Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yohane M’batizi—Chitsanzo Chabwino pa Nkhani Yokhalabe Wosangalala

Yohane M’batizi—Chitsanzo Chabwino pa Nkhani Yokhalabe Wosangalala

KODI pali utumiki wina mumpingo umene mumaulakalaka koma n’zosatheka kuuchita panopa? Mwina ndi udindo umene unaperekedwa kwa munthu wina. Apo ayi, mwina ndi utumiki umene inuyo munkauchita nthawi inayake. Koma panopa simungathe kuchita zambiri chifukwa cha uchikulire, matenda, mavuto azachuma kapena udindo wa m’banja. Mwinanso n’kutheka kuti munasiya kuchita utumiki wina chifukwa cha kusintha kwa zinthu m’gulu la Yehova. Kaya zifukwa zake n’zotani, n’kutheka kuti mumaona kuti simukuchita zonse zimene mumafuna kuchita potumikira Mulungu. N’zosadabwitsa kuti zoterezi zikachitika, nthawi zina munthu amakhumudwa. Koma kodi mungatani kuti musakhumudwe kwambiri, musakwiye kapena kusungira ena zifukwa? Nanga mungatani kuti muzisangalalabe?

Chitsanzo cha Yohane M’batizi chingatithandize kudziwa zoyenera kuchita kuti tizisangalalabe. Yohane ankachita utumiki wapadera kwambiri koma ayenera kuti sankayembekezera zimene zinachitika pa moyo wake. Mwina sankaganiza kuti adzakhala m’ndende nthawi yaitali kuposa imene anachita utumiki wakewo. Ngakhale zinali choncho, Yohane ankakhalabe wosangalala ndipo sanasinthe kwa moyo wake wonse. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza? Nanga tingatani kuti tizikhalabe osangalala pakachitika zinthu zokhumudwitsa?

UTUMIKI WOSANGALATSA

Cha mu April mu 29 C.E., Yohane anayamba utumiki wake wokonzekeretsa anthu kuti alandire Mesiya ndipo ankanena kuti: “Lapani, pakuti ufumu wakumwamba wayandikira.” (Mat. 3:2; Luka 1:12-17) Anthu ambiri anamvera uthenga wake. Magulu a anthu ochokera m’madera osiyanasiyana anabwera kudzamva uthenga wake ndipo ambiri analapa n’kubatizidwa. Yohane anachenjezanso molimba mtima atsogoleri achipembedzo kuti adzaweruzidwa ngati sasintha. (Mat. 3:5-12) Cha mu October mu 29 C.E., utumiki wa Yohane unafika pa chimake pamene anabatiza Yesu. Kungoyambira nthawi imeneyo, Yohane ankauza anthu kuti atsatire Yesu, yemwe anali Mesiya wolonjezedwa.​—Yoh. 1:32-37.

Popeza Yohane anali ndi utumiki wapadera kwambiri, Yesu ananena kuti: “Mwa onse obadwa kwa akazi, sanabadwepo wamkulu woposa Yohane M’batizi.” (Mat. 11:11) N’zosachita kufunsa kuti Yohane anasangalala kwambiri ndi madalitso amene  anapeza. Masiku anonso, anthu ambiri apeza madalitso osaneneka. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Terry. Iye ndi mkazi wake dzina lake Sandra akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 50. M’baleyu anati: “Ndakhala ndi mwayi wochita zinthu zosangalatsa potumikira Yehova. Ndinachita upainiya, ndinatumikira pa Beteli, ndinakhala mpainiya wapadera, woyang’anira dera, woyang’anira chigawo ndipo panopa ndikuchitanso upainiya wapadera.” Timasangalala tikapatsidwa utumiki winawake, koma chitsanzo cha Yohane chikusonyeza kuti tiyenera kuchita khama kuti tizikhalabe osangalala zinthu zikasintha pa moyo wathu.

