6.) Iye anasankha kutsatira chitsanzo cha anthu abwino osati cha bambo ake. Ankatsanzira chitsanzo cha anthu monga Yesaya, Mika ndi Hoseya omwe anali aneneri a Yehova. Hezekiya ankamvera zimene aneneriwo ankanena ndipo zinamuthandiza kuti akonze zinthu  zoipa zimene bambo ake analakwitsa. Anayeretsa kachisi, kuchotsa mafano m’dziko lonse ndiponso kupempha Yehova kuti akhululukire anthu machimo awo. (2 Mbiri 29:1-11, 18-24; 31:1) Pamene Senakeribu mfumu ya Asuri anaopseza kuti aukira mzinda wa Yerusalemu, Hezekiya anachita zinthu molimba mtima ndipo anasonyeza kuti ankakhulupirira Yehova. Iye anadalira Yehova ndipo analimbikitsa anthu ake kuchita chimodzimodzi. (2 Mbiri 32:7, 8) Pa nthawi ina, Hezekiya anayamba mtima wodzikuza koma Yehova atamudzudzula, anadzichepetsa n’kusintha. (2 Mbiri 32:24-26) Iye ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe chifukwa sanalole kuti chitsanzo choipa cha bambo ake chimulepheretse kukhala munthu wabwino. M’malomwake anachita zinthu zimene zinamuthandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

12. Mofanana ndi Hezekiya, kodi anthu ambiri masiku ano asankha kuchita chiyani?

12 Anthu ambiri m’dzikoli ndi ankhanza ndipo alibe chikondi. Choncho ana ambiri amakula popanda makolo owakonda komanso kuwasamalira. (2 Tim. 3:1-5) Palinso Akhristu ambiri amene anakulira m’mabanja oterewa. Komabe anasankha kutumikira Yehova ndipo ali naye pa ubwenzi wolimba. Mofanana ndi Hezekiya, iwo amasonyeza kuti munthu amene anakulira m’banja limene munkachitika zinthu zoipa akhoza kukhala wabwino. Paja Mulungu anatipatsa ufulu wosankha zochita. Choncho tingagwiritse ntchito ufuluwu n’kusankha kumutumikira ndiponso kumulemekeza ngati mmene Hezekiya anachitira.

“NDINETU KAPOLO WA YEHOVA”

13, 14. (a) Kodi n’kutheka kuti Mariya ankadera nkhawa zinthu ziti Gabirieli atamuuza kuti adzabereka Mwana wa Mulungu? (b) Kodi Mariya anamuyankha bwanji Gabirieli?

13 Patapita zaka zambiri kuchokera m’nthawi ya Hezekiya, panalinso mtsikana wina wa ku Nazareti amene anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo anapatsidwa ntchito yapadera. Mtsikanayu anali Mariya mwana wa Heli. Iye anali wodzichepetsa kwambiri ndipo anapatsidwa ntchito yoti adzabereke ndi kulera Mwana wa Mulungu. Yehova ayenera kuti ankakonda kwambiri Mariya ndipo ankakhulupirira kuti angagwire bwino ntchitoyi. Koma kodi mukuganiza kuti Mariya anamva bwanji atapatsidwa ntchito imeneyi?

“Ndinetu kapolo wa Yehova” (Onani ndime 13 ndi 14)

14 Nthawi zambiri timangoganizira za mwayi waukulu umene Mariya anapatsidwawu, koma sitiganizira nkhawa zimene mwina anali nazo atapatsidwa ntchitoyi. Mwachitsanzo, mngelo Gabirieli anamuuza kuti adzakhala ndi pakati ngakhale kuti sanagone ndi mwamuna aliyense. Gabirieli sananene kuti auza achibale ndiponso anzake a Mariya zimene zichititse kuti Mariyayo akhale ndi pakati. Choncho mwina Mariya ankadera nkhawa zimene anthu angaganize akamva kuti ndi woyembekezera. Ayeneranso kuti ankadera nkhawa kwambiri  kuti amuuza bwanji Yosefe, yemwe anali naye pa chibwenzi. Kodi akanamufotokozera bwanji kuti akhulupirire zoti sanachite zosayenera? Komanso, kodi mukuganiza kuti Mariya ankamva bwanji akaganizira udindo waukulu womwe anali nawo wolera Mwana wa Mulungu? Sitingadziwe nkhawa zonse zimene Mariya anali nazo atamva nkhaniyi. Komabe chimene tikudziwa n’choti anayankha Gabirieli kuti: “Ndinetu kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.”—Luka 1:26-38.

