“Chitani zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.”—1 PET. 5:7.

NYIMBO: 60, 23

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa tikaona kuti zinthu zodetsa nkhawa zikuchuluka? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

TIKUKHALA m’nthawi yovuta ndipo zinthu zodetsa nkhawa ndi zambiri. Satana Mdyerekezi ndi wokwiya kwambiri ndipo “akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Pet. 5:8; Chiv. 12:17) Choncho n’zosadabwitsa kuti ngakhale atumiki a Yehovafe nthawi zina timakhala ndi nkhawa. Ndipotu atumiki a Yehova akale monga Mfumu Davide nthawi zina ‘ankalimbana ndi masautso.’ (Sal. 13:2) Tisaiwalenso kuti mtumwi Paulo ‘ankadera nkhawa mipingo yonse.’ (2 Akor. 11:28) Ndiye kodi tingatani ngati tikuda nkhawa kwambiri ndi zinazake?

2 Atate wathu wakumwamba anathandiza atumiki ake m’mbuyomo kuti achepetse nkhawa ndipo angatithandizenso ifeyo. Paja Baibulo limati: ‘Mutulireni nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ (1 Pet. 5:7) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyeni tikambirane zinthu 4. Tizipemphera kuchokera mumtima, tiziwerenga Mawu a Mulungu ndiponso kuwasinkhasinkha, tizipempha mzimu  wa Mulungu komanso tizifotokozera munthu amene angatithandize. Tikamakambirana njira zimenezi, yesani kuona zimene inuyo mungachite kuti musamade nkhawa kwambiri.

“UMUTULIRE YEHOVA NKHAWA ZAKO”

3. Kodi ‘tingatulire bwanji Yehova nkhawa zathu’?

3 Chinthu choyamba chimene tingachite kuti titulire Yehova nkhawa zathu, ndi kupemphera kwa iye mochokera pansi pamtima. Tikakhala ndi nkhawa tiyenera kufotokozera Atate wathu wakumwamba. Davide anachonderera Yehova kuti: “Inu Mulungu, mvetserani pemphero langa.” Mu Salimo lomweli ananenanso kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.” (Sal. 55:1, 22) Mukakhala ndi malingaliro osautsa, n’kuchita zonse zomwe mungathe polimbana ndi vuto lanu, pemphero lochokera pansi pamtima lingakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri. (Sal. 94:18, 19) Koma kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji?

4. Tikakhala ndi nkhawa, kodi pemphero lingatithandize bwanji?

4 Werengani Afilipi 4:6, 7Yehova angayankhe pemphero lathu lochonderera komanso lochokera pansi pamtima. Koma kodi angayankhe bwanji? Angatipatse mtendere wamumtima umene ungatithandize kuti tisiye kuda nkhawa kwambiri. Anthu ambiri angavomereze kuti zoterezi zinawachitikirapo. Pamene anali ndi nkhawa komanso mantha Yehova anawathandiza kukhala ndi mtendere wamumtima umene umaposa kuganiza mozama kulikonse. Zoterezi zikhoza kukuchitikiraninso inuyo. Ngati muli ndi vuto linalake, “mtendere wa Mulungu” ungakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri. Muzikhulupirira lonjezo la Yehova lakuti: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”—Yes. 41:10.

MAWU A MULUNGU ANGATITHANDIZE KUPEZA MTENDERE WAMUMTIMA

5. Kodi Mawu a Mulungu angatithandize bwanji kukhala ndi mtendere wamumtima?

5 Chinthu chachiwiri chimene chingatithandize kuti tikhale ndi mtendere wamumtima, ndi kuwerenga Baibulo komanso kusinkhasinkha. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kothandiza? M’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kupewa nkhawa kapena kudziwa zoyenera kuchita tikhala ndi nkhawazo. Musaiwale kuti Baibulo ndi lothandiza chifukwa mfundo zake ndi zochokera kwa Mulungu. Mukhoza kulimbikitsidwa kwambiri mukamaliwerenga tsiku ndi tsiku n’kumaganizira zimene mungachite potsatira mfundo zake. Ndipotu Yehova ananena kuti munthu akamawerenga Mawu ake amakhala ‘wolimba mtima, amachita zinthu mwamphamvu ndipo sachita mantha.’—Yos. 1:7-9.

