Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Woweruza wa Dziko Lonse Lapansi” Amachita Zachilungamo

“Woweruza wa Dziko Lonse Lapansi” Amachita Zachilungamo

Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama.”​DEUT. 32:4.

NYIMBO: 112, 89

1. Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira zoti Yehova ndi wachilungamo? (Onani chithunzi choyambirira.)

PA NTHAWI ina Abulahamu anafunsa kuti: “Kodi Woweruza wa dziko lonse lapansi sadzachita cholungama?” (Gen. 18:25) Abulahamu anafunsa funsoli chifukwa choti sankakayikira kuti Yehova adzaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora mwachilungamo. Iye ankakhulupirira kuti Yehova sangaphe “munthu wolungama limodzi ndi woipa.” Abulahamu ankaona kuti Mulungu ndi wachilungamo ndipo ‘sangachite zimenezo.’ Patapita zaka 400 Yehova ananena kuti iyeyo ndi “Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”​—Deut. 31:19; 32:4.

2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zosatheka kuti Yehova achite zopanda chilungamo?

2 N’chifukwa chiyani Abulahamu sankakayikira zoti Yehova  amaweruza mwachilungamo? Chifukwa chakuti Yehova ndi wachilungamo kuposa wina aliyense. Izi zikutanthauza kuti mfundo zake ndi zachilungamo ndipo amaweruza moyenera. Ndipotu Baibulo limanena kuti Yehova “amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera.”​—Sal. 33:5.

3. Perekani chitsanzo cha zinthu zina zopanda chilungamo zimene zimachitika m’dzikoli.

3 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amachita zinthu mwachilungamo ndipo sasangalala ndi zinthu zopanda chilungamo zomwe zili ponseponse m’dzikoli. Mwachitsanzo, anthu ena anamangidwapo chifukwa chonamiziridwa kuti anapalamula mlandu ndipo anakhala kundende kwa zaka zambiri. Koma panopa chifukwa choti madokotala amatha kuyeza DNA ya munthu, zinadziwika kuti anthuwa anangonamiziridwa ndipo anatulutsidwa m’ndende. Kunena zoona, zimakhala zowawa kwambiri munthu akatsekeredwa m’ndende pa mlandu woti anangonamiziridwa. Koma Akhristufe nthawi zina tingachitiridwe zinthu zopanda chilungamo zowawa kwambiri kuposa zimenezi.

MUMPINGO

4. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingayese chikhulupiriro chathu?

4 Akhristufe timadziwa kuti tingathe kuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo ndi anthu a m’dzikoli. Koma zimakhala zovuta ngati taona kuti zinthu zopanda chilungamozo watichitira ndi munthu wamumpingo. Ndiye kodi inuyo mungatani zoterezi zitakuchitikirani? Kodi mungakhumudwe kwambiri mpaka kufooka?

5. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa Mkhristu wina akachitiridwa zinthu zopanda chilungamo mumpingo?

5 Paja tonsefe si angwiro ndipo timalakwitsa zinthu zina. Choncho nthawi zina Akhristu anzathu angatichitire zinthu zopanda chilungamo kapenanso ifeyo tingawachitire iwowo. (1 Yoh. 1:8) Ngakhale kuti zoterezi sizichitikachitika, zikachitika siziyenera kutidabwitsa kwambiri. Ubwino wake ndi wakuti Yehova watipatsa malangizo amene angatithandize kuti tikhalebe okhulupirika Akhristu anzathu akatichitira zinthu zopanda chilungamo.​—Sal. 55:12-14.

6, 7. (a) Kodi m’bale wina anakumana ndi zinthu zopanda chilungamo ziti? (b) Kodi ndi makhalidwe ati amene anamuthandiza kuti achite zoyenera?