15. N’chiyani chikusonyeza kuti Mariya anali ndi chikhulupiriro cholimba?

15 Zikuonekeratu kuti Mariya anali ndi chikhulupiriro cholimba. Anali wokonzeka kuchita chilichonse chimene Mulungu akufuna monga kapolo wake. Iye ankakhulupirira kuti Mulungu amusamalira ndiponso kumuteteza. Koma kodi zinatheka bwanji kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba chonchi? Munthu sabadwa ali kale ndi chikhulupiriro. Koma amakhala nacho akamachita khama komanso chifukwa chodalitsidwa ndi Mulungu. (Agal. 5:22; Aef. 2:8) Kodi Mariya ankachita zotani kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba? Tiyeni tione.

16. N’chiyani chikusonyeza kuti Mariya ankamvetsera kwambiri anthu ena akamalankhula?

16 Mariya ankamvetsera kwambiri anthu ena akamalankhula. Baibulo limati tizikhala ‘ofulumira kumva ndiponso odekha polankhula.’ (Yak. 1:19) Mariya ankachita zimenezi chifukwa Baibulo limasonyeza kuti ankamvetsera kwambiri, makamaka zinthu zokhudza Yehova. Kenako ankaganizira kwambiri zimene wamvazo. Mwachitsanzo, pa nthawi yakubadwa kwa Yesu, abusa anauza Mariya uthenga wochokera kwa angelo. Komanso Yesu ali ndi zaka 12, ananena mawu enaake okhudza Mulungu. Mariya anamvetsera mosamala mawu onsewa, kuwaganizira komanso ankawakumbukirabe.—Werengani Luka 2:16-19, 49, 51.

17. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mariya ankalankhula?

17 Zimene Mariya ankalankhula. M’Baibulo muli mawu ochepa chabe amene Mariya analankhula, moti mawu ake aatali amapezeka pa Luka 1:46-55. Zimene analankhula palembali zimasonyeza kuti ankadziwa bwino Mawu a Mulungu. Zambiri zimene ananena zikufanana ndi zimene Hana, yemwe anali mayi ake a Samueli, ananena m’pemphero. (1 Sam. 2:1-10) Zikuoneka kuti m’mavesi amenewa, Mariya anatchula mawu a m’malemba pafupifupi 20. Izi zikusonyeza kuti Mariya ankakonda kwambiri kulankhula mfundo zimene anaphunzira kwa Mulungu ndipo anali naye pa ubwenzi wolimba.

18. Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Mariya?

18 Nthawi zina nafenso Yehova angatipatse ntchito yooneka ngati yovuta. Zikatere tizitsatira chitsanzo cha Mariya. Tiyenera kulandira ntchitoyo modzichepetsa n’kukhulupirira kuti Yehova atithandiza kuti tiigwire bwino. Tingatsanzirenso Mariya tikamamvetsera zimene ena akunena zokhudza Yehova, tikamaganizira kwambiri zimene tamvazo ndiponso tikamauza ena mfundo za m’Baibulo zomwe taphunzira.—Sal. 77:11, 12; Luka 8:18; Aroma 10:15.

19. Kodi tidzapeza madalitso otani tikamatsanzira chikhulupiriro cha anthu akale?

19 M’nkhaniyi taona kuti Rute, Hezekiya ndiponso Mariya anali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu ngati mmene zinalili ndi Abulahamu. Koma palinso anthu ena ambiri amene anali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Tiyeni tiziyesetsa kutsanzira chikhulupiriro cha anthu onsewa. (Aheb. 6:11, 12) Tikamachita zimenezi, tikhoza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova mpaka kalekale.