6. Kodi zimene Yesu anaphunzitsa zingatithandize bwanji?

6 M’Baibulo timapezamonso mawu olimbikitsa a Yesu. Zimene ankaphunzitsa komanso kulankhula zinkathandiza kwambiri anthu amene ankamumvetsera. Anthu ambiri ankapita kwa iye chifukwa ankawalimbikitsa komanso kuwatonthoza. (Werengani Mateyu 11:28-30.) Yesu anasonyeza kuti ankaganiziranso anthu ena. (Maliko 6:30-32) Mawu ake a pa Mateyu 11:28-30 akugwiranso ntchito kwa ifeyo. Ngakhale kuti Yesu salinso padzikoli, angatitsitsimule ngati mmene anachitira ndi atumwi ake. Tikutero chifukwa choti iye ndi Mfumu kumwamba ndipo akupitirizabe kutisonyeza chifundo. Angatithandize “pa nthawi imene tikufunika thandizo” chifukwa cha nkhawa. Choncho tingati Yesu amatithandiza kuti tikhale olimba mtima, tikhale ndi chiyembekezo komanso tizidziwa zochita tikakhala ndi nkhawa.—Aheb. 2:17, 18; 4:16.

 MAKHALIDWE AMENE MZIMU WA MULUNGU UMATULUTSA

7. Kodi Yehova amatani tikamupempha mzimu woyera?

7 Yesu ananena kuti Atate wathu wakumwamba adzapereka mzimu woyera kwa anthu amene amamupempha. (Luka 11:10-13) Choncho chinthu chachitatu chimene chingatithandize tikakhala ndi nkhawa, ndi mzimu woyera. Mzimuwu umatithandiza kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu ali nawo. (Werengani Agalatiya 5:22, 23; Akol. 3:10) Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa, timagwirizana kwambiri ndi anzathu. Izi zimathandiza kuti tipewe zinthu zimene zikanatibweretsera nkhawa. Koma kodi makhalidwewa angatithandize bwanji?

8-12. Kodi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa angatithandize bwanji?

8 “Chikondi, chimwemwe, mtendere.” Tikamayesetsa kulemekeza anzathu timapewa kukhala ndi nkhawa. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikamasonyeza anzathu chikondi ndi ulemu zimathandiza kuti tipewe zinthu zimene zikanayambitsa mikangano komanso nkhawa ndipo timakhala mwamtendere.—Aroma 12:10.

9 “Kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino.” Anthufe timakhala mwamtendere tikamatsatira malangizo akuti: “Khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.” (Aef. 4:32) Tikamachita zimenezi timapewa kukulitsa nkhani ndipo izi zimathandiza kuti tisamakhale ndi nkhawa. Makhalidwe amene tatchulawa amathandizanso tikakumana ndi mavuto chifukwa choti tonse si angwiro.

10 “Chikhulupiriro.” Masiku ano, nkhani zimene zimadetsa nkhawa kwambiri ndi zokhudza ndalama kapena chuma. (Miy. 18:11) Koma munthu amene amakhulupirira kwambiri kuti Yehova adzamusamalira, sada nkhawa ndi zimenezo. N’chifukwa chiyani tikutero? Kutsatira malangizo a Paulo akuti, “mukhale okhutira ndi zimene muli nazo” kumathandiza kuchepetsa nkhawa. Paja Paulo ananenanso kuti: “Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’ Moti tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’”—Aheb. 13:5, 6.

11 “Kufatsa ndi kudziletsa.” Kunena zoona makhalidwe amenewa ndi othandizanso kwambiri. Angatithandize kupewa kulankhula kapena kuchita zinthu zimene zingayambitse nkhawa. Mwachitsanzo, ngati ndife ofatsa komanso odziletsa, tingapewe “kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe.”—Aef. 4:31.