6 Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Willi Diehl. M’baleyu anayamba kutumikira pa Beteli ya ku Switzerland kuyambira mu 1931 ndipo ankachita utumiki wake mokhulupirika. Mu 1946, analowa kalasi ya nambala 8 ya Sukulu ya Giliyadi ku United States. Atamaliza sukuluyi, anatumizidwa kuti akhale woyang’anira dera ku Switzerland komwe kuja. M’baleyu analemba m’mbiri ya moyo wake kuti: “Mu May 1949 ndinadziwitsa ofesi ya nthambi ya ku Switzerland kuti ndikufuna kukwatira.” Abale anamuyankha kuti sakhalanso ndi udindo uliwonse koma angokhala mpainiya wokhazikika. M’baleyu anati: “Sankandilola kukamba nkhani,. . . komanso abale ambiri ankationa ngati ochotsedwa moti sankatipatsa moni.”

7 Ndiye kodi m’baleyu anatani? Iye anati: “Tinkadziwa kuti kukwatira si tchimo. Choncho tinadalira Yehova ndipo tinkapemphera kwa iye nthawi zonse.” Zonsezi zinkachitika chifukwa choti abale ena anali ndi maganizo olakwika pa nkhani ya ukwati. Koma kenako abale a ku ofesi ya nthambi anathandizidwa kudziwa zolondola pa nkhani ya kukwatira ndipo m’baleyu anapatsidwanso  maudindo ake a poyamba aja. Apatu tingati Yehova anamudalitsa chifukwa cha kukhulupirika kwake. * Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zoterezi zitachitikira ineyo ndingakhalebe wokhulupirika ngati mmene m’baleyu anachitira? Kodi ndingadikire Yehova moleza mtima kapena ndingayambe kupeza njira zanga zothetsera vutolo?’​—Miy. 11:2; werengani Mika 7:7.

8. N’chiyani chingapangitse kuti tiganize molakwika kuti m’bale wina sanachite chilungamo?

8 Nthawi zina tikhoza kuganiza molakwika kuti m’bale wina sanachitire chilungamo ifeyo kapena munthu wina. Izi zikhoza kuchitika chifukwa choti si ife angwiro kapena chifukwa choti sitikudziwa zonse. Koma kaya zimene tikuganizazo ndi zoona kapena ayi, tiyenera kuipempherera nkhaniyo, kudalira Yehova komanso kukhalabe okhulupirika. Izi zingatithandize kuti ‘tisakwiyire Yehova.’—Werengani Miyambo 19:3.

9. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi komanso yotsatira?

9 Tiyeni tsopano tikambirane zitsanzo zitatu za atumiki a Mulungu akale omwe sanachitiridwe chilungamo. Munkhaniyi tikambirana zimene Yosefe anachitiridwa ndi abale ake. Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene Yehova anachitira Mfumu Ahabu komanso zimene zinachitikira mtumwi Petulo ku Antiokeya wa ku Siriya. Tikamakambirana nkhanizi muziona zimene mukuphunzirapo kuti muzichita zoyenera komanso mukhalebe pa ubwenzi ndi Yehova, makamaka ngati mukuona kuti inuyo simunachitiridwe chilungamo.

YOSEFE ANACHITIRIDWA ZINTHU ZOPANDA CHILUNGAMO

10, 11. (a) Fotokozani zinthu zopanda chilungamo zimene zinachitikira Yosefe. (b) Pa nthawi imene Yosefe anali kundende, kodi anali ndi mwayi wochita chiyani?

10 Yosefe anali mtumiki wa Yehova wokhulupirika koma anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Amene anamuchitira si anthu osawadziwa okha, koma azichimwene akenso. Zimene zinachitika ndi zoti, ali ndi zaka 17 azichimwene ake anamugulitsa kuti akakhale kapolo. Anthu amene anamugulawo anapita naye ku Iguputo. (Gen. 37:23-28; 42:21) Ali kumeneko ananamiziridwa kuti amafuna kugwirira mkazi ndipo anaikidwa m’ndende popanda kumuzenga mlandu. (Gen. 39:17-20) Yosefe anakhala kapolo komanso mkaidi kwa zaka 13. Ndiye kodi Akhristu anzathu akatichitira zinthu zopanda chilungamo, tingaphunzire chiyani kwa Yosefe?