KHALANIBE NDI MTIMA WOYAMIKIRA

Chinthu chachikulu chimene chinathandiza Yohane kuti azikhalabe wosangalala n’chakuti sanasiye kuyamikira utumiki umene anali nawo. Mwachitsanzo, Yesu atabatizidwa, utumiki wa Yohane unayamba kuchepa pomwe utumiki wa Yesu unayamba kuwonjezereka. Ophunzira a Yohane ataona zimenezi anadandaula ndipo anauza Yohaneyo kuti: “Iyenso [Yesu] akubatiza ndipo anthu onse akupita kwa iye.” (Yoh. 3:26) Yohane anawayankha kuti: “Iye amene ali ndi mkwatibwi ndiye mkwati. Koma mnzake wa mkwati, akaimirira ndi kumvetsera zimene akunena, amakhala n’chimwemwe chochuluka chifukwa cha mawu a mkwatiyo. Choncho chimwemwe changa chasefukiradi.” (Yoh. 3:29) Yohane sankafuna kupikisana ndi Yesu ndipo sanaganize kuti utumiki wake unali wosafunika kwenikweni chifukwa cha udindo waukulu wa Yesu. Koma Yohane anakhalabe wosangalala chifukwa ankaona kuti udindo wake wokhala “mnzake wa mkwati” unali wamtengo wapatali.

Yohane ankasangalalabe chifukwa ankaona zinthu moyenera ngakhale kuti utumiki wake sunali wophweka. Mwachitsanzo, iye anali Mnaziri kuyambira atangobadwa choncho sankayenera kumwa vinyo. (Luka 1:15) Ponena za moyo wa Yohane wodzimana zinthu zambiri, Yesu ananena kuti: “Yohane anabwera ndipo sanali kudya kapena kumwa.” Koma Yesu ndi ophunzira ake sanali Anaziri ndipo ankatha kuchita zinthu ngati anthu ena onse. (Mat. 11:18, 19) Yohane ankadziwanso kuti ophunzira a Yesu, ngakhale ena amene poyamba anali ophunzira ake, ankachita zozizwitsa. Koma iye sanakhalepo ndi mphamvu imeneyi. (Mat. 10:1; Yoh. 10:41) Yohane sanalole kuti zimenezi zimusokoneze koma anapitiriza kuchita mwakhama utumiki umene Yehova anamupatsa.

Ifenso tingakhalebe osangalala tikamaona kuti utumiki umene tikuchita panopa ndi wamtengo wapatali. Terry, amene tamutchula kale uja, anati: “Ndinkaika maganizo anga onse pa utumiki uliwonse umene ndinapatsidwa.” Pofotokoza za utumiki wa nthawi zonse umene wakhala akuchita, iye ananena kuti: “Sindimanong’oneza bondo ngakhale pang’ono. Zimene ndimangokumbukira ndi zinthu zambiri zosangalatsa.”

Tikhoza kusangalala kwambiri potumikira Mulungu tikamaganizira kuti mwayi wokhala “antchito anzake a Mulungu” ndi umene umachititsa kuti utumiki wathu kapena udindo wathu ukhale wamtengo wapatali. (1 Akor. 3:9) Chinthu chamtengo wapatali chimaoneka bwino ngati chikusamaliridwa. Mofanana ndi zimenezi, tikamaganizira kwambiri mwayi wotumikira Mulungu tikhoza kupewa maganizo oipa amene angatilepheretse kukhala osangalala. Tidzapewanso kuyerekezera zimene ifeyo timachita ndi zimene anzathu amachita. Sitidzaganiza kuti utumiki wathu ndi wachabechabe chifukwa choti anthu ena ali ndi maudindo aakulu kuposa athu.​—Agal. 6:4.