12 Tiyenera kukhala odzichepetsa kuti tizidalira “dzanja lamphamvu la Mulungu” komanso kuti ‘tizimutulira nkhawa zathu zonse.’ (1 Pet. 5:6, 7) Kudzichepetsa kumatithandiza kuzindikira kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse. (Mika 6:8) Choncho m’malo modalira mphamvu ndi nzeru zathu, timadalira Yehova kuti azitithandiza. Ndiyeno tikaona kuti akutithandiza komanso kutikonda, sitida nkhawa kwambiri.

“MUSAMADE NKHAWA”

13. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti, “Musamade nkhawa”?

13 Pa Mateyu 6:34 (werengani), pali malangizo a Yesu akuti: “Musamade nkhawa.” Koma mwina mungaone kuti malangizo amenewa ndi ovuta kuwatsatira. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti ‘tisamade nkhawa’? N’zodziwikiratu kuti sankatanthauza kuti mtumiki wa Mulungu  sangakhale ndi nkhawa. Paja taona kale kuti Davide komanso Paulo anada nkhawa. Choncho apa Yesu ankangothandiza ophunzira ake kuzindikira kuti kuda nkhawa pa zinthu zosafunika kapena kuda nkhawa kwambiri sikuthetsa mavuto. Tsiku lililonse limakhala ndi mavuto ake. Choncho Mkhristu sayenera kuphatikiza nkhawa za tsikulo ndi za dzulo kapenanso za mawa. Ndiye kodi tingatsatire bwanji malangizo a Yesuwa kuti tizichepetsa nkhawa?

14. Kodi mungatani ngati mukudziimba mlandu chifukwa cha zinthu zimene munalakwitsa?

14 Nthawi zina timakhala ndi nkhawa chifukwa cha zimene tinalakwitsa m’mbuyomu. Tingamadziimbebe mlandu chifukwa cha zomwe tinachita mwinanso zaka zambirimbiri zapitazo. Pa nthawi ina Mfumu Davide ankaona kuti ‘zolakwa zake zakwera kupitirira mutu wake.’ Iye anati: “Ndikulira mofuula chifukwa cha kuvutika kwa mtima wanga.” (Sal. 38:3, 4, 8, 18) Ndiye kodi Davide anatani? Iye anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo komanso amukhululukire. Kenako anati: “Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake.”—Werengani Salimo 32:1-3, 5.

15. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuda nkhawa kwambiri ndi mmene zinthu zilili panopa? (b) Kodi mungatani kuti muchepetse nkhawa? (Onani bokosi lakuti, “ Zinthu Zina Zothandiza Kuchepetsa Nkhawa.”)

15 Nthawi zina timada nkhawa chifukwa cha mmene zinthu zilili panopa. Mwachitsanzo, pamene Davide ankalemba Salimo 55 n’kuti akuda nkhawa kuti aphedwa. (Sal. 55:2-5) Komabe sanalole nkhawa zakezo kumulepheretsa kuti azikhulupirira Yehova. M’malomwake anapemphera za nkhaniyo mochokera pansi pa mtima. Koma ankadziwanso kuti ayenera kuchita zinthu zina zimene zingamuthandize kuchepetsa nkhawa zakezo. (2 Sam. 15:30-34) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Davide? M’malo moda nkhawa kwambiri ndi vuto lathu, tizipemphera, kupeza njira zochepetsera nkhawa ndipo kenako tizisiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova.