11 Yosefe ali m’ndende, woperekera chikho cha Farao anamangidwanso. Usiku wina, woperekera chikhoyo analota maloto ndipo Yehova anathandiza Yosefe kuti amasulire malotowo. Yosefe ananena kuti munthuyo adzamasulidwa n’kukapitiriza ntchito yake. Pa nthawiyi, Yosefe anapezerapo mwayi wofotokozera munthuyo zimene zinamuchitikira. Koma tingaphunzire zambiri pa zimene Yosefe ananena ndi zimene sananene.​—Gen. 40:5-13.

12, 13. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yosefe anayesetsa kuti athane ndi vuto lake? (b) Kodi ndi mfundo ziti zimene Yosefe sanauze woperekera chikho uja?

12 Werengani Genesis 40:14, 15. Pofotokoza zimene zinamuchitikira, Yosefe anati anachita ‘kubedwa.’ Apa zikuonekeratu kuti iye sanachitiridwe chilungamo. Yosefe anafotokozanso kuti sanali wolakwa pa mlandu  umene anamumangira. Choncho anapempha woperekera chikhoyo kuti akafotokozere Farao zimenezi. Iye ankafuna kuti munthuyo amuthandize kuti atuluke m’ndendemo.

13 Monga taonera, Yosefe sanangokhala osachita kalikonse pa mavuto ake. Iye ankadziwa kuti anthu akhala akumuchitira zinthu zopanda chilungamo. Choncho anafotokozera munthuyo zimene zinachitika n’cholinga choti amuthandize. Koma chochititsa chidwi n’chakuti Yosefe sanauze aliyense kuti abale ake ndi amene anamugulitsa. Iye sanauzenso Farao za nkhaniyi moti abale akewo atafika ku Iguputo n’kugwirizananso naye, Farao anawalandira bwino n’kuwauza kuti: “Zabwino za dziko lonse la Iguputo ndi zanu.”​—Gen. 45:16-20.

Zolankhula zathu zingakulitse nkhani n’kufika poipa kwambiri (Onani ndime 14)

14. N’chiyani chingatithandize kuti tisalankhule zoipa ngati wina watichitira zopanda chilungamo?

14 Mkhristu akaona kuti sanachitiridwe chilungamo ayenera kupewa miseche. N’zoona kuti timafunika kupempha thandizo kwa akulu komanso kuwauza ngati munthu wina wachita tchimo lalikulu. (Lev. 5:1) Koma zinthu zambiri zimene anthu amalakwitsa sizikhala machimo aakulu ndipo zimakhala zotheka kuzithetsa popanda kuuza akulu kapena munthu aliyense. (Werengani Mateyu 5:23, 24; 18:15.) Tiyenera kutsatira mfundo za m’Baibulo pothetsa nkhani zoterezi. Nthawi zina tikhoza kuzindikira kuti amene tinalakwitsa ndi ifeyo poganiza kuti munthu wina anatichitira zinthu zopanda chilungamo. Zikatero tikhoza kusangalala kuti sitinaikulitse nkhaniyo poipitsa mbiri ya Mkhristu mnzathu. Tizikumbukira kuti kaya zimene tikuganizazo n’zoona kapena ayi, kulankhula zoipa za munthuyo, kumangowonjezera mavuto. Ngati ndife okhulupirika kwa Yehova komanso abale athu tidzapewa zimenezi.  Paja wamasalimo ananena kuti munthu ‘amene akuyenda mosalakwitsa zinthu sanena miseche ndi lilime lake. Sachitira mnzake choipa, ndipo satonza bwenzi lake lapamtima.’​—Sal. 15:2, 3; Yak. 3:5.