MUZIGANIZIRA KWAMBIRI ZINTHU ZOKHUDZA YEHOVA

N’kutheka kuti Yohane ankadziwa kuti utumiki wake udzatha pa nthawi ina koma mwina sankadziwa kuti zimenezi zidzachitika mwadzidzidzi. (Yoh. 3:30) Mu 30 C.E., patangopita miyezi 6 kuchokera pamene anabatiza Yesu, Yohane anamangidwa ndi Mfumu Herode. Koma Yohane ankayesetsabe kuchita zimene angathe pochitira umboni choonadi. (Maliko 6:17-20) Kodi n’chiyani chinamuthandiza kukhalabe wosangalala ngakhale kuti zinthu zinasintha? Iye ankaganizira kwambiri zinthu zokhudza Yehova.

Yohane ali m’ndende anamva anthu akunena kuti utumiki wa Yesu ukuyenda bwino kwambiri. (Mat. 11:2; Luka 7:18) Yohane ankadziwa kuti Yesu ndi Mesiya koma sankadziwa bwinobwino mmene angakwaniritsire zonse zimene Malemba amanena zokhudza  Mesiyayo. Popeza Malembawo ankati Mesiya adzapatsidwa ufumu, mwina ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ayamba kulamulira posachedwa? Kodi mwina zimenezo zithandiza kuti ndimasulidwe?’ Pofuna kumvetsa bwino udindo wa Yesu, Yohane anatuma ophunzira ake awiri kukamufunsa kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?” (Luka 7:19) Ophunzirawo atabwerako, Yohane ayenera kuti ankamvetsera mwachidwi pamene ankanena kuti Yesu ankachita zinthu zodabwitsa. Yesu anauza ophunzirawo kuti akauze Yohane kuti: “Akhungu akuona, olumala akuyenda, akhate akuyeretsedwa, ogontha akumva, akufa akuukitsidwa ndipo aumphawi akumva uthenga wabwino.”​—Luka 7:20-22.

N’zosakayikitsa kuti mawu amenewa analimbikitsa kwambiri Yohane. Anatsimikizira kuti Yesu akukwaniritsa maulosi onena za Mesiya. Ngakhale kuti Yesu sanachititse kuti Yohane amasulidwe kundende, Yohaneyo anadziwa kuti utumiki wake sunapite pachabe. Yohane ankasangalalabe ngakhale kuti zinthu sizinali bwino pa moyo wake.

Kuganizira mmene ntchito yolalikira ikuyendera bwino padziko lonse kungatithandize kukhalabe osangalala

Ifenso tikamaganizira kwambiri zinthu zokhudza Yehova tidzatha kupirira mavuto moleza mtima komanso mosangalala. (Akol. 1:9-11) Chofunika ndi kuwerenga Baibulo ndiponso kusinkhasinkha mfundo zake. Zimenezi zingatithandize kuti tiziona kuti utumiki wathu sudzapita pachabe. (1 Akor. 15:58) Mlongo Sandra ananena kuti: “Kuwerenga chaputala chimodzi cha Baibulo tsiku lililonse kwandithandiza kwambiri kuti ubwenzi wanga ndi Yehova ulimbe. Kwandithandizanso kuti ndiziganizira kwambiri za iyeyo osati za ineyo.” Tingachite bwino kuganiziranso zinthu zabwino zimene zikuchitika pa ntchito yolalikira. Zimenezi zingatithandize kuika maganizo pa zimene Yehova akuchita osati pa zimene zikutichitikira ifeyo. Mlongo Sandra ananenanso kuti: “Pulogalamu ya JW Broadcasting® imatithandiza kwambiri kuti tizimva kuti sitili kutali ndi gulu la Yehova komanso tizisangalalabe ndi utumiki wathu.”

Yohane M’batizi anachita utumiki wake wa nthawi yochepa “ali ndi mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya” ndipo iye analinso ‘munthu ngati ife tomwe.’ (Luka 1:17; Yak. 5:17) Tiyeni tizimutsanzira pa nkhani yoganizira kwambiri zinthu zokhudza Yehova ndiponso kuyamikira utumiki wathu. Tikatero tidzakhalabe osangalala ngakhale zinthu zitasintha pa moyo wathu.