16. Kodi kuganizira tanthauzo la dzina la Mulungu kungalimbitse bwanji chikhulupiriro chanu?

16 Nthawi zina Akhristufe timada nkhawa chifukwa cha zinthu zimene tikuganiza kuti zidzachitika m’tsogolo. Komabe si bwino kuchita zimenezi. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa si nzeru kumada nkhawa ndi zinthu zimene sitikudziwa bwinobwino kuti zidzayenda bwanji. Komanso nthawi zambiri zinthu zimene timaopa kuti zidzachitika sizichitika n’komwe. Chinanso n’chakuti palibe vuto limene tingakumane nalo loti Mulungu sangathe kutithandiza titamupempha. Paja dzina lake limatanthauza kuti, “Amachititsa Zinthu Kuchitika.” (Eks. 3:14) Tanthauzo la dzina la Mulunguli limatitsimikizira kuti iye amaonetsetsa kuti cholinga chake chokhudza anthu chakwaniritsidwa. Choncho tisamakayikire kuti Mulungu amadalitsa atumiki ake okhulupirika ndipo amawathandiza akakhala ndi nkhawa chifukwa cha zinthu za m’mbuyomu, za panopa komanso za m’tsogolo.

 MUZIFOTOKOZERA MUNTHU AMENE ANGAKUTHANDIZENI

17, 18. Kodi kufotokozera munthu wodalirika mavuto athu kungatithandize bwanji?

17 Chinthu china chimene chingakuthandizeni kuchepetsa nkhawa ndi kufotokozera mavuto anu munthu wodalirika. Mungafotokozere mwamuna kapena mkazi wanu, mnzanu wapamtima kapena mkulu mumpingo. Paja Baibulo limanena kuti: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miy. 12:25) Mukafotokozera mnzanu momasuka, mumayamba kumvetsa zinthu n’kuona zimene mungachite. Baibulo limanenanso kuti: “Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima, koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.”—Miy. 15:22.

18 Yehova amagwiritsanso ntchito misonkhano yampingo potithandiza kuti tisamade nkhawa. Kumisonkhano timakumana ndi abale ndi alongo amene amatikonda komanso ‘timalimbikitsana’ nawo. (Aroma 1:12; Aheb. 10:24) Zimenezi zimatithandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri.

UBWENZI WANU NDI YEHOVA NDI WOFUNIKA KWAMBIRI

19. Kodi inuyo mukuganiza kuti ubwenzi ndi Yehova ungakuthandizeni bwanji?

19 Mkulu wina wa ku Canada anaona kuti kutulira Yehova nkhawa zathu n’kothandiza kwambiri. Mkuluyu ndi mphunzitsi komanso mlangizi ndipo ntchito yakeyi imamupanikiza kwambiri. Kuwonjezera pamenepa iye amadwalanso matenda a nkhawa. Ndiye kodi amathana bwanji ndi mavuto akewa? Iye anati: “Ndinaona kuti kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova n’kumene kumandithandiza kwambiri. Nawonso abale ndi alongo komanso anzanga amandithandiza ndikakhala ndi nkhawa. Ndimafotokozeranso mkazi wanga momasuka zonse zimene zili mumtima mwanga. Akulu anzanga komanso woyang’anira dera anandithandizanso kuti ndiziona zinthu moyenera. Ndinapita kuchipatala ndipo ndili ndi ndandanda yabwino yochitira zinthu. Ndimayesetsanso kupeza nthawi yopuma komanso yochita masewera olimbitsa thupi. Pang’ono ndi pang’ono nkhawa zanga zinayamba kuchepa. Pakakhala vuto loti sindingathane nalo pandekha, ndimangolisiya m’manja mwa Yehova.”

20. (a) Kodi tingatulire bwanji Yehova nkhawa zathu? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

20 M’nkhaniyi takambirana zimene tingachite potulira Yehova nkhawa zathu. Tiyenera kupemphera kwa iye kuchokera mumtima komanso kuwerenga Mawu ake ndi kuwasinkhasinkha. Taonanso kuti makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa angatithandize. Tiyeneranso kufotokozera mnzathu wodalirika mavuto amene akutidetsa nkhawa. Pomaliza taona kuti misonkhano imatithandizanso kuti tichepetse nkhawa. M’nkhani yotsatira tidzaona kuti Yehova amatilimbikitsa potilonjeza kuti adzatipatsa mphoto.—Aheb. 11:6.