MUZIKUMBUKIRA KUTI CHOFUNIKA KWAMBIRI NDI UBWENZI WANU NDI YEHOVA

15. Kodi Yosefe anadalitsidwa bwanji chifukwa choti anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

15 Pali mfundo ina yofunika kwambiri imene tingaphunzire kwa Yosefe. Pa zaka 13 zimene anazunzika anasonyeza kuti ankaona zinthu mmene Yehova amazionera. (Gen. 45:5-8) Iye sankaimba mlandu Yehova pa mavuto akewo. N’zoona kuti ankakumbukira zoipa zimene anthu anamuchitira, koma sanalole kuti zimuchititse kukhala wokwiya. Chofunika kwambiri n’choti sanalole kuti zochita za anthu ena zisokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. Patapita nthawi, Yehova anathetsa mavuto a Yosefe komanso anamudalitsa iyeyo ndi banja lake. Zonsezi zinatheka chifukwa choti Yosefe anali wokhulupirika.

16. Mkhristu mnzathu akatichitira zinthu zopanda chilungamo, n’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Yehova?

16 Ifenso tiziona kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ndi wofunika kwambiri ndipo tiziuteteza. Tisamalole kuti zochita za ena zitisiyanitse ndi Mulungu wathu amene timamukonda komanso kumulambira. (Aroma 8:38, 39) M’malomwake Akhristu anzathu akatichitira zinthu zopanda chilungamo, tizitsanzira Yosefe. Tizidalira Yehova komanso tiziyesetsa kukhala ndi maganizo ake pa nkhaniyo. Tikachita zonse zimene tingathe mogwirizana ndi Malemba, tizisiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova ndipo tizikhulupirira kuti iye adzakonza zinthu pa nthawi yake komanso m’njira yoyenera.

MUZIKHULUPIRIRA “WOWERUZA WA DZIKO LONSE LAPANSI”

17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yehova, yemwe ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi”?

17 Anthu a m’dzikoli akhoza kutichitira zinthu zambiri zopanda chilungamo. Koma nthawi zina, amene angatichitire zimenezi angakhale Mkhristu mnzathu. Komabe pena tikhoza kungoganiza kuti Mkhristu mnzathu watichitira zopanda chilungamo. Kaya zachitikadi kapena tikungoganiza, tisamalole kuti zinthu zimenezo zitifooketse. (Sal. 119:165) M’malomwake tiziyesetsa kukhalabe okhulupirika komanso tizidalira Yehova ndipo tizipemphera kwa iye. Tizikumbukiranso kuti sitingadziwe zonse zokhudza nkhaniyo ndipo n’kutheka kuti ifeyo tikungolakwitsa kuganiza kuti pachitika zinthu zopanda chilungamo. Chitsanzo cha Yosefe chizitikumbutsa kuti si bwino kulankhula zoipa chifukwa zimenezo zingangochititsa kuti zinthu ziipireipire. Komanso m’malo moyamba kupeza njira zathu zothetsera vutolo, tizikhala okhulupirika n’kumayembekezera Yehova moleza mtima. Tikatero tidzasangalatsa Yehova ndipo adzatidalitsa ngati mmene anachitira ndi Yosefe. Tiyeni tonse tizikhulupirira kuti Yehova, yemwe ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” nthawi zonse amachita chilungamo popeza “njira zake zonse ndi zolungama.”​—Gen. 18:25; Deut. 32:4.

18. Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

18 M’nkhani yotsatira tidzakambirana zitsanzo ziwiri za atumiki a Mulungu akale amene anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Zitsanzo zimenezi zidzatithandiza kuzindikira kuti kudzichepetsa komanso kukhululuka kungatithandize kuti tizitsanzira Yehova pa nkhani ya chilungamo.

^ ndime 7 Kuti mudziwe mbiri ya moyo wa m’baleyu, onani nkhani yakuti, “Yehova Ndiye Mulungu Wanga, Amene Ndim’khulupirira” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